Project Hope     home >>stonecroft>> mavesi a m'baibulo >> phunziro 3 >> phunziro 4
YESU NDI NDANI? - Mavesi a m'Baibulo - Phunziro #4
Women's Empowerment Program
Sports Bible Club
Living Water Bible Club

Kuwerenga Baibulo kwa Mlungu ndi Mlungu

Mateyu 5:1-2, 17-20
1Ndipo m'mene Iye anaona makamu, anakwera m'phiri; ndipo m'mene Iye anakhala pansi, anadza kwa Iye ophunzira ace; 2ndipo anatsegula pakamwa, nawaphunzitsa iwo, nati:
17Musaganize kuti ndinadza Ine kudzapasula cilamulo kapena ane, neri: sindinadza kupasula, koma kukwaniritsa. 18Pakuti indetu ndinena kwa inu, Kufikira litapitirira thambo ndi dziko, kalemba kakang'ono kamodzi kapena kansonga kace kamodzi sikadzaeokera kucilamulo, kufikira zitacitidwa zonse.19Cifukwa cace yense wakumasula limodzi la malangizo amenewa ang'onong'ono, nadzaphunzitsa anthu comweco, adzachulidwa wamng'onong'ono mu Ufumu wa Kumwamba; koma yense wakucita ndi kuphunzitsa awa, iyeyu adzachulidwa wamkuru mu Ufumu wa Kumwamba.20Pakuti ndinena ndi inu, ngati cilungamo canu sicicuruka coposa ca alembi ndi Afarisi, simudzalowa konse mu Ufumu wa Kumwamba.

Yohane 6:35-38
35Yesu anati kwa iwo, Ine ndine mkate wamoyo; iye amene adza kwa Ine sadzamva njala, ndi iye amene akhulupirira Ine sadzamva ludzu nthawi zonse. 36Koma ndinati kwa inu, kuti mungakhale mwandiona, simukhulupirira. 37Cinthu conse cimene anandipatsa Ine Atate cidzadza kwa Ine; ndipo wakudza kwa Ine sindidzamtaya iye kunja. 38Pakuti ndinatsika Kumwamba, si kuti ndicite cifuniro canga, koma cifuniro ca iye amene anandituma Ine.

Machitidwe 2:23-24
23ameneyo, woperekedwa ndi uphungu woikidwa ndi kudziwiratu kwa Mulungu, inu mwampacika ndi kumupha ndi manja a anthu osayeruzika; 24yemweyo Mulungu anamuukitsa, atamasula zowawa za imfa, mwakuti sikunali kotheka kuti iye agwidwe nayo.

1 Yohane 3:5-6
5Ndipo mudziwa kuti iyeyu anaonekera kudzacotsa macimo; ndipo mwa Iye mulibe cimo. 6Yense wakukhala mwa iye sacimwa; yense wakucimwa sanamuona iye, ndipo sanamdziwa iye.

Aheberi 2:14-15
14Popeza tsono ana ndiwo a mwazi ndi nyama, Iyenso momwemo adalawa nao makhalidwe omwewo kuti mwa imfa akamuononge iye amene anali nayo mphamvu ya imfa, ndiye mdierekezi; 15nakamasule iwo onse amene, cifukwa ca kuopa imfa, m'moyo wao wonse adamangidwa ukapolo.

Chibvumbulutso 3:20-21
20Taona, ndaima pakhomo, ndigogoda; wina akamva mau anga nakatsegula pakhomo, ndidzalowa kwa iye, ndipo ndidzadya naye, ndi iye ndi Ine. 21Iye wakulakika, ndidzampatsa akhale pansi ndi Ine pa mpando wacifumu wanga, monga Inenso ndinalakika, ndipo ndinakhala pansi ndi Atate wanga pa mpando wacifumu wace.

Chibvumbulutso 5:9-10
9Ndipo ayimba nyimbo yatsopano, ndi kunena, Muyenera kulandira bukulo, ndi kumasula zizindikilo zace; cifukwa mwaphedwa, ndipo mwagulira Mulungu ndi mwazi wanu anthu a mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse, 10ndipo mudawayesa iwo ufumu ndi ansembe kwa Mulungu wathu; ndipo acita ufumu padziko.

