home >>buku
lophunzitsira lotsogolera >>phunziro 5 >>phunziro 6
Buku Lophunzitsira Lotsogolera - Phunziro #6
Ndidzamuona Yesu?
Cholinga cha phunziro
• Kuzindikira kufunika kwa kuuka kwa Yesu
Khristu ndi kumulandira m'moyo
mwathu.
•Kuzindikira Mkristu sangakhale m'moyo wa umulungu mwa mphamvu
kapena
zinthu zake.
• Mwachidule onetserani zidzachitike ku tsogolo.
•Onetserani kufunika kogawana uthenga wabwinondi anzathu.
Pemphero
Wokondedwa Atate ku mwamba, Zikomo potiphunzitsa zambiri za chimene
Yesu ali.
Tiphunzitseni tidziwe za mbiri kuchokera mu Buku Lanu pamene tikuphunzira
phunzirori.
Tikufuna tidziwe ngati tidzamuonadi Yesu. Mu dzina lache, ame.
Fundo zotsogolera
Mudadabwapo, ndidzamuona Yesu? Zimenezo azyankhidwa mu kuwerenga
kwathu kwa mau.
Munthu m'modzi awerenge mayankho onse ku maphunziro athu a
Baibulo a sabata
ndi sabata. Kenaka, iwo ali ndi mayankho osiyana atha kunena.
Kuwerenga Baibulo kwa Sabata:
(Use your Bible or Africa Bible Verse
Handbook) Werengani gawo la baibulo pansipa ndipo mulembe fundo ya tanthauzo
logwira
ntima limene malimva pa kuwerengedwa kulikonse.
Yohane 1:14-18
Yohane 14:1-11
1 Yohane 5:10-12
Mateyu 16:24-27
Afilipi 2:5-11
1 Atesolonika 4:15-18
Yohane 5:24-29
|
Taphunzira mayankho a mafunso ambiri mu phunziro ili. Funso loyamba
ndi kubwereza
zonwe taphunzira.
1 a. Yesu ndi ndani kwa inu? . . . . . |
Ena ayankha ponena ndi Mpulunutsi wawo, ena ati ndi Mulungu, ena
adzamutcha
ndi maina Ache.Gulu liyankha malingana ndi kufunika kwa Khristu m'moyo
wawo ndi
zimene aphunzira pa maphunzirowa.
b. Kodi Yesu anati lamulo lofunikira kwambiri
ndi liti? Mateyu 22:36-40 . . . . . (Konda
Mulungu ndi mtima wako onse.)
|
M'mau ochepa, Yesu watiuza m'mene tingakhalire moyo wa chikhristu.
kukonda Mulungu ndi mtima wathu onse, ndi kukonda wina aliyense.
Pochita izi,
tikumvera zonse zimene malamulo onse a Mulungu.
c. Yesu anachita zinthu zambiri zofunika akanali
pa dziko lapansi. Ntchito yofunikira
kwa mbiri ndi chifukwa chimene anabwerera. Chimnali chani?
Marko 10:45 . . . . . (kupereka moyo
wake chifukwa cha machimo athu kuti tiomboledwe)
|
Kusankha kuti amumvera Iye kapena ayi. Mulungu adadziwa anthu azasankha
kuchimwa
osati ku mvera Iye. Pakudziwa ichi, Mulungu anapangiratu njira yoti
munthu akhululukidwe
ndi kukhalanso pa chiyanjano ndi Iye.
2. Lembani mu magawo awa. sankhani ku mau awa:
mlowa malo |
fuko |
chosatheka |
kufa thupi |
losachima |
kubadwa |
mwa |
namwali |
makumi |
anayi |
Mulungu |
kuikidwa |
m'manda |
kulipira |
kulamulira |
chikhululukiro |
umuyaya |
chitatu |
mtanda |
mwana |
wa nkhosa |
tchimo |
|
|
Dipo (Mulungu) analilamula kuti lichitike pa pa anthu
ochimwa inali (imfa). Nthawi
isanayambe, Mulungu anati osalakwa (olowa m'malo) kufa
m'malo a munthu
ochimwa.Anthu amapereka sembe ya nyama yopanda banga—makamaka
(nkhosa)—akafuna Mulungu kuwakhululukira machimo
awo. Mwazi wa nkhosa
umene anaupereka sunachots (tchimo). Inali chifanizo
cha nsembe yoyera imene
Mulungu anayitumiza. Imaphimba tchimo lawo, kufikira Yesu kubwera
pa dziko
(ndikudzafa) chifukwa cha machimo a dziko lapansi.
