home >>buku
lophunzitsira lotsogolera >>phunziro 3 >>phunziro 4
Buku Lophunzitsira Lotsogolera - Phunziro #4
Chifukwa chani Yesu anabwera?
Cholinga cha Phunziro
• Kuzindikira kuti zotsatila za tchimo ndi imfa.
• Kuzindikira kulephera kwa munthu kudzilipirira Yekha
dipo.
• Kuphunzira chifukwa chimene Yesu anasiya ulemerero
wa kumwamba ndi kubwera ku dziko lino lauchimo.
• Kuzindikira kufunika kwa Infa ya Yesu ya pa mtanda.
Limbikitsani gulu kuganizira wena amene angawalimbikitse kuti
azibwera ku
maphunziro a Baibulo, amene ayambe m'masabata ochepa akubwerawa.
Zofunikira! Ngati wina wafunsa m'mene angakhalire Mkristu, mukhale
okonzeka
kuyankha. mutha kufotokoza dongosolo ya chipulumutso, osachititsa
manyazi
wina. Perekani mwayi kuti munthu apemphere alandire Yesu.
Pemphero
Wokondedwa Atate a Kumwamba, zikomo pa zonse matiphunzitsa za Mwana
Wanu, Yesu
Khristu. Tikufuna tidziwe nchifukwa chani anabwera ku dziko la pansi.
Tiphunzitseninso
kuchokera m'mau anu. Tapemphera mu dzina la Yesu, ame.
Ndemanga zotsogolera
Kodi munazindikirapo ichi kuti mutha kudziwa maganizo a mMulungu
kuchokera mu Buku
limene anatipatsa? Titha kudziwa zimene Mulungu amagzaniza pa zosiyanasiyana
chifukwa watiuza mu Buku lake lodabwitsa. Choti tichite ndikungolitenga
ndi kuliwerenga.
Ndizimene tikuchita pa maphunzirowa—kutenga maganizo a mulungu
m'moyo mwathu.
Pa mayambiriro a phunziro lililonnse, tapatsidwa magawo a Baibulo
oti tiwerenge amene
ali ogwirizana ndi phunziro. Kuwerenga Baibulo ndi kupemphera itha
kukhala nthawi
yabwino yoyanjana ndi Mulungu, chifukwa tikuwerenga ndi kumva Malingaliro
a Mulungu.
Tsopano tiwerenge kuyankha kwathu mu kuwerenga kwathu kwa sabata
ino.
Kuwerenga
Baibulo kwa Sabata:
(Use your Bible or Africa Bible Verse
Handbook) Werengani gawo la Baibulo pansipa ndipo mulembe m'mau anu
zimene limanena
za chifukwa chimene Yesu anabwerera ku dziko lapansi.
Mateyu 5:1-2, 17-20
(Yesu anati anabwera kudzapanga chiphunzitso cha Chipangano
cha Kale kuti chikhale choona.)
Yohane 6:35-38
(Yesu anabwra kudzapanga chifuniro cha Atate)
Machitidwe 2:23-24
(Yesu anabwera kudzafa ndi kuukutsidwa. Mulungu anakonza kuti
Yesu apereke moyo Wake ndi kuukitsidwa kwa akufa)
1 Yohane 3:5-6
(Yesu anawoneka kuti achotse tchimo.)
Aheberi 2:14-15
(Imfa ya Yesu inawononga satana ndi imfa.)
Chibvumbulutso 3:20-21
(Yesu akugogoda pa khomo pa mitima ya anthu, kuti akapereke
chigonjetso kwa iwo amuitana Iye miyoyo yawo.)
Chibvumbulutso 5:9-10
(Imfa ya nsembe ya Yesu idzabweretsa anthu ochokera ku mtundu,
chiyankhulo, fuko ndi mtundu wonse kutumikira Mulungu.)
|
Taphunzira chani panopa? Mu phunziro loyamba, taphunzira kuti Yesu
anali ndi maina
ambiri. Ndi dzina liti lomwe lili ndi tanthauzo lofunika kwa inu.
lero . . . .?
Maina ambiri akutikumbutsa kuti Iye ndi Mulungu ndi amodzi. Tapeza
kale maina awiri a
mainawo. Mukuwakumbukira? Akupezeka pa Yesaya 9:6 . . .
.?
Ali Mulungu wankulu ndi Tate Wosatha.
Pa phunziro 2, taphunzira zinthu zina zimene Yesu anaphunzitsa
mu Ziphunzitso zonse,
mafanizo, ndi mauneneri. Amatiphunzitsa m'mene tingakhalire m'moyo
wa umulungu—
Moyo umene umamusangalatsa Mulungu ndi munthu.
