|  
               
               Stonecroft Stonecroft Training Mndandanda wa Utatu Malangizo Otsogolera Mavesi a m'BaibuloAdult Stonecroft International The International Team  English YDT Teachings Maphunziro a AnaMalawi Moringa Projects    |  | home >>stonecroft>> 
     mavesi a m'baibulo  >>   phunziro 2  >>   phunziro 3             
            
             
            YESU NDI NDANI? - Mavesi a m'Baibulo - Phunziro #3 
 
 Kuwerenga Baibulo kwa Mlungu ndi Mlungu Marko 1:16-2816Ndipo pakuyenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, anaona Simoni 
              ndi Andreya, mbale wace wa Simoni, alinkuponya psasa m'nyanja; pakuti 
              anali asodzi. 17Ndipo Yesu ananena nao, Idzani pambuyo panga, ndipo 
              ndidzakusandutsani inu asodzi a anthu. 18Ndipo pomwepo anasiya makoka 
              ao, namtsata Iye. 19Ndipo atapita patsogolo pang'ono, anaona Yakobo, 
              mwana wa Zebedayo, ndi Yohane mbale wace, iwonso anali m'combo nakonza 
              makoka ao.20Ndipo pomwepo anawaitana: ndipo anasiya atate wao Zebedayo 
              m'combomo pamodzi ndi anchito olembedwa, namtsata. 21Ndipo iwo analowa 
              m'Kapemao; ndipo pomwepo pa dzuwa la Sabata iye analowa m'sunagoge 
              naphunzitsa, 22Ndipo anazizwa ndi ciphunzitso cace; pakuti anaphunzitsa 
              monga mwini mphamvu, si monga alembi. 23Ndipo pomwepo panali munthu 
              m'sunagoge mwao ali ndi mzimu wonyansa; ndipo anapfuula iye 24kuti, 
              Tiri ndi ciani ife ndi Inu Yesu wa ku Nazarete? Kodi mwadza kudzationonga 
              ife? Ndikudziwani, ndinu Woyerayo wa Mulungu. 25Ndipo Yesu anaudzudzula, 
              kuti, Khala uli cete, nuturuke mwa iye. 26Ndipo mzimu wonyansa, 
              pomng'amba, ndi kupfuula ndi mau akuru, unaturuka mwa iye. 27Ndipo 
              anazizwa onse, kotero kuti anafunsana mwa iwo okha, kuti, Ici nciani? 
              ciphunzitso catsopano! ndi mphamvu alamula ingakhale mizimu yonyansa, 
              ndipo imvera Iye.28Ndipo mbiri yace inabuka pompaja ku dziko lonse 
              la Galileya lozungulirapo.
 Marko 1:29-3929Ndipo pomwepo, poturuka m'sunagoge, iwo analowa m'nyumba ya Simoni 
              ndi Andreya pamodzi ndi Yakobo ndi Yohane, 30Ndipo mpongozi wace 
              wa Simoni anali gone wodwala malungo; ndipo pomwepo anamuuza za 
              iye:31ndipo anadza namgwira dzanja, namuutsa; ndipo malungo anamleka, 
              ndipo anawatumikira iwo.
 32Ndipo madzulo, litalowa dzuwa, anadza nao kwa Iye onse akudwala, 
              ndi akugwidwa ndi ziwanda. 33Ndipo mudzi wonse unasonkhana pakhomo. 
              34Ndipo anaciritsa anthu ambiri akudwala nthenda za mitundu mitundu, 
              naturutsa ziwanda zambiri; ndipo sanalola ziwandazo zilankhule, 
              cifukwa zinamdziwa Iye.
 35Ndipo m'mawa mwace anauka usikusiku, naturuka namuka kucipululu, 
              napemphera kumeneko. 36Ndipo Simoni ndi anzace anali naye anamtsata,37nampeza, 
              nanena naye, Akufunani inu anthu onse. 38Ndipo ananena nao, Tiyeni 
              kwina, ku midzi iri pafupi apa, kuti ndilalikire komwekonso; pakuti 
              ndadzera nchito imene. 39Ndipo analowa m'masunagoge mwao m'Galileya 
              monse, nalalikira, naturutsa ziwanda.
 Marko 3:13-1913Ndipo anakwera m'phiri, nadziitanira iwo amene anawafuna Iye mwini; 
              ndipo anadza kwa Iye. 14Ndipo anaika khumi ndi awiri, kuti akhale 
              ndi Iye, ndi kuti akawatume kulalikira, 15ndi kuti akhale nao ulamuliro 
              wakuturutsa ziwanda.16Ndipo Simoni anamucha Petro; 17ndi Yakobo 
              mwana wa Zebedayo, ndi Yohane mbale wace wa Yakobo, iwo anawacha 
              Boanerge, ndiko kuti, Ana a bingu; 18ndi Andreya, ndi Filipo, ndi 
              Bartolomeyo, ndi Mateyu, ndi Tomasi, ndi Yakobo mwana wa Alifeyo, 
              ndi Tadeyo, ndi Simoni Mkanani, 19ndi Yudase Isikariote, ndiye amene 
              anampereka Iye.
 Marko 4:35-4135Ndipo dzuwa lomwelo, pofika madzulo, ananena kwa iwo, Tiolokere 
              tsidya lina. 36Ndipo posiya khamulo anamtenga apite nao, monga momwe 
