home >>stonecroft>>mfundo
za paziphuinzitso za m'baibulo>>buku lophunzitsira lotsogolera >>phunziro 1
Buku Lophunzitsira Lotsogolera - Phunziro #1
Baibulo limati
Chani za Yesu?
Yesu ndi
Ndani?
Sauli, munthu wachiyuda amene amamanga ndi kupha akristu
oyambirira, anafunsa funso lofunikira. Ndifunso lofunikira
limene tingafunse. Anafunsa, "Ndinu ndani, Ambuye?"
Analandira yankho pompopompo "
Ndine Yesu amene ukumulondalonda..."
(Machitidwe 9:5).
Munthu waukaliyu (amene anapamgitsa chipolowe mu chalitchi
choyambirira ku Yerusalem) analandira uthenga woyenera, anakhala
munthu wosandulika. Anali atatakasidwa ndi chikhulupiriro
chabodza. Ankaganiza kuti anali kukondweretsa Mulungu pochita
ntchito zake zakupha, koma iye amkalondalonda Iye.
Timachita zomwezo, pamene tikukhulupirira zinthu zimene zili
zabodza. Timachita zinthu zimene zili zoyipa kwa ife eni—nkhakhalenso
kwa anzathu. Njira yokhayo kuti tikhale ndi chidziwitso chenicheni
ndi kuzindikira ndi kukhulupirira choonadi. Maphunziro a Baibulowa
akumana ndi chosowa chanu cha choonadi. Akukankhirani ku chitsime
cha zoonadi zonse, Mau a Mulungu. Mulungu akuti,
“Thambo ndi dziko lapansi
zidzachoka,
koma mau anga sadzachokaHeaven.”
—Mateyu 24:35
Mau a Mulungu ndi oona ndipo adzaima mpaka kalekale. Anthu
ali ndi zidziwitso zolakwika za Yesu. |
People have many incorrect and strange ideas
about Jesus. Since our behavior is influenced and motivated by what
we believe, it is important that we have accurate information about
who Jesus is, who God is and who we are. When you have finished
this study, you will know beyond a shadow of a doubt who Jesus really
is.
Mumakhulupirira kuti Yesu ndi ndani?
Lero timamva maganizo osiyanasiyana. Ena amati ndiye amene anayambitsa
chipembedzo....mtsogoleri wa nkulu wa chikristu...mphunzitsi
wa nkulu wa chikhalidwe...munthu woyamba kuzunzidwa mwankhanza
mum'bado wake.
Titha kudziwa zoona pokhapoka tikakhulupirira uthenga wochokera
ku chitsime cha choonadi. Pali choonadi chimodzi—Mulungu.
Watipatsa ife Buku, limene limatiuza m'mene tingamudziwire
Iye komanso m'mene tingakhalire moyo womusangalatsa Iye ndi
ife.
Yesu sali ngati m'modzi wa atsogoleri a chipembedzo pa dziko
la pansi. Sali ngati munthu wankulu wa m'Baibulo ngati Abraham,
Mose, kapena Davide. Nthawi zonse tikamalemba tsiku kapena
chaka, timazindikira kuti zaka zikwi ziwiri (2000) zapitazo
Yesu Khristu anabwera ndi kugawa mbiri m'magawo awiri:
|
Tsopano, tiwone zimene chipangano chatsopano chimanena za Yesu.
Kumayambiriro kwa utumiki wa Yesu, ngakhale ophunzira ake anafunsa
chimene Yesu anali. Vundukulani pamene pali funso mu chipangano
cha tsopano pa Marko 4:41.....Ophunzira ake adazindikira
kuti sanali munthu wamba. ngakhale m'masiku amenewo, anthu anali
ndi zidziwitso zachilendo za chimene Yesu anali.
Werengani Mateyu 16:13-16.......Anthu amadziwa
sanali munthu wamba. Amadziwa anali winawake wapadeladela. Ankawona
ngati ndi Yohane M'batizi, amene anadulidwa mutu, wa uka kwa akufa.
