Project Hope     home >>stonecroft>> mavesi a m'baibulo >> phunziro 4 >> phunziro 5
YESU NDI NDANI? - Mavesi a m'Baibulo - Phunziro #5
Women's Empowerment Program
Sports Bible Club
Living Water Bible Club

Kuwerenga Baibulo kwa Mlungu ndi Mlungu

Machitidwe 1:6-11
6Pamenepo iwowa, atasonkhana pamodzi, anamfunsa iye, nanena, Ambuye, kodi nthawi yino mubwezera ufumu kwa Israyeli? 7Koma anati kwa iwo, Sikuli kwa inu kudziwa nthawi kapena nyengo, zimene Atate anaziika m'ulamuliro wace wa iye yekha. 8Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga m'Yerusalemu, ndi m'Yudeya lonse, ndi m'Samariya, ndi kufikira malekezero ace a dziko. 9Ndipo m'mene adanena izi, ali cipenyerere iwo, ananyamulidwa; ndipo mtambo unamlandira iye kumcotsa kumaso kwao. 10Ndipo pakukhala iwo cipenyerere kumwamba pomuka iye, taonani, amuna awiri obvala zoyera anaimirira pambali pao; 11amenenso anati, Amuna a ku Galileya, muimiranji ndi kuyang'ana kumwamba? Yesu amene walandiridwa kunka Kumwamba kucokera kwa inu, adzadza momwemo monga munamuona alinkupita Kumwamba.

Machitidwe 2:32-35
32Yesu ameneyo, Mulungu anamuukitsa; za ici tiri mboni ife tonse. 33Potero, popeza anakwezedwa ndi dzanja Lamanja la Mulungu, nalandira kwa Atate lonjezano la Mzimu Woyera, anatsanulira ici, cimene inu mupenya nimumva. 34Pakuti Davine sanakwera Kumwamba ai; koma anena yekha, Ambuye anati kwa Mbuye wanga, Khalani ku dzanja lamanja langa, 35Kufikira ndikaike adani ako copondapo mapazi ako.

Aheberi 4:14-16
14Popeza tsono tiri naye Mkuluwansembe wamkuru, wopyoza miyamba, Yesu Mwana wa Mulungu, tigwiritsitse cibvomerezo cathu. 15Pakuti sitiri naye mkulu wa ansembe wosatha kumva cifundo ndi zofoka zathu; koma wayesedwa m'zonse monga momwe ife, koma wopanda ucimo. 16Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wacifumu wacisomo, kuti tilandire cifundo ndi kupeza cisomo ca kutithandiza nthawi yakusowa.

Agalatia 2:15-20
15Ife ndife Ayuda pacibadwidwe, ndipo sitiri ocimwa a kwaamitundu; 16koma podziwa kuti munthu sayesedwa wolungama pa: nchito ya lamulo, koma mwa cikhulupiriro ca Yesu Kristu, ifedi tinakhulupirira kwa Yesu Kristu, kuti tikayesedwe olungama ndicikhulupiriro ca Kristu, ndipo si ndi nchito za lamulo; pakuti palibe munthu adzayesedwa wolungama ndi nchito za lamulo. 17Koma ngati ife, pofuna kuyesedwa olungama mwa Kristu, tipezedwanso tiri ocimwa tokha, kodi Kristu ali mtumikiwa ucimo cifukwa cace? Msatero ai. 18Pakuti ngati izi zomwezi ndazigumula ndizimanganso, ndidzitsimikizira ndekha ndirt wolakwa.19Pakuti ine mwa lamulo ndafa ku lamulo, kuti ndikhale ndi moyo kwa Mulungu.20Ndinapacikidwa ndi Kristu; koma ndiri ndi mayo; wosatinso ine ai, koma Kristu ali ndi moyo mwa ine; koma moyo umene ndiri nao: tsopano m'thupi, ndiri nao m'cikhulupiriro ca Mwana wa Mulungu, amene anandikonda, nadzipereka yekha cifukwa ca ine.

