home >>buku
lophunzitsira lotsogolera >>phunziro 4 >>phunziro 5
Buku Lophunzitsira Lotsogolera - Phunziro #5
Yesu alikuti tsopano?
Cholinga cha Phunziro
• Perekani chizindikiro cha mbiri ya kale kuti Yesu
Khristu adauka kwa akufa.
• Kumvetsetsa kuti chifukwa cha imfa ndi kuuka kwa Khristu machimo
athu akhululukidwa.
• Onetsani kuti Akristu sangakhale m'moyo wa umulungu mwa mpamvu
zawo ndi zimene iwo alinazo.
•Kumvetsetsa kodzipereka kwa Khristu kuti tione chigonjetso
cha moyo wa
Pemphero
Mulungu wa mpamvu, tsekulani maso athu ndi makuti athu pamene tiwerenga
tonse limodzi. Zimene tikuwerenga m'mau anu ndi zofunika kwambiri.
mutikuze ife, Ambuye.
Tithandizeni tikule mukumvetsetsa kwa chimene inu uli. Tapemphera
mu dzina la Yesu, Ame.
Fundo zotsogolera
Maphunziro a sabata ndi sabata a sabata yathayi anali olimbikitsa
pamene timaphunzira
kuti Yesu alikuti tsopano. Tiyambe kunene pogawana m'mene tazilandirira?
Kuwerenga Baibulo kwa Sabata:
(Use your Bible or Africa Bible Verse
Handbook) Werengani gawo pansipa ndipo lembani kuyi ganizo
kuti Yesu alikuti lero. Machitidwe 1:6-11 (Kumwamba)
Machitidwe 2:32-35 (Ku dzanja la manja la Mulungu)
Aheberi 4:14-16 (Mu kupezeka kwa Mulungu)
Agalatia 2:15-20 (Khristu amakhala mwa wokhulupirira.)
Aefeso 3:14-21 (Khristu amapanga nyumba mu mitima ya
Akhristu.)
Akolose 1:27-29 (Khristu amakhala mwa iwo amene amuitana.)
1 Petulo 3:22 (Yesu ali ku dzanja la manja la Mulunhu
ku mwamba, kulamulira angero onse ndi mphamvu ndi ulamuliro.)
|
Taphunzira zambiri za Yesu Khristu mu maphunziro athu tangomalizawa.
Kodi bwanji
titangotenga nthawi yathu kuonanso?
Yesu ndi ndani?. . . . . (Atha kupereka mayankho ambiri, khalani
otsimikizika kuti
akuphatikizirapo kunenea kuti "Mwana wa Mulungu" ndi "Mpulumutsi")
Kodi njira ya kaphunzitsidwe ka Yesu inali yotani-—pa zimene
tzikuchitika pano, pa
mafanizo, kapena pa maphunziro zandale?. . . . . (mafanizo)
Kuchoka ku zimene taphunzira kufikira pano, nenani limodzi la chiphunzitso
chodziwika
bwino cha Yesu. . . . . (chiphunzitso cha pa phiri)
Mafunso enawa ndi ziganizo zimene zili zoona kapena za bodza. Makonzeka?
Zoona kapena zabodza—Yesu anapereka mauneneri
ambiri. . . . . (Zoona. Ananenera za zimene zichitike kwa iye
ndi za malekezero a dziko.)
Zoona kapena zabodza—Yesu amakhala ndi nthawi
yayikulu ali yekha kutali ndi anthu?. . . (Zabodza)
Zoona kapena zabodza—Pakuti Yesu amayenera
kukhala Mfumu ya Ayuda, Amakhala ndi nthawi yake ndi olamulira,
kuwatetemula pa fundo zake za utsogoleri wake.. . . . . (Zabodza)
Zoona kapena zabodza—Zokhumba za anthu amene
amamulondola Yesu zimasokoneza za moyo Wake. Zimene amaziika patsogolo
ndi kuika zokhumba za anthu pamwamba pa zokhumba zake—ngakhale
kukakhala kudya.. . . . . (Zoona. Marko 6:31)
Zoona kapena zabodza—Baibulo limati osagwira
ntchito asadye. . . . (Zoona. 2 Ateselonika 3:10)
Chifukwa chani Yesu anakhala munthu? . . . . .
