Project Hope     home >>buku lophunzitsira lotsogolera >>phunziro 2 >>phunziro 3
Buku Lophunzitsira Lotsogolera - Phunziro #3
Women's Empowerment Program
Sports Bible Club
Living Water Bible Club

Yesu Anachita Chani?

Cholinga cha Phunziro

• Zindikirani kukhudza kwa chikhalidwe cha Yesu, chiphunzitso Chake, mphamvu
Yake pa mphamvu za chilengedwe, ndikukhudza Kwake mu mbiri.—zonsezi
zikusonyeza Iye anali Mulungu mwini.
• Zindikirani ntchito ndi mdalitso.
•Zindikirani kufunika kogwira ntchito ndi kupumula.

Pemphero

Wokondedwa Mulungu, Baibulo limatiuza Yesu ndi Mwana Wanu. Limatiuza ali ndi
chikhalidwe ndi chilengedwe cha Inu. Tiphunzitseni tidziwe choonadi cha Yesu pamene
tikuphunzira. Tapemphera mu dzina la Yesu, ame.

Ndemanga zotsogolera

Sabata ino kuwerenga kwathu kwa Baibulo kunali kokhudzana ndi zinthu zimen Yesu
adachita. pakugawana mayankho athu, tiwona kuti anali wochulukidwa.
Werengani Baibulo ndipo mulembe m'mau anu zimene Yesu amachita.


Kuwerenga Baibulo kwa Sabata:

(Use your Bible or Africa Bible Verse Handbook)

Marko 1:16-28, (Yesu adaitana amuna anayi ndi kuyamba utumiki Wake.)

Marko 1:29-39, (Yesu anachilitsa ambiri ndipo analalikira mu Galileya.)

Marko 3:13-19, (Yesu asankha ophunzira khumi ndi awiri.)

Marko 4:35-41, (Yesu ayimitsa namondwe oopya.)

Marko 6:30-44, (Yesu apereka chakudya kwa amuna zikwi zisanu 5,000 . Onani: Mateyu 14:21akuti akazi ndi ana anadya nawo nthawi yomweyo)

Marko 10:2-16, (Yesu anayankha funso ndi kudalitsa ana.)

Yohane 2:13-22, (Yesu ayeretsa kachisi.)

Yesu anayeretsa kachisi kawiri. Gawo limene tinawerenga kunyumba lidali koyamba.
Tsopano werengani chimene anachita pa mamaliziro a utumiki Wake. Tsegulani pa
mu chipangano cha Tsopano Marko 11:15-17 . . . . .

Mu maphunziro athu awiri oyamba., tinaona zimene Baibulo limanena za Yesu, zimene
ananena, zimene anaphunzira. Tiphunzira za chimene Yesu anachita.

Olemba onse a uthenga wabwino sanalembe zonse zimene Yesu anachita. sanalembe
mbiri yake mwandandanda wake. anangolembapo zofunikira zimene anthu amayenera
kudziwa za Yesu.

Marko anali woyamba ku lemba uthenga wabwino wa Yesu. Analembera anthu a ku Roma
kuti akhale ndi mau andi ntchito zowe Yesu anachita. Marko anagwira ntchito ndi Paulo
komanso Barnaba, anthu oyambirira kupereka uthenga ku dziko la Roma. Kenaka, maliko
anagwira ntchito ndi Peturo, komwe anaphunzira zambiri za ziphunzitso ndi machitachita
aYesu. Buku la Marko limatsindika ntchito za Yesu ngati mtumiki wa ngwiro wa Khristu.
Uthenga wa Bwino wa Mateyu unalembedwa kuti ufotokoze za Yesu ngati Mesiya wa
Ayuda. Ayuda anayenera kuona Yesu akukwaniritsa mauneneri a ku Chipangano cha
Kale, akubweranso kwake ngati mfumu. Mateyu anafotokoza momwe dziko linamukanira
UYesu ndi ufumu wake. Buku la mateyu ndi latanthauzo kwa iwo amene amawerenga
Chipangano cha Kale.

