Stonecroft
Stonecroft Training
Mndandanda wa Utatu
Malangizo Otsogolera
Mavesi a m'Baibulo
Adult Stonecroft International
The International Team
English YDT Teachings
Maphunziro a Ana
Malawi Moringa Projects
|
|
home >>stonecroft>>
mavesi a m'baibulo >> phunziro 1 >> phunziro 2
YESU NDI NDANI? - Mavesi a m'Baibulo - Phunziro #2
Kuwerenga Baibulo kwa Mlungu ndi Mlungu
Mateyu 5:1-12
1Ndipo m'mene Iye anaona makamu, anakwera m'phiri; ndipo m'mene
Iye anakhala pansi, anadza kwa Iye ophunzira ace; 2ndipo anatsegula
pakamwa, nawaphunzitsa iwo, nati:
3Odala ali osauka mumzimu; cifukwa uli wao Ufumu wa Kumwamba.
4Odala ali acisoni; cifukwa adzasangalatsidwa.
5Odala ali akufatsa; cifukwa adzalandira dziko lapansi.
6Odala ali akumva njala ndi ludzu la cilungamo; cifukwa adzakhuta.
7Odala ali akucitira cifundo; cifukwa adzalandira cifundo.
8Odala ali oyera mtima; cifukwa adzaona Mulungu.
9Odala ali akucita mtendere; cifukwa adzachedwa ana a Mulungu.
10Odalaaliakuzunzidwacifukwa ca cilungamo: cifukwa uli wao Ufumu
wa Kumwamba.
11Odala muli inu m'mene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani
monama zoipa ziri zonse cifukwa ca Ine.
12Sekerani, sangalalani: cifukwa mphotho yanu ndi yaikuru m'Mwamba:
pakuti potero anazunza aneneri anakhalawo musanabadwe inu.
Mateyu 5:13-16
13Inu ndinu mcere wa dziko lapansi; koma mcerewo ngati uka: sukuluka,
adzaukoleretsa ndi ciani? Pamenepo sungakwanirenso kanthu konse,
koma kuti ukaponyedwe kunja, nupondedwe ndi anthu.
14Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi. Mudzi wokhazikika pamwamba
pa phiri sungathe kubisika. 15Kapena sayatsa nyali, ndi kuibvundikira
m'mbiya, koma aiika iyo pa coikapo cace; ndipo iunikira onse: ali
m'nyumbamo. 16Comweco muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu,
kuti pakuona nchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.
Mateyu 6:1-15
1Yang'anirani kuti musacite zolungama zanu pamaso pa anthu kuti
muonekere kwa iwo; pakuti ngati mutero mulibe mphotho ndi Atate
wanu wa Kumwamba.2Cifukwa cace pamene pali ponse upatsa mphatso
zacifundo, usamaomba lipenga patsogolo pako, monga amacita onyenga
m'masunagoge, ndi m'makwalala, kotero kuti atamandidwe ndi anthu.
Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao. 3Koma iwe
popatsa mphatso zacifundo, dzanja lako lamanzere lisadziwe cimene
licita dzanja lako lamanja; 4kotero kuti mphatso zako zacifundo
zikhale zam'tseri; ndipo Atate wako wakuona m'tseri adzakubwezera
iwe.
5Ndipo pamene mupemphera, musakhale monga onyengawo; cifukwa iwo
akonda kuimirira ndi kupemphera m'masunagoge, ndi pa mphambano za
makwalala, kuti aonekere kwa anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo
alandiriratu mphotho zao. 6Koma iwe popemphera, Iowa m'cipinda cako,
nutseke citseko cako, nupemphere Atate wako ali m'tseri, ndipo Atate
wako wakuona m'tseri adzakubwezera iwe. 7Ndipo popemphera musabwereze-bwereze
cabe iai, monga amacita anthu akunja, cifukwa ayesa kuti adzamvedwa
ndi kulankhula-lankhula kwao. 8Cifukwa cace inu musafanane nao:
pakuti Atate wanu adziwa zomwe muzisowa, inu musanayambe kupempha
Iye. 9Cifukwa cace pempherani inu comweci:
Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe. 10Ufumu wanu udze.
Kufuna kwanu kucitidwe, monga Kumwamba comweco pansi pano. 11Mutipatse
ife lero cakudya cathu calero. 12Ndipo mutikhululukire mangawa athu,
monga ifenso takhululukira amangawa anthu. 13Ndipo musatitengere
kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo.
14Pakuti ngati mukhululukira anthu zolakwa zao adzakhululukira inunso
Atate wanu wa Kumwamba. 15Koma ngati simukhululukira anthu zolakwa
zao, Atate wanunso sadzakhululukira zolakwa zanu.
Mateyu 6:24-34
24Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri: pakuti pena
adzamuda mmodziyo, ndi kukonda winayo; pena adzakangamira kwa mmodzi,
nadzanyoza wina.
Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Cuma. 25Cifukwa cace
ndinena kwa inu, Musadere nkhawa moyo wanu, cimene mudzadya ndi
cimene mudzamwa; kapena thupi lanu, cimene mudzabvala. Kodi moyo
suli woposa cakudya, ndi thupi loposa cobvala? 26Yang'anirani mbalame
za kumwamba, kuti sizimafesa ai, kapena sizimatema ai, kapena sizimatutira
m'nkhokwe; ndipo Atate wanu wa Kumwamba azidyetsa. Nanga inu mulibe
kusiyana nazo kuziposa kodi?
27Ndipo ndani wa inu ndi kudera nkhawa angathe kuonjezera pa msinkhu
wace mkono umodzi?28Ndipo muderanji nkhawa ndi cobvala? Tapenyetsani
maluwa a kuthengo, makulidwe ao; sagwiritsa nchito, kapena sapota:
29koma ndinena kwa inu, kuti angakhale Solomo mu ulemerero wace
wonse sanabvala monga limodzi la amenewa. 30Koma ngati Mulungu abveka
cotero maudzu a kuthengo, akhala lero, ndi mawa oponyedwa pamoto,
nanga si inu kopambana ndithu, inu akukhulupirira pang'ono? 31Cifukwa
cace musadere nkhawa, ndi kuti, Tidzadya ciani? kapena, Tidzamwa
ciani? kapena, Tidzabvala ciani? 32Pakuti anthu akunja azifunitsa
zonse zimenezo; pakuti Atate wanu wa Kumwamba adziwa kuti musowa
zonse zimenezo. 33Koma muthange mwafuna Ufumu wace ndi cilungamo
cace, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu. 34Cifukwa cace
musadere nkhawa za mawa; pakuti mawa adzadzidera nkhawa iwo okha,
Zikwanire tsiku zobvuta zace.
