Project Hope     home >>stonecroft>> mavesi a m'baibulo >> phunziro 5 >> phunziro 6
YESU NDI NDANI? - Mavesi a m'Baibulo - Phunziro #6
Women's Empowerment Program
Sports Bible Club
Living Water Bible Club

Kuwerenga Baibulo kwa Mlungu ndi Mlungu

Yohane 1:14-18
14Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wace, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi cisomo ndi coonadi.
15Yohane acita umboni za iye, napfuula nati, Uyu ndiye amene ndinanena za iye, Wakudzayo pambuyo panga analipo ndisanabadwe ine; cifukwa anakhala woyamba wa ine. 16Cifukwa mwa kudzala kwace tinalandira ife tonse, cisomo cosinthana ndi cisomo. 17Cifukwa cilamulo cinapatsidwa mwa Mose; cisomo ndicoonadi zinadza mwa Yesu Kristu. 18Kulibe munthu anaona Mulungu nthawi zonse; Mwana wobadwa yekha wakukhala pa cifuwa ca Atate, Iyeyu anafotokozera.

Yohane 14:1-11
1Mtima wanu usabvutike; mukhulupirira Mulungu, khulupirirani Inenso.2M'nyumba ya Atate wanga alimo malo okhalamo ambiri. Ngati sikudali kutero, ndikadakuuzani inu; pakuti ndipita kukukonzerani inu malo. 3Ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa Ine ndekha; kuti kumene kuli Ineko, mukakhale inunso. 4Ndipo kumene ndinkako Ine, mudziwa njira yace. 5Tomasi ananena ndi Iye, Ambuye, sitidziwa kumene munkako; tidziwa njira bwanji? 6Yesu ananena naye, ine ndinenjira, ndi coonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.
7Mukadazindikira ine mukadadziwa Atate wanganso; kuyambira tsopano mumzindikira iye, ndipo mwamuona iye. 8Filipo ananena ndi iye, Ambuye, tionetsereni ife Atate, ndipo citikwanira. 9Yesu ananena naye, Kodi ndiri ndiinu nthawi yaikuru yotere, ndipo sunandizindikira, Filipo? iye amene wandiona Ine waona Atate; unena iwe bwanji, Mutionetsere Atate? 10Sukhulupirira kodi kuti ndiri Ine mwa Atate, ndi Atate ali mwa Ine? Mau amene ndinena Ine kwa inu sindilankhula kwa Ine ndekha; koma Atate wokhala mwa Ine acita nchito zace.11Khulupirirani Ine, kuti Inendiri mwa Atate ndi Atate ali mwa Ine; koma ngati si comweco, khulupirirani Ine cifukwa ca nchito zomwe.

1 Yohane 5:10-12
10Iye amene amkhulupirira Mwana wa Mulungu ali nao umboni mwa iye; ye wosakhulupirira Mulungu ananuyesa iye wonama; cifukwa sanakhulupirira umboni wa Mulungu anaucita wa Mwana wace. 11Ndipo uwu ndi umboniwo, kuti Mulungu anatipatsa ife moyo wosatha, ndipo moyo umene uli mwa Mwana wace. 12Iye wakukhala ndi Mwana ali nao moyo; wosakhala ndi Mwana wa Mulungu alibe moyo.

Mateyu 16:24-27
24Pomwepo Yesu anati kwa ophunzira ace, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge mtanda wace, nanditsate Ine.25Pakuti iye amene afuna kupulumutsa moyo wace adzautaya: koma iye amene ataya moyo wace cifukwa ca Ine, adzaupeza. 26Pakuti munthu adzapindulanji, akalandira dziko lonse, nataya moyo wace? kapena munthu adzaperekanji cosintha ndi moyo wace? 27Pakuti Mwana wa munthu adzabwera mu ulemerero wa Atate wace, pamodzi ndi angelo ace; ndipo pomwepo Iye adzabwezera kwa anthu onse monga macitidwe ao.

Afilipi 2:5-11
5Mukhale nao mtima m'kati mwanu umene unalinso mwa Kristu Yesu, 6ameneyo, pokhala nao maonekedwe a Mulungu, sanaciyesa colanda kukhala wofana ndi Mulungu,7koma anadzikhuthula yekha, natenga maonekedwe akapolo, nakhala m'mafanizidwe a anthu; 8ndipo popezedwa m'maonekedwe ngati munthu, anadzicepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya pamtanda.9Mwa icinso Mulungu anamkwezetsa iye, nampatsa dzina limene liposa maina onse, 10kuti m'dzina la Yesu bondo liri lonse lipinde, la za m'mwamba ndi za padziko, ndi za pansi pa dziko, 11ndi malilime onse abvomere kuti Yesu Kristu ali Ambuye, kucitira ulemu Mulungu Atate.