Amitundu amayenera kumva za Yesu, Luka analemba kwa Aherena. Anali dotolo wa
Chiherena amene anayenda ndi Paulo. Analemba ndandanda wonse wofunikira umene tili
nawo wa moyo wa Yesu-Uthenga wa Bwino wa Luka. Analemba mosamala, anawerenga
zolemba za atumwi, ndipo anafunsira kwa iwo amene anawona ndi maso. Zimene
analemba za kuima ndi kubadwa kwa Yesu anayenera kuti anafunsira kwa Maria.
Tikukhulupirira izi chifukwa zimene analemba za Maria sizinari zoti zimanenedwa ku gulu.
Mwachitsanzo, mauthenga ena abwino sanafotokoze maganizo a Maria monga m'mene
Luka anachitira. (Luka 1:29, 34; 2:19, 51).

Yohane, m'modzi mwa ophunzira, anatsindika kuti Yesu anali mwana wa Mulungu.
Pachiyambi pa buku lake, Uthenga wa Bwino wa Yohane, Yohane akufotokoza za
uchikhalire wake wa Christu ndi kuti Ndiye wolenga zonse. Akufotokoza kuti Mwana ali ndi
chikhalidwe cha Atate. Akufotokoza monveka bwino Yesu ndi m'modzi ndi Atate. Izi ndi
zovuta kumvetsa koma ma vesi ofunikira anayi a Yohane akutsimikizira Yesu ndi wolenga.
Ma vesiwa akutsimikizira za kuti Yesu ndi Mlengi. Ma vesiwa akuyimira upadeladela wa
Yesu, umodzi Wake ndi Mulungu, Mulungu mu thupi la munthu, ndi Umwana Wake.
werengani Yohane 1:1-3, 14. . . . . Mau ndi Yesu. Chifukwa chake "Mau' ali
muchilembo chachikulu mu Chipangano chanu cha Tsopano.

Yesu amagwira ntchito

1 a. Kodi Yesu anali ndi zaka zingati pamene amayamba utumiki wake?
Luke 3:23 . . . . . (Anali ndi zaka makumi atatu-30.)

b. Anatumiza Yeus kudziko ndani? 1 Yohane 4:9 . . . . . (Mulungu)

 

2 a. Chimene Yesu amanena kuti atate wake amachita ndi chani?
Yohane 5:17. . . . . (Nthawi zonse kugwira ntchito.)

b. Chifukwa cha ichi, ndichani chimene Yesu ananena kuti wayenera?. . . . .
(Akuyeneranso kugwira ntchito.)

3. Nenani mau ochepa zimene mwa izi zili mBaibulo zimavumbulutsa za zimene
Yesu anachita

a. Marko 1:21 . . . . . (Anaphunzitsa anthu.)

b. Marko 1:32-34 . . . . . (Anachiza odwala ndi kutchotsa ziwanda.)

c. Marko 1:35 . . . . . (Anapemphera.)

d. Marko 1:38 . . . . . (Analalikira.)

e. Marko 6:7-12. . . . . (Anatumiza ophunzira kukalalikira.)

Mauthenga Abwino anayi amafotokoza ma mirakuli 34 a Yesu. Pa mapeto pa Uthenga wa
Bwino, Yohane akufoytokoza za pamene panafikira ntchito za Yesu Khristu. Tsekulani
Yohane 21:25. . . . . kuchoka apa, tikuona kuti Chipangano cha Tsopano
sichikulemba za zimene Yesu anachita.

Zozwizwitsa Zache

4. Zozwizwitsa Yesu anachita zinabvumbulutsa mphamvu Zache zimene
zinapatsidwa ndi ulamuliro wa Mulungu pa zinthu zonse:

chikhalidwe,................ imfa, .................ziwanda, ................zozwizwitsa, ...................matenda

Werengani ma mirakuli awa ndipo muzilinganize ndi mau oyenerera mu baibulo.