Mateyu 7:1-12
1Musaweruze, kuti mungaweruzidwe. 2Pakuti ndi kuweruza kumene muweruza
nako, inunso mudzaweruzidwa; ndipo ndi muyeso umene muyesa nao,
kudzayesedwa kwa inunso. 3Ndipo upenya bwanji kacitsotso kali m'diso
la mbale wako, koma mtanda uli m'diso la iwe mwini suuganizira?
4Kapena udzati bwanji kwa mbale wako, Tandilola ndicotse kacitsotso
m'diso lako; ndipo ona, mtandawo ulimo m'diso lakoli. 5Wonyenga
iwe! tayamba kucotsa m'diso lako mtandawo, ndipo pomwepo udzapenyetsa
kucotsa kacitsotso m'diso la mbale wako.
6Musamapatsa copatulikaco kwa agaru, ndipo musamaponya ngale zanu
patsogolo pa nkhumba, kuti zingazipondereze ndi mapazi ao, ndi potembenuka
zingang'ambe inu.
7Pemphani, ndipo cidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza;
gogodani, ndipo cidzatsegulidwa kwa inu; 8pakuti yense wakupempha
alandira; ndi wakufunayo apeza; ndi kwa wogogodayo citsegulldwa.
9Kapena munthu ndani wa inu, amene pompempha mwana wace mkate, adzampatsa
mwala?10Kapena pompempha nsomba, adzampatsa iye njoka kodi? 11Comweco,
ngati inu, muli oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kopambana
kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa zinthu zabwino kwa
iwo akumpempha Iye? 12Cifukwa cace zinthu ziri zonse mukafuna kuti
anthu acitire inu, inunso muwacitire iwo zotero; pakuti ico ndico
cilamulo ndi aneneri.
Mateyu 7:13-20
13Lowani pa cipata copapatiza; cifukwa cipata ciri cacikuru, ndi
njira yakumuka nayo kukuonongeka iri yotakata; ndipo ali ambiri
amene alowa pa ico. 14Pakuti cipata ciri copapatiza, ndi icepetsa
njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akucipeza cimeneco ali owerengeka.
15Yang'anirani mupewe aneneri onyenga, amene adza kwa inu ndi zobvala
zankhosa, koma m'kati mwao ali afisi alusa. 16Mudzawazindikira ndi
zipatso zao. Kodi achera mphesa paminga, kapena nkhuyu pamtula?
17Comweco mtengo wabwino uli wonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo
wamphuci upatsa zipatso zoipa, 18Sungathe mtengo wabwino kupatsa
zipatso zoipa, kapena mtengo wamphuci kupatsa zipatso zokoma. 19Mtengo
uli wonse wosapatsa cipatso cokoma, audula, nautaya kumoto. 20Inde
comweco pa zipatso zao mudzawazindikira iwo.
Mateyu 7:21-27
21Si yense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa
Kumwamba; koma wakucitayo cifuniro ca Atate wanga wa Kumwamba. 22Ambiri
adzati kwa Ine tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenera
mau m'dzina lanu, ndi m'dzina lanunso kuturutsa mizimu yoipa, ndi
kucita m'dzina lanunso zamphamvu zambiri? 23Ndipo pamenepo ndidzafukulira
iwo, Sindinakudziwani inu nthawi zonse; cokani kwa Ine, inu akucita
kusayeruzika. 24Cifukwa cimeneci yense amene akamva mau anga amenewa,
ndi kuwacita, ndidzamfanizira iye ndi munthu wocenjera, amene anamanga
nyumba yace pathanthwe; 25ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje,
ndipo zinaomba mphepo, zinagunda pa nyumbayo; koma siinagwa; cifukwa
inakhazikika pathanthwepo.
26Ndipo yense akamva mau anga amenewa, ndi kusawacita, adzafanizidwa
ndi munthu wopusa, yemwe anamanga nyumba yace pamcenga; 27ndipo
inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda
pa nyumbayo; ndipo inagwa; ndi kugwa kwace kunali kwakukuru.
Yohane 8:56-59
5613 Atate wanu Abrahamu anakondwera kuona tsiku langa; ndipo anaona,
nasangalala. 57Ayuda pamenepo anati kwa iye, Simunafikire zaka makumi
asanu, ndipo munaona Abrahamu kodi?
58Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, asanayambe
kukhala Abrahamu ndipo 14 Ine ndiripo. 59Pamenepo 15 anatola miyala
kuti amponye iye; koma Yesu anabisala, naturuka m'Kacisi.
1. a. Yohane 13:19
19Kuyambira tsopano ndinena kwa inu, cisadacitike, kuti pamene citacitika,
mukakhulupire kuti ndine amene.
b. Yohane 8:12
12Pamenepo Yesu analankhulanso nao, nanena, Ine ndine kuunika kwa
dziko lapansi; iye wonditsata ine sadzayenda mumdima, koma adzakhala
nako kuunika kwa moyo.
c. Yohane 10:9
9Ine ndine khomo; ngati wina alowa ndi Ine, adzapulu-mutsidwa, nadzalowa,
nadzaturuka, nadzapeza busa.
d. Yohane 10:11
11Ine ndine Mbusa Wabwino; mbusa wabwino ataya moyo wace cifukwa
ca nkhosa.
e. Yohane 10:36
36kodi inu munena za iye, amene Atate anampatula namtuma ku dziko
lapansi, Ucita mwano; cifukwa ndinati, Ndiri Mwana wa Mulungu?
f. Yohane 11:25
25Yesu anati kwa iye, Ine ndine kuuka ndi moyo; wokhulupirira Ine,
angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo;
g. Yohane 6:48
48 Ine ndine mkate wamoyo,
h. Yohane 14:6
6Yesu ananena naye, ine ndinenjira, ndi coonadi, ndi moyo. Palibe
munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.
3. Mateyu 5:21-26
21Munamva kuti kunanenedwa kwa iwo akale, Usaphe; koma yense wakupha
adzakhala wopalamula mlandu: 22koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense
wokwiyira mbale wace wopanda cifukwa adzakhala wopalamula mlandu;
ndipo amene adzanena ndi mbale wace, Wopanda pace iwe, adzakhala
wopalamula mlandu wa akuru: koma amene adzati, Citsiru iwe: adzakhala
wopalamula gehena wamoto.
23Cifukwa cace ngati ulikupereka mtulo wako pa guwa la nsembe, ndipo
pomwepo ukakumbukira kuti mbale wako ali ndi kanthu pa iwe, 24usiye
pomwepo mtulo wako kuguwako, nucoke, nuyambe kuyanjana ndi mbale
wako, ndipo pamenepo idza nupereke mtulo wako. 25Fulumira kuyanjana
ndi mnzako wamlandu, pamene uli naye panjira; kapena mnzako wamlandu
angakupereke iwe kwa woweruza mlandu, ndi woweruzayo angapereke
iwe kwa msilikari, nuponyedwe iwe m'nyumba yandende. 26Indetu ndinena
ndi iwe, sudzaturukamo konse, koma utalipa kakobiri kakumariza ndiko.