Mu phunziro 3, taona Yesu akuchita zozizwa. Amachilitsa iwo amene
ali wodwala. Tsiku
ndi tsiku amayangana ndi chifundo iwo amene anali osautsidwa ndipo
amawapatsa
zosowa zawo. anaukitsa akufa, kutulutsa ziwanda, kubwezeretsa ziwalo
zakufa,
ndikudyetsa makamu a wanthu modabwitsa.
Aneneri ananenera Mulungu adzabwera ndi kuwapulumutsa. Atsogoleri
a chipembedzo,
amene amadziwa za Chipangano cha Kale uneneri wa Yesaya, amayenera
kudziwa chimene Yesu anali pamene anamuona akuchiritsa anthu. Tsegulani
limodzi la mauneneri wa Yesaya pa mamalizilo a buku ili. Yesaya
35:4-6 . . . . .
Mu phunziro lathu, tiphunzira chifukwa chimene Yesu anabwerera.
Sanabwere kudzalalikira ziphunzitso zikulu zikulu kapena kudzachilitsa
anthu. 37
Chifukwa chain anabwera pa dziko lapansi? Baibulo pa funso 1 likutipatsa
zifukwa zimene Iye anabwerera.
1. Chifukwa chani Yesu anabwera pa
tdziko la pansi? Baibulo likutipatsa zifukwa
zambiri pansipa.
a. Mateyu 5:17. . . . . (kupangitsa
ziphunzitso za Mulungu zoona)
b. Yohane 1:18. . . . . (kuonetsera
Mulungu kwa anthu)
|
Yesu ndi Mulungu komanso munthu. Ndizosangalatsa kuti amatchedwa
mwana wa Mulungu komanso mwana wa munthu. —kuonetsa umulungu
wake ndi umunthu wake.
c. Mateyu 20:28 . . .
. . (kupulumutsa ndi kupereka moyo wake kuti
anthu apulumutsidwet)
d. Luka 4:42-43. . . . . (kulalikira
Uthenga wa Bwino wa Ufumu wa Mulungu)
e. Luka 19:10. . . . . (kupulumutsa
ndi kufunafuna chotayikacho)
f. Yohane 3:17. . . . . (kukhala Mpulumutsi
wa dziko)
g. Yohane 10:7-10. . . . . Onani vesi 10.
(kupereka kwa okhulupirira moyo wodzala mu kuchuluka kwake)
h. 1 Timoteyo 1:15. . . . . (kupulumutsa
ochimwato)
|
Ma vesi ambiliwa akukamba zinthu zimodzi mosiya. kuombera nkota,
ma vesiwa amati
chani za chifukwa chimene Yesu anabwerera?. . . . . (Yesu anabwera
kuzakhakla mpulumutsi wathu) Tikufunika mpulumutsi chifukwa
ndife ochimwa.
Baibulo limati Mulungu analenga angelo ndi anthu mkuwapatsa chisankho
chosankha
chabwino kapena choyipa. Ngati sitisankha Mulungu tachimwa.
Satana, wokongola, ngelo wa mphamvu, anali woyamba kuchimwa. mu
kudzikuza kwake
amafuna kutenga malo a Mulungu. Yesaya 14:12-14,
ikufotokoza maonekedwe a kudzikuza a satana ndi m'mene anachokera
ku mwamba........Satana atachimwa kumuchimwira Mulungu, anamnyenga
Adamu ndi Hava kuti asamvere Mulungu. Hava ananyengedwa ndi satana
koma koma adamu adasankha kusamvera.
Werengani Aroma 5:12 . . . . .
Kuyambira nthawi imeneyo, munthu yense amene anakhalapo anachimwa.
Angakonde kuwerenga zimene Baibulo linanena ku Aroma 3:23
“Yese
wachimwa ndi kutalikilana ndi kupezeka kopulumutsa kwa
Mulungu.”
—Aroma 3:23
Chilango cha uchimo chinalengezedwa ndi Mulungu kwa Adamu
ndi Hava pa chiyambi. Chilango chinali cha imfa ya kuuzimu
ndi kuthupi. Genesis 2:17 ikuti, “Koma mtengo wa kudziwitsa
chabwinio ndi choyipa musadye, pakuti tsiku limene mudzadya
mudzafa. |
Werengani Aroman 6:23
“Pakuti tchimo lili ndi dipo lake—imfa; koma
mphatso ya ulele ya
Mulungu ndi moyo wosatha mu ubale ndi Khristu Yesu Mbuye wathu.”