Mamirakuli mphamvu pa

a. Luka 4:33-36 . . . . . . . . . . . . . . . . . . . (ziwanda)

b. Luka 5:4-10 . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . (chilengedwe)

c. Marko 1:40-42 . . . . . . . . . . . . . . . . . . (matenda)

d. Mateyu 15:1-9 . . . . . . . . . . . . . . . . . (chikhalidwe)

e. Luka 7:11-17 . . . . . . . . . . . . . . . . . . . (imfa)

Think of it! Jesus has power and authority over demons. nature, disease, tradition, and death!

“Mphamvu yache ndiyotani mwa ife okhulupirira. . . .”

—Aefeso 1:19


Yesu akuona khamu likubwera kwa Iye ndi zosowa zawo. Akuwafikira ndi ndi chifundo ndipo akusiya kulankhula nawo. Akuwakonda ndi kuwafikira pamene ali. Sanadzipature pakuwatumikira. Yesu analinawo manja ogwirira ntchito pamene anali pa dziko lino.

Ntchito ya chilungamo, kuchitira anthu, ntchito ya ulemu wapadeladela. Ntchito ikukwezedwa ngati mnyamata, Yesu amagwira ntchito ku Nazareti, kumene amakhala ndi banja lake. Moyo Wake, Mau Ake anali obvomerezeka ndi Mulungu. Werengani Luka 3:21-22. . . . . Mulungu analankhula kuchoka kumwamba, kutsimikizira Christu kukhala Mwana Wake ndipo ananena kuti anali okondwera Naye ndi zonse amachita.

Baibulo limati Yesu anagwira ntchito. Kuwerenga kwathu kwa Baibulo pa sabata likutiuza
zinthu zosiyana zisanu ndi ziwiri zomwe Yesu anachita. Zonse zimene Yesu anachita zitha kungonenedwa ngati m'mene zaperekedwera pa funso 5.

Cholinga cha ntchito

5 a. Ntchito ya Yesu inali chani?
Yohane 6:38 . . . . . (kuchita chifuniro cha Mulungu)

b. Tingadziwe bwanji kuti zimene Yesu amanena zimachoka kwa Mulungu?
Yohane 7:16-17. . . . . (Ngati tili ofuna kuchita chifuniro cha Mulungu, tidziwa kuti zimachokera kwa Mulungu.)

c. Tikangodziwa cholinga cha Mulungu, Amatithanndiza bwanji?
Afilipi 2:13 . . . . . (Mulungu amapanga okhulupirira kukhala ofuna kumvera Iye)


6. Mulungu amapangitsa okhulupirira kukhala moyo wa bwino mu dziko
loyipa. Aroma 12:2 . . . . . (Okhulupirira asamakhale ndi zimene moyo wadziko umaziona kuti nde kukhala) Alole Mulungu kuwasintha po sintha malingaliro awo)


Munthu analengedwa mu chifanizo, ndi kuthekera ko gwira ntchito-kugwiritsa ntchito nzeru, chisankho, maimvaimva, ndi luso. Ntchito ndi yofunika kwa Mulungu. Akunena za mbiri za ntchito mu Baibulo. Kuyambira pa chiyambi cha nthawi, tchimo lisanalowe pa dziko lapansi, Mulugu anapatsa munthu ntchito yoti agwire. Anampatsa munthu nctito kuti ikhale chochita chake pa dziko. ndi chamwayi.

Chifukwa choti Mulungu anapatsa munthu ntchito akadali m'munda wa Edeni chikuonetsera ntchito ndi mdalitso. werengani mu buku lathu lophunzirira. Genesis 1:27-28. . . . .
Ntchito yake inali chani? . . . . . (kudzala dziko lapansi ndi kukhala ndi ulamuliro pa zolengedwa zonse. Munthu analengedwa kukhala mfumu ya dziko.