(Maliko 6:14-16). Ena amati ndi Eliya, m'neneri wa Chipangano cha
Kale amene anatengedwa kunka kumwamba osafa (2 Mafumu 2:11). Poti
a Yuda amayembekezera kuti Eliya adzabweranso, anakhulupirira kuti
Yesu ndi Eliya amene wabweranso ku dziko lapansi. Ena ankaganiza
kuti Yesu ndi Yeremiya—mneneri wina wa Chipangano cha Kale
amene anaphedwa zaka zakale zoyambirira. Onsewo amalakwitsa.
Tsopano, tsatani mu buku lanu lamaphunziro pa tsamba 8 pamene tikuwerenga
gawo lina tsopano kuti tili ndi chidziwitso cha chenicheni cha chimene
Yesu ali , Chimene Mulungu ali, ndi chimene ife tili. Mukamaliza
maphunzirowa, mudziwa chenicheni cha chimene Yesu ali
Baibulo limatiuza zinthu zambiri zodabwitsa za
Yesu. Mwachitsanzo, Yesu analipo chikhalire nthawi isanayambe.
Malo ambiri mu Baibulo amafotokoza Yesu analipo pachiyambi dziko
lisanalengedwe.
Baibulo limati,
“Ndipo Iye ali woyamba wa sonse.
. .”
—Akolose 1:17
|
Yesu analipo asanabadwe ngati munthu.
Wakhala ali chikhalire ndipo adzakhala mpaka muyaya. Palibe
mtsogoleri wa chipembedzo amwene ananena kuti adzakhala muyaya,
koma Yesu ananena. Anati,
“ . . . Asanayambe
kukhala Abraham ndipo 'Ine ndiripo'.”
—Yohane 8:58
Izi zitanthauza Yesu analipo. INE AMENE NDILI ndi dzina la
Mulungu.
Pa Exodo 3:14, zaka zikwi ziwiri Yesu asanabadwe, Mulungu
anadzionetsera Yekha kwa Mose ngati "INE AMENE NDILI"
Muchiheberi dzinali litanthauza kukhala kwa chikhalire.
Yesu anaziyerekeza Yekha ndi Mulungu (Yohane 5:18) |
Chiphunzitso cha Yesu Khristu chinali choonadi. Sanabweze kapena kusintha
zimene ananena. sanakaike, kulota kapena kuyankhula mosatsimikizika.
Kafukufuku wa moyo wake anasonyeza mwa Iye munali umulungu wonse.
Analibe tchimo. Amakhululukira tchimo. Amalandira malambiro.
Zonsezi zikutisonyezera Iye anali Mulungu. Yesu ndi wapadeladela.
Upadeladela wake ukuonetseredwa mwa kubadwa kwache kudzera mwa namwali,
Moyo wake wopanda tchimo, ziphunzitso zache zamphamvu zimene zinatembenuza
dziko. zosenzi zikungosonyeza moyo wake wangwiro.
Kuzindikira Choonadi
Baibulo buku lofunika kuposa buku linalililonse pa dziko lonse.
Kuwerenga Baibulo ndi kulilingalira limabweretsa kusintha kwapamwamba
pa moyo wanu wa uzimu. Pamene muwerenga, kumbukirani ndi uthenga
wa Mulungu kwa inu ngati munthu.
Ganizani mozama ndi mwapemphero za maphunziro
mukuphunzirawa.
zifunseni mafunso awa:
Baibulo pa gawo ili likuti chani?
Zindikirani choona cha Mulungu
Baibulo pa gawo ili likuti chani?
Mvetsetsani chimene Mulungu akunena. |
Mulungu akundilankhula chani?
Chitengeni choonacho muchichite pa moyo wanu.
Mwapempero lingalilani m'mene
Mulungu akufunira kuti Muyankhe
Muvera lamulo kapena kusintha
m'mene mumaonera zinthu?
|
Gulu lilandirane pakuwerenga gulu la ziganizo zotsatilazi
Uthenga
wa Bwino
Mabuku oyambirira a Chipangano cha Tsopano sanalembedwe kukhala
a mbiri ya Yesu. analembedwa ndi anthu osiyanasiyana kwa magulu
osiyanasiyana ndi zifukwa zosiyanasiyana. mabuku amenewa amatchedwa
uthenga wabwino.