Aefeso 3:14-21
14Cifukwa ca ici ndipinda maondo anga kwa Atate, 15amene kucokera kwa iye pfuko lonse la m'mwamba ndi la padziko alicha dzina, 16kuti monga mwa cuma ca ulemerero wace akulimbikitseni inu ndi mphamvu mwa Mzimu wace, m'kati mwanu, 17kuti Kristu akhale cikhalire mwa cikhulupiriro m'mitima yanu; kuti, ozika mizu ndi otsendereka m'cikondi, 18mukakhozetu kuzindikira pamodzi ndi oyera mtima onse, kupingasa, ndi utali, ndi kukwera, 19ndi kuzama nciani; ndi kuzindikira cikondi ca Kristu, cakuposa mazindikiridwe, kuti mukadzazidwe kufikira cidzalo conse ca Mulungu.
20Ndipo kwa iye amene angathe kucita koposa-posatu zonse zimene tizipempha, kapena tiziganiza, monga mwa mphamvu ya kucita mwa ife, 21kwa iye ukhale ulemerero mu Mpingo ndi mwa Kristu Yesu, kufikira mibadwo yonse ya nthawi za nthawi. Amen.

Akolose 1:27-29
27kwa iwo amene Mulungu anafuna kuwazindikiritsa ici 6 cimene ciri cuma ca ulemerero wa cinsinsi pakati pa amitundu, ndiye Kristu mwa inu, ciyembekezo ca ulemerero;
28amene timlalikira ife, ndi kucenjeza munthu ali yense 7 ndi kuphunzitsa munthu ali yense mu nzeru zonse, 8 kuti tionetsere munthu ali yense wamphumphu mwa Kristu; 29kucita ici ndidzibvutitsa ndi kuyesetsa 9 monga mwa macitidwe ace akucita mwa ine ndi mphamvu.

1 Petulo 3:22
22amene akhala pa dzanja lamanja la Mulungu, atalowa m'Mwamba; pali angelo, ndi maulamuliro, ndi zimphamvu, zomgonjera.

Marko 6:31
31Ndipo Iye ananena nao, Idzani inu nokha padera ku malo acipululu, mupumule kamphindi, Pakuti akudza ndi akucoka anali piringu piringu, ndipo analibe nthawi yokwanira kudya.

2 Atesalonika 3:10
10 Pakuti ngakhale pamene tinali nanu, tinakupatsani lamulo lakuti, “Munthu wosafuna kugwira ntchito, asadye.”

Genesis 3:15
“. . . Adzalalira mutu wako, ndipo udzalalira chitendene Chake”

Mateyu 28:11-15
11Ndipo pameneiwo analikupita, onani, ena a alonda anafika kumzinda, nauza ansembe akuru zonse zimene zinacitidwa. 12Ndipo pamene anasonkhana pamodzi ndi akuru, anakhala upo, napatsa asilikariwo ndalama zambiri, 13nati, Kazinenani, kuti ophunzira ace anadza usiku, namuba Uja m'mene ife tinali m'tulo. 14Ndipo ngati ici cidzamveka kwa kazembe, ife tidzamgwetsa mtima, ndipo tidzakukhalitsani opanda nkhawa. 15Ndipo iwo analandira ndalamazo, nacita monga anawalangiza: ndipo mbiri iyo inabuka mwa Ayuda, kufikira lero lomwe.

1. Machitidwe a Atumwi 1:1-11
11 Iwo anati, “Inu, anthu a ku Galileya, chifukwa chiyani mukuyima ndi kumayang'ana m'mitambo? Yesu amene wachotsedwa pakati panu ndi kupita kumwamba, adzabweranso m'njira yomweyi mwamuona akupita kumwamba.”

Luka 24:36-44
36Ndipo pakulankhula izi iwowa, iye anaimirira pakati pao; nanena nao, Mtendere ukhale nanu. 37Koma anaopsedwandi kucita mantha, 1 nayesa alikuona mzimu. 38Ndipo anati kwa iwo, Mukhala bwanji obvutika? ndipo matsutsano am auka bwanji m'mtima mwanu? 39Penyani manja anga ndi mapazianga, kuti Ine ndine mwini: 2 ndikhudzeni, ndipo penyani; pakuti mzimu ulibe, mnofu ndi mafupa, monga muona ndirinazo Ine. 40Ndipo m'mene ananena ici, anawaonetsera iwo manja ace ndi mapazi ace. 41Koma pokhala iwo cikhalire osakhulupirira cifukwa ca cimwemwe, nalikuzizwa, anati kwa iwo, 3 Muli nako kanthu kakudya kuno? 42Ndipo anampatsa iye cidutsu ca nsomba yokazinga. 43Ndipo 4 anacitenga, nacidya pamaso pao.
44Ndipo anati kwa iwo, 5 Awa ndi mauwo ndinalankhula nanu, paja ndinakhala ndi inu, kuti ziyenera kukwanitsidwa zonse zolembedwa za Ine m'cilamulo ca 6 Mose, ndi aneneri, ndi masalmo.

