home >>buku
lophunzitsira lotsogolera >>phunziro 1 >>phunziro 2
Buku Lophunzitsira Lotsogolera - Phunziro #2
Yesu anati chani?
Cholinga cha phunziro
• Kufotokoza za Yesu ngati Mwana wa Mulungu pa
upadeladela wake umene
ananena za Iye ndi zimene ena ananena za Iye.
• Kuzindikira mphamvu ndi uthunthu wa ziphunzitso
ndi mauneneri, amene
amasonyeza anali Mulungu.
Mu maphunziro athu a baibulo a sabata ndi sabata, mafunso adzasiyana.
Poti zigawo
za mbaibulo ndi zazitali ndipo amawerenga kunyumba, sizofunika kuwerenga
pa
gulu. Funsani munthu m'modzi awerenge yankho. Ngati ena ali ndi
yankho losiyana,
atha kuyankha. Werengani yankho loperekedwa mu buku lotsogolera
ngati
mowombera nkota. Kenaka pitilizani pa gawo lililonse la Baibulo.
Pemphero
Atate wokondedwa wa kumwamba, Buku ilo munalemba ndi lamphamvu!
Ndilodzala ndi
choonadi! Tikufuna tiphunzire zimene Yesu adaphunzitsa anthu. Tsegulani
maso athu kuti kuti tione ndi kumvetsa mau Ake. Tapemphera mu dzina
Lake lodabwitsa, ame.
Mau Otsogolera
Mu maphunziro athu apa Sabata, tikuwerenga Chiphunzitso cha pa
Phiri.Titha kuyamba
maphunziro athu pakupatsirana kupereka mayankho pa gawo lathu mu
Baibulo.
Werengani vesi pansipa ndipo mulembe m'mawu anu
chinthu chimodzi chimene Yesu ananena kwa anthu. |
Kuwerenga Baibulo kwa Sabata:
(Use your Bible or Africa Bible Verse
Handbook) Mateyu 5:1-12,
(Timasangalala pamene tikukhala m'mene Mulungu amanenera kuti
tidzikhala)
Mateyu 5:13-16,
(Yesu anatiphunzitsa kuti anthu okhulupirira Iye ndi nchere
ndi kuunika kwa dziko.)
Mateyu 6:1-15,
(Yesu anatiphunzitsa ife mnene tingapempherere)
Mateyu 6:24-34,
(Tisamadandaule.)
Mateyu 7:1-12,
(Tisaweruze wena. Tichitire wena m'mene ife tikangondere wina
kutichitira) Mateyu 7:13-20,
(Yesu anatiphunzitsa njira yoyenera kukhala ndi m'mene
tingazindikirire aphunzitsi onyenga)
Mateyu 7:21-27,
(Tilole Yesu akhale Mbuye wa miyoyo yathu ndi kumanga miyoyo
yathu pa maziko olimba a chikhulupiriro mwa Mulungu.)
|
Ngati gulu la mbiri silinamalize kuwerengedwa kwa Baibulo pa
sabata, mutha kuwerenga ma gawo ena pomaliza pa zigawo maphunzirondipo
alembe nkhani yofunsidwayo. Kupangira limodzi kutha kuwathandizira
m'mene angapangire
akamaphunzira pa okha.
Tipitirira kuphunzira mayankho ku funso "Yesu ndi Ndani?"
pa zimene Yesu ananena za Iye
ndi kuphunzira maina ena amene anadzicha Yekha.
Limodzi mwa maina linali "Ine ndilipo" tinatchulako dzinali
mongodutsa sabata yatha. Ndidzina la Mulungu. Ine ndilipo litanthauza
ali nthawi zonse, analiko nthawi zonse, ndipo adzakhala
nthawi zonse. limanditsimikizira uthunthu ndi kukhala kosamaliza."