Mateyu 5:3-12
3Odala ali osauka mumzimu; cifukwa uli wao Ufumu wa Kumwamba.
4Odala ali acisoni; cifukwa adzasangalatsidwa.
5Odala ali akufatsa; cifukwa adzalandira dziko lapansi.
6Odala ali akumva njala ndi ludzu la cilungamo; cifukwa adzakhuta.
7Odala ali akucitira cifundo; cifukwa adzalandira cifundo.
8Odala ali oyera mtima; cifukwa adzaona Mulungu.
9Odala ali akucita mtendere; cifukwa adzachedwa ana a Mulungu.
10Odalaaliakuzunzidwacifukwa ca cilungamo: cifukwa uli wao Ufumu
wa Kumwamba.
11Odala muli inu m'mene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani
monama zoipa ziri zonse cifukwa ca Ine.
12Sekerani, sangalalani: cifukwa mphotho yanu ndi yaikuru m'Mwamba:
pakuti potero anazunza aneneri anakhalawo musanabadwe inu.
Mateyu 5:13-16
13Inu ndinu mcere wa dziko lapansi; koma mcerewo ngati uka: sukuluka,
adzaukoleretsa ndi ciani? Pamenepo sungakwanirenso kanthu konse,
koma kuti ukaponyedwe kunja, nupondedwe ndi anthu.
14Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi. Mudzi wokhazikika pamwamba
pa phiri sungathe kubisika. 15Kapena sayatsa nyali, ndi kuibvundikira
m'mbiya, koma aiika iyo pa coikapo cace; ndipo iunikira onse: ali
m'nyumbamo. 16Comweco muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu,
kuti pakuona nchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.
Mateyu 5:17-20
17Musaganize kuti ndinadza Ine kudzapasula cilamulo kapena ane,
neri: sindinadza kupasula, koma kukwaniritsa. 18Pakuti indetu ndinena
kwa inu, Kufikira litapitirira thambo ndi dziko, kalemba kakang'ono
kamodzi kapena kansonga kace kamodzi sikadzaeokera kucilamulo, kufikira
zitacitidwa zonse.19Cifukwa cace yense wakumasula limodzi la malangizo
amenewa ang'onong'ono, nadzaphunzitsa anthu comweco, adzachulidwa
wamng'onong'ono mu Ufumu wa Kumwamba; koma yense wakucita ndi kuphunzitsa
awa, iyeyu adzachulidwa wamkuru mu Ufumu wa Kumwamba.20Pakuti ndinena
ndi inu, ngati cilungamo canu sicicuruka coposa ca alembi ndi Afarisi,
simudzalowa konse mu Ufumu wa Kumwamba.
Mateyu 5:27-30
27Munamva kuti kunanenedwa, Usacite cigololo; 28koma Ine ndinena
kwa inu, kuti yense wakuyang'ana mkazi kumkhumba, pamenepo watha
kucita naye cigololo mumtima mwace.
29Koma ngati diso lake lamanja likulakwitsa iwe, ulikolowole, nulitaye;
pakuti nkwabwino kwa iwe, kuti cimodzi ca ziwalo zako cionongeke,
losaponyedwa thupi lako lonse m'gehena. 30Ndipo ngati dzanja lako
lamanja likulakwitsa iwe, ulidule, nulitaye; pakuti nkwabwino kwa
iwe kuti cimodzi ca ziwalo zako cionongeke, losamuka thupi lako
lonse kugehena.
Mateyu 5:31-32
31Kunanenedwanso, Yense wakucotsa mkazi wace ampatse iye cilekaniro:32koma
Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakucotsa mkazi wace, kosati cifukwa
ca cigololo, amcititsa cigololo: ndipo amene adzakwata wocotsedwayo
acita cigololo.
Mateyu 5:33-37
33Ndiponso, munamva kuti kunanenedwa kwa iwo akale, Usalumbire konama,
koma udzapereka kwa Ambuye zolumbira zako: 34koma Ine ndinena kwa
inu, 6Musalumbire konse, kapena kuchula Kumwamba, cifukwa kuli cimpando
ca Mulungu; 35 kapena kuchula dziko lapansi, cifukwa liri popondapo
mapazi ace; kapena kuchula Yerusalemu, cifukwa kuli mzinda wa Mfumu
yaikurukuru. 36 Kapena usalumbire ku mutu wako, cifukwa sungathe
kuliyeretsa mbu kapena kulidetsa bii tsitsi limodzi. 37 Kama manenedwe
anu akhale, Inde, inde; Iai, iai; ndipo coonjezedwa pa izo cicokera
kwa woipayo.
Mateyu 5:38-42
38Munamva kuti kunanenedwa, Diso kulipa diso, ndi dzino kulipa dzino:39koma
ndinena kwa inu, Musakanize munthu woipa; koma amene adzakupanda
iwe pa tsaya lako Lamanja, umtembenuzire linanso. 40Ndipo kwa iye
wofuna kupita nawe kumlandu ndi kutenga malaya ako, umlolezenso
copfunda cako. 41Ndipo amene akakukakamiza kumperekeza njira imodzi,
upite naye ziwiri. 42Kwa iye wopempha iwe umpatse, ndipo kwa iye
wofuna kukukongola usampotolokere.
Mateyu 5:43-48
43Munamva kuti kunanenedwa, 14 Uzikondana ndi mnansi wako, ndi kumuda
mdani wako: 44koma Ine ndinena kwa inu, 15 Kondanani nao adani anu,
ndi 16 kupempherera iwo akuzunza inu;
45kotero kuti mukakhale ana a Atate wanu wa Kumwamba; cifukwa Iye
amakwezera dzuwa lace pa oipa ndi pa abwino, namabvumbitsira mvula
pa olungama ndi pa osalungama.
46Cifukwa kuti 17 ngati muwakonda akukondana ndi inu mphotho yanji
muli nayo? kodi angakhale amisonkho sacita comweco? 47Ndipo ngati
mulankhula abale anu okha okha, mucitanji coposa ena? Kodi angakhale
anthu akunja sacita comweco?48Cifukwa cace inu 18 mukhale angwiro,
monga Atate wanu wa Kumwamba ali wangwiro.
Mateyu 6:1-4
1Yang'anirani kuti musacite zolungama zanu pamaso pa anthu kuti
muonekere kwa iwo; pakuti ngati mutero mulibe mphotho ndi Atate
wanu wa Kumwamba.2Cifukwa cace pamene pali ponse upatsa mphatso
zacifundo, usamaomba lipenga patsogolo pako, monga amacita onyenga
m'masunagoge, ndi m'makwalala, kotero kuti atamandidwe ndi anthu.
Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao. 3Koma iwe
popatsa mphatso zacifundo, dzanja lako lamanzere lisadziwe cimene
licita dzanja lako lamanja; 4kotero kuti mphatso zako zacifundo
zikhale zam'tseri; ndipo Atate wako wakuona m'tseri adzakubwezera
iwe.