Poyankha funso lamaliza, 'chifukwa chani Yesu anakhala munthu?"
gulu litha kupereka mayankho ambiri ndikuwanena mu njira zambiri.
Yesu anaperekedwa ndi ophunzira Wake Yudas ndipo anaweruzidwa kuti
akaphedwe
pomukhomera pa mtana chifukwa ananena anali mwana wa Mulungu, Izi
zinalai
zodabwitsa kwa Iye. Zinachitika malingana ndi dongosolo lomwe Mulungu
anakonzeratu
nthawi isanayambe.
Mulungu anavumbulutsa dongosolori kudzera mu Baibulo. Kwa nthawi
yoyamba Anatiuza
za dongosolo Lake mu Genesis Adam ndi Hava atachita kusamvera Mulungu.
Werengani
Genesis 3:15. . . . .
Pamene Mulungu ananena za chiweruzo cha Adamu ndi Hava, anamuuza
kuti mbewu ya
mkazi (wobadwa mwa namwali) 1 adzaphwanya mutu satana ndipo satana
adzalalira
chitendene Chake, kapena kunyula chitendene cha mbewu ya mkazi.
Kupachikidwa ndi
imfa ya Yesu zinali zoipa zimene satana akanachita, koma "anangolalira
chitendene" cha
Yesu chifukwa anauka kwa akufa ndipo anapeza chigonjetso pa satana
ndi imfa.
Tsopano mukuona imfa ndi kuuka kwa Yesu ndikofunika?
Kusamvera kwa satana ndi Adamu kunabweretsa tchimo ndi imfa pa
dziko.
Lye anamwalira pa kupachikidwa anakwiriridwa. mu masiku atatu Anauka
kwa akufa, chimene chinaphwanya mphamvu ya satana pa imfa. Chifukwa
chake, onse otsata Yesu alibe chifukwa choopera imfa. Yesu watenga
kale chilango cha machimo awo, ndipo akamulandira Iye ngati mpulumutsi,
amawapatsa moyo wosatha.
Umboni wa Mbaibulo wa chiukitso cha Yesu imatsimikizira thupi la
Yesu linaukitsidwa kwa
akufa. Titha kuwerenga umboni wa wobodza wa adani a Yesu. Amayesetsa
kuphimba
chimene chinachitika. Werengani Mateyu 28:11-15. . . . .
Zonse zimene adani a Yesu amayenera kuchita kuzizilitsa umboni
wa kuuka kwa thupi
lake Lake kunali kuti zitulutse thupi la kufa! Sakanatha kuchita
izi chifukwa anali ndi moyo!
1. Luka analemba za zimene zidzachitike iye akauka. Werengani
Machitidwe 1:1-11, dzalani mu magawo awa
ndi mawu awa. . . . .
wamoyo |
kumbuyo |
40 |
atumwi |
mtambo |
kumwamba |
kulankhula |
zoyera |
Yesu |
|
|
|
Kwa masiku (40) atauka kwa akufa, Yesu anaonekera
kwa (atumwi) nthawi za
mbiri ndi mjira zosiyana kuonetsera kuti anali ndi (wamoyo).
Anamuona Iye ndipo
analankhula naye. Iye (anauza) iwo za zinthu zimene
zidzachitika.
Tsiku lina, pamene Yesu analankhula nawo, anakwera ku (mwamba)
akumuona.
(Mtambo) unamubisa. Anthu awiri ovala zoyera anawauza (Yesu),
amene watengedwa (kumwamba), (adzabweranso) imnene amuonera
akukwera ku mwamba.
|
Tsegulani ndipo muwerenge Luka 24:36-44. . . . .