Atsogoleri achipembedzo mu nthawi ya Yesu anafuna kumuponya miyala
chifukwa anadzitcha yekha Ine ndilipo" Anazindikira Ine ndilipo
kukhala dzina la Mulungu. Izi zalembedwa mu Chipangano chathu cha
Tsopano." Yohane 8:56-59 . . . . .
1. Mulungu anadzivumbulutsa Yekha kwa mose ngati
InGod introduced Himself to
Moses as INE NDINE AMENE NDIRI (Exodo 3:14). Kawiiri mu Uthenga
Wabwino,
Yesu akudzichula kuti NDINE. Akumaliza ziganizo zimene zikuonka
zosamaliza.
(NDINE…) ndi mau amene amafotokoza za chimene ali kwa
iwo omukhulupirira Iye.)
Werengani ziganizozi ndipo mumalize.
a. Yohane 13:19. . . . . Ndine (Amene
ndili)
b. Yohane 8:12. . . . .. Ndine (kuunika
kwa dziko)
c. Yohane 10:9. . . . .. Ndine (njira)
d. Yohane 10:11. . . . Ndine (m'busa
wabwino)
e. Yohane 10:36. . . . Ndine (mwana
wa Mulungu)
f. Yohane 11:25. . . . Ndine (kuuka
ndi moyo)
g. Yohane 6:48. . . . . Ndine (mkate
wa moyo)
h. Yohane 14:6. . . . . Ndine (njira,
choonadi, ndi moyo) |
Jesus is the way to God. He is the
truth about God He is the very life of God in those
who receive Him.
Maina operekedwa kwa Yesu mu phunziro 1 ndi funso
lapambuyo akuonetsera
chikhalidwe Chake.
Pa mthawi zosiya m'miyoyo yathu, maina ena aYesu ndi athanthauzo
lomvekabwino
kwa ife. Mwachitsanzo, pa nthawi imene tikufuna chitetezo
ndi citsogozo, dzina,
"Mbusa wa Bwino" litha kukhala la tanthauzo lalikulu
kwa ife. Pamene tikuwerenga
Baibulo ndi kumadya chakudya cha uzimu, ndi "Mkate wa
Moyo" wathu.
2. Ndi dzina liti limene lili ndi tanthauzo pa nyengo mukudutsa
pano.. . . . . (Lolani
munthu wina aliyense ayankhe. ena atha kufuna afotokoze za
m'mene dzinalo
likuthandauzira kwa mbiri kwa iwo, koma onetsetsani asalankhule
kwa nthawi yayitari.)
|
Yesu anaphunzitsa mu njira zitatu—P a chiphunzitso chake,
pa mafanizo, pa mauneneri Ake. Choyamba tiona limodzi la chiphunzitso
cha Yesu.
"Chiphunzitso cha pa Phiri"
Chiphunzitso chimene Yesu analalikira Chiphunzitso ndi “Malankhulidwe
opereka malangizo mu chipembedzo kapena chikhalidwe”
|
Marko ndi Luka analemba za chiphunzitsochi mu Uthenga Wabwino.
Koma, Mateyu amene alinali m'modzi wophunzira wa Yesu analemba motambasula.Ndizotheka
kuti Yesu analalikira Chiphunzitsochi, gapena gawo la ichi, kawirikawiri
akamayenda mu dziko.
Sabata yatha, tikamawerenga, ndi kumaliza za funso 3, timawerenga
chiphunzitso chonse cha Phiri. Nde sitiwerenganso. Onani kuchuluka
kwa zinthu zimene Yesu ananena pa Chiphunzitso cha pa Phiri.
3. Werengani Chiphunzitso cha pa Phiri chodziwika bwino chimene
chikupezeka pa, Mateyu 5:1-7:29. Lembani mitu ndi za Mbaibulo
zili pansinzi zimene zili zopindulitsa kwa inu.
Chitsanzo:
Kuphunzitsa za kukwiya. . . . . . . . . . . . . . . . . .
. . . . . . . . . . . . . . . . . . . ..... .. . . Mateyu
5:21-26
Mayankho:
Chimwemwe chenicheni. . . . . . . . . . . . . . . . . . .