Yesaya 9:6
Pakuti kwa ife, mwana wa khanda wabadwa, kwa ife mwana wa mwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lache, ndipo adzamutcha dzina lache Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wa Mphamvu, Atate Wosatha,
Kalonga wa Mtendere.

Yesaya 35:4-6
. . .Mulungu wanu adza ndikubwezera chilango, ndi mphoto ya Mulungu; Adzabwera ndikudzakupulumutsa.
Ndipo maso a a khungu adzatseguka, ndipo makutu a osamva sadzaimitsidwa. Ndipo alumala adzajowa ngati nswala, Ndipo lilime la osalankhula lidzaimba. . .

1. a.Mateyu 5:17
17Musaganize kuti ndinadza Ine kudzapasula cilamulo kapena ane, neri: sindinadza kupasula, koma kukwaniritsa.

b. Yohane 1:18
18Kulibe munthu anaona Mulungu nthawi zonse; Mwana wobadwa yekha wakukhala pa cifuwa ca Atate, Iyeyu anafotokozera.

c.Mateyu 20:28
28monga Mwana wa munthu sanadza kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wace dipo la anthu ambiri.

d. Luka 4:42-43
42Ndipo kutaca anaturuka iye nanka ku malo acipululu; ndi makamu a anthu analikwnfunafuna iye, nadza nafika kwa iye, nayesa kumletsa iye, kuti asawacokere. 43Koma anati kwa iwo, Kundiyenera Ine ndilalikire Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu ku midzi yinanso: cifukwa ndinatumidwa kudzatero.

e. Luka 19:10
10Pakuti Mwana wa munthu anadza kufunafuna ndi kupulumutsa, cotayikaco.

f. Yohane 3:17
17Pakuti Mulungu sanatuma Mwana wace ku dziko lapansi, kuti akaweruze dziko lapansi, koma kuti dziko lapansi likapulumutsidwe ndi iye.

g. Yohane 10:7-10
7Cifukwa cace Yesuananenanso nao, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ine ndine khomo la nkhosa. 8Onse amene anadza m'tsogolo mwa Ine ali akuba, ndi olanda: koma nkhosa sizinamva iwo. 9Ine ndine khomo; ngati wina alowa ndi Ine, adzapulu-mutsidwa, nadzalowa, nadzaturuka, nadzapeza busa. 10Siikudza mbala, koma kuti ikabe, ndi kupha, ndi kuononga, Ndadza Ine kuti akhale ndi moyo, ndi kukhala nao wocuruka.

h. 1 Timoteyo 1:15
15Mauwa ali okhulupirika ndi oyenera konse kuti awalandire, kuti Kristu Yesu anadza ku dziko lapansi kupulumutsa ocimwa; wa iwowa ine ndine woposa;

Yesaya 14:12-14
Wagwadi kuchokera kumwamba, iwe nthatha, mwana wa mbanda kucha! Wagwetsedwa pansi, iwe olefula amitundu!
Ndipo iwe umati mu ntima mwako, “Ndidzakwera kumwamba, ndidzakweza mpando wanga wachifumu
pamwamba pa nyenyezi za Mulungu; ndidzakhala pamwamba pa phiri la khamu, m'malekezero a ku mpoto;
ndidzakwera pamwamba pa mitambo, ndidzafanana ndi Wam'mambamwamba.”

Aroma 5:12
12Cifukwa cace, monga ucimo unalowa m'dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa ucimo; cotero imfa inafikira anthu onse, cifukwa kuti onse anacimwa.

Genesis 2:17
17koma mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa, usadye umenewo; cifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.

Machitidwe 4:11-12
11Iye ndiye mwalawo woyesedwa wopanda pace ndi inu omanga nyumba, umene unayesedwa mutu wa pangondya. 12Ndipo palibe cipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwanalo.

Aroma 3:23
23pakuti onse anacimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu;

Marko 1:11
11ndipo mau anaturuka m'thambo, Mwana wanga wokondedwa ndiwe, mwa Iwe ndikondwera bwino.