Mateyu 6:5-15
5Ndipo pamene mupemphera, musakhale monga onyengawo; cifukwa iwo
akonda kuimirira ndi kupemphera m'masunagoge, ndi pa mphambano za
makwalala, kuti aonekere kwa anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo
alandiriratu mphotho zao. 6Koma iwe popemphera, Iowa m'cipinda cako,
nutseke citseko cako, nupemphere Atate wako ali m'tseri, ndipo Atate
wako wakuona m'tseri adzakubwezera iwe. 7Ndipo popemphera musabwereze-bwereze
cabe iai, monga amacita anthu akunja, cifukwa ayesa kuti adzamvedwa
ndi kulankhula-lankhula kwao. 8Cifukwa cace inu musafanane nao:
pakuti Atate wanu adziwa zomwe muzisowa, inu musanayambe kupempha
Iye. 9Cifukwa cace pempherani inu comweci: Atate wathu wa Kumwamba,
Dzina lanu liyeretsedwe. 10Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kucitidwe,
monga Kumwamba comweco pansi pano. 11Mutipatse ife lero cakudya
cathu calero. 12Ndipo mutikhululukire mangawa athu, monga ifenso
takhululukira amangawa anthu. 13Ndipo musatitengere kokatiyesa,
koma mutipulumutse kwa woipayo.
14Pakuti ngati mukhululukira anthu zolakwa zao adzakhululukira inunso
Atate wanu wa Kumwamba. 15Koma ngati simukhululukira anthu zolakwa
zao, Atate wanunso sadzakhululukira zolakwa zanu.
Mateyu 6:16-18
16Ndipo pamene ponse musala kudya, musakhale ndi nkhope yacisoni,
ngati onyengawo; pakuti aipitsa nkhope zao, kuti aonekere kwa anthu
kuti alimkusala kudya. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu
mphotho zao. 17Koma iwe, posala kudya, dzola mutu wako, ndi kusamba
nkhope yako: 18kuti usaonekere kwa anthu kuti ulikusala kudya, koma
kwa Atate wako ali m'tseri: ndipo Atate wako wakuona m'tseri adzakubwezera
iwe.
Mateyu 6:19-21
19Musadzikundikire nokha cuma pa dziko lapansi, pamene njenjete
ndi dzimbiri ziononga; ndi pamene mbala ziboola ndi kuba: 20koma
mudzikundikire nokha cuma m'Mwamba, pamene njenjete kapena dzimbiri
siziononga, ndipo mbala siziboola ndi kuba; 21pakuti kumene kuli
cuma cako, komwe udzakhala mtima wakonso.
Mateyu 6:22-23
22Diso ndilo nyali ya thupi; cifukwa cace ngati diso lako liri la
kumodzi, thupi lako lonse lidzakhala lowalitsidwa. 23Koma ngati
diso lako liri loipa, thupi lako lonse lidzakhala lodetsedwa. Cifukwa
cace ngati kuwala kumene kuli mwa inu kuli mdima, mdimawo ndi waukuru
ndithu!
Mateyu 6:24-34
24Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri: pakuti pena
adzamuda mmodziyo, ndi kukonda winayo; pena adzakangamira kwa mmodzi,
nadzanyoza wina. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Cuma.
25Cifukwa cace ndinena kwa inu, Musadere nkhawa moyo wanu, cimene
mudzadya ndi cimene mudzamwa; kapena thupi lanu, cimene mudzabvala.
Kodi moyo suli woposa cakudya, ndi thupi loposa cobvala?
26Yang'anirani mbalame za kumwamba, kuti sizimafesa ai, kapena sizimatema
ai, kapena sizimatutira m'nkhokwe; ndipo Atate wanu wa Kumwamba
azidyetsa. Nanga inu mulibe kusiyana nazo kuziposa kodi? 27Ndipo
ndani wa inu ndi kudera nkhawa angathe kuonjezera pa msinkhu wace
mkono umodzi?28Ndipo muderanji nkhawa ndi cobvala? Tapenyetsani
maluwa a kuthengo, makulidwe ao; sagwiritsa nchito, kapena sapota:
29koma ndinena kwa inu, kuti angakhale Solomo mu ulemerero wace
wonse sanabvala monga limodzi la amenewa.
30Koma ngati Mulungu abveka cotero maudzu a kuthengo, akhala lero,
ndi mawa oponyedwa pamoto, nanga si inu kopambana ndithu, inu akukhulupirira
pang'ono? 31Cifukwa cace musadere nkhawa, ndi kuti, Tidzadya ciani?
kapena, Tidzamwa ciani? kapena, Tidzabvala ciani? 32Pakuti anthu
akunja azifunitsa zonse zimenezo; pakuti Atate wanu wa Kumwamba
adziwa kuti musowa zonse zimenezo. 33Koma muthange mwafuna Ufumu
wace ndi cilungamo cace, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa
inu. 34Cifukwa cace musadere nkhawa za mawa; pakuti mawa adzadzidera
nkhawa iwo okha, Zikwanire tsiku zobvuta zace.
Mateyu 7:1-6
1Musaweruze, kuti mungaweruzidwe. 2Pakuti ndi kuweruza kumene muweruza
nako, inunso mudzaweruzidwa; ndipo ndi muyeso umene muyesa nao,
kudzayesedwa kwa inunso. 3Ndipo upenya bwanji kacitsotso kali m'diso
la mbale wako, koma mtanda uli m'diso la iwe mwini suuganizira?
4Kapena udzati bwanji kwa mbale wako, Tandilola ndicotse kacitsotso
m'diso lako; ndipo ona, mtandawo ulimo m'diso lakoli. 5Wonyenga
iwe! tayamba kucotsa m'diso lako mtandawo, ndipo pomwepo udzapenyetsa
kucotsa kacitsotso m'diso la mbale wako.
6Musamapatsa copatulikaco kwa agaru, ndipo musamaponya ngale zanu
patsogolo pa nkhumba, kuti zingazipondereze ndi mapazi ao, ndi potembenuka
zingang'ambe inu.
Mateyu 7:7-12
7Pemphani, ndipo cidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza;
gogodani, ndipo cidzatsegulidwa kwa inu; 8pakuti yense wakupempha
alandira; ndi wakufunayo apeza; ndi kwa wogogodayo citsegulldwa.
9Kapena munthu ndani wa inu, amene pompempha mwana wace mkate, adzampatsa
mwala?10Kapena pompempha nsomba, adzampatsa iye njoka kodi? 11Comweco,
ngati inu, muli oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kopambana
kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa zinthu zabwino kwa
iwo akumpempha Iye? 12Cifukwa cace zinthu ziri zonse mukafuna kuti
anthu acitire inu, inunso muwacitire iwo zotero; pakuti ico ndico
cilamulo ndi aneneri.