1 Atesolonika 4:15-18
15Pakuti ici tinena kwa inu m'mau a Ambuye, kuti ife okhala ndi moyo, otsalira kufikira kufikanso kwa Ambuye, sitidzatsogolera ogonawo.

16Pakuti Ambuye adzatsika Kumwamba mwini yekha ndi mpfuu, ndi mau a mngelo wamkuru, ndi lipenga la Mulungu; ndipo akufa mwa Ambuye adzayamba kuuka; 17pamenepo ife okhala ndi moyo, otsalafe, tidzakwatulidwa nao pamodzi m'mitambo, kukakomana ndi Ambuye mumlengalenga, ndipo potero tidzakhala ndi Ambuye nthawi zonse. 18Comweco, tonthozanani ndi mau awa,

Yohane 5:24-29
24Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti iye wakumva mau anga, ndi kukhulupirira iye amene anandituma Ine, ali nao moyo wosatha, ndipo salowa m'kuweruza, koma wacokera kuimfa, nalowa m'moyo. 25Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti ikudza nthawi, ndipo Iripo tsopano, imene akufa adzamva mau a Mulungu; ndipo iwo akumva adzakhala ndi moyo. 26Pakuti monga Atate ali ndi moyo mwa iye yekha, momwemonso anapatsa kwa Mwana kukhala ndi moyo mwa iye yekha; 27ndipo anampatsa iye mphamvu ya kucita mlandu, pakuti ali Mwana wa munthu.28Musazizwe ndi ici, kuti ikudza nthawi, imene onse ali m'manda adzamva mau ace, 29nadzaturukira, amene adacita zabwino, kukuuka kwa moyo; koma amene adacita zoipa kukuuka kwa kuweruza.

1. b. Mateyu 22:36-40
36Mphunzitsi, lamulo lalikuru ndi liti la m'cilamulo? 37Ndipo Yesu anati kwa iye, Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse. 38Ili ndilo lamulo lalikuru ndi loyamba. 39Ndipo laciwiri lolingana nalo ndili, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini. 40Pa malamulo awa awiri mpokolowekapo cilamulo conse ndi aneneri.

c. Marko 10:45
45Pakuti ndithu, Mwana wa munthu sanadza kutumikiridwa, koma kutumikira, ndi kupereka moyo wace dipo la kwa anthu ambiri.

3. Chibvumbulutso 1:7
7Taonani, adza ndi mitambo; ndipo diso liri lonse lidzampenya iye, iwonso amene anampyoza; ndipo mafuko onse a pa dziko adzamlira iye. Terotu. Amen.

Yohane 19:33-34
33koma pofika kwa Yesu, m'mene anamuona iye, kuti wafa kale, sanatyola miyendo yace; 34koma mmodzi wa asilikari anamgwaza ndi nthungo m'nthiti yace, ndipo panaturuka pomwepo mwazi ndi madzi.

4. a. Mateyu 24:21-31
21pakuti pomwepo padzakhala masauko akuru, monga sipadakhale otero kuyambira ciyambi ca dziko, kufikira tsopano, inde ndipo sipadzakhalanso. 22Ndipo akadaleka kufupikitsidwa masiku awo, sakadapulumuka munthu ali yense: koma cifukwa ca osankhidwawo masiku awo adzafupikitsidwa. 23Pomwepo munthu akanena kwa inu, Onani, Kristu ali kuno, kapena uko musambvomereze;24cifukwa Akristu onama adzauka, ndi aneneri onama nadzaonetsa zizindikiro zazikuru ndi zozizwa: kotero kuti akanyenge, ngati nkotheka, osankhidwa omwe. Onani ndakuuziranitu pasadafike. 25Cifukwa cace akanena kwa inu, Onani, Iye ali m'cipululu; musamukeko. 26Onani, ali m'zipinda; musabvomereze. 27Pakuti monga mphezi idzera kum'mawa, nionekera kufikira kumadzulo; kotero kudzakhalanso kufika kwace kwa Mwana wa munthu. 28Kumene kuli konse uli mtembo, miimba Idzasonkhanira konko.
29Koma pomwepo, atapita masauko a masiku awo, dzuwa lidzadetsedwa, ndi mwezi sudzaonetsa kuwala kwace, ndi nyenyezi zidzagwa kucokera kumwamba, ndi mphamvu za kumwamba zidzagwedezeka: 30ndipo pomwepo padzaoneka m'thambo cizindikiro ca Mwana wa munthu; ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzadziguguda pacifuwa, nidzapenya Mwana wa munthu alinkudza pa mitambo ya kumwamba, ndi mphamvu ndi ulemerero waukuru. 31Ndipo Iye adzatumiza angelo ace ndi kulira kwakukuru kwa lipenga, ndipo iwo adzasonkhanitsa osankhidwa ace ku mphepo zinai, kuyambira malekezero a thambo kufikira malekezero ace ena.