2.a. Luka 18:31-33
31Ndipo anadzitengera khumi ndi awiriwo, nati kwa iwo, Taonani, tikwera kunkaku Yerusalemu, ndipo zidzakwaniritsidwa kwa Mwana wa munthu zonse zolembedwa ndi aneneri. 32Pakuti adzampereka kwa amitundu, nadzamseka, nadzamcitira cipongwe, nadzamthira malobvu; ndipo atamkwapula adzamupha iye; 33ndipo tsiku lacitatu adzauka.

b. Mateyu 12:38-40
38Pomwepo alembi ndi Afarisi ena anayankha Iye nati, Mphunzitsi, tifuna kuona cizindikiro ca Inu. 39Koma Iye anayankha nati kwa iwo, Akubadwa oipa acigololo afunafuna cizindikiro; ndipo sicidzapatsidwa kwa iwo cizindikiro, komatu cizindikiro ca Yona mneneri; 40pakuti monga Yona anali m'mimba mwa cinsomba masiku atatu ndi usiku wace, comweco Mwana wa munthu adzakhala mumtima mwa dziko lapansi masiku atatu ndi usiku wace.

c. Marko 8:31-32a
31Ndipo anayamba kuwaphunzitsa, kuti kuyenera kuti Mwana wa munthu akamve zowawa zambiri, nakakanidwe ndi akuru ndi ansembe akulu, ndi alembi, nakaphedwe, ndipo mkuca wace akauke.32Ndipo mauwo ananena poyera.

3. Luke 23:4
4Ndipo Pilato anati kwa ansembe akuru ndi makamu a anthu, Ndiribe kupeza cifukwa ca mlandu ndi munthu uyu.

4. Marko 14:61-64
61Koma anakhala cete, osayankhakanthu. Mkulu wa ansembe anamfunsanso, nanena naye, Kodi Iwe ndiwe Kristu, Mwana wace wa Wolemekezeka? 62Ndipo Yesu anati, Ndine amene; ndipo mudzaona Mwana wa munthu alikukhala ku dzanja lamanja la mphamvu, ndi kudza ndi mitambo ya kumwamba. 63Ndipo mkulu wa ansembe anang'amba maraya ace, nanena, Tifuniranjinso mboni zina?64Mwamva mwano wace; muyesa bwanji? Ndipo onse anamtsutsa Iye kuti ayenera kufa.

Yesaya 53:3-6
Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu; munthu wa zisoniyo, ndiwodziwa zowawa; ndipo ananyozedwa monga munthu wombisira anthu nkhope zao; ndipo ife sitinamulemekeza. Zoonadi Iye ananyamula zowawa zathu, ndikusenza zisoni zathu; koma kwa ife tinamuyesa okhomedwa, wokanditdwa ndi Mulungu, ndi wobvutidwa. koma Iye analasidwa chifukwa cha mphulupulu zathu; chilango chochitengera ife tachilitsidwa. Tonse tasochera ngati nkhosa; tonse tayenda yense mjira ya mwini yekha; ndipo Yehova anaika pa Iye mphulupulu ya ife tonse. Yesu ndi Ndani? — Buku lotsogolera