Awiri amabukuwa—Uthenga Wabwino wa Mateyu ndi Uthenga
Wabwino wa Yohane—unalembedwa ndi anthu awiri amene
anayenda ndi Yesu kwa zaka zitatu. anali mu gulu la anthu
khumi ndi awiri amene Yesu adawasankha ngati atumwi. Pa mu
chipangano cha Tsopano pali mndandanda wa mau amene akupereka
tanthauzo la mau amene simukuwadziwitsitsa. Onani tanthauzo
la mtumwi. . . . .
Kuyambira pa ndi gawo losonyeza maphunziro. izi zimathandiza
mukafuna kufufuza kuchoka mu Baibulo za phunziro limene mukufuna
kuphunzira. Mateyu adalemba uthenga wa bwino wa Mateyu kutsimikizira
a Yuda kuti iye ndiye Mesiya amene adakhala akumufunafuna.
Yohane adalemba uthenga wabwino wa Yohane kutsimikizira owerenga
kuti Yesu adali Mwana wa Mulungu.
Uthenga wa bwino wa Mariko udalembedwa ndi mnyamata Maliko,
amene adagwira ntchito ndi Paulo komanso Barnaba ndi Petulo.
Marko adalemba kwa amitundu kuwauza za Yesu ndi zimene
adachita.
Uthenga wa bwino wa Luka udalembedwa ndi dotolo wa chihelena
amene anapanga kafukufuku ndi ku fusa anthu amene anali kumudziwa
Yesu.
Chifukwa uthenga wabwino uluonse umalembedwa kwa anthu osiyanasiyana,
onsewo amayimira mbali zosiyana za moyo wa Khristu.
|
Tsopano, tikaona zimene Baibulo limakamba za Yesu Christu kuti ndi
ndani. Pali zambiri zimene zimakamba za Yesu mu Chipangano cha kale
ndi Chipangano cha Tsopano. Tionako zochepa mu chipangano cha tsopano
pompano. Tiyambe ndi funso loyamba mu buku lathu lophunzirira.
Sankhani wina awerenge funso loyamba, werengani za buku limene
likuyenderana ndi Baibulo, funsani funso. Patsani gulu lanu nthawi
yo lemba mayankho mu mau awo mu mabuku awo wophunzirira.
1. Yohane anati chani pomaliza
pa uthenga wake wabwino? Yohane 21:25 . . .
(Use your Bible or Africa Bible
Verse Handbook |
Tikadziwana ndi anthu timafuna tidziwe mayina awo. Mu Baibulo, mayina
amafotokoza za mbiri za munthu kusiyana ndi muchikhalidwe chathu.
Amafotokoza za chimene munthuyo ali ndi zimene amachita. Mbuye wathu
ndi wankulu palibe amene angatiuze zonse zimene tingafune kudziwa
za Iye.
Perekani ma vesiwa kwa anthu osiyanasiyana kuti afufuze. Auzeni
akhale okonzeka kuwerenga akafunsidwa.
Poti pali ma vesi ambiri mu funso lachiwiri, kodi mungakonde kuti
ambiri mwa inu mufufuze vesi ndi kuwerenga ku gulu?
a. Mateyu 1:21
b. Mateyu 1:23
c. Mateyu 3:17
d. Mateyu 12:8
e. Mateyu 16:16
f. Mateyu 19:16
Vesi lililonse likawerengedwa, mutha kulemba dzina kapena mayina
a Yesu mu buku lanu lophunzirira.
2. Ndi mayina ena ati amene Yesu amatchulidwa
mu buku la Mateyu?
a. Mateyu 1:21 . . . . .
|
Chimene Iye amatchedwa? . . . . . (Yesu)
Yesu atanthauza “Mpulumutsi.” Mbali yomaliza ya vesi
tangowerengayi ikutiuza chifukwa chimene Yesu anapatsidwa dzina
limene limathandauza Mpulumutsi. Adzapulumutsa anthu ku dipo limene
akanapereka chifukwa cha machimo awo.