Koma kufa, Amayenera kukhala ndi thupi la munthu (thupi),
chifukwa anali
Mulungu, ndipo kunali (kosatheka) kuti Mulungu afe.
Chifukwa chache, anasankha
ndi kukonzekeretsa (fuko) limene anakonzekeretsa
thupi la Iye. (anawapatula) iwo
ku (mafuko) a dziko lapansi ndikuwapatsa malamulo
kuti atsate a kukhala mwa
(chiyero)
Nthawi itakwana, malingana ndi dongosolo Lache, anabwera ku
Dziko ngati
Myuda, (vwobadwa mwa namwali) mwana. Anakhala m'moyo
(wosachimwa)
(anayikidwa m'manda) koma pa tskiku (lachitatu)
Anawuka kwa akufa,
kudzionetsera Yekha anali wa moyo. ataonedwa ndi anthu ambiri
kwa masiku
makumi anayi, Anakwera ku mwamba.
Ngongol (idaperekedwa) younse. Mbali yathu ndi kulandira
(chikhululukiro) cha
Mulungu ndi mphatso ya moyo (wosatha). Ichi chitanthauza
tikulandira imfa ya
Yesu pa mtanda ngati dipo la matchimo athu. Timalola This
means that we accept
Jesus Christ’s death on the cross as payment for our
personal sin debt. Timalola
Mulungu (alamulire) miyoyo yathu. |
Kodi chifukwa chani ndikofunika kuti wina aliyense adziwe zinthu
izi? ndizofunika chifukwa chikhulupiriro chmapanga chikhalidwe.
Chimene timakhulupirira chimapanga chimene timachita ndi m'mene
timachitira. Chifukwa chake ndikofunika kukhala ndi kumvetsetsa
kwa bwino za chimene Yesu ali.
Chikhulupiriro
chimaumba Chikhalidwe.
|
Mochulukira tikudziwa ndi kukhulupirira za chikhalidwe chenicheni
cha Mulungu, mochulukira tidzalingallira za Iye ndipo mochulukira
tidzakhumba kukhala m'moyo wa chiyero, wangwiro ndi omvera.
Mau a Yesus ndi ntchito zache zinaonetsera kuti ndi Messiah. Kubwera
kwake kunaloseredwa zaka zambiri, koma anthu sanakhulupirire.Anayenera
kusankha kukhulupirira kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu-Messia-kapena
kukana kuti sanali chimene amanena kuti anali
Sabata yatha tinakambirana za m'mene tingayambire moyo wa Chikhristu
poitana Yesu
Khristu kuti alowe m'moyo wathu ndikudzipereka kwa Iye.
Kodi alipo amene ali ndi funso pa za moyo wa tsopano mwa Christu?.....Kodi
alipo wina
amene angatiuze za m'mene moyo wake wasinthira kuyambira atakhala
Mkristu?
Ngati tili nawo ena mu gulu amene ali ndi mafunso okhudzana
ndi chipulumutso,
apatseni kabuku koti Mukhulupirira? ndipo werengani pamodzi
ngati simunapange
izi mu phunziro 5.
Tsopano, titha kuyankha funso mu mutu wa phunziro lathu. Kodi Baibulo
limati chani za
zoti tidzomuona kapena sitidzamuona Yeus? yankho lili mu funso lotsatira
mu mabuku
athu ophunzirira.
3. Yesus akabwera msogolo, adzamuone ndani? Chibvumbulutso
1:7 . . . . . (Aliyense, Kuphatikizapo iwo amene
akufuna kudzamuona Iye, kuphatikizapo iwo sakufuna kumuona Iye.) |
Ngati wina angafunse kuti "iwo anamulasa" limathanthauza
chain -
Yohane 19:33-34.
Ofufuza za Baibulo samagwirizana pa za nthawi yeni yeni imene Yesu
adzabwera, poti
masiku ake mu baibulo sanalembedwe. Titha kukhala okonzeka podziwa
kuti zidzachitika
mu nthawi yoikika ndi Mulungu.
Wina aliyense adzamuona. koma ena adzakhala ndi chidwi kumuona
kusiyana ndi wena.
Tonse tidzagwada-ena mumupembedza ena momuopa.
4.Baibulo limati kudzakhala nthawi ya masautso
ndi chizunzo pa dziko la pansi.