5. Marko 14:43–72
43Ndipo pomwepo, Iye ali cilankhulire, anadza Yudase, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, ndipo pamodzi naye khamu la anthu, ali nao malupanga ndi mikunkhu, ocokera kwa ansembe akuru ndi alembi ndi akuru. 44Ndipo wakumpereka Iye anawapatsa cizindikilo, nanena, Iye amene ndidzampsompsona, ndiyetu; mgwireni munke naye cisungire. 45Ndipo atafika, pomwepo anadza kwa Iye, nanena, Rabi; nampsompsonetsa. 46Ndipo anamthira manja, namgwira.47Koma mmodzi wina wa iwo akuimirirapo, anasolola lupanga lace, nakantha kapolo wace wa mkulu wa ansembe, namdula khutu lace.
48Ndipo Yesu anayankha nati kwa iwo, Kodi mwaturuka ndi malupanga ndi mikunkhu kundigwira ine monga wacifwamba? 49Masiku onse ndinali nanu m'Kacisi ndirikuphunzitsa, ndipo simunandigwira Ine; koma ici cacitika kuti malembo akwanitsidwe.50Ndipo iwo onse anamsiya Iye, nathawa. 51Ndipo mnyamata wina anamtsata Iye, atapfundira pathupi bafuta yekha; ndipo anamgwira; 52koma iye anasiya bafutayo, nathawa wamarisece.
53Ndipo ananka naye Yesu kwa mkulu wa ansembe; ndipo anasonkhana kwa iye ansembe akuru onse ndi akuru a anthu, ndi alembi, 54Ndipo Petro adamtsata Iye kutali, kufikira kulowa m'bwalo la mkulu wa ansembe; ndipo anali kukhala pansi pamodzi ndi anyamata, ndi kuotha moto. 55Ndipo ansembe akuru ndi akuru a milandu onse anafunafuna umboni wakutsutsa nao Yesu kuti amuphe Iye; koma sanaupeza. 56Pakuti ambiri anamcitira umboni wonama, ndipo umboni wao sunalingana. 57Ndipo ananyamukapo ena, namcitira umboni wakunama, nanena kuti, 58Ife tinamva Iye alikunena, kuti, Ine ndidzaononga Kacisi uyu wopangidwa ndi manja, ndi masiku atatu ndidzamanga wina wosapangidwa ndi manja. 59Ndipo ngakhale momwemo umboni wao sunalingana. 60Ndipo mkulu wa ansembe ananyamuka pakati, namfunsa Yesu, nanena, Suyankha kanthu kodi? Nciani ici cimene awa alikucitira mboni?61Koma anakhala cete, osayankhakanthu. Mkulu wa ansembe anamfunsanso, nanena naye, Kodi Iwe ndiwe Kristu, Mwana wace wa Wolemekezeka? 62Ndipo Yesu anati, Ndine amene; ndipo mudzaona Mwana wa munthu alikukhala ku dzanja lamanja la mphamvu, ndi kudza ndi mitambo ya kumwamba. 63Ndipo mkulu wa ansembe anang'amba maraya ace, nanena, Tifuniranjinso mboni zina?64Mwamva mwano wace; muyesa bwanji? Ndipo onse anamtsutsa Iye kuti ayenera kufa. 65Ndipo ena mayamba kumthira malobvu Iye, adi kuphimba nkhope yace, ndi cumbwanyula, ndi kunena naye, Lota; ndipo anyamatawo ananpanda Iye kofu. 66Ndipo pamene Petro anali iansi m'bwalo, anadzapo mmodzi va adzakazi a mkulu wa ansembe; 67ndipo anaona Petro alikuotha noto, namyang'ana iye, nanena, wenso unali naye Mnazarene, Yesu. 68Koma anakana, nanena, Sindidziwa kapena kumvetsa cimene ucinena iwe; ndipo anaturuka kunka kucipata; ndipo tambala analira. 69Ndipo anamuona mdzakaziyo, nayambanso kunena ndi iwo akuimirirapo, Uyu ngwa awo. 70Koma anakananso. Ndipo patapita kamphindi, akuimirirapo ananenanso ndi Petro, Zedi uli wa awo; pakutinso uti Mgalileya. 71Koma iye anayamba kutemberera, ndi kulumbira, Sindimdziwa munthuyu mulikunena. 72Ndipo pomwepo tambala analira kaciwiri. Ndipo Petro anakumbukila umo Yesu anati kwa iye, kuti, Tambala asanalire kawiri udzandikana katatu. Ndipo pakuganizira ici analira misozi.