. . . . . . . . . . . . . . . ........ . . . . . .Mateyu 5:3-12
Nchele ndi Kuunika . . . . . . . . . . . . . . . . . . . .
. . . . . . . . . . . . . . . . . . ..... . . . . . .Mateyu
5:13-16
Chiphunzitso cha Chilamulo. . . . . . . . . . . . . . . .
. . . . . . . . . . . . . . . ...... . . . . . .Mateyu 5:17-20
Chiphunzitso cha chigololo. . . . . . . . . . . . . . . .
. . . . . . . . . . . . . . . . .... . . .. . . .Mateyu 5:27-30
Chiphunzitso cha kusudzula. . . . . . . . . . . . . . . .
. . . . . . . . . . . . . . . . .... . . . . . .Mateyu 5:31-32
Chiphunzitso cha pangano. . . . . . . . . . . . . . . . .
. . . . . . . . . . . . . . . .... . . . . . . .Mateyu 5:33-37
Chiphunzitsochobwezera. . . . . . . . . . . . . . . . . .
. . . . . . . . . . . . . . .. ... . . . . . . .Mateyu 5:38-42
Kukonda adani . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . .
. . . . . . . . . . . . . . . . . .. . . ... . . . . . .Mateyu
5:43-48
Chiphunzitso cha Chikondi. . . . . . . . . . . . . . . . .
. . . . . . . . . . . . . . . . ........ . . . . . .Mateyu
6:1-4
Chiphunzitso cha Pemphero. . . . . . . . . . . . . . . . .
. . . . . . . . . .. .. . . ..... . . . . . . .Mateyu 6:5-15
Chiphunzitso cha Kusala. . . . . . . . . . . . . . . . . .
. . . . . . . . . . . . . . . . ... . . . . . . .Mateyu 6:16-18
Chuma Kumwamba. . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . .
. . . . . . . . . . . . . . . . ... . . . . . . .Mateyu 6:19-21
Nyali ya thupi. . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . .
. . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . ... . . . . .
. .Mateyu 6:22-23
Mulungu ndi Chuma. . . . . . . . . . . . . . . . . . . . .
. . . . . . . . . . . . ... . . . . ... . . . . . .Mateyu
6:24-34
Kuwereza Ena. . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . .
. . . . . . . . . . . . . .. . .. . . . ........ . . . . .
.Mateyu 7:1-6
Funsa, Funa, Gogoda. . . . . . . . . . . . . . . . . . . .
. . . . . . . . . . . . . . . ... ...... . . . . . .Mateyu
7:7-12
Khomo lopapatiza. . . . . . . . . . . . . . . . . . . . .
. . . . . . . . . . . . . . . . . . .. . . ..... . . .Mateyu
7:13-14
Mtengo ndi zipatso zache. . . . . . . . . . . . . . . . .
. . . . . . . . . . . . . . ... . . . ... . . . .Mateyu 7:15-20
Sindikudziwani. . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . .
. . . . . . . . . . . . . . . . . . . . . ... ... . . . .Mateyu
7:21-23
Omanga nyumba awiri. . . . . . . . . . . . . . . . . . . .
. . . . . . . . . . . . . . . .. . . . .... . . .Mateyu 7:24-27
Ulamuliro wa Yesu. . . . . . . . . . . . . . . . . . . . .
. . . . . . . . . . . . . .. . . . . . . . . .. . . Mateyu
7:28-29) |
Yesu amaphunzitsa m'mafanizo.
Fanizo lomwe Yesu ananena
Fanizo ndi kankhani kakafupikamene kamafotokoza
za uzimu ndi chikhalidwe.
|
Amagwiritsa ntchito zitsanzo zimene amazitenga kuchoka ku
chilengedwe ndi ku zinthu zochita pa moyo wa tsiku ndi tsiku kuti
afotokoze choonadi cha
chikhalidwe ndi cha uzimu.