Mateyu 7:13-14
13Lowani pa cipata copapatiza; cifukwa cipata ciri cacikuru, ndi
njira yakumuka nayo kukuonongeka iri yotakata; ndipo ali ambiri
amene alowa pa ico. 14Pakuti cipata ciri copapatiza, ndi icepetsa
njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akucipeza cimeneco ali owerengeka.
Mateyu 7:15-20
15Yang'anirani mupewe aneneri onyenga, amene adza kwa inu ndi zobvala
zankhosa, koma m'kati mwao ali afisi alusa. 16Mudzawazindikira ndi
zipatso zao. Kodi achera mphesa paminga, kapena nkhuyu pamtula?
17Comweco mtengo wabwino uli wonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo
wamphuci upatsa zipatso zoipa, 18Sungathe mtengo wabwino kupatsa
zipatso zoipa, kapena mtengo wamphuci kupatsa zipatso zokoma. 19Mtengo
uli wonse wosapatsa cipatso cokoma, audula, nautaya kumoto. 20Inde
comweco pa zipatso zao mudzawazindikira iwo.
Mateyu 7:21-23
21Si yense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa
Kumwamba; koma wakucitayo cifuniro ca Atate wanga wa Kumwamba. 22Ambiri
adzati kwa Ine tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenera
mau m'dzina lanu, ndi m'dzina lanunso kuturutsa mizimu yoipa, ndi
kucita m'dzina lanunso zamphamvu zambiri? 23Ndipo pamenepo ndidzafukulira
iwo, Sindinakudziwani inu nthawi zonse; cokani kwa Ine, inu akucita
kusayeruzika.
Mateyu 7:24-27
24Cifukwa cimeneci yense amene akamva mau anga amenewa, ndi kuwacita,
ndidzamfanizira iye ndi munthu wocenjera, amene anamanga nyumba
yace pathanthwe; 25ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba
mphepo, zinagunda pa nyumbayo; koma siinagwa; cifukwa inakhazikika
pathanthwepo.
26Ndipo yense akamva mau anga amenewa, ndi kusawacita, adzafanizidwa
ndi munthu wopusa, yemwe anamanga nyumba yace pamcenga; 27ndipo
inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda
pa nyumbayo; ndipo inagwa; ndi kugwa kwace kunali kwakukuru.
Mateyu 7:28-29
28Ndipo panakhala pamene Yesu anatha mau amenewa, makamu a anthu
anazizwa ndi ciphunzitso cace: 29pakuti anawaphunzitsa monga mwini
mphamvu, wosanga alembiao.
1 Akolinto 2:13-16
13Zimenenso tilankhula, si ndi mau ophunzitsidwa ndi nzeru za munthu,
koma ophunzitsidwa ndi Mzimu; ndi kulinganiza zamzimu ndi zamzimu.
14Koma munthu wa cibadwidwe ca umunthu salandira za Mzimu wa Mulungu:
pakuti aziyesa zopusa; ndipo sakhoza kuzizindikira, cifukwa ziyesedwa
mwauzimu. 15Koma iye amene ali wauzimu ayesa zonse, koma iye yekha
sayesedwa ndi mmodzi yense. 16Pakuti wadziwa ndani mtima wa Ambuye,
kuti akamlangize iye? Koma ife tiri nao mtima wa Kristu.
4. Mateyu 13:1-58
1Tsiku lomwelo Yesu anaturuka m'nyumbamo, nakhala pansi m'mbali
mwa nyanja. 2Ndipo makamu ambiri a anthu anasonkhanira kwa Iye,
kotero kuti Iye analowa m'ngalawa, nakhala pansi, ndipo khamu lonse
linaima pamtunda.3Ndipo Iye anawauzira zinthu zambiri m'mafanizo,
nanena, Onani, wofesa anaturuka kukafesa mbeu, 4Ndipo m'kufesa kwace
zina zinagwa m'mbali mwa njira, ndipo zinadza mbalame, nizilusira
izo. 5Koma zina zinagwa pamiyala, pamene panalibe dothi lambiri;
ndipo pomwepo zinamera, pakuti sizinakhala nalo dothi lakuya, Ndipo
m'mene dzuwa linakwera zinapserera; 6ndipo popeza zinalibe mizu
zinafota. 7Koma zina zinagwa paminga, ndipo mingayo inayanga, nizitsamwitsa
izo. 8Koma zina zinagwa pa nthaka yabwino, ndipo zinabala zipatso,
zina za makumi khumi, zina za makumi asanu ndi limodzi, zina za
makumi atatu. 9Amene ali ndi makutu, amve.
10Ndipo ophunzirawo anadza, nati kwa Iye, Cifukwa canji muphiphiritsira
iwo m'mafanizo?
11Ndipo Iye anayankha nati, Cifukwa kwapatsidwa kwa inu kudziwa
zinsinsi za Ufumu wa Kumwamba, koma sikunapatsidwa kwa iwo. 12Pakuti
yense amene ali nazo, kudzapatsidwa kwa iye, ndimo adzakhala nazo
zocuruka; koma yense amene alibe, cingakhale comwe ali naco cidzacotsedwa
kwa iye.13Cifukwa cace ndiphiphiritsira iwo m'mafanizo; cifukwa
kuti akuona samaona, ndi akumva samamva, kapena samadziwitsa. 14Ndipo
adzacitidwa kwa iwo mau adanenera Yesaya, amene ati.
Pakumva mudzamva, ndipo simudzazindikira konse; Pakupenya mudzapenya,
ndipo simudzaona konse;
15Cifukwa unalemera mtima wa anthuawa, Ndipo m'makutu ao anamva
mogontha, Ndipo maso ao anatsinzina;
Kuti asaone konse ndi maso, Asamve ndi makutu, Asazindikire ndi
mtima wao, Asatembenuke, Ndipo ndisawaciritse iwo.
16Koma maso anu ali odala, cifukwa apenya; ndi makutu anu cifukwa
amva.17Pakuti indetu ndinena kwa inu, kuti aneneri ambiri ndi anthu
olungama analakalaka kupenya zimene muziona, koma sanaziona; ndi
kumva zimene muzimva, koma sanazimva.
18Ndipo tsono mverani inu fanizolo la wofesa mbeu uja. 19Munthu
ali yense wakumva mau a Ufumu, osawadziwitsai, woipayo angodza,
nakwatula cofesedwaco mumtima mwace. Uyo ndiye wofesedwa m'mbali
mwa njira.20Koma iye amene afesedwa pamiyala, uyu ndiye wakumva
mau, ndi kuwalandira pomwepo ndi kusekera; 21ndipo alibe mizu mwa
iye, koma akhala nthawi yaing'ono; ndipo pakudza nsautso kapena
zunzo cifukwa ca mau, iye akhumudwa pomwepo. 22Ndipo iye amene afesedwa
kuminga, uyu ndiye wakumva mau; ndipo kulabadira kwa dziko lapansi,
ndi cinyengo ca cuma citsamwitsa mau, ndipo akhala wopanda cipatso.