b. Marko 13:32-37
32Koma za tsiku ilo, kapena nthawi yace sadziwa munthu, angakhale angelo m'Mwamba, angakhale Mwana, koma Atate ndiye. 33Yang'anirani, dikirani, pempherani: pakuti simudziwa nthawi yace. 34Monga ngati munthu wa paulendo, adacoka kunyumba kwace, nawapatsa akapolo ace ulamuliro, kwa munthu ali yense nchito yace, nalamulira wapakhomo adikire.
35Cifukwa cace dikirani; pakuti simudziwa inu nthawi yace yakubwera mwini nyumba, kapena madzulo, kapena pakati pausiku, kapena pakulira tambala, kapena mamawa; 36kuti angabwere balamantha nakakupezani muli m'tulo.37Ndipo cimene ndinena ndi inu ndinena kwa onse, Dikirani.

c. Luka 21:25-28, 34-36
28Komapoyamba kucitika izi weramukani, tukulani mitu yanu; cifukwa ciomboledwe canu cayandikira.
34Koma mudziyang'anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha; 35pakuti Iidzatero ndi kufikira anthu onse akukhala pankhope pa dziko lonse lapansi. 36Koma inu dikirani nyengo zonse ndi kupemphera, kutimukalimbike kupulumuka zonse zimene zidzacitika, ndi kuimirira pamaso pa Mwana wa munthu.

5. Ahebri 9:27
27Ndipo popeza 8 kwaikikatu kwa anthu kufa kamodzi, ndipo 9 atafa, ciweruziro;

6. a. 2 Akorinto 5:10
10Pakuti ife tonse tiyenera kuonetsedwa ku mpando wa kuweruza wa Kristu, kuti yense alandire zocitika m'thupi, monga momwe anacita, kapena cabwino kapena coipa.

b. Machitidwe 17:30-31
30Nthawi za kusadziwako tsono Mulungu analekerera; koma tsopanotu alinkulamulira anthu onse ponse ponse atembenuke mtima; 31cifukwa anapangira tsiku limene adzaweruza dziko lokhalamo anthu m'cilungamo, ndi munthu amene anamuikiratu; napatsa anthu onse citsimikizo, pamene anamuukitsa iye kwa akufa.

c. Chibvumbulutso 20:11-15
11Ndipo ndinaona, mpando wacifumu waukuru woyera, ndi iye wakukhalapo, amene dziko ndi m'mwamba zinathawa pamaso pace, ndipo sanapezedwamalo ao. 12Ndipo ndinaona akufa, akuru ndi ang'ono alinkuima ku mpando wacifumu; ndipo mabuku anatsegulidwa; ndipo buku lina Iinatsegulidwa, ndilo la moyo; ndipo akufa anaweruzidwa mwa zolembedwa m'mabuku, monga mwa nchito zao. 13Ndipo nyanja inapereka akufawo anali momwemo, ndipo imfa ndi Hade zinapereka akufawo anali m'menemo; ndipo anaweruzidwa yense monga mwa nchito zace, 14Ndipo imfa ndi Hade zinaponyedwa m'nyanja yamoto. Iyo ndiyo imfa yaciwiri, ndiyo nyanja yamoto. 15Ndipo ngati munthu sanapezedwa wolembedwa m'buku la moyo, anaponyedwa m'nyanja yamoto.

1 Timoteyo 2:3-4
3Pakuti ici ncokoma ndi colandirika pamaso pa Mulungu Mpulumutsi wathu; 4amene afuna anthu onse apulumuke, nafike pozindikira coonadi.

Mateyu 25:41
41Pomwepo Iye adzanena kwa iwo a ku dzanja lamanzere, Cokani kwa Ine otembereredwa inu, ku mota wa nthawi zonse wokolezedwera mdierekezi ndi amithenga ace:

Afilipi 2:10-11
10kuti m'dzina la Yesu bondo liri lonse lipinde, la za m'mwamba ndi za padziko, ndi za pansi pa dziko, 11ndi malilime onse abvomere kuti Yesu Kristu ali Ambuye, kucitira ulemu Mulungu Atate.