Mu Baibulo fanizo linali ndi tanthauzo lobisika limene limafunika
kufotokozeredwa. Yesu amagwiritsa kanenedweka kuti abise tanthauzo
kwa adani ake. Pa chifukwa ichi, iwo ofuna kumukola amakanika kupeza
choyankhula chatchutchutchu kuti
achigwiritse ntchito pomukola.
Chomodzi chosangalatsa ndi mafanizo ndichakuti amapereka choonadi
cha mphamvu mu njira yochititsa chidwi, imene anthu omvera samadzidzimukiratu
panthawiyo.
Baibulo limatiphunzitsa angamvetse ndani zimene Yesu ananena. Mtumwi
Paulo amati chani za ichi pa 1 Akolinto 2:13-16? . . . .
. Iyi imati anthu amene alibe Mzimu wa
Mulungu mwa iwo sangamvetse zimene Yesu ananena. Mau ake amaoneka
achabechabe
kwa iwo omwe sali Akhristu.
Ophunzitsa Baibulo Charles Ryrie anati choona chophunzitsidwa mu
Baibulo ndi zinsinsi,
chifukwa sizinavumbulutsidwe mu Chipangano cha Kale. Zinavumbulutsidwa
ndi Khristu mu
Chipangano Chatsopano kwa iwo anaika chikhulupiriro mwa Iye.
Mu funso 4, tikupeza mafanizo asanu ndi awiri kuchokera ku Mateyu
13. Mungakonde
kuwerenga funso lotsatira ndi kunene choyamba?
4. Patsiku lina. pambali pa mtsinje,
Yesu analalikira chiphunzitso cha mphamvu
chimene chili ndi mafanizo asanu ndi awiri. Tsekulani tsamba
34-38 ndipo werengani
ulalikiwu—Mateyu 13:1-58. Werengani maina a mafanizo asanu
ndi mu gawo ili:
1. (odzala)
2. (namsongole)
3. (njere ya mpiru)
4. (chotupitsa mkate)
5. (chuma chobisika)
6. (khola)
7. (khoka)
Ananenera za Iye, pamodzi, Yesu ananena mafanizo 60 amene
analembedwa mu Uthenga Wabwino. Ena amabwerezedwa mu mauthenga
ena abwino. Imodzi yodziwika bwino ndi fanizo la Ofesa.
5. Mateyu, Marko, and Luka ikunena za matambasulidwe a Yesu
pa fanizoli.
Werengani Luka 8:11-15 . . . . .
a. Kodi wofesa amadzala chani? . . . . . (Mau a Mulungu)
b. Chimene chimalepheretsa ? . . . . . (Satana amalanda,
mau sakhazikika; mavuto
akabwera timazisiya; nkhawa za moyo uno, ndi chikondi cha
chuma zimawatsamwitsa.)
c. Chifukwa chani nthaka ina imapindura kusiyana ndi yina?.
. . . . (Ndi nthaka ya
bwino— anthu amamva mau a Mulungu, kuwamvetsetsa, kuwakhulupirira,
ndi
kuwamvera.)
|
Kulimbikitsa gulu kuti ligawane, mutha kuyamba ndi kupereka mayankho
anu ku funso 6.
Limbikitsanani kulingalira zosintha.
6. Lingalirani za fanizo lanthaka.
a. Ndi nthaka yanji imene moyo wanu ukuyimira?. . . . . (Mafunso
asiyana.)
b. Ndi kusintha kwa ntundu wanji komwe kukufunika kuti moyo
wanu usinthe
ndikukhala nthaka ya bwino.. . . . (Mafunso asiyana.)
|
Tsopano tiona ma uneneri ena a Yesu.
Mauneneri
amene Yesu ananeneratu
Uneneri umachokera "pakuyankhula motsogozedwa
ndi Mulungu" |
Pa Phunziro 1, timawerenga za mauneneri a aneneri a Chipangano
cha kale amene ananena za kubwera kwa Yesu ndi m'mene mauneneriwo
anakwaniritsidwira. Kodi mukudziwa kuti Yesu Khristu anatipatsa
mauneneri?