2.a. Yohane 20:14-18
14M'mene adanena izi, anaceuka m'mbuy'o, naona Yesu ali ciriri, ndipo sanadziwa kuti ndiye Yesu. 15Yesu ananena naye, Mkazi, uliranji? ufuna yani? Iyeyu poyesa kuti ndiye wakumunda, ananena ndi iye, Mbuye ngati mwamnyamula iye, ndiuzeni kumene mwamuika iye, ndipo ndidzamcotsa.16Yesu ananena naye, Mariya. Iyeyu m'mene anaceuka, ananena ndi iye m'Cihebri, Raboni; cimene cinenedwa, Mphunzitsi. 17Yesu ananena naye, Usandikhudze, pakuti sindinatha kukwera kwa Atate; koma pita kwa abale anga, ukati kwa iwo, Ndikwera kunka kwa Atate wanga, ndi Atate wanu, ndi Mulungu wanga, ndi Mulungu wanu. 18Mariya wa Magadala anapita nalalikira kwa akuphunzirawo, kuti, Ndaona Ambuye; ndi kuti ananena izi kwa iye.

b. Luka 24:13-15
13Ndipo taonani, awiri a mwa iwo analikupita tsiku lomwelo kumudzi dzina lace Emau, wosiyana ndi Yerusalemu mastadiya makumi asanu ndi limodzi. 14Ndipo iwowa anakambirana nkhani za izi zonse zidacitika. 15Ndipo kunali m'kukambirana kwao ndi kufunsana, Yesu mwini anayandikira, natsagana nao.

c. Yohane 20:26-29
26Ndipo pakupita masiku asanu ndi atatu akuphunzira ace analinso m'nyumbamo, ndi Tomasi pamodzi nao: Yesu anadza, makomo ali citsekere, naimirira pakati, nati, Mtendere ukhale ndi inu. 27Pomwepo ananena kwa Tomasi, Bwera naco cala cako kuno, nuone manja anga; ndipo bwera nalo dzanja lako, nuliike ku nthiti yanga, ndipo usakhale wosakhulupira, koma wokhulupira. 28Tomasi anayankha nati kwa iye, Ambuye wanga, ndi Mulungu wanga. 29Yesu ananena kwa iye, Cifukwa wandiona Ine, wakhulupira; odala iwo akukhulupira, angakhale sanaona.

d. 1 Akolinto 15:5
5ndi kuti anaonekera kwa Kefa; pamenepo kwa khumi ndi awiriwo;

e. Yohane 21:1
1Zitapita izi Yesu anadzionetseranso kwa akuphunzira ace ku nyanja ya Tiberiya. Koma anadzionetsera cotere.

f. 1 Akolinto 15:6
6pomwepo anaoneka pa nthawi imodzi kwa abale oposa mazana asanu, amene ocuruka a iwo akhala kufikira tsopano, koma ena agona;

g. 1 Akolinto 15:7
7pomwepoanaonekera kwa Yakobo; pamenepo kwa: atumwi onse;

3. Aheberi 12:2
2Yesu, ameneyo, cifukwa ca cimwemwe coikidwaco pamaso pace, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala pa dzanja lamanja la mpando wacifumu wa Mulungu,

4. Aheberi 7:24-25
24koma iye cifukwa kuti akhala iye nthawi yosatha ali nao unsembe wosasinthika,25kucokera komwekoakhoza kupulumutsa konse konse iwo akuyandikira kwa Mulungu mwa iye, popeza ali nao moyo wace cikhalire wa kuwapembedzera iwo.

Yohane 14:16-20
16Ndipo Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani inu Nkhoswe yina, kuti akhale ndi inu ku nthawi yonse, 17ndiye Mzimu wa coonadi; amene dziko lapansi silingathe kumlandira, pakuti silimuona iye, kapena kumzindikira iye. Inu mumzindikira iye; cifukwa akhala ndi inu nadzakhala mwa inu. 18Sindidza-kusiyani inu mukhale ana amasiye; ndidza kwa inu. 19Katsala kanthawi, ndipo dziko lapansi silindionanso Ine; koma inu mundiona; popeza Ine ndiri ndi moyo inunso mudzakhala ndi moyo. 20Tsiku lo mwelo mudzazindikira kuti ndiri Ine mwa Atate wanga, ndi inu mwa Ine, ndi Ine mwa inu.

