Stonecroft
Stonecroft Training
Mndandanda wa Utatu
Malangizo Otsogolera
Mavesi a m'Baibulo
Adult Stonecroft International
The International Team
English YDT Teachings
Maphunziro a Ana
Malawi Moringa Projects
|
|
home >>stonecroft>>
kodi yesu ndani? >> mavesi a m'baibulo >> phunziro 1
YESU NDI NDANI? - Mavesi a m'Baibulo - Phunziro #1
Machitidwe 9:5
Koma anati, Ndiouyani Mbuye? Ndipo anati, Ndine Yesu amene umlondalonda;
Marko 4:41
41Ndipo iwo anacita mantha akuru, nanenana wina ndi mnzace, Uyu
ndani nanga, kuti ingakhale mphepo ndi nyanja zimvera Iye?
Mateyu 16:13-16
13Ndipo Yesu, pamene anadza ku dziko la ku Kaisareya wa Filipi,
anafunsa ophunzira ace, kuti, Anthu anena kuti Mwana wa munthu ndiye
yani? 14Ndipo iwo anati, Ena ati, Yohane Mbatizi; koma ena, Eliya;
ndipo enanso Yeremiya, kapena mmodzi wa aneneri. 15Iye ananena kwa
iwo, Koma inu mutani kuti Ine ndine yani? 16Ndipo Simoni Petro anayankha
nati, Inu ndinu Kristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.
Maliko 6:14-16
14Ndipo mfumu Herode anamva izi; pakuti dzina lace lidamveka; ndipo
ananena, kuti, Yohane Mbatizi wauka kwa akufa, ndipo cifukwa cace
mphamvu izi zicitacita mwa Iye. 15Koma ena ananena, kuti, Ndiye
Eliya, Anati enanso, Ndiye mneneri, monga ngati mmodzi wa aneneriwo,
16Koma Herode pamene anamva, ananena, Yohane amene ndamdula mutu,
wauka iyeyo.
2 Mafumu 2:11
11Ndipo kunacidka, akali ciyendere ndi kukambirana, taonani, anaoneka
gareta wamoto ndi akavalo amoto, nawalekanitsa awiriwa; Eliya nakwera
kumwamba ndi kabvumvulu.
Exodo 3:14
14Ndipo Molungu anati kwa Mose, INE NDINE YEMWE NDIRI INE. Anatinso,
Ukatero ndi ana a Israyeli, INE NDINE wandituma kwa inu.
Yohane 5:18
18Cifukwa ca ici Ayuda anaonjeza kufuna kumupha, si cifukwa ca kuswa
dzuwa la Sabata kokha, komatu amaehanso Mulungu Atate wace wa iye
yekha; nadziyesera wolingana ndi Mulungu.
1. Yohane 21:25
25Koma palinso zina zambiri zimene. Yesu anazicita, zoti zikadalembedwa
zonse phe, ndilingalira kuti dziko lapansi silikadakhala nao malo
a mabuku amene akadalembedwa. Amen.
2. a. Mateyu 1:21
21Ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamucha dzina lace Yesu;
pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ace ku macimo ao.
b. Mateyu 1:23
23Onani namwali adzaima, Nadzabala mwana wamwamuna,
Ndipo adzamucha dzina lace, Emanueli; ndilo losandulika, Mulungu
nafe.
c. Mateyu 3:17
17ndipo onani, mau akucokera kumiyamba akuti, Uyu ndiye Mwana wanga
wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.
d. Mateyu 12:8
8pakuti Mwana wa munthu ali mwini tsiku la Sabata.
e. Mateyu 16:16
16Ndipo Simoni Petro anayankha nati, Inu ndinu Kristu, Mwana wa
Mulungu wamoyo.
f. Mateyu 19:16
16Ndipo onani, munthu anadza kwa Iye, nati, Mphunzitsi, cabwino
nciti ndicicite, kuti ndikhale nao mayo wosatha?
3. a. Marko 5:6-7
6Ndipo pakuona Yesu kutali, anathamanga, namgwadira Iye; 7ndipo
anapfuula ndi mau olimba, nanena, Ndiri ndi ciani ine ndi Inu, Yesu
Mwana wa Mulungu Wamkurukuru? Ndikulumbirirani pa Mulungu, msandizunze.
b. Luka 5:5
5Ndipo Simoni anayankha, nati, Ambuye, tinagwiritsa nchito usiku
wonse osakola kanthu, koma pa mau anu ndidzaponya makoka.
c. Yohane 1:35-36
35 Pa tsiku lotsatira Yohane analinso pamenepo pamodzi ndi awiri
a ophunzira ake. 36 Iye ataona Yesu akudutsa anati, “Taonani
Mwana Wankhosa wa Mulungu!”
d. Yohane 1:49
49Natanayeli anayankha Iye, Rabi, 14 Inu ndinu Mwana wa Mulungu,
15 ndinu Mfumu ya Israyeli,
e. 1 Akolinto 1:6-7
6mongaumboni wa Kristu unakhazikika mwa inu; 7kotero kuti sicikusowani
inu caufuru ciri conse; pakulindira inu bvumbulutso la Ambuye wathu
Yesu Kristu;
4. Mateyu 1:1-17
1BUKU la kubadwa kwa Yesu Kristu, mwana wa Davide, mwana wa Abrahamu.
2Abrahamu anabala Isake; ndi Isake anabala Yakobo; ndi Yakobo anabala
Yuda ndi abale ace; 3ndi Yuda anabala Farese ndi Zara mwa Tamare;
ndi Farese anabala Ezronu; ndi Ezronu anabala Aramu; 4ndi Aramu
anabala Aminadabu; ndi Aminadabu anabala Naasoni; ndi Naasoni anabala
Salimoni;5ndi Salimoni anabala Boazi mwa Rahabe; ndi Boazi anabala
Obede mwa Rute; ndi Obede anabala Jese; 6ndi Jese anabala Davide
mfumuyo.