—Aroman 6:23
|
Pali njira imodzi imene tingapulumutsidwire? Machitidwe 4:11-12
. . . . .
Komanso, chifukwa chani tikufuna Mpulumutsi?. . . . . (chifukwa
tamuchimira Mulungu)
Tamuchimwira Mulungu. Tatsutsana naye ndi kusankha kukhala osiyana
ndi Iye. zimenezo
ndi uchimo. Chifukwa chake tikufuna mpulumutsi.—kutipulumutsa
ku dipo la tchimo.
Yesu ndi mlowa malo wathu
Kuyambira ku Chipangano cha Kale, mulungu amavumbulutsa
kuti mlowamalo
wosalakwa, wosachimwa afe chifukwa cha tchimo la wina. koma
tangowerenga
Aroma 3:23, imene ikuti onse anachimwa. Sipanakhaleko munthu
ochimwa,
kupatulako Yesu Khristu. |
Chifukwa chimene anabwerera ku dziko la pansi. anabwera kudzakhala
mlowa m'malo
wosalakwa. panalibe njira ina imene tikanakhululukidwa! Yesu anayenera
kubwadwa mwa
namwali, kuti askhale ndi chikhalidwe cha tchimo la Adamu—chimene
anthu onse
anayamwira. anakhala m'moyo wosachimwa ngati mwana, m'nyamata, ndi
wankulu.
Titha kuwerenga chikhalidwe chopanda uchimo cha Yesu pa 2 Akorinto
5:21 mu mabuku athu ophunzirira. . . . . .
“Khristu
analibe tchimo Christ . . . .”
—2 Akolinto 5:21
|
Yesu ali ndi zaka 30, anayamba utumiki wake pa dziko lino. Panthawiyo
adabatizidwa
ndipo Mulungu analankhula kumwamba kunena kuti akondwera ndi moyo
wa Yesu ndi
zonse anachita. Werengani izi Marko 1:11. . . . .
(Mulungu anati, “Ndikondwera nwawe.”)
2. Yesu ananeneratu momveka bwino
kuti adzaphedwa ndi kuuka kwa akufa.
Anawuza yani, ndipo anawawuza chani tikawerenga pansipa?
a. Luka 18:31-33 . . . . . (Yesu anauza
ophunzira kuti adzaperekedwa kwa amitundu. Anafotokoza za
chimene adzachitidwe asanaphedwe)
b. Mateyu 12:38-40 . . . . . (Anauza
adani Ake, aphunzitsi a chilamulo ndi afarisi, adzaikidwa
m'manda masiku atatu.)
c. Marko 8:31-32a . . . . . (Anauza
ophunzira adzaphedwa ndipo akatha masiku atatu adzauka)
|
Munaona kuti vesi 32 Yesu ananeneratu izi kwa iwo? komano mochulukir
anthu
amamulondola Yesu, mochulukira atsogoleri a chipembedzo ndi afalisi
amamukana ndi
kumusautsa. Koma nthawi inafika yoi aYeus aperekedwe ndipo anagwidwa.
Koma tiyeni tiwerenge ngati adani ake akanatha kumuwereza Yesu.
3. Kodi adani a Mulungu akanampeza
Iye olakwa? Luke 23:4 . . . . . (Ayi)
4. Poti Yesu sanachimwepo kapena kuphwanya lamulo lililonse,
chifukwa chani
anaweruzidwa kuti afe. Marko 14:61-64 . . . . .
(Anaweruzidwa kuti afe chifukwa anali Mesiya, mwana wa
Mulungu.)
|
Zinali zoona kuti Yesu ndi Mesiya Mwana wa Mulungu. Olamulira amati
choona ndi chabodza anamuweruza Iye amene anali Mlengi.
Yesu sanadzikire kumbuyo. Anabwera kudziko kudzafera machimo a
wena.
Kuperekedwa, kuweruzidwa ku bwalo la milandu, kukwapulidwa, ndi
kukhomedwa pa
mtanda zizinali zodabwitsa kwa Iye. Zosenzi zinanenedwa zaka zambiri
kumbuyoku.
Yesu amadziwa zonse izi zidzachitika. Dzilko lisanalengedwe.,
Anakonza kubwera
ku dziko kufa ngati Mlowa malo wa munthu. Iyi inali njira yokhayo
imene anthu
akanapulumutsidwira kuchoka ku zotsatira za tchimo. Yesu anadziwa
mazunzo
amene amayenera kudutsamo. |
Werengani mauneneri okhudza Iye mu Yesaya 53:3- 6. . .
. .