Ananeneratu za kukanidwa ndi Petulo, kukanidwa ndi ophunzira ake,
kukumana ndi ophunzira ake mu Galileya idadutsa nthawi yakufa ndi
kuuka kwake ndi kubwera kwake kwa chiwiri.
Werengani Funso 7, imene imabvumbulutsa ena mwa mauneneri.
7. Chipangano cha Tspopano chili ndi
ma ulosi ambiri a Yesu. Ochepa ndi awa ali
pansipa. Lembani fundo ya Baibulo yolondola.
Marko 8:38
Marko14:72
Luka 24:5-7
Yohane 5:25-29
Yohane 12:32-33
Za m'Baibulo
a. Kukanidadwa ndi ophunzira ................................(Marko
14:72 . . . . .)
b. Imfa yake...............................................................
(Yohane 12:32-33 . . . . .)
c. Chiukitso Chake..................................................
(Luka 24:5-7 . . . . . )
d. Chiukitso chathu ..................................................(Yohane
5:25-29 . . . . .)
e. Kubweranso kwake ............................................(Marko
8:38 . . . . .)
|
Ngati gule lingafunse “—nthaw yakwana—”
pa Yohane 5:25-29, Ikunena kuti Yesu amanena nthawi imene anautsa
Lazalo kwa akufa. (Yohane 11:17-44).
Yesu ananenea za mbiri za masiku otsiriza. Tsegulani pa Mateyu
24:1-3. . . .
Kodi ndi mafunso awiri ati omwe ophunzira anafunsa Yesu?.What two
questions did the
disciples ask Jesus? . . . . . (Kodi kachisi adzagumulidwa liti?
Kodi chizindikiro choti Yesu akubwera chidzakhala chotani?)
Ulosi wa kachisi unakwaniritsidwa mu chaka cha A.D. 70—zaka
37 kuchokera mu nthawi imene Yesu anali pa dziko lino.—pamene
Aroma "anaonongeratu Yerusalem ndi kachisi [ndipo] miyala inaikidwa
kuti idzitunga golide amene amatayikira pansi."
Yesu anayankha funso lachiwiri. Tsegulani Mateyu 24:36-39.
. . . . Yesu, mu
umunthu wake, ananena palibe koma ndi Atate okha amene akudziwa
tsiku lakubwera
kwake.Tisakhulupirire anthu amene amayika masiku akubwera kwa Yesu!
Yesu anati zambiri zidzachitika asanabwere. Takhala ndi chilala,
zibvomerezi, ndi zigumula. Koma izi zidzachitika mowirikiza ndi
mwamphamvu pamene Yesu wayandikira kubwera.
Tikadziwa Yesu ngati mpulumutsi, titha kumukhulupirira za tsogololathu.
Tisasiye phunziro limene Yesu ananena posaphunzira gwero la mau
ake.
8. Mau amene Yesu amayankhula amachoka
kuti? Yohane 17:5-8 . . . . . (Tate)
|
Onani Yesu anati zonse zimene anena zikuchoka kwa Atate Ake. Tsopano
tatsimikiziridwa mau ake ndi choonadi. Zonse zimene Yesu ananena ndi
kuchita zimachoka kwa Mulungu, Atate ake.
Ngakhale adani aYesu, alonda ogwira ntchito kwa Asembe akuluakulu
ndi a pharisi, anasangalatsidwa ndi zimene Yesu amanena. Onani Yohane
7:45-46 . . . . .
Zinali zoona. Palibe analankhula ngati m'mene Yesu amalankhulira!
Mu chipangano cha Kale timawerenga
nthawi zimene Mulungu analankhula kwa
aneneri, asembe, ndi mafumu. Baibulo linalemba izi kunena "
Baibulo linanena izi kuti "Mulungu anati......kapena
Mau a Mbuye anabwera........" Mulungu analankhulanso
kwa anthu mu chipangano chatsopano.