Marko 15:1-47
1Ndipo pomwepo mamawa anakhala upo ansembe akuru, ndi akuru a anthu, ndi alembi, ndi akuru a milandu onse, namanga Yesu, namtenga, nampereka kwa Pilato. 2Ndipo Pilato anamfunsa Iye, Kodi ndiwe Mfumu ya Ayuda? Ndipo anayankha, nanena naye, Mwatero. 3Ndipo ansembe akuru anamnenera Iye zinthu zambiri. 4Ndipo Pilato anamfunsanso, nanena, Suyankha kanthu kodi? taona, akunenera Iwe zinthu zambiri zotere. 5Koma Yesu sanayankhanso kanthu; kotero kuti Pilato anazizwa. 6Ndipo adafuwamasulira paphwando wandende mmodzi, amene iwo anampempha, 7Ndipo analipo wina dzina lace Baraba, womangidwa pamodzi ndi opanduka, amene anapha munthu mumphandumo. 8Ndipo khamu la anthu anabwera nayamba kupempha kuti acite monga adafuwacitira. 9Ndipo Pilato anawayankha, nanena nao, Kodi mufuna kuti ndikumasulireni Mfumu ya Ayuda?10Pakuti anazindikira kuti ansembe akuru anampereka Iye mwanjiru. 11Koma ansembe akuru anasonkezera khamulo, kuti makamaka awamasulire Baraba.12Ndipo Pilato anawayankhanso, nati kwa iwo, Pamenepo ndidzacita ciani ndi Iye amene mumchula Mfumu ya Ayuda? 13Ndipo anapfuulanso, Mpacikeni pamtanda. 14Ndipo Pilato ananena nao, Pakuti Iye anacita coipa cotani? Koma iwo anapfuulitsatu, Mpacikeni Iye. 15Ndipo Pilato pofuna kuwakhazika mtima anthuwo, anawamasulira Baraba, napereka Yesu, atamkwapula, akampacike pamtanda.
16Ndipo asilikari anacoka naye nalowa m'bwalo, ndilo Pretorio; nasonkhanitsa gulu lao lonse. 17Ndipo anambveka Iye cibakuwa, naluka korona waminga, nambveka pa Iye; 18ndipo anayamba kumlankhula Iye, kuti, Tikuoneni, Mfumu ya Ayuda! 19Ndipo anampanda Iye pamutu pace ndi bango, namthira malobvu, nampindira maondo, namlambira. 20Ndipo atatha kumnyoza anambvula cibakuwaco nambveka Iye zobvala zace. Ndipo anaturuka naye kuti akampacike Iye pamtanda. 21Ndipo anakangamiza wina wopitirirapo, Simoni wa ku Kurene, alikucokera kuminda, atate wao wa Alesandere ndi Rufu, kuti anyamule mtanda wace.22Ndipo anamtenga kunka naye ku malo Golgota, ndiwo, osandulika, Malo-a-bade. 23Ndipo anampatsa vinyo wosanganiza ndi mure; koma Iye sanamlandira.24Ndipo anampacika Iye, nagawana zobvala zace mwa iwo okha, ndi kucita maere pa izo, kuti adziwe yense adzatengaciani. 25Ndipo panali ora lacitatu, ndipo anampacika Iye. 26Ndipo lembo la mlandu wace linalembedwa pamwamba, MFUMU YAAYUDA. 27Ndipo anapacika pamodzi ndi Iye acifwamba awiri; mmodzi ku dzanja lace lamanja ndi wina kulamanzere.[ 28]29Ndipo iwo akupitirirapo anamcitira mwano, napukusa mitu yao, nanena, Ha!
Iwe wakupasula Kacisi, ndi kummanga masiku atatu, 30udzipulumutse mwini, nutsike pamtanda. 31Moteronso ansembe akuru anamtonza mwa iwo okha pamodzi ndi alembi, nanena, Anapulumutsa ena; sakhoza kudzipulumutsa yekha. 32Atsike tsopano pamtanda, Kristu Mfumu ya Israyeli, kuti tione, ndi kukhulupirira. Ndipo iwo akupacikidwa naye anamlalatira.
33Ndipo pofika ora lacisanu ndi cimodzi, panali mdima pa dziko lonse, kufikira ora lacisanu ndi cinai. 34Ndipo pa ora lacisanu ndi cinai Yesu anapfuula ndi mau okweza, Eloi, Eloi, lama sabakitani? ndiko kusandulika,
Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?
35Ndipo ena akuimirirapo, paku mva, ananena, Taonani, aitana Eliya 36Ndipo anathamanga wina, nadzaza cinkhupule ndi vinyo wosasa naciika pabango, namwetsa Iye nanena, Lekani; tione ngati Eliys adza kudzamtsitsa. 37Ndipo Yesr anaturutsa mau okweza, napereka mzimu wace.
38Ndipo cinsart cocinga ca m'Kacisi cinang'ambika pakati, kuyambira kumwamba kufikira pansi. 39Ndipo pamene kenturiyo, woimirirapo popenyana ndi Iye, anaona kuti anapereka mzimu kotero, anati, Zoonadi, munthu uyu anali Mwana wa Mulungu. 40Ndipo analinso kumeneko akazi akuyang'anira kutali; mwa iwo anali Maliya wa Magadala, ndi Maliya amace wa Yakobo wamng'ono ndi wa Yose, ndi Salome; 41amene anamtsata Iye, pamene anali m'Galileya, namtumikira; ndi akazi ena ambiri, amene anakwera kudza ndi Iye ku Yerusalemu.
42Ndipo atafika tsono madzulo, popeza mpa tsiku lokonzera, ndilo la pambuyo pa Sabata, 43anadzapo Y osefe wa ku Arimateya, mkulu wa mirandu womveka, amene yekha analikuyembekezera Ufumu wa Mulungu; nalimba mtima nalowa kwa Pilato, napempha mtembo wace wa Yesu. 44Ndipo Pilato anazizwa ngati adamwaliradi; naitana kenturiyo, namfunsa ngati adamwalira kale.45Ndipo pamene anacidziwa ndi kenturiyo, anamninkha Yosefe ntembowo.46Ndipo anagula oafuta, namtsitsa Iye, namkulunga n'bafutamo, namuika m'manda osenedwa m'thanthwe; nakunkhunicira mwala pa khomo la manda.47Ndipo Maliya wa Magadala ndi Maliya amace wa Yose anapenya pomwe anaikidwapo.