23Ndipo iye amene afesedwa pa nthaka yabwino, uyu ndiye wakumva
mau nawadziwitsa; amene abaladi zipatso, nazifitsa, ena za makumi
khumi, ena za makumi asanu ndi limodzi, ena za makumi atatu.
24Fanizo lina Iye anawafotokozera iwo, nanena, Ufumu wa Kumwamba
ufanizidwa ndi munthu, amene anafesa mbeu zabwino m'munda mwace;25koma
m'mene anthu analinkugona, mdani wace anadza, nafesa namsongole
pakati pa tirigu, nacokapo. 26Koma pamene mmera unakula, nubala
cipatso, pomwepo anaonekeranso namsongole. 27Ndipo anyamata ace
a mwini nyumbayo anadza, nati kwa iye, Mbuye, kodi simunafesa mbeu
zabwino m'munda mwanu? nanga wacokera kuti namsongoleyo? 28Ndipo
iye ananena kwa iwo, Munthu mdani wanga wacicita ici. Ndipo anyamata
anati kwa iye, Kodi mufuna tsopano kuti timuke, tikamsonkhanitse
uyo pamodzi? 29Koma iye anati, lai, kuti kapena m'mene mukasonkhanitsa
namsongoleyo, mungazulenso tirigu pamodzi naye.
30Kazilekeni zonse ziwiri, zikulire pamodzi kufikira pakututa; ndimo
m'nyengo yakututa ndidzauza akututawo, Muyambe kusonkhanitsa namsongole,
mummange uyu mitolo kukamtentha, koma musonkhanitse tirigu m'nkhokwe
yanga.
31Fanizo lina Iye anawafotokozera iwo, nanena, Ufumu wa Kumwamba
uli wofanafana ndi kambeu kampiru, kamene anakatenga munthu, nakafesa
pamunda pace; 32kamene kakhaladi kakang'ono koposa mbeu zonse, koma
katakula, kali kakakuru kuposa zitsambazonse, nukhala mtengo, kotero
kuti mbalame za mlengalenga zimadza, nizibindikira mu nthambi zace.
33Fanizo lina ananena kwa iwo; Ufumu wa Kumwamba uli wofanafana
ndi cotupitsa mikate, cimene mkazi anacitenga, nacibisa m'miyeso
itatu ya ufa, kufikira wonse unatupa.
34Zonsezi Yesu anaziphiphiritsira m'mafanizo kwa makamu anthu; ndipo
kopanda fanizo sanalankhula kanthu kwa iwo; 35kuti cikacitidwe conenedwa
ndi mneneri, kuti, Ndidzatsegula pakamwa panga ndi mafanizo;
Ndidzaulula zinthu zobisika ciyambire kukhazikidwa kwace kwa dziko
lapansi.
36Pomwepo Iye anasiya makamuwo, nalowa m'nyumba; ndimo ophunzira
ace anadza kwa Iye, nanena, Mutitanthauzire fanizo lija la namsongole
wa m'munda.37Ndipo Iye anayankha nati, Wofesa mbeu yabwino ndiye
Mwana wa munthu;38ndipo munda ndiwo dziko lapansi; ndi mbeu yabwino
ndiyo ana a Ufumuwo; ndi namsongole ndiye ana a woipayo; 39ndipo
mdani amene anamfesa uwu ndiye mdierekezi: ndi kututa ndico cimariziro
ca nthawi ya pansi pano; ndi otutawo ndiwo angelo. 40Ndipo monga
namsongole asonkhanitsidwa pamodzi, natenthedwa pamoto, matero mudzakhala
m'cimariziro ca nthawi ya pansi pano.41Mwana wa munthu adzatuma
angelo ace, ndipo iwo adzasonkhanitsa pamodzi, ndi kucotsa mu Ufumu
wace zokhumudwitsa zonse, ndi anthu akucita kusayeruzika, 42ndipo
adzawataya iwo m'ng'anjo yamoto; kumeneko kudzakhala kulira ndi
kukukuta mano. 43Pomwepo olungamawo adzawalitsa monga dzuwa, mu
Ufumu wa Atate wao. Amene ali ndi makutu amve.
44Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi cuma cobisika m'munda; cimene
munthu anacipeza, nacibisa; ndipo m'kucikonda kwace acoka, nagulitsa
zonse ali nazo, nagula munda umenewu.
45Ndiponso Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi munthu wa malonda,
wakufuna ngale zabwino: 46ndipo m'mene anaipeza ngale imodzi ya
mtengo wapatari, anapita, nagulitsa zonse anali nazo, naigula imeneyo.
47Ndiponso, Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi khoka loponyedwa
m'nyanja, ndi 1 kusonkhanitsa pamodzi za mitundu yonse; 48limene
podzala, analibvuulira pamtunda; ndipo m'mene anakhala pansi, anazisonkhanitsa
zabwino m'zotengera, koma zoipa anazitaya kuthengo. 49Padzatero
pa cimariziro ca nthawi ya pansi pano: angelo adzaturuka, 2 nadzawasankhula
oipa pakati pa abwino, 50nadzawataya m'ng'anjo yamoto; komweko kudzakhala
kulira ndi kukukuta mano.
51Mwamvetsa zonsezi kodi? lwo anati kwa Iye, inde. 52Ndipo Iye anati
kwa iwo, Cifukwa cace, mlembi ali yense, wophunzitsidwa mu Ufumu
wa Kumwamba, ali wofanana ndi munthu mwini banja, amene aturutsa
m'cuma cace zinthu zakale ndi zatsopano.
53Ndipo panali, pamene Yesu anatha mafanizo awa, anacokera kumeneko.54Ndipo
3 pofika ku dziko la kwao, anaphunzitsa iwo m'sunagoge mwao, kotero
kuti anazizwa, nanena, Uyu adazitengakuti nzeru zimenezi ndi zamphamvu
izi?554 Kodi uyu si mwana wa mmisiri wa mitengo? kodi dzina lace
la amace si Mariya? ndi 5 abale ace si Yakobo ndi Yosefe ndi Simoni
ndi Yuda? 56Ndipo alongo ace sali ndife onsewa? Ndipo iyeyo adazitenga
zinthu zonsezi kuti?57Ndipo iwo anakhumudwa cifukwa ca Iye. Koma
Yesu anati kwa iwo, 6 Mneneri sakhala wopanda ulemu koma ku dziko
la kwao ndiko, ndi kubanja kwace.58Ndipo Iye, cifukwa ca kusakhulupirira
kwao, sanacita kumeneko zamphamvu zambiri.