9. Kwa ndani kumene Mulungu anapereka mau Ake ndi uthenga
mu Chipangano cha
Tsopano munsimu?
a. Marko 1:10-11. . . . . (kwa Yesu
)
b. Yohane 1:32-33 . . . . . (Yohane
mbatizo)
c. Machitidwe 11:4-9 . . . . . (kwa Peturo)
|
Mulungu analanhkula mu njira zina kwa anthu ena. tsegulani tsamba
330 mu Chipangano
chanu cha Tsopano ndikupeza Machitidwe 10:3-6. Tiuzeni
m'mene Mulungu analankhulira
ndi Korneliyo.. . . . . (kudzela m'masomphenya angelo).
Pano, Mulungu akuyankhula ndi wa a mitundu, zimene zinadabwitsa
Ayuda. Amaona ngati Mulungu amayankhula ndi Ayuda okha!
Pamene atsogo;eri a mpingo wa ku Antiokeya amatumikira Ambuye,
ndi kusala kudya,
Mulungu analankhula nawo bwanji? Machitidwe 13:2-3 . . .
. . (mwa Mzimu woyera).
Mulungu amalankhula nawo mwa Mzimu woyera. Anawauza atumize Sauli,
amenenso ali ochedwa Paulo, ndi Barnaba ngati atumwi kwa Amitundu.
Mulungu amayankhulanso kwa ife lero. Werengani Aheberi
1:1-2a. M'mau anu izi zitanthauzanji? . . . . (Mulungu
amayankhula nafe kudzera mwa mwana wake, Yesu)
Tangoganizani! Mulungu amayankhula ku mitima yathu nthawi zonse
tikamaewerenga
Baibulo. Mbali yathu ndi kumverea ndi kuchita.
Muwerenge Miyambo 8:34-35. . . . .
Mulungu akulankhula ndi anthu lero. Tikamva uthenga ochokera ku
mau a Mulungu,
timadziwa Mulungu akuyankhula nafe. Werengani 1 Atesolonika
2:13 mu
chipangano chanu Chatsopano.. . . . .
Mulungu watiuza kale zonse zimene tikuyenera kudziwa za moyo-kumbuyo,
panopa, ndi
kutsogolo. Wasungu Buku lake mu mibado mibado ndipo wasunga zolemba
zoyambirira. Kodi sizopatsa kaso kuti tikuwerenga malingaliro a
Mulungu m'mau ake?
10. Mwaphunzira chani za Yesu ndi
zimene anachita. . . . . (Lolani wina aliyense anene
yanho lake.) |
Kudzera mu kuona Baibulo, taphunzira Yesu ndi Mulungu. Amachedwa Mwana
wa Mulungu.
Zonse ananena pozoyankhula Zache, muziphunzitso Zache, mu mauneneri
Ake, mu mafanizo Ake, ndi mauneneri ake amachoka kwa Mulungu. Tikudziwa
zonse Yesu ananena ndi zoonaChoona cha Mulungu.
Sabata ya mawa, phunziro lathu likutchedwa 'Yesu Anapanga Chani?"
Tidzaphunzira kufunika ko gwira ntchito ndi kupumula.
Pa phunziro 3 mpaka 6, mudzalemba pemphero lanu kutseka nthawi
yowerengera ku
nyumba. Izi zikupatsani danga loyamika Ambuye ndikumufunsa akuthandizeni
kuchita
choonadi cha Baibulo pa moyo wanu. Pemphero lanu silidzagawidwa
pa gulu.
Pemphero lotsekera
Ambuye Yesu, zikomo tikudziwa zonse zimene munanena ndi zoona.
Palibe analankhula ngati Munalankhulira. Titha kudalira malonjezano
Anu. Zikomo potiphunzitsa. Tapemphera mu dzina Lanu, ame.
|