Werengani zimene zidzachitike pa dziko Yesu asanabwerenso,
ndipo mulembe
zimene zakupatsani chidwi powerenga izi.
a. Mateyu 24:21-31
b. Marko 13:32-37
c. Luka 21:25-28, 34-36 |
5. Kodi chimachitika n'chiyani munthu akamwalira?
Ahebri 9:27. . . . .(Chiweruzo.)
|
Chofunikira kwambiri kuti tichite tsopano, ndikuonetsetsa kuti
tamulandira Yesu Khristu ngati Yekhayo amene angatipulumutse ku
chilango cha Mulungu pa tchimo. Ngati talandira Khristu, chiweluzo
chikudza ndi chokhacho cha zinthu zimene tinachita. Tione Baibulo
limati chani za ichi.
6. a. 2 Akorinto 5:10 . . . . . (Tonse
timalandira mphoto yotiyenera, malingana ndi m'mene tamutumikirira
Iye.) b. Machitidwe 17:30-31. . . . .
(Khristu, amene anauka kwa akufa, adzaweruza dziko lonse
ndi chilungamo.)
c. Chibvumbulutso 20:11-15 . . . . .
(Ngati dzina la munthu silinalembedwa mu buku la moyo, adzaponyedwa
mu nyanja ya moto.)
Anthu akamakamba za kupulumutsidwa, amakamba za kupulumutsidwa
ku chilango chosatha mu nyanja ya moto.
Tikamawerenga za chimene Mulungu amanena za chiwerezo chache
cha chilungamo, timazindikira kuti kulandira Yesu kumatipulumutsa
ife kuchilango chotiyenera. Tikuyenera kukhala ofuna kudzipereka
mwathunthu kwa Iye. Mitima yathu ikhale yodzala ndi matamando
kwa Iye pa chipulumutso chake chachikulu! |
Kodi ndi ndani amene Mulungu akufuna kupulumutsa? 1 Timoteyo
2:3-4. . . . . (Aliyense)
Mulungu safuna alo munthu m'modzi apite ku gahena.
Iye anapangira gahena
kukhala ya satana ndi amithenga ake.—osati anthun (Mateyu
25:41). Anthu ali
omasuka kusankha Mulungu kapena satana.
|
Werengani Afilipi 2:10-11. . . . . Izi zikutiuza
anthu adzagwada pa maundo awo ndi kubvomereza, "Yesu Khristu
ndi Mbuye." Anthu ambiri sanena kuti Yesu ndi Mbuye panopa,
koma ikudza nthawi yomwe aliyense adzaona chimene Iye ali ndi kubvomereza.
Koma idzakhala nthawi itatha.
Tsiku likubwera limene Yesu adzabweranso pa dziko lapansi! Zonse
zimene anthu
anakundika pa dziko lino zidzaonongedwa. Tsekulani pa 1
Yohane 2:15-17 . . . . . Izi zikutiuza kuti onse amene
ayika chikhulupiriro chao pa zinthu za padziko lino adzazitaya,
poti za padziko zidzapita. Tidzaweluzidwa ndi zimene talora Yesu
kuchita mwa ife ndi kudzera mwa ife.
Tikalandira Yesu timasinthidwa 2 Akolinto 5:17. . . . .
Tikakhala ndi moyo wake mwa ife, timasanthulika. Sitikhalanso akapolo
a tchimo. Yesu amatsimikizira kuti upulumuka kapena ayi, kaya tipatsidwa
mphoto kapena ayi.
Mwa ife wapeza kale chipambano. Tili nayo mphamvu yakukaniza satana.
Mzimu wa
Mulungu mwa ife umafuna tidzimvera Mulungu. Pamene tasankha kuchita
zomwe Mzimu
wa Mulungu akufuna tichite, timakhala m'moyo winanawina. Pali nthawi
zina zimene
timapanga zisankho zolakwika ndi kuchita zomwe tikufuna. M'mawu
ena, timachimwa.
Tikuyenera kukumbukira zomwe tauzidwa kuchita, 1 Yohane
1:8-10 . . . . .
Tikuyenera kubvomereza ndikubwenzeretsa ubale wathu ndi Mulungu.
Tikadalira mwa Yesu, tichite chani? 1 Yohane 4:7-11. . .
. . (lolani chikondi chilamulire zimene timachita ndi
kunena)
Tikalapa, timabwerera kusiya za moyo wakale wosakhala ndi Mulungu
ndi kukhala moyo wosangalatsa Mulungu. Timasankha kumvera Iye. Chimenecho
ndi chifukwa chimodzi chimene timawerengera mawu a Mulungu-kuti
tidziwe zimene Iye amafuna ife kuti tichite.