Dzina limene Mulungu adampatsa Iye limatchedwa ndani? . . . . .
(Immanuel)
Vesilo limatiuza za Chimene dzinalo limaimira. Kodi Immanuel atanthauzanji?
. . . . . (Mulungu nafe.)
Mulungu adamutcha ndani? . . . . . (Mwana, Mwana wokondedwa)
Kutanthauza kuti iyeyo ndiye Mwana Yekhayo wa padeladela wa Mulungu
Awa ndi maina awiri amene Yesu anadzitcha Yekha. Mainayo ndi ati?
. . . . .
(Mwana wa Munthu ndi Mbuye wa Sabata)
Yesu amaulura kuti iye ndi munthu komanso ndi Mulungu. Amadzicha
Yekha Mawna wa Munthu ndi
e. Mateyu 16:16 . . . . . |
Mwana wa Mulungu mu malembo ena mbaibulo. Petulo anati Yesu ndi ndani?
. . . . . (Mesiya, Mwana wa Mulungu wa moyo)
Mu vesi 17, Yesu anati Mulungu wavumbulutsira dzina limeneli kwa
Petulo. Mu malingaliro a Yuda, Mesiya amathanthauza mtsogoleri
wodzodzedwa ndi Muliungu.
Mwana wa Mulungu wa moyo amathandauza Yesu anali ofana
ndi Mulungu ndipo ndi wachikhalire ndi Mulungu.
Amatchedwa Yani? . . . . . (Mphunzitsi) Mphunzitsi amavumbulutsa
choonadi, ndipo Yesu anavumbulutsa choonadi.
Funso lotsatira likutipatsa maina ambiri a Yesu. Dzina linalililonse
latsopano likubvumbulutsa chikhalidwe chimene chikufotokoza za Iye
momveka bwino. Lembani mainawa mu buku lanu lophunzirira pamene
tikupitirira kuphunzira.
Poti pali mavesi ambiri pa funso la chitatu, wina aliyense asankhe
vesi limodzi kuti awerenge:
a. Marko 5:6-7
b. Luka 5:5
c. Yohane 1:35-36
d. John 1:49
e. 1 Akolinto 1:6-7
Kodi wina akonda kuti ayambe kutiwertengera funso lachitatu ndi
kuona mu buku lathu limene limayenderana ndi Baibulo mu gawo "a."?
3. Kodi Yesu amatchedwa yani mu mabuku
limene likuyenderana ndi Bailo?
a. Marko 5:6-7. . . . . |
Yesu amatchedwa ndani? . . . . . (Yesu Mwana wa Mulungu wa M'wamba
W'wamba)
Yesu ndi dzina lache la padziko lino. Ngati Mwana wa Mulungu wa
M'wamba M'wamba , ndi woyenera kulambilidwa ndi ife. Simoni Petulo
anamutcha ndani? . . . . . (Mbuye)
What did Simon Peter call Him? .... (Master)
Yesu ndi amene akhristu amamutumikira. ngati wokhulupirira, ndife
adzakazi ake..
c. Joyane 1:35-36 . . . . . |
Yohane m'batizi anati Yesu ndi ndani? . . . . . (Mwana wa Nkhosa
wa Mulungu)
Dzina ili limasonyeza Yesu kukhala nsembe ya ngwiro yotumizidwa
kukaphedwa chifukwa cha matchimo a anthu onse kulikonse ali. Pa
Aloma 6:23 mphoto ya uchimo ndi imfa. Nsembe ya nkhosa mu Chipangano
cha Kale (Levitiko 14:12-13) ikuyimirira infa ya Yesu Khristu. Mulungu
anati adzatumiza nsembe ya ngwiro kukafera m'malo a anthu ochimwa.