5. Pa zomangidwa zonse, imfa, ndi kukwiriridwa
kwa Yesu, kuyamba pa
Marko 14:43–15:47.
Izi zinalembedwa M'mauthenga Abwino onse anayi. Wolemba wina
aliyense
akutsindika zinthu zosiyana malingana ndi m'mene amawonera.
mu zolemba zina,
timaphunzira kunali ziweruzo zambiri chifukwa kunali kovuta
kuti amuweruze pa
chinthu choyipa. Timaphunziranso zina zimene Yesu ananena
pa mtanda.
Mateyu analemba zinthu kwa zimene anthu a Chiyu amafuna kumva
(Mateyu 27:27–28:15). Analemba za boma kutumiza asilikali
kukatseka manda. Mateyu akufotokoza izo zidzchitika pamene
Yesu anawuka kwa akufa.
Yohane anakamba zambiri za anthu amene Yesu anakamba nawo
atauka kwa akufa.Anafotokoza za boma kutumiza asilikali kukatseka
ndi kulondera manda. (Yohane 19:16-21:25).
Luka analemba ma buku awiri, Uthenga wa Bwino wa Luka ndi
buku la Machitidwe.
Mu ma buku onse. (Luka 23:26–24:52 and Machitidwe 1:1-11),
anafotokoza za m'mene Yesu anatengedwera ku mwamba masiku
makumi anayi atatha chiukireni kwa akufa. |
Yeus ananyamula machimo athu pa Iye Yekha. Ananyamula machimo anthu
onse a munthawi zonse. Werengani 2 Akolinto 5:21 . . . .
.
Satana, mdyerekeezi, ndiwogonjetsedwa chifukwa cha imfa ndi kuuka
kwa Yesu.
Werengani zomwe zabvumbulutsidwa 1 Yohane 3:8-10 . . . .
.
Mutha kufunsa, "Ngati satana wagonjetsedwa, chifukwa chani
lero ali ndi mwayi ochita ntchito zache? Amapambana pa zifukwa zitat.
1) Anthu amasankha kumvera satana osati Mulungu.
2) Akhristu sazindikira satana ndi wogonjetsedwa, Mulungu waapatsa
mphamvu zokhala
ndi moyo wa chigonjetso. Timawerenga izi pa Aefeso 1:18-22
. . . . .
3) Kugonjetsedwa kwa satana kunawoneretsedwa pamene Khristu anawuka
kwa akufa.
Satana ali ndi ufulu wochita zinthu mpaka Yesu adzabwere. Satana
adzalandila chilango
pamathero. Buku la Chibvumbulutso limanena nthawi yache pa Chibvumbulutso
20:1-3, 7-10, ngati mukufuna kaoneni zimenezo kunyumba.
Yesu anabwera koyamba kudzatipatsa chipulumutso. Akubweranso kudzapereka
chiweruzo.
6. Baibulo limaphnzitsa momveka bwino Yesu anabwera
pa dziko ndi kufa m'malo mwako chifukwa cha machimo ako. poti
Yesu anafa chifukwa cha iwe, yankho lanu lidzakhala lotani?
. . . . . (Mutha kufunsa munthu wina aliyense payekhapayekha
kuti apereke yankho ku funsoli.) |
7. Lowezani Machitidwe 4:12.
Lembani Machitidwe 4:12 pano. (Chipulumutso chimapzeka
mwa iye yekha basi, pa dziko lonse palibe amene Mulungu wapereka
kuti atipulumutse.)
|
Phunziro ya sabata ya mawa ndi l;osangalatsa kwambiri. tidzaphunzira
za chozizwa
chachikulu chomwe sichinachitikepo.
Poti pemphero pa funso 8 ndi lamunthu payekha, sizofunika kuti
anene. pitani ku
pemphero lotseka.
8. Uzani ambuye kuti ndinu ayamika
bwanji kuti Iye amakukondani ndipo
anakuferani pa mtanda kulipira dipo la tchimo lanu. Lembani
pemphero lanu apa. |
Pemphero Lotsekera
Tikuyamikani, Atate wa kumwamba, chifukwa cha chiplumutso munapereka
kwa ife.
Zikomo chifukwa cha chikondi chanu . Tikuthokozani Atate kumwamba,
chifukwa cha
chipulumutso mudapereka kwa ife. zikomo chifukwa cha chikondi chanu
chosasinthasintha pa ife ngat anthu. Tiphunzitseni tichite zonse
mwatiphunzitsa pa moyo
wathu. Tapemphera mu dzina la mphamvu la Yesu Khristu, ame.
|