5. Luka 8:11-15
11Koma fanizoli litere: Mbeuzo ndizo mau a Mulungu, 12Ndipo za m'mbali
mwa njira ndiwo anthu amene adamva; pamenepo akudza mdierekezi,
nacotsa mau m'mitima yao, kuti angakhulupirire ndi kupulumuka.13Ndipo
za pathanthwe ndiwo amene, pakumva, alandira mau ndi kukondwera;
koma alibe mizu; akhulupirira kanthawi, ndipo pa nthawi ya mayesedwe
angopatuka. 14Ndipo zija zinagwa ku mingazi, ndiwo amene adamva,
ndipo m'kupita kwao atsamwitsidwa ndi nkhawa, ndi cuma, ndi zokondweretsa
za moyo, ndipo sakhwimitsa zipatso zamphumphu. 15Ndipo zija za m'nthaka
yokoma, ndiwo amene anamva mau nawasunga mu mtima woona ndi wabwino,
nabala zipatso ndi kupirira.
7. Marko 8:38
38Pakuti yense wakucita manyazi cifukwa ca Ine, ndi ca mau anga
mu mbadwo uno wacigololo ndi wocimwa, Mwana wa munthu adzacitanso
manyazi cifukwa ca iyeyu, pamene Iye adzafika nao angelo ace oyera,
mu ulemerero wa Atate wace.
Marko14:72
72Ndipo pomwepo tambala analira kaciwiri. Ndipo Petro anakumbukila
umo Yesu anati kwa iye, kuti, Tambala asanalire kawiri udzandikana
katatu. Ndipo pakuganizira ici analira misozi.
Luka 24:5-7
5ndipo m'mene anakhala ndi mantha naweramira pansi nkhope zao, anati
kwa iwo, Mufuniranji wamoyo pa akufa?6Palibe kuno iye, komatu anauka;
kumbukilani muja adalankhula nanu, pamene analinso m'Galileya, 7ndi
kunena, kuti, Mwana wa munthu ayenera kuperekedwa m'manja a anthu
ocimwa, ndi kupacikidwa pamtanda, ndi kuuka tsiku lacitatu.
Yohane 5:25-29
25Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti ikudza nthawi, ndipo Iripo
tsopano, imene akufa adzamva mau a Mulungu; ndipo iwo akumva adzakhala
ndi moyo. 26Pakuti monga Atate ali ndi moyo mwa iye yekha, momwemonso
anapatsa kwa Mwana kukhala ndi moyo mwa iye yekha; 27ndipo anampatsa
iye mphamvu ya kucita mlandu, pakuti ali Mwana wa munthu.28Musazizwe
ndi ici, kuti ikudza nthawi, imene onse ali m'manda adzamva mau
ace, 29nadzaturukira, amene adacita zabwino, kukuuka kwa moyo; koma
amene adacita zoipa kukuuka kwa kuweruza.
Yohane 12:32-33
32Ndipo Ine, m'mene ndikakwezedwa kudziko, ndidzakoka anthu onse
kwa Ine ndekha. 33Koma ananena ici ndi kuzindikiritsa imfa yanji
akuti adzafa nayo.
Yohane 5:25-29
25Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti ikudza nthawi, ndipo Iripo
tsopano, imene akufa adzamva mau a Mulungu; ndipo iwo akumva adzakhala
ndi moyo. 26Pakuti monga Atate ali ndi moyo mwa iye yekha, momwemonso
anapatsa kwa Mwana kukhala ndi moyo mwa iye yekha; 27ndipo anampatsa
iye mphamvu ya kucita mlandu, pakuti ali Mwana wa munthu.28Musazizwe
ndi ici, kuti ikudza nthawi, imene onse ali m'manda adzamva mau
ace, 29nadzaturukira, amene adacita zabwino, kukuuka kwa moyo; koma
amene adacita zoipa kukuuka kwa kuweruza.
Yohane 11:17-44
17Ndipo pamene Yesu anadza, anapeza kuti pamenepo atakhala m'manda
masiku anai. 18Koma Betaniya anali pafupi pa Yerusalemu, nthawi
yace yonga ya mastadiya khumi ndi asanu; 19koma ambiri a mwa Ayuda
adadza kwa Marita ndi Mariya, kudzawatonthoza mtima pa mlongo wao.
20Pamenepo Marita, pakumva kuti Yesu alinkudza, anamuka kukakomana
ndi iye; koma Mariya anakhalabe m'nyumba. 21Ndipo Marita anati kwa
Yesu, Ambuye, mukadakhala kuno mlongo wanga sakadafa. 22Koma ngakhale
tsopano ndidziwa kuti zinthu ziri zonse mukapempha Mulungu, adzakupatsani
Mulungu. 23Yesu ananena naye, Mlongo wako adzauka. 24Marita ananena
ndi iye, Ndidziwa kuti adzauka m'kuuka tsiku lomariza. 25Yesu anati
kwa iye, Ine ndine kuuka ndi moyo; wokhulupirira Ine, angakhale
amwalira, adzakhala ndi moyo; 26ndipo yense wakukhala ndi moyo,
nakhulupirira Ine, sadzamwalira nthawi yonse. Kodi ukhulupirira
ici? 27Ananena ndi iye, Inde Ambuye; ndakhulupirira ine kuti Inu
ndinu Kristu, Mwana wa Mulungu, wakudza m'dziko lapansi. 28Ndipo
m'mene anati ici anacoka naitana Mariya mbale wace m'tseri, ndi
kuti, Wafika Mphunzitsi, akuitana iwe. 29Koma iyeyo, pakumva, ananyamuka
msanga, nadza kwa iye.30(Koma Yesu sanafike kumudzi, koma anali
pamalo pomwe Marita adakomana ndi Iye) 31Pamenepo Ayuda okhala naye
m'nyumba, ndi kumtonthoza iye, pakuona Mariya ananyamuka msanga,
naturuka, namtsata iye, ndi kuyesa kuti amuka kumanda kukalira komweko.
32Pomwepo Mariya, pofika pamene panali Yesu, m'mene anamuona iye,
anagwa pa mapazi ace, nanena ndi iye, Ambuye, mukadakhala kuno Inu,
mlongo wanga sakadamwalira. 33Pamenepo Yesu, pakumuona iye alikulira,
ndi Ayuda akumperekeza iye alikulira, anadzuma mumzimu, nabvutika
mwini, 34nati, Mwamuika iye kuti? Ananena ndi iye, Ambuye, tiyeni,
mukaone. 35Yesu analira. 36Cifukwa cace Ayuda ananena, Taonani,
anamkondadi! 37Koma ena mwa iwo anati, Kodi uyu wotsegulira maso
wosaona uja, sanakhoza kodi kucita kuti sakadafa ameneyunso?