Chifukwa chake Yesu amatchedwa Mwanawankhosa wa Mulungu
Mwana wa Nkhosa Mulungu. Kodi ndi maina awiri ati amene Natanieli
anamucha Yesu pa tsambali? . . . . . (Mwana wa Mulungu, Mfumu
ya Israeli)
e. 1 Akolinto 1:6-7 . . . . . |
Paulo anamutcha yani apa? . . . . . (Mbuye Yesu Khristu)
Awa ndi maina atatu amene amakonda kugwiritsidwa ntchito ngati
dzina limodzi. Tikamutcha mbuye, tikutanthauza tikugongera ku utsogoleri
ndi ulamuliro wake wa u Mbuye.
Pali mayina ambiri okamba za Yesu amene tikanatha kuona kuti kodi
Yesu ndi ndani?
Ophunzira amamucha Mbuye, Mphunzitsi. Anapereka moyo wawo ku ulamuliro
wake. Mutha kufunsa, "Kodi Baibulo ndi buku lokhalo limene
limatidziwitsa za Yesu."
Ayi, pali mabuku ena akale ambiri amene amatiuza za chimene Yesu
anali. Si Baibulo lokha limene lingati phunzitse za Yesu—ngakhale
kuti Baibulo ndi buku lokhalo limene limafotokoza za choonadi cha
Yesu. Pali olemba ambiri amene analemba za Yesu ndi zimene amachita
zo sintha moyo wa anthu mu nyengo Yake. nagati miukufuna kuwerenga
phunzirori, muwerenge buku lotchedwa Evidence That Demands a Verdict
lolembedwa ndi Josh McDowell.
Mukaona kuti mau obvuta kufotokoza kapena kunena mu Buku lano
lotsogolera, musade nazo nkhawa pa za katchulidwe ka mauwo. Pitilizani.
Titha kuphunzira kuti Yesu ndi ndani pogwiritsa ntchito mabuku
a chiyuda kapena achikunja. Ambiri olemba zambiri amamutcha Yesu
ngati choonadi cha mbiri. Pali mabuku atatu ambiri: Makalata a Pliny
(PLEHN-ee), amene anali govanala wa ku Asia; mabuku a Tacitus (TAS-ih-tuhs),
amene anali katsiri wotsogola wa malamulo ndi Lives of the Caesars
wolemba Suetonius (swee-TOH-nee-uhs), amene anali wophunzira
ndi wolemba za mbiri ya munthu. Adziwa za mbiri a ku Romawa analemba
za Yesu ndi za ophunzira ake.
Josephus (Joh-SEE-fus), Wodziwa za mbiri wa chi
Yuda amene anabadwa mu chaka cha A.D. 37 amene anali wosakhulupirira
, analemba zoona za kupachikidwa kwa Yesu. Ngakhale kuti Josephus
samakhulupirira kuti Yesu ndi Mesiya, analemba izi zokhudzana
ndi Yesu:
“Tsopano, panali munthu uyu wa nzeru , ngati nkoyenera
kumutcha munthu, poti anali wochita ntchito za bwino, mpunzitsi
wa anthu wa choonadi. Anakopa Ayuda ngakhale a Mitundu. Anali
Khristu, ndipo pamene Pilato pa kukhumba kwa anthu akuluakulu
mwa ife, analamula apachikidwe pa mtanda, iwo anankonda Iye
poyamba sanantaye; poti anaonekeranso kwa iwo wamoyo pa tsiku
la chitatu, monga momwe aneneri a uzimu analoserandi zikwi
khumi za zinthu zodabwitsa zokhudza Iye. Ndipo mtundu wa Akhristu
wotchedwa chifukwa cha Iye ukanalipo osatha mpaka lero.”
—Antiquities
|
Mu buku lache lotchedwa Evidence That Demands a Verdict,
Josh McDowell akuti wosakhulupirira amene wafufuza za Yesu atha
kudziwa mosakayika kuti Chipangano Cha Tsopano chitha kudalilika
pa zokamba zake za Yesu. Wofufuza mwa chilungamo zanganyozere kapena
kulimbikitsa zimene ena amanena kuti nkhani ya Yesu ndi nthano kapena
zikhulupiriro chabe. Josh McDowell anati kufotokoza mwachindunji
za Yesu sikungasokonewzedwe ."
Ndi maumboni ambiri zopezekeratu, tikuyenera kukhala ndi chitsimikizo
chachikulu cha zimene Baibulo limanena za moyo wa Yesu.
