home >>stonecroft>> mayendedwe otsogolera
Stonecroft - Mayendedwe Otsogolera
Mayendedwe Otsogolera
Cholinga
Kufikira — Zophunzirazi zimathandizira kupereka
njira zopindulitsa pa kufalitsa uthenga wa chipulumutso chodzera
mwa Yesu Khristu kwa wena. Iwo amene ali mu gulu alikulumbikitsidwa
kuitana anzao, a mubanja lawo, ogwira ntchito nao limodzi ndi iwo
amene amakhala nawo khomo loyandikana.
Kupanga maphunziro aophunzira —Obadwa kumene
mwatsopano ndi a Khristu okhwima atha kuphunzira za mbiri za Mulungu
ndi kukula mu ubale ndi Iye. Maphunzirowa amafotokoza za m'mene
ungagwiiritsire malemba pa nyengo za tsiku ndi tsiku.
Kusiyana
Chimene chimapangitsa maphunziro a Baibulo a Stonecroft kukhala
osiyana ndi ina onse ndi chani?
• Uthenga wabwino Chipangano cha Tsopano — Maphunzirowa
apangidwa kuti agwiritsidwe ntchito ndi Chipangano cha Tsopano chifukwa
matsamba ake apangidwa kuti kupeza mau ena mbaibulo kusakhale kovuta.
(Manambala a matsamba ndi olingana ndi GoodNews4th Edition Chipangano
cha tsopano) Baibulo la GoodNews ndilovomerezeka ndi mipingo ya
mbiri.
• Maphunzirowa alembedwa mu njira yosavuta kugwiritsa ntchito
kwa iwo amene akuyamba kumene maphunziro a Baibulo pa dziko lonse
la pansi.
• Buku lotsogolera ndi longothandizira, koma si mphunzitsi.
Njira
Maphunziro a Baibulo a Stonecroft ndi osavuta kuwerenga.
Zounikira mu buku lotsogolera zili m'malire. sizikuyenera kuwerengedwa
mokweza. Mau olembedwa mu bokosi alinso mu buku lophunzirira. Izi
zikuyenera kuwerengedwa mokweza ndi iwo amene akuchita nawo maphunziro
a Baibulowa.
Ndandanda wa madontho (. . . . .) umasonyeza kuti buku lotsogolera
limalola gulu kuti litenge nawo mbali pakuyankha funso, kuwerenga
vesi la m'Baibulo ndi kukambirana za phunziroli.
Malembo akuluakulu a mBaibulo, otsatana ndi madontho asanu , akuyimira
vesi imene ikuyenera kuwerengedwa mokweza ndi m'modzi mwa anthu
a pa gulu lanu pamene mukuphunzira. Pamene zosonyezera ma lemba
a m'Baibulo zalembedwa m'malembedwe olembedwa nthawi zonse, zikuthanthauza
kuti ndi zazitali kwambiri kuti ziwerengedwe pa gulu kapena ndizosafunikira
kuti mungapezeko yankho.
Musadayambe Kuphunzira
Zofunikira—
• Khalani obvomerezeka ngati Otsogolera Stonecroft pakutsiriza
ndondomeko yolembera maphunziro a baibulo.
• Phunzirani cholinga, chindunji, ndi mdandanda wa maphunziro.
• Tengani zipangizo zophunzirira za maphunziro anu ku Stonecroft
Ministries-(800) 525-8627.
• Zophunzira zofunikira pa maphunzirowa:
* Mabuku ophunzirira
* Mabuku otsogolera
* Baibulo or the Africa Bible Verse Handbook
for students that do not have their own Bible
* Ukhulupirira? Mabuku ang'onoang'ono a iwo amene akufunsa m'nene
angalandirire Yesu ngati mpulumutsi.
* Makadi a uthenga
• Pezani malo oyenerera ochitira maphunziro anu. Ganizirani
zochitira maphunziro anu mu nyumba, malo ogwirira ntchito, malo
odyera, malo ochezera, malo ogulitsira khofi, ndi ena ambiri.