Tito 3:4-7
4Koma pamene kukoma mtima, ndi cikondi ca pa anthu, ca Mpulumutsi wathu Mulungu zidaoneka, 5zosati zocokera m'nchito za m'cilungamo, zimene tidazicita ife, komatu monga mwa cifundo cace anatipulumutsa ife, mwa kutsuka kwa kubadwanso ndi makonzedwe a Mzimu Woyera, 6amene anatsanulira pa ife mocurukira, mwa Yesu Kristu Mpulumutsi wathu; 7kuti poyesedwa olungama ndi cisomo ca Iyetu, tikayesedwe olowa nyumba monga mwa ciyembekezo ca moyo wosatha.

Machitidwe 1:9
9Ndipo m'mene adanena izi, ali cipenyerere iwo, ananyamulidwa; ndipo mtambo unamlandira iye kumcotsa kumaso kwao.

5. Aroma 5:8-9
8Koma g Mulungu atsimikiza kwa ife cikonai cace ca mwini yekha m'menemo, kuti pokhala ife cikhalire ocimwa, Kristu adatifera ife. 9Ndipo tsono popeza inayesedwa olungama ndi mwazi wace, makamaka ndithu tidzapulumuka mkwiyo wa Mulungu mwa Iyeyo.

Aroma 5:10
10Pakuti ngati, pokhala ife adani ace, tinayanjanitsidwa ndi Mulungu mwa imfa ya Mwana wace, makamaka ndithu, popeza ife tayanjanitsidwa, tidzapulumuka ndi moyo wace.

Yohane 6:37
37Cinthu conse cimene anandipatsa Ine Atate cidzadza kwa Ine; ndipo wakudza kwa Ine sindidzamtaya iye kunja

Mateyu 11:28
28Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu.

7. a. Agalatiya 2:20
20Ndinapacikidwa ndi Kristu; koma ndiri ndi mayo; wosatinso ine ai, koma Kristu ali ndi moyo mwa ine; koma moyo umene ndiri nao: tsopano m'thupi, ndiri nao m'cikhulupiriro ca Mwana wa Mulungu, amene anandikonda, nadzipereka yekha cifukwa ca ine.

b. 1 Akorinto 3:16-17
16Kodi simudziwa kuti muli Kacisi wa Mulungu, ndi kuti Mzimu wa Mulungu agonera mwa inu? 17Ngati wina aononga kacisi wa Mulungu, ameneyo Mulungu adzamuononga; pakuti kacisi wa Mulungu ali wopatulika, ameneyo ndi inu.

1 Akorinto 6:19
19Kapena simudziwa kuti thupi lanu liri kacisi wa Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu? Ndipo simukhala a inu nokha.

c. Aroma 8:9-11
9Koma inu simuli m'thupi ai, koma mumzimu, ngatitu Mzimu wa Mulungu akhalabe mwa inu. Koma ngati munthu alibe Mzimu wa Kristu, siali wace wa Kristu. 10Ndipo ngati Kristu akhala mwa inu, thupilo ndithu liri lakufa cifukwa ca ucimo; koma mzimu uli wamoyo cifukwa ca cilungamo. 11Koma ngati Mzimu wa iye amene adaukitsa Yesu kwa akufa akhalabe mwa inu, iye amene adaukitsa Kristu Yesu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu akufa, mwa Mzimu wace wakukhala mwa inu.

Yesaya 57:15
Pakuti atero Iye amene ali wantali wotukulidwa, amene akhala mwa chikhalire, amene dzina lache ndiye Woyera, Ndikhala m'malo atali ndi oyera, pamodzi ndi onse amene ali ndi mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, ndi kutsitsimusa mtima wa osweka.

Machitidwe a Atumwi 4:12
12 Chipulumutso sichipezeka mwa wina aliyense; pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo limene lapatsidwa kwa anthu limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.”

 
 

 

YESU NDI NDANI?

Mavesi a m'Baibulo

 
 
Copyright ©  2023 www.UnitedCaribbean.com. All rights reserved. Disclaimer Click to Contact us