38Pamenepo Yesu, ndi kudzumanso mwa iye yekha anadza kumanda. Koma
panali phanga, ndipo mwala unaikidwa pamenepo. 39Yesu ananena, Cotsani
mwala. Marita, mlongo wace wa womwalirayo, ananena ndi iye, Ambuye,
adayamba kununkha: pakuti wagona masiku anai. 40Yesu ananena naye,
Kodi sindinati kwa iwe, kuti, ngati ukhulupira, udzaona ulemerero
wa Mulungu? 41Pomwepo anacotsa mwala. Kama Yesu anakweza maso ace
kupenya kumwamba nati, Atate, ndiyamika Inu kuti munamva Ine.
42Koma ndadziwa Ine kuti mumandimva Ine nthawi zonse; koma cifukwa
ca khamu la anthu alikuimirira pozungulira ndinanena ici, kuti akhulupire
kuti Inu munandituma Ine. 43Ndipom'mene adanena izi, ana pfuula
ndi mau akuru, Lazaro, turuka. 44Ndipo womwalirayo anaturuka womangidwa
miyendo ndi manja ndi nsaru za kumanda; ndi nkhope yace inazingidwa
ndi mlezo. Yesu ananena nao, Mmasuleni iye, ndipo mlekeni amuke.
Mateyu 24:1-3
1Ndipo Yesu anaturuka kuKacisi; ndipo ophunzira ace anadza kudzamuonetsa
cimangidwe ca Kacisiyo. 2Koma Iye anayankha nati kwa iwo, Simuona
izi zonse kodi? indetu ndinena kwa inu, Sipadzakhala pano mwala
umodzi pa unzace, umene sudzagwetsedwa.
3Ndipo pamene Iye analikukhala pansi pa phiri la Azitona, ophunzira
anadza kwa Iye pa yekha, nanena, Mutiuze ife zija zidzaoneka liti?
ndipo cizindikiro ca kufika kwanu nciani, ndi ca mathedwe a nthawi
ya pansi pano?
Mateyu 24:36-39
36Koma za tsiku ilo ndi nthawi yace sadziwa munthu ali yense, angakhale
angelo a Kumwamba, kapena Mwana, koma Atate yekha. 37Ndipo 1 monga
masiku a Nowa, kotero kudzakhala kufika kwace kwa Mwana wa munthu.38Pakuti
monga m'masiku aja, cisanafike cigumula, anthu analinkudya ndi kumwa,
analikukwatira ndi kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analowa
m'cingalawa, 39ndipo iwo sanadziwa kanthu, kufikira kumene cigumula
cinadza, cinapululutsa iwo onse, kotero kudzakhala kufika kwace
kwa Mwana wa munthu.
8. Yohane 17:5-8
5Ndipo tsopano, Atate Inu, lemekezani Ine ndi Inu nokha ndi ulemerero
umene ndinali nao ndi Inu lisanakhale dziko lapansi. 6Ndalionetsera
dzina lanu kwa anthu amene mwandipatsa Ine m'dziko lapansi; anali
anu, ndipo mwandipatsa Ine iwo; ndipo adasunga mau anu. 7Azindikira
tsopane kuti zinthu ziri zonse zimene mwandipatsa Ine zicokera kwa
Inu; 8cifukwa mau amene munandipatsa Ine ndinapatsa iwo; ndipo analandira,
nazindikira koona kuti ndinaturuka kwa Inu, ndipo anakhulupira kuti
Inu munandituma Ine.
Yohane 7:45-46
45Pamenepo anyamatawo anadza kwa ansembe akulu ndi Afarisi; ndipo
iwowa anati kwa iwo, Simunamtenga iye bwanji? 46Anyamatawo anayankha,
7 Nthawi yonse palibe munthu analankhula cotero.
9. a. Marko 1:10-11
10Ndipo pomwepo, alimkukwera poturuka m'madzi, anaona Iye thambo
litang'ambika, ndi Mzimu alikutsikira pa Iye monga nkhunda: 11ndipo
mau anaturuka m'thambo, Mwana wanga wokondedwa ndiwe, mwa Iwe ndikondwera
bwino.
b. Yohane 1:32
32Ndipo Yohane anacita umboni, nati, 8 Ndinaona Mzimu alikutsika
kucokera Kumwamba monga nkhunda; nakhalabe pa iye.
c. Machitidwe 11:4-9
4Koma Petro anayamba kuwafotokozera cilongosolere, nanena, 5Ndinali
ine m'mudzi wa Yopa ndi kupemphera; ndipo m'kukomoka ndinaona masomphenya,
cotengera cirikutsika, ngati cinsaru cacikuru cogwiridwa pa ngondya
zace zinai; ndi kutsika kumwamba, ndipo cinadza pali ine; 6cimeneco
ndidacipenyetsetsa ndinacilingirira, ndipo ndinaona nyama za miyendo
inai za padziko ndi zirombo, ndi zokwawa, ndi mbalame za m'mlengalenga.
7Ndipo ndinamvanso mau akunena ndi ine, Tauka Petro; ipha, nudye.
8Koma ndinati, Iaitu, Ambuye; pakuti kanthu wamba, kapena konyansa
sikanalowe m'kamwa mwanga ndi kale lonse. 9Koma mau anayankha nthawi
yaciwiri oturuka m'mwamba, Cimene Mulungu anaciyeretsa, usaciyesera
cinthu wamba.
Machitidwe 10:3-6
3Iye anapenya m'masomphenya poyera, mngelo wa Mulungu alinkudza
kwa iye, ngati ora lacisanu ndi cinai la usana, nanena naye, Komeliyo.
4Ndipo pompenyetsetsa iye ndi kuopa, anati, Nciani, Mbuye? Ndipo
anati kwa iye, Mapemphero ako ndi zacifundo zako zinakwera zikhala
cikumbutso pamaso pa Mulungu.
Machitidwe 13:2-3
2Ndipo pa kutumikira Ambuye iwowa, ndi kusala cakudya, Mzimu Woyera
anati, Mundipatulire Ine Bamaba ndi Saulo ku nchito imene odinawaitanirako.
3Pamenepo, m'mene adasala cakudya ndi kupemphera ndi kuika manja
pa iwo, anawatumiza amuke.
Aheberi 1:1-2a
1KALE Mulungu analankhula ndi makolo mwa aneneri m'manenedwe ambiri
ndi mosiyana-siyana, 2koma pakutha pace pa masiku ano analankhula
ndi ife ndi
Miyambo 8:34-35
34Ngwodala amene andimvera, nadikira pa zitseko zanga tsiku ndi
tsiku,
Ndi kulinda pa mphuthu za makoma anga;
35Pakuti wondipeza ine apeza moyo;
Yehova adzamkomera mnma.
1 Atesolonika 2:13
13Ndipo mwa icinso ife tiyamika Mulungu kosalekeza, kuti, pakulandira
mau a Uthenga wa Mulungu, simunawalandira monga mau a anthu, komatu
monga momwe ali ndithu, mau a Mulungu, amenenso acita mwa inuokhulupirira.
|
|