1 Yohane 2:15-17
15Musakonde dziko lapansi, kapena za m'dziko apansi. Ngati wina akonda dziko lapansi, cikondi ca Atate lsiciri mwa iye. 16Pakuti ciri conse ca m'dziko lapansi, cilakolakoca thupi ndi cilakolako ca maso, matamandidwe a moyo, sizicokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi. 17Ndipo dziko lapansi lipita, ndi cilakolako cace; koma iye amene acita cifuniro ca Mulungu akhala ku nthawi yonse.

2 Akolinto 5:17
17Cifukwa cace ngati munthu ali yense ali mwa Kristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano,

1 Yohane 1:8-10
8Tikati kuti tiribe ucimo, tidzinyenga tokha, ndipo mwa ife mulibe coonadi.9Ngati tibvomereza macimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama iye, kuti atikhululukire macimo athu, ndi kutisambitsa kuticotsera cosalungama ciri conse.10Tikanena kutisitidacimwa, timuyesa iye wonama, ndipo mau ace sakhala mwa ife.

1 Yohane 4:7-11
7Okondedwa, tikondane wins ndi mnzace: cifukwa kuti cikond cicokera kwa Mulungu, ndipo yense amene akonda, abadwa kucokera kwa Mulungu, namzindikira Mulungu, 8iye wosakonda sazindikira Mulungu; cifukwa Mulungu ndiye cikondi. 9Umo cidaoneka cikondi ca Mulungu mwa ife, kuti Mulungu anamtuma Mwana wace wobadwa yekha alowe m'dziko lapansi, kuti tikhale ndi moyo mwa iye. 10Umo muli cikondi, sikuti ife tinakonda Mulungu, koma kuti iye anatikonda ife, ndipo anatuma Mwana wace akhale ciombolo cifukwa ca macime athu. 11Okondedwa, ngati Mulungu anatikonda ife kotero, ffenso tiyenera kukondana wina ndi mnzaceo

7. a. 2 Akorinto 7:1
1Pokhala nao tsono malonjezano amenewa, okondedwa, tidzikonzere tokha kuleka codetsa conse ca thupi ndi ca mzimu, ndi kutsirfza ciyero m'kuopa Mulungu.

b. Mateyu 6:19-21
19Musadzikundikire nokha cuma pa dziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri ziononga; ndi pamene mbala ziboola ndi kuba: 20koma mudzikundikire nokha cuma m'Mwamba, pamene njenjete kapena dzimbiri siziononga, ndipo mbala siziboola ndi kuba; 21pakuti kumene kuli cuma cako, komwe udzakhala mtima wakonso.

1 Yohane 2:16-17
16Pakuti ciri conse ca m'dziko lapansi, cilakolakoca thupi ndi cilakolako ca maso, matamandidwe a moyo, sizicokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi. 17Ndipo dziko lapansi lipita, ndi cilakolako cace; koma iye amene acita cifuniro ca Mulungu akhala ku nthawi yonse.

c. Yakobo 1:2-4
2Muciyese cimwemwe cokha, abale anga, m'mene mukugwa m'mayesero a mitundu mitundu; 3pozindikira kuti ciyesedwe ca cikhulupiriro canu cicita cipiriro.

d. 2 Timothy 4:1-5
1Ndikucitira umboni pamaso pa Mulungu ndi Kristu Yesu, amene adzaweruza amoyo ndi akufa, ndi pa maonekedwe ace ndi ufumu wace; 2lalikira mau; cita nao pa nthawi yace, popanda nthawi yace; tsutsa, dzudzula, cenjeza, ndi kuleza mtima konse ndi ciphunzitso. 3Pakuti idzafika nthawi imene sadzalola ciphunzitso colamitsa; komatu poyabwa m'khutu adzadziuniikitsa aphunzitsi monga mwa zilakolako za iwo okha: 4ndipo adzalubza dala pacoonadi, nadzapatukira kutsata nthanu zacabe. 5Koma iwe, khala maso m'zonse, imva zowawa, cita nchito ya mlaliki wa Uthenga Wabwino, kwaniritsa utumiki wako.

e. 1 Akorinto 15:58
58Cifukwa cace, abale anga okondedwa, khalani okhazikika, osasunthika, akucuruka mu ncbitoya Ambuye, nthawi zonse, podziwa kuti kucititsa kwanu sikuli cabe mwa Ambuye.

Masalimo 16:11
11Mudzandidziwitsa njira ya moyo: Pankhope panu pali cimwemwe cokwanira; M'dzanja lanu lamanja muli zokondweretsa zomka muyaya.

 

 
 

 

YESU NDI NDANI?

Mavesi a m'Baibulo

 
 
Copyright ©  2023 www.UnitedCaribbean.com. All rights reserved. Disclaimer Click to Contact us