Amayenera kupanga ntchito ziti? Werengani Genesis 2:15. . . . .Onani mau "kusunga ndi
kusamala" Adamu amayenera kulima ndi kuyang'anira munda wa Edeni.

Koma ntchito inaonongeka ndi kuchepsedwa chifukwa cha tchimo la munthu. Pa tsamba
lomwelo, werengani Genesis 3:17. . . . . Tchimo litalowa mu dziko, Mulungu anati munthu
adzaenera kumva kuwawa kutchoka ku nthaka yotembereredwa kuti akhale ndi moyo.
tchimo lidapangitsa ntchito kukhala chinthu cholemetsa.

Baibulo silikamba za ntchito ngati yoyipa. Ena amaganiza kuti ntchito ndi chinthu choipayoyenera kupewedwa ngati kuli kotheka. Mu buku la Mlaliki mu Chipangano cha Kale
lidalembedwa kusonyeza uchabechabe wa moyo wodalira chuma cha dziko. Ikuti ntchito
yonse ya munthu nja chabe. Izi ndi zoona ngati cholinga cha ntchitoyo chili
chongngokwaniritsira zokhumba zodzikonda za moyo uno.

Pamene tikugwira motsogozedwa ndi Mulungu, Amapitiliza kulenga kudzera mwa ife.
Ntchito zathu zimangopitiliza ntchito ya Mulungu pa chilengedwe. Timatenga zipangizo
zomwe Mulungu analenga ndi kugwiritsa ntchito nzeru zache kuti tizipangire zinthu zatsopano zoti tidzisangalala nazo. Mulungu analenga mitengo, kuchoka ku mitengo timapanga zipangizo zochapila, mapepala, zidz zoyimbira, ndi nyumba. Mulungu analenga magetsi ndipo ife timaphunzira m'mene tingapangire kuti tidziagwiritsa ntchitozootchera mkate, makina a komputa. Pali nzeru imene ife ngati ogwira ntchito ndi Mulungu pakupitiliza ntchito yake yolenga zinthu zimene zimamusangalatsa ndi kupereka tanthauzo ku ntchito imene timagwira.

Ntchito yathu imatipatsa zokhumba za moyo uno. Ntchito imapereka chosowa ku maimvaimva athu. Timapeza chimwemwe popereka zosowa kwa iwo amene timawakonda.

Kudzera mu nthcito akhristu amaphunzira mwambo, kudzidalira, komanso kutumikira wena. Pamene akugwirira ntchito iwo eni ndi mabanja awo, amapeza mwayi ouza ena za Yesu.

Iwo ogwira ntchito ndi Khristu aone kusiyana pa chikhalidwe chawo,
pakudzipereka, ndi kudzilemekeza ndi ulemu umene amapatsa wena. Adzakhala
ozindikira za kuchilimika kwa Chikristu pochita zinthu zangwiro mu chokhumba chawo
kukhala ndi zimene akufuna. osakhulupirira adzazindikira kuti Akhristu ndi apadeladela.


7. Chipangano cha Kale chimatsindika kuti Mulungu amaitana anthu kuti akagwire
ntchito. Kodi baibulo limati chani pa za ntchito?

a. 2 Atesalonika 3:10 . . . . .(Mulungu amayembekezera kuti tigwire ntchito. ngati sitigwira ntchito sitikuyenera kuti tidye)

b. Aroma 12:11. . . . .(Tikuyenera kugwira ntchito ndi kutumikira Mulungu ndi mtima wonse)


Funsani wina awerenge ma vesi awa mu Chipangano cha Tsopano kenaka funsani
wina awerenge ma vesi ndi mau apadela aperekedwa pa funso 8.



8. Lembani ma vesi awa, kulowetsa m'malo “olembedwa ntchito” kwa “akapolo” ndi
“olemba ntchito” kwa “mbuye.” Aefeso 6:5-8 . . . . .