Yesu anafunsa ophunzira Ake amukhudze. Yesu anali ndi mnofu ndi mafupa.
Anampatsa chakuday juti adye ndipo anadya Nsomba. Zinali zoona. Yesu
analinso wamoyo!
Thupi lake linali la ulemerero—lopanda malire ngati thupi
la nyama.
2. Baibulo linalemba mowirikiza kuti Yesu anaonekera
kwa anthu atauka kwa
akufa. Werengani ma gawo a Baibulo alipansiwa ndipo mulembe
kwa iwo amene
Yesu aanawaonekera..
a. Yohane 20:14-18. . . . . (Mariya
Magadalena)
b. Luka 24:13-15. . . . . (omutsatira
Yesu awiri)
c. Johane 20:26-29 . . . . . (Thomasi
ndi ophunzira wena)
d. 1 Akolinto 15:5. . . . . (Petulo
kenaka ndi atumwi onse)
e. Yohane 21:1. . . . . (O\ophunzira
pa nyanja ya Tiberiya)
f. 1 Akolinto 15:6. . . . . (500 +)
g. 1 Akolinto 15:7. . . . . (Yakobo
kenaka atumwi onse)
|
Yesu atauka kwa akufa, anali pa dziko mu thupi Lache la ulemerero
kwa masiku makumi
anayi. pa nthawi imeneyo, analankhula ndi okhulupirira ambiri mu
nthawi zosiyana.
Kenaka, kunja kwa mzinda wa Bethany mu kupezeka kwa ena mwa iwo
amamutsatira,
Anawadalitsa ndipo anakwera kumwamba.
3. Yesu alikuti lero? Aheberi
12:2 . . . . . (kukhala pa dzanja la manja la mpando
wa Mulungu) 4. Yesu akutichitira chani lero? Aheberi
7:24-25 . . . . . (Nthawi zonse akutilirira kapena
kutipembedzera.)
|
Baibulo limatiuza kuti kumene kuli Yesu ndikumene kuli Mulungu.
Ndi zoona. Ali ndi moyo.
Thupi lake la ulemerero lidakwera kumwamba komwe Mulungu ali, ali
pa mbali pa
Mulungu.
Koma tsopano mutha kumalingalira, Munene bwanji kuti ali kumwamba
pamene anthu akuti ndinamuitana Yesu kuti alowe mu mtima mwanga
ndipo ndikudziwa ali m'moyo mwanga? Mwakhala mukudabwa. Ngati Yesu
ali kumwamba, angakhalenso bwanji mitima ya anthu nthawi?
Yankho ndi lakuti akukhala mwa ife mwa Mzimu Woyera. Kumbukirani,
mzimu sukhala ndi
mnofu. Mzimu woyera utha kukhala paliponse nthawi imodzi!
Yesu asanapachikidwe anati adzatumiza Mzimu Woyera, amene anamutcha
nkhoswe. Werengani Yohane 14:16-20 . . . . . Tikamuitana
Yesu m'moyo mwathu amwabwera ndi Mzimu woyera kutiphunzitsa ndi
kutitsogolera kuti tipange zisankho za bwino.
Tsekulani Tito 3:4-7 . . . . . Ma vesi awa akutiuza
kuti timapulumutsidwa ndi imfa komanso
kuuka kwa Kristu mwa Mzimu Woyera, amene amatipatsa kubadwa kwa
tsopano.
Nde yankho ku funso loti "Yesu alikuti pano?" ndi funso
losangalatsa limene tinalimva mu
maphunziro athu a sabata ndi sabata pa (Machitidwe 1:9). Ali kumwamba
kutipembedzera ndi kutipempherera, mwa Mzimu Wake akukhala mwa munthu
wina aliyense amene wamulandira m'moyo wake. Timamulandira Yesu
pakulapa ndi kusiya njira zathu zochimwa. Kenaka mphamvu Yake mwa
ife imatithangatira kukhala moyo wosangalatsa Mulungu.