Baibulo lonse limafotokoza za Yesu Christu Ma buku 39 oyambirira
a Chipangano Cha Kale, amapereka mauneneri ambiri okhudzana ndi
Iye. Ma buku ena onse 27 a Chipangano cha Tsopano, amafotokoza za
mbiri ya moyo Wake pa dziko lapansi ngakhalenso moyo wake atauka
kwa akufa. Mabuku anayi a Uthenga Wabwino —Mateyu, Marko,
Luka, ndi Yohane—amapanga pafupifupi theka la Chipangano cha
Tsopano. Ali ndi zambiri zofotokoza za Yesu.
Maumboni ena a mphamvu okhudza choonadi cha Baibulo amaonetseredwa
kudzera mu mauneneri a Chipangano cha kale kukwaniritsidwa mu Chipangano
Cha Tsopano. Chipangano cha Kale chili ndi mazana amauneneri okhudza
kubwera kwa Mesiya, Yesu Khristu.
Tsopano tiyamba kuwerenga mulandirana mu ma buku athu ophunzirira.
Ndiwerenga uneneri ndi kufaniziridwa kwake mu Chipangano Cha Kale.
Ndipo mutha kumalandirana powerenga kukwaniritsidwa kwake mu chipangano
cha tsopano.
Ma uneneri ochepa okhudza
Mesiya
Uneneri |
Kukwaniritsidwa |
Adzabadwa mwa namwali. |
Kubadwa mwa namwali Yesu |
Yesaya 7:14
(742B.C.)
Chifukwa chache Ambuye mwini yekha
adzakupatsani chizindikiro, taonani namwali
adzaima, nadzabala mwana wa mwamuna,
nadzamucha dzina lache Imanueli. (NASB)
|
Mateyu 1:22-23
Ndipo zonsezi zinakhala kuti chikachitidwe chonenedwa ndi
Ambuye mwa mneneri, ndi kuti, Onani namwali adzaima, nadzabala
mwana wa mwamuna dzina lace, Emanueli;
(ndilosandulika, “Mulungu nafe”). |
Malo ake obadwira
|
Kubadwa kwa Yesu mu Betelehem.
|
Micah 5:2 (710B.C.)
Ambuye akuti, “Betelehemu Efrata, ndiwe
wa ngono kuti ukhale mwa zikwi za Yuda, mwa iwe mudzatuluka
wowereza mu Israyeli;
matulukiro ake ndiwo a kale lomwe, kuyambira nthawi yosayamba.
|
Mateyu 2:1a
Yesu adabadwa mu mzinda
wa Betelehemu wa Yudea mu nthawi imene Herodi adali mfumu. |
Adzakanidwa ndi anthu Ache.
|
Yesu adakanidwa.
|
Isaiah 53:3 (712B.C.)
Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu; munthu wa zisoni,
ndiwodziwa zowawa; ndipo ananyozedwa monga munthu ombisira
anthu nkhope zao; ndipo ife sitinamulemekeza. |
Yohane 1:11
Anadza kwa zache za Iye yekha, koma dziko silidamuzindikira
Iye. |
Adzaperekedwa ndi bwenzi |
Yesu adaperekedwa ndi m'modzi mwa ophunzira.
|
Salimo 41:9 (1062B.C.)
Ngakhale bwenzi langa leni leni, amene
ndamkhulupirira, ndiye amene anadyako mkate wanga, adandikwezera
chidendene chache. |
Marko 14:10
Ndipo Yudase Iskariote, ndiye mmodzi wa khumi ndi awiriwo, anachoka
napita kwa ansembe akulu, kuti akampereke Iye kwa iwo. |
Adzauka kwa akufa. |
Yesu anauka patatha masiku atatu m'manda. |
Salimo 16:10 (1040
B.C.) …akuti simudzasiya moyo wanga kumanda;
simudzalora okondedwa wanu avunde. |
Mateyu 28:5-6
Koma ngelo anayankha nati kwa akaziwo,
"Musaope inu; pakuti ndidziwa inu muli kufuna Yesu, amene
anapachikidwa. Iye mulibe muno iai; pakuti anauka, monga ananena
.idzani muno mudzaone malo omwe anagonamo Ambuye.” |
Ma ulosi onse anakwaniritsidwa mwa Christu, ngakhale anali opyoza
umunthu wa Yesu.