Ngati ndinu wolemba ntchito, mutha kufuna kuwerenga vesi 9.

Tikuyenera kugwira ntchito ngati tikuchitira Mulungu osati anthu. Kodi izi ndizongopanga anthu kapena zikuchokera kwa Ambuye? Funso lotsatira likutipatsa ife yankho.

9. Kodi ma vesi awa amatiuza chani m'mene tikuyenera kugwirira ntchito?

a. 1 Akorinto 10:31 . . . . . (Chitani zonse ku ulemerero wa Ambuye.)

b. 1 Akorinto 16:14 . . . . . (Onetserani chikondi pa zonse mukuchita.)

c. Akolose 3:23 . . . . . (Gwirani ndi mtima wanu onse ngati mukugwirira Ambuye.)

Ngati tipanga zonse ku ulemerero wa Mulungu, ntchito zathu zonse
ziyeretsedwa —
kutanthauza zimapaturidwa ku kugwiritsidwa ntchito ndi Mulungu


Ntchito imene Mulungu akutipatsa ikufunika kuti tikhale owona mtima ndi angwiro. ntchitoyo ikhale yaulemu ndiyochitidwa mobweretsa ulemu wa muyaya kwa Iye.

Ntchito yanu ndi yotani? . . . . . (Lolani wina aliyense ayankhe.)

Kodi ntchito izi tinngazitenge kuti ndi za ukhristu?. . . . . (Lolani wina aliyense afotokoze chifukwa chimene anayankhira m'mene ayankhilamo)

Ntchito inailiyonse itha kukhala ya ukhristu ngati tamulandira Yesu ngati Mpulumutsi ndi Mbuye ndikumulola Iye atsogolere miyoyo yathu.

Kodi anthu angachite chani pa ntchito kapena kwina kuli konse kumene amataya nthawi yao, chimenecho chimavumbulutsa kuti ndi Akhristu? . . . . .

Lolani gulu likambirane ichi. zokambirana ziphatikizidwepo ndi chikhalidwe, ungwiro,
chifundo, kuona mtima, chilankhulo chabwino, ndi zochitika pa moyo wanu.

Kodi Baibulo limati chani za kudziwidwa ndi iwo otizungulira kuti ndife Akhristu. Onani pa
John 13:34-35. . . . .

Chikondi chimaonetsera Khristu akukhala mwa munthuyo. Zonse zimene Khristu anachita ndi kunene zikuonetsera chikondi cha Mulungu, chimene Iye ali ndi chimene ali. Imene ndi ntchito yathu. Tikuyenera tionetsere chikondi cha Mulungu kwa iwo otizungulira.

China chimene tiyenera kuchiganizira tikamakamba za ntchito ndi kupuma ndi kupumula.
Mulungu anawapatsa Ayuda ndandanda wa masiku antchito ndi tsiku loyenera kupumula,
zimene amayenera kutsata. Masiku ogwira ntchito asanu ndi limodzi, tsiku lopuma limodzi.
Exodo 31:15. . . . .

Sabata lidakhazikitsidwa ngati mbali ya Chilamulo cha Mose,, chimene Mulungu
anapereka kwa Ayuda. Akhristu ambiri anatenga la mulungu ngati Tsiku la Ambuye,
m'malo mwa loweluka, sabata, chifukwa akusangalala kuukitsidwa kwa Yesu Khristu.

Kodi mukudziwa chimene sitikhalira pansi pa Lamulo la Mose? Baibulo limati Yesu
anakwaniritsa malamulo onse, ndipo sitilinso pansi pa malamulo oposa 300 a mwambo
ndi chikhalidwe. Tsono kuti Yesu anakwaniritsa Chilamulo, onse olandira mphatso yache
ali afulu a ukapolo wa Chilamulo cha Mose. Werengani Mateyu 5:17.. . . . .