              anali, mungalawa. Ndipo panali ngalawa zina pamodzi ndi Iye. 37Ndipo 
              panauka namondwe wamkuru wa mphepo, ndi mafunde angabvira mungalawa, 
              motero kuti ngalawa inayamba kudzala. 38Ndipo Iye mwini anali kutsigiro, 
              nagona tulo pamtsamiro; ndipo anamuutsa Iye nanena kwa Iye, Mphunzitsi, 
              kodi simusamala kuti titayika ife? 39Ndipo anauka, nadzudzula mphepo, 
              nati kwa nyanja, kuti, Tonthola, khala bata. Ndipo mphepo inaleka, 
              ndipokunagwa bata lalikuru.40Ndipo ananena nao, Mucitiranji mantha? 
              kufikira tsopano mulibe cikhulupiriro kodi? 41Ndipo iwo anacita 
              mantha akuru, nanenana wina ndi mnzace, Uyu ndani nanga, kuti ingakhale 
              mphepo ndi nyanja zimvera Iye?
 Marko 6:30-4430Ndipo atumwi anasonkhana kwa Yesu; namuuza ziri zonse adazicita, 
              ndi zonse adaziphunzitsa, 31Ndipo Iye ananena nao, Idzani inu nokha 
              padera ku malo acipululu, mupumule kamphindi, Pakuti akudza ndi 
              akucoka anali piringu piringu, ndipo analibe nthawi yokwanira kudya. 
              32Ndipo anacokera m'ngalawa kunka ku malo acipululu padera. 33Ndipo 
              anthu anawaona alikumuka, ndipo ambiri anawazindikila, nathamangira 
              limodzi kumeneko pamtunda, ocokera m'midzi monse, nawapitirira. 
              34Ndipo anaturuka Iye, naona khamu lalikuru la anthu, nagwidwa cifundo 
              ndi iwo, cifukwa anali ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo anayamba 
              kuwaphunzitsa zinthu zambiri. 35Ndipo pamene dzuwa lidapendeka ndithu, 
              anadza kwa Iye ophunzira ace, nanena, Malo ana nga cipululu, ndi 
              dzuwa lapendeka ndithu; 36muwauze kuti amuke, alowe kumiraga ndi 
              ku midzi yozungulira, akadzigulire okha kanthu kakudya. 37Koma Iye 
              anayankha nati kwa iwo, Apatseni kudya ndinu. Ndipo iwo ananena 
              naye, Kodi tikapita ife ndi kugula mikate ya pa marupiya atheka 
              mazana awiri, ndi kuwapatsa kudya? 38Ndipo Iye ananena nao, kuti, 
              Muli nayo mikate ingati? pitani, mukaone. Ndipo m'mene anadziwa 
              ananena, lsanu, ndi nsomba ziwiri. 39Ndipo anawalamulira kuti akhalitse 
              pansi onse magulu magulu pamsipu. 40Ndipo anakhala pansi mabungwe 
              mabungwe a makumi khumi, ndi a makumi asanu.41Ndipo Iye anatenga 
              mikate isanuyo ndi nsomba ziwirizo nayang'anakumwamba, nadalitsa, 
              nagawa mikate; napatsa kwa ophunzira kuti apereke kwa iwo; ndi nsomba 
              ziwiri anagawira onsewo. 42Ndipo anadya iwo onse, nakhuta. 43Ndipo 
              anatola makombo mitanga khumi ndi iwiri, ndiponso za nsomba. 44Ndipo 
              amene anadya mikate iyo anali amuna zikwi zisanu.
 Marko 10:2-162Ndipo anadza kwa Iye Afarisi, namfunsa Iye ngati kuloledwa kuti 
              munthu acotse mkazi wace, namuyesa Iye. 3Ndipo Iye anayankha nati 
              kwa iwo, Kodi Mose anakulamulirani ciani? 4Ndipo anati, Mose analola 
              kulembera kalata wakulekanira, ndi kumcotsa. 5Koma Yesu anati kwa 
              iwo, Cifukwa ca kuuma kwa mitima yanu anakulemberani lamulo ili. 
              6Koma kuyambira pa ciyambi ca malengedwe anawapanga mwamuna ndi 
              mkazi.7Cifukwa cace mwamuna adzasiya atate wace ndi amai wace, ndipo 
              adzaphatikizana ndi mkazi wace; 8ndipo awiriwa adzakhala thupi limodzi: 
              kotero kuti salinso awiri, koma thupi limodzi. 9Cifukwa cace cimene 
              Mulungu anacimanga pamodzi, asacilekanitse munthu. 10Ndipo m'nyumba 
              ophunzira anamfunsanso za cinthu ici. 11Ndipo Iye ananena nao, Munthu 
              ali yense akacotsa mkazi wace, nakakwatira wina, acita cigololo 
              kulakwira mkaziyo;12ndipo ngati mkazi akacotsa mwamuna wace, nakwatiwa 
              ndi wina, acita cigololo iyeyu.
 13Ndipo analinkudza nato kwa Iye tiana, kuti akatikhudze; ndipo 
              ophunzirawo anawadzudzula. 14Koma pamene Yesu anaona anakwiya, ndipo