Konzekerani ma phunziro anu—
• Malizani maphunziro pakulemba mu buku lophunzirira musanawerenge
buku lotsogolera. Izi zikuthandizani kuti kuti mumvetse maganizo
a wena kuti mumvetse mayankho awo.
• Phunzirani kuwerenga maphunziro mokweza, ngati ndikotheka.
Lembani nzere kunsi kwa liwu kapena chiganizo chofunika zimene zikuthandizireni
popereka phunziro ku gulu. Ganizirani nthawi imene muifune powerenga
mau kuti mudziwe nthawi imene mungafune pokambirana.
• Tsimikizirani malo, nthawi, ndi chisamaliro cha mwana,
ngati ndikofunika.
• Pemphererani iwo amene akudzakhala nawo pa maphunziro a
Baibulowo.
Pophunzira mau a Mulungu
Gawani mabuku ophunzirira ndi Chipangano cha Tsopano ndipo mutolele
malipiro. Sonkhani ndalama za pokhalira mwana, ngati nkoyenera.
Tolelani malipiro ndipo ndipo bwezani zipangizo zina zapadela mwansanga.
Yambani phunziro ndi pemphero. Ngati wina anena chofunika kupempherera,
gulu lilembe pa malo olembapo zopempherera ku mbuyo kwa buku lophunzirira
ngati chikumbutso choti chipemphereredwe sabata imeneyo. Ngati chopempherelacho
ndi chofunika mwa nsanga, chipempherereni potsegula ndi pemphero.
Kumbukirani, pakukumana koyamba munthu aliyense adzalemba yankho
lake mu buku lophunzirira pamene mukuphunzira. Limbikitsani gulu
kuwerenga phunziro musanakumane kuti mukumbukire pophunzira.
Werengani ndipo mupereke uthenga mu buku lotsogolera mokambirana,
pamene mukuyang'anana.
Werengani ndi ku phunzirani ndi gulu lonse; simukufunika kukhala
katswiri wa Baibulo.
Buku lotsogolera limaika lokha ndondomeko pa:
• Nthawi yoyamba ndi kutsiriza.
• Kugwiritsa ntchito buku lotsogolera ndi Baibulo ngati zothandizira.
Palibe china choonjezera chimene chimafunika.
• Limbikitsani wina aliyense kuti atengepo mbali ndipo muonetsetse
kuti palibe wina amene akutenga mbali yayikulu pa kulankhula kwambiri
kuposa anzake.
• Pangani maphunzirowa kukhala olunjika pa Yesu Khristu,
osati pa za chiphunzitso cha mpingo, za ndale, kapena za moyo wa
padziko. (DZIWANI: pa za maphunziro a m'matchalitchi, mafunso a
ziphunzitso za mpingo amayankhidwa mu njira zina.)
Yanganani mu gulu mwanu amene angapange zotsogolera zabwino pa
maphunziro akutsogolo.
Ngati otsogolera, khalani chitsanzo chosonyeza nzeru ndi kuganiza
kwa bwino poyankhula. Letsani anthu kuyankhula zinthu zimene zizikuyenera
kulankhulidwa pa gulu. Pambali pa gulu, pempherani nawo ndipo alimbikitseni
afufuze uphungu wa uMulungu oyenerera.
Funsani ophunzirawo kuti aganize za anthu amene angathe kuwaitana
kumaphunziro ena. Alimbikitseni kuti ayambe kupempherera wina ndi
mzake potchula ma ina awo.
Zokumbutsa Zofunika
• Ngati simutha kutsogolera maphunziro pa chifukwa chilichonse,
munthu ovomerezeka ndi wophunzitsidwa akuyenera kulowa m'malo mwanu.
• Mukafuna kudziwa za mbiri zokhudzana ndi ndomdomeko, zipangizo
zophunzirira, kapena m'mene mungachitire, funsani ku Stonecroft
Bible Studies pa (800) 525-8627. Email connections@stonecroft.org
“Khalani a tcheru,
imani molimba mu chikhulupiriro, khalani olimba mtima, khalani amphamvu.
Chitani ntchito zanu zonse mwa chikondi.”
—1 Akorinto 16:13-14
Atsogoleri amatsogolera
|