Kodi tikhale oyamika bwanji kuti tikukhala mwa Yesu amene anatikwaniritsira zofunika za
chilamulo. Moyo wa ngwiro, kufa m'malo mwathu, ndi kuukitsidwa kwa akufa kwa Ambuye
Yesu Khristu kunatimasula kuchiphinjo choyesetsa ku kwaniritsa malamulo onse a Mose.

Yesu anauza ophunzira kufunika kopumula ku zolemetsa za ntchito. Werengani
Marko 6:31. . . . . Tikakamba zopumula, sitikunena holide. Koma kubvomera
ku chiitano mwa Yesu kumene kwa tambasulidwa pa Mateyu 11:28-30.. . . . .
Izi zikutanthauza tisiye kulimbikira kwathu kuti tichite zambiri koma tikhale ndi nthawi
yathu pa Yesu ndi kumudziwa Iye. Njora imodzi ndikumvera Yesu akutilankhula,
ndikuwerenga Baibulo ndi kulingalira zimene Yesu akunena.

Kupumula ndi ntawi yodziwana ndi Mulungu komanso anthu. Titha kupuma uku tikucheza ndi wena, kumvera ndi kusangalala ndi maanja anthu ndi anzathu. kupumula uku kumatitsitsimula. lingalilani momwe mumakhalira nyengo yanu ya tchuthi kapena mukakhala mulibe chochita.

Kodi imakhaladi nyengo yanu yopuma?

10 a. Mulungu watiuza zimene Iye akufuna tichite pa Yohane 6:29. Ndi chani? . . . . . (kukhulupirira mwa Iye anamtumiza)

b. Mulungu anatumiza Ndani? Yohane 3:16. . . . . (Yesu, kuti akhale Mpulumutsi wathu)


Ntchito yathu ndi zochita za bwino zizikatipezetsa malo okhala kumwamba. Koma
kumulandira Iye ngati Mbuye ndi kukhulupirira Iye ngati mpulumutsi. Koma zimene
timachita tikakhala ma Ambuye zimayesedwa, ndipo timalipiridwa, 1 Akolinto 3:13-15.. . . .

Pamene tikuchita ndi cholinga chabwino ndipo tikapanga motsogoleledwa ndi Ambuye ndi
mphamvu zake zimene amazipereka, ntchito za moyo wathu zidzaima ku mayeso. Koma
tikamachita ntchito ndi mphamvu zathu kuti titenge ulemerero, ntchitozo sizingapambane
pa mayeso. Ntchito yabwino imene timachita idzalipilidwa koma siikatipulumutsa.

Mulungu akufuna ife tikhale otsogozedwa ndi Iye. Kulembedwa ntchito kwathu kwa
thunthu ndi kukhala Nkhristu. Ntchito ya ku dziko imangotothandiza kupeza zinthu
zofunika m'moyo uno.

Tikuchita ntchito ya ukhristu ntawi zonse tikugwira ntchito iliyonse
tikakhala kuti tikukhala m'moyo wa umulungu. Sabata ya mawa tiphunzira za mbiri za
chifukwa chimene Yesu anabwerera. tifufuza chinthu chimodzi chofunika kwa mbiri
chimene anatichitira.

Poti pemphero mu funso 11 ndi lapanokha, sizofunikira kuti munene.

11. Yamikani ambuye pa ntchito imene machita. Muuzeni m'mene mukumvera za
ntchitoyo. Lembani pemphero apa.

Pemphero Lotsekera

Atate athu akumwamba, zikomo chifukwa cha ntchito mwatipatsa kuti ife tichite ndi
kutipatsa chitsanzo. Tikufuna musangalale nafe monga umo munasangalalira ndi Yesu.
tikufuna zonse tizichita zibweretse ulemerero ku dzina lanu. Tapemphera mu dzina la
mphamvu la Yesu Khristu, ame.

 

 
 

 

YESU NDI NDANI?

Buku Lothandiza

 
 
Copyright ©  2023 www.UnitedCaribbean.com. All rights reserved. Disclaimer Click to Contact us