Ndipo Davide anabala Solomo mwa mkazi wa Uriya; 7ndi Solomo anabala
Rehabiamu; ndi Rehabiamu anabala Abiya; ndi Abiya anabala Asa; 8ndi
Asa anabala Yosafate; ndi Yosafate anabala Yoramu; ndi Yoramu anabala
Uziya;9ndi Uziya anabala Yotamu; ndi Yotamu anabala Ahazi; ndi Ahazi
anabala Hezekiya; 10ndi Hezekiya anabala Manase; ndi Manase anabala
Amoni; ndi Amoni anabala Yosiya; 11ndi Yosiya anabala Yekoniya ndi
abale ace pa nthawi yakutengedwa kunka ku Babulo.
12Ndipo pambuyo pace pa kutengedwako ku Babulo, Yekoniya anabala
Salatieli; ndi Saiatieli anabala Zerubabele; 13ndi Zerubabele anabala
Abiyudi; ndi Abiyudi anabala Eliyakimu; ndi Eliyakimu anabala Azoro;
14ndi Azoro anabala Sadoki; ndi Sadoki anabala Akimu; ndi Akimu
anabala Eliyudi; 15ndi Eliyudi anabala Eleazara; ndi Eleazara anabala
Matani; ndi Matani anabala Yakobo; 16ndi Yakobo anabala Yosefe,
mwamuna wace wa Mariya, amene Yesu, wochedwa Kristu, anabadwa mwa
iye.
17Motero mibadwo yonse kuyambira pa Abrahamu kufikira kwa Davide
ndiyo mibadwo khumi ndi inai; ndi kuyambira pa Davide kufikira pa
kutengedwa kunka ku Babulo mibadwo khumi ndi inai; ndi kuyambira
pa kutengedwa kunka ku Babulo kufikira kwa Kristu mibadwo khumi
ndi inai.
Yohane 2:1-11
1Ndipo tsiku lacitatu pariali ukwati m'Kana wa m'Galileya; ndipo
amace wa Yesu anali komweko. 2Ndipo Yesu yemwe ndi akuphunzira ace
anaitanidwa ku ukwatiwo. 3Ndipo pakutha vinyo, amace wa Yesu ananena
naye, Alibe vinyo,4Yesu nanena naye, Mkazi, ndiri ndi ciani ndi
inu? nthawi yanga siinafike.5Amace ananena kwa atumiki, Cimene ciri
conse akanena kwa inu, citani.
6Ndipopanali pamenepo mitsuko yamiyala isanu ndi umodzi yoikidwako
monga mwa mayeretsedwe a Ayuda, yonse ya miyeso iwiri kapena itatu.
7Yesu ananena nao, Dzazani mitsukoyo ndi madzi. Naidzaza, nde nde
nde. 8Ndipo ananena nao, Tungani tsopano, mupite nao kwamkulu wa
phwando. Ndipo anapita nao. 9Koma pamene mkuluyo analawa madzi osanduka
vinyowo, ndipo sanadziwa kumene anacokera (koma atumiki amene adatiinga
madzi anadziwa), mkuluyo anaitana mkwati, 10nanena naye, Munthu
ali yense amayamba kuika vinyo wokoma; ndipo anthu atamwatu, pamenepo
wina wosakoma; koma iwe wasunga vinyo wokoma kufikira tsopano lino.
11Ciyambi ici ca zizindikilo zace Yesu anacita m'Kana wa m'Galileya
naonetsera ulemerero wace; ndipo akuphunzira ace anakhulupirira
iye.
Marko 1:9-11
9Ndipo kunali masiku omwewo, Yesu anadza kucokera ku Nazarete wa
ku Galileya, nabatizidwa ndi Yohane m'Yordano. 10Ndipo pomwepo,
alimkukwera poturuka m'madzi, anaona Iye thambo litang'ambika, ndi
Mzimu alikutsikira pa Iye monga nkhunda: 11ndipo mau anaturuka m'thambo,
Mwana wanga wokondedwa ndiwe, mwa Iwe ndikondwera bwino.
Yesaya 9:6
Pakuti kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa;
ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lace, ndipo adzamucha dzina lace
Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga
wa mtendere.
Akolose 1:15-20
15amene ali fanizo la Mulungu wosaonekayo, wobadwa woyamba wa cilengedwe
conse; 16pakuti mwa iye, zinalengedwa zonse za m'mwamba, ndi za
padziko, zooneka ndi zosaonekazo, kapena mipando yacifumu, kapena
maufumu, kapena maukulu, kapena maulamuliro; zinthu zonse zinalengedwa
mwa iye ndi kwa iye. 17Ndipo iye ali woyamba wa zonse, ndipo zonse
zigwirizana pamodzi mwa iye. 18Ndipo iye ali mutu wa thupi, Eklesiayo;
ndiye ciyambi, wobadwa woyamba woturuka mwa akufa; kuti akakhale
iye mwa zonse woyambayamba. 19Pakuti kunamkomera Atate kuti mwa
iye cidzalo conse cikhalire, 20mwa Iyenso kuyanjanitsa zinthu zonse
kwa iye mwini, atacita mtendere mwa mwazi wa mtanda wace; mwa Iyetu,
kapena za padziko, kapena za m'mwamba.
15amene ali fanizo la Mulungu wosaonekayo,
wobadwa woyamba wa cilengedwe conse; Akolose 1:15-20
|
|