5. Kodi imfa ya Yesu inapindula chani kwa ife?
Aroman 5:8-9. . . . . (Anafa m'malo mwathu
ndi kutipanga ife tikhale pa chiyanjano chabwino ndi Mulungu,
Tate.)
|
Werengani vesi lotsatira Aroma 5:10. . . . . Infa
ya Yesu yatipanga ife abwenzi a Mulungu. tinali adani ake, koma tsopano
zimenezo zinasinthika. Kulandira kwathu pa imfa Yake ndi chiukitso
Chake zitha kutipulumutsa ku zotsatira za tchimo.
Mbali yomaliza ya vesi ili likutibvumbulutsira choonadi chodabwitsa!
Pamene tamuitana Yesu m'moyo mwathu ngari Mpulumutsi ndi Mbuye, sitilinso
chimodzomodzi. Moyo Wake wa chiukitso uli mwa ife ndipo Mzimu Woyera
amakhala mwa ife mu umunthu wathu.
Chifukwa chache nkoyenera kudzipereka kwa Mbuye Yesu. Amwabwera ndi
kukhala
moyo Yake judzera mwa Ife.
Chimenecho ndii chinsinsi cha moyo wa Khristu. Sitingakhale mwa ife
tokha. Palibe angakhale moyo wa tsopano wa Khristu mwa iye yekha.
Ndipokhapokha Yesu mwa inu mutha kukhala moyo wa Chikhristu.
Chisankho nchowonekeratu. Kodi timakhulupiriradi Mulungu anatumiza
Yesu kuti
tikhululukidwe ndi kulandira moyo wosatha? Yohane 3:36 ikuti, Iye
amene akhulupirira Mwanayo ali nao moyo wosatha; koma iye amene
sakhulupirira Mwanayo sadzaona moyo, koma mkwiyo wa Mulungu ukhala
pa iye.
Titha kumadziwa Baibulo ndikuyesetsa kukonza moyo wathu, koma sitingalowe
kumwamba popanda mphamvu ya Mulungu. Timalowa kumwamba popanga chisankho
chokhulupirira ndi chomulandira Yesu kuti ndiye amene ananena kuti
li chimene ali.
Sitikuyenera kuyeretsa moyo wathu tisanabwere kwa Yesu. Titha kubwera
m'mene tilili. Werengani lonjezo lomwe Yesu anapereka kwa iye obwera
kwa Iye.
Tsekulani Yohane 6:37 . . . . .
Lonjezo lina anapereka kwa onse obwera kwa Iye lili pa Mateyu
11:28 . . . . .
Funso 6 likufotokoza za m'mene tingalandirire Yesu. Muwerenga kunyumba.
Koma,
mwina muli ndi funso, tiwerenganso kawiri.
6. Yesu anafa pa mtanda ndi kuukanso kuti
tikakhululukidwe ndi kukhala pa ubale
ndi Iye. Tikuyenera kumfusa Yesu atikhululukire ndi kumuitana
kulowa m'moyo
mwathu. Ichi ndi chinthu chimene tikuyenera kuchita pa tokha.
Palibe angatichitire
ichi. Ngati simukukumbukira nthawi imene munamuitana Yesu
kulowa mu mtima
mwanu mutha kumuitana pompano.
Kuika chikhulupiriro chanu mwa Yesu ndi kulandira chikhululukiro
ndi mphatso ya moyo wosatha.—
a. Zindikirani Yesu anakulengani inu kuti mukakhale pa chiyanjano
ndi Iye. Amakukoni ndipo amafuna inu mumkonde ndi zanu zonse.
b. Zindikirani ndinu ochimwa. Simungadzipulumutse nokha.
c. Khulupirirani Yesu anafa pa mtanda kupereka dipo la tchimo
lanu, kuti anauka kwa akufa, ndipo kuti ali wamoyo lero. Khulupirirani
izi mu mtima mwanu osati mu mutu mwanu mokha.
d. Lankhulani ndi Mulungu m'moyo mwanu:
1) Funsani Yesu alowe m'moyo mwanu.