Onani funso 4.
4. Ziganizo zili mmusimu zikukamba za mbiri za Yesu. Onani pa
mafunso oti
muyankhe, ndi zofananiza malemba a chiganizo ndi mau oyenerera
mbaibulo:
a. Makolo Ake .......................b. Ubatizo Wake .....................c.
Wake choyamba chake
|
Glance over
Mateyu 1:1-17. . . . . (a Makolo Ake)
|
Ngati wina ali ndi funso pa za mbado wa Yesu, zitha kuthandiza
mutafotokoza izi:
“Mateyu 1:16: Chifukwa choti Maria anatenga pakati akanali
namwali, Mateyu akunena
za Yosefe ngati mwamuna wa Maria, koma osati bambo a Yesu. Mbado
wolembedwa
ndi Mateyu akufotokoza (mbando wobvomerezeka) kudzera mwa Yosefe.
Mbado wa
Maria unalembedwa pa Luka 3:23-38.Maria ndi Yosefe anali mu mbado
wa Davide.
Mateyu akufotokoza za mbado kuyambira kwa Abraham, Pamene Luka
akuyambira kwa
Adam.. Mateyu akulembera kwa Ayuda, nde Yesu akuonetsedwa ngati
ochokera kwa
Tate wao Abraham. Luka akulembera kwa Amitundu, nde akufotokoza
za Yesu ngati
Mpulumutsi wa anthu onse.”
Glance over
Yohane 2:1-11. . . . . Read verse
11 (c Wake choyamba chake)
|
Read Marko 1:9-11
. . . . .(b Ubatizo Wake) |
Chipangano cha tsopano chanu chimakuwuzani za moyo wa Yesu ndi
m'mene mungakhalire m'moyo wa Chikhristu.
When we need to read parts of the Old Testament
refer to the Africa Bible Verse Handbook if you do not have a Bible.
Mbuye Yesu Christu ndi Mulungu nafe. Titha kuona kuti ndi Mulungu.
Titha kuona kuti ndi
Mulungu tikawerenga ulosi wa kubadwa kwache ku Yesaya 9:6
. . . . . Onani Yesu
akutchedwa Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wa mphamvu, Atate wosatha,
Kalonga wa
Mtendere.
Ndimayina ati amene ali mainanso a Mulungu? . . . . .
(Mulungu wa mphamvu ndi Atate Wosatha)
Baibulo limatiuza za mbiri za Yesu ndipo kufotokozera kwina kwa
mphamvu kuli mu
Chipangano cha Tsopano pa Akolose 1:15-20. Onani
zonse zimene zanenedwa za Yesu monga pa mavesi awa.. . . . .
Fundo ya yikulu tikuipeza pa vesi 15.
“Khristu ndi fanizo la Mulungu wosaonekayo..."
—Akolose 1:15
|
Tangolingalirani mphamvu ya fundoyi!
Sabata la mawa tidzaphunzira phunziro 2. Tidzaphunzira zimene Yesus
ananena za Iye ndi
zimene anaphunzitsa. Mudzawerenga chiphunzitso cha Yesu pamene muwerenga
Baibulo pa lanu pa tsamba 15. Musanabwere sabata ya mawa, yankhani
funso mu Buku lanu
Lophunzirira.
Muli ndi funso?
Sangalalani ndi phunziro la sabata ya mawa. Tiyeni tiyamike Mulungu
chifukwa cha danga
lophunzira mau Ake.
Pemphero Lotseka
Zikomo Ambuye Mulungu. Taphunzira za mbiri za Yesu mu phunziro
ili. Tiphunzitseni za mbiri pamene tikupitiliza maphunziro awa.
Tithanndizeni kupeza nthawi yowerenga phunziro ya sabata ya mawa.
Tapemphera mu dzina la Yesu, ame.
|