2 Akolinto 5:21
21Ameneyo sanadziwa ucimo anamyesera ucimo m'malo mwathu; kuti ife tikhale cilungamo ca Mulungu mwa iye.

1 Yohane 3:8-10
8iye wocita cimo ali wocokera mwa mdierekezi, cifukwa mdierekezi amacimwa kuyambira paciyambi. Kukacita ici Mwana wa Mulungu adaonekera, ndiko kuti akaononge nchito za mdierekezi, 9Yense wobadwa kucokera mwa Mulungu sacita cimo, cifukwa mbeu yace ikhala mwa iye; ndipo sakhoza kucimwa, popeza wabadwa kucokera mwa Mulungu. 10M'menemo aoneka ana a Mulungu, ndi ana a mdierekezi: yense wosacita cilungamo siali wocokera mwa Mulungu; ndi iye wosakonda mbale wace.

Aefeso 1:18-22
18ndiko kunena kuti maso amitima yanu awalitsike, ktiti mukadziwe inu ciyembekezo ca kuitana kwace nciani; cianinso cuma ca ulemerero wacolowa cace mwa oyera mtima, 19ndi ciani ukuru woposa wa mphamvu yace ya kwa ife okhulupira, monga mwa macitidwe a mphamvu yace yolimba, 20imene anacititsa mwa Kristu, m'mene anamuukitsa kwa akufa, namkhazikitsa pa dzanja lace lamanja m'zakumwamba, 21 pamwamba pa ukulu wonse, ndi ulamuliro ndi mphamvu, ndi ufumu, ndi dzina liri lonse lochedwa, si m'nyengo yinoya pansi pano yokha, komanso mwaiyo ikudza; 22ndipo anakonza zonse pansi pa mapazi ace, nampatsa iye akhale mutu pamtu pa zonse,

Chibvumbulutso 20:1-3, 7-10
1Ndipo ndinaona mngelo anatsika Kumwamba, nakhala naco cifungulo ca phompho, ndi unyolo waukuru m'dzanja lace. 2Ndipo anagwira cinjoka, njoka yakaleyo, ndiye mdierekezi ndi Satana, nammanga iye zaka cikwi, 3namponya kuphompho, natsekapo, nasindikizapo cizindikilo pamwamba pace, kuti asanyengenso amitundu kufikira kudzatha zaka cikwi; patsogolo pace ayenera kumasulidwa iye kanthawi. 7Ndipo pamene zidzatha zaka cikwi, adzamasulidwa Satana m'ndende yace;8nadzaturuka kudzasokeretsa amitundu ali mu ngondya zinai za dziko, Gogo, ndi Magogo, kudzawasonkhanitsa acite nkhondo: ciwerengero cao ca iwo amene cikhala ngati mcenga wa kunyanja. 9Ndipo anakwera nafalikira m'dziko, nazinga tsasa la oyera mtima ndi mudzi wokondedwawo: ndipo unatsika mota wakumwamba nuwanyeketsa. 10Ndipo mdierekezi wakuwasokeretsa anaponyedwa m'nyanja ya mota ndi sulfure, kumeneko kulinso ciromboco ndi mneneri wonyengayo; ndipo adzazunzidwa usana ndi usiku ku nthawi za nthawi.

7. Machitidwe 4:12
12Ndipo palibe cipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwanalo.

 

 
 

 

YESU NDI NDANI?

Mavesi a m'Baibulo

 
 
Copyright ©  2023 www.UnitedCaribbean.com. All rights reserved. Disclaimer Click to Contact us