2) Bvomerezani ndipo mulape machimo anu, zimene zitanthauza
kubwerera ku
machimo anu ndi kutembenukira kwa Mulungu.
3) Mufunseni akhululukire machimo anu.
4) Perekani moyo wanu kwa Yesu. Mloleni akhale mbuye wanu.
e. Uzani ena zimene mwachita.
f. Uzani gulu lanu la za chisankho chanu chimene mwapanga.
g. Ngati mwalandira Yesu Christu ngati mpulumutsi, lembani
tsiku. Ndi tsiku loti
mudzilikumbukira! Ngati munamulandira pa kale, lembani tsiku
limene
munamulandirira (perekani tsiku longoganizira kapena zaka
ngati simuli
otsimikizika za nthawi imene munamulandira Yesu)
|
Kodi alipo ali ndi funso pa za mbali iliyonse ya funso 6?. . . .
.
7.Kodi ma vesi awa amavumbulutsa chani pa za iwo
amene afunsa Yesu Khristu
kuti alowe mu mtima mwawo. a. Agalatiya 2:20 . .
. . . (Khristu amakhala mwa iwo.)
b. 1 Akorinto 3:16-17 . . . . .
1 Akorinto 6:19 . . . . .
(Mzimu wa Mulungu ukhala mwa iwo)
c. Aroma 8:9-11 . . . . . (Mzimu wa
Mulungu umawathandiza kukhala m'moyo wosiyana)
|
Mulungu sakhala mu chinyumba chomanga kapena chalichi. Amakhala
ku mwamba ndi
m'mitima ya anthu. Onani Yesaya 57:15. . . . .
Mzimu woyera wa Mulungu umakhala mwa ife tikamulandira Yesu mmitima
mwathu.
Mulungu anatigula ndi kutilipirira pamene Mwana Wake anafa pa mtanda.
Ndife a
Mulungu. Sitili tokha. Mzimu Woyera mwa ife umatipatsa chikhumbokhumbo
chomvera
Mulungu ndi mphamvu yakuchita chimenecho.
Sabata yatha, tinayamba kuphunzira Machitidwe 4:12. Poti funso
8 inali njira yosavuta
lowonelanso vesi, angakopnde kulinena ndandi?. . . . .
8. Berezani vesi loloweza imene mwapatsidwa polemba
mau obisika m'mene muli
mipata pansipa: Machitidwe 4: (12)
Ndipo palibe (Cipulumutso) mwa wina yense, pakuti
palibe (dzina) lina pansi pa thambo la (kumwamba,)
lopatsidwa mwa (anthu,) limene tiyenera kupulumutsidwanalo.
|
Pakuti pemphero mu funso 9 ndi lapanokha, sizofunikira kuti
mugawane ndi wena.
9. Yamikani Ambuye pakukuwonetserani m'mene mungakhalire
pa ubale ndi Iye.
Mufunseni adziwonetsere Yekha m'moyo wanu. Onjezerani maganizo
anu ndipo
lembani pemphero lanu apa. |
Tsopano, tipemphere kutseka nthawi yathu.
Pemphero Lotsekera
Wokondedwa Mbuye Yesu, taphunzira za mbiri za inu. Zikomo chifukwa
cha Mzimu wanu
Woyera, amene munamutumiza kudzatiphunzitsa ndi kutitsogolera. Tiphunzitseni
njira
zimene tingaphunzitsirrire wena zimene taphunzira. Tiphunzitseni
pamene tikuwerenga
phunziro lomaliza. Tapemphera mu dzina la Lanu, ame.
|