Khalani mukudziwa
za Umuyaya!
7 a.Kozi zimene maphunzira zikupindura chani pa moyo wanu
wa tsiku ndi tsiku?
2 Akorinto 7:1 . . . . . (Mayankho adzakhala
osiyana ndipo adzakhalanso ndi fundo zochokera apa)
b. Kodi maonedwe anu pa zakukhala ndi zinthu ndi zimene mukulingalira
mutatenga ndi kukhala nazo asintha motani? Mateyu
6:19-21 . . . . . (Ngati mukufuna zamnbiri, werenganinso
1 Yohane 2:16-17.)
c.Kodi zoti Mzimu Woyera akukhala mwa okhulupirira zimathawathandizira
bwanji m'maonedwe awo pa za ziphinjo ndi zokhumudwitsa? Yakobo
1:2-4 .. . . . (Aziziona amwayi akamakumana ndi
mayesero.)
d. Kodi chidziwitso cha dongosolo la Mulungu chikuyenera
kuchita chani pa maonedwe a okhulupirira pa za kugawa uthenga
wabwino kwa wena. 2 Timothy 4:1-5. . . . . (Okhulupirira
akuyenera alalikire Uthenga Wabwino modekha ndi mokakamira
posatengera kuti ena aulandira bwanji)
e. Kodi 1 Akorinto 15:58, amalimbikitsa
bwanji okhulupirira kuti akhale wamachawi mu ntchito ya Mulungu?
. . . . . (Zonse zimene wokhulupirirra amachita mu utumiki
wa Ambuye ndi zantengo wapatali)
|
Ngati Akhristu, tikuyenera kugwiritsa ntchito nthawi yathu pa dziko
lino kuwuza
wena za chipulumutso!
8. Maphunziro a Mau a Mulungu amasintha miyoyo.
Maphunziro awa akusinthani
bwanji myo wanu? ..........(Limbikitsani onse kuti afotokoze
mayankho awo) |
Mnene funsoli layankhidwira lifotokoza za kumvetsetsa kwawo
kwa chipulumutso
ndikuwunikira pamene pakufunika kufotokozera. Gawo linali lithandiza.
Ndife ana a Mulungu tikamulora Yesu kuti atikhululukire machimo
athu ndikutipatsa moyo
wosatha chifukwa cha nsembe Yake kwa ife pa mtanda. Yesu ndi Mpulumutsi
wathu,
Mulungu ndi Tate wathu ndipo Mzimu woyera amakhala mwa ife kutiunikira
nthawi ndi
nthawi.
Ambuye akukonza malo a okhulupirira kuti akakhale mukupezeka kwake
muyaya.
Sikudzakhala tchimo kapena imfa kumeneko, ndipo Baibulo limati mukupezeka
kwake
muli zokoma za muyaya (Masalimo 16:11)!
Kuzindikira malonjezano a Mulungu zimatithandizira kupirira ku
mayeselo, zokhoma, ndi
zofoketsa zimene zimabwera m'moyo uno ndi kutilimbikitsa kuti tikhale
tikulimba mtima
mu nthawi yochepa tilikhale pa dziko lapansili. Okhulupirira akuyembekezera
kudzakhala
muyaya m'malo abwino amene Mulungu anawakonzera.
Tsopano titha kuyankha funso la phunziro lathu, "Ndidzamuona
Yesu?".......(Alileyense adzamuona Yesu ndipo adzabvomereza
ali Ambuye)
Tisanatseke ndi pemphero, alipo amene akufuna kutiuza za pemphero
limene analemba pa funso lachisanu ndi chinayi?
9. Lembani pemphero kufotokozera mathokozo anu
kwa Mulungu potumiza Mwana
Wake, Yesu Khristu. Pazokambirana, mudzakhala ndi kusankha kogawa
pemphero
lanu. Lembani pempher lanu apa.
|
Pemphero Lotsekera
Tate wathu wakumwamba, zikomo chifukwa chobwera pa dziko kudzatifera,
zikomo chifukwa chobwera pa dziko mkudzadzitengera chilango machimo
athu. Zikomo polola kukhala m'moyo wathu. Zikomo chifukwa cha lonjezo
simudzatisiya tokha! Tithandizeni kupereka miyoyo yathu kuti uilamulire.
Malizani zimene mayamba m'moyo wa wina aliyense. Tapemphera mu dzina
la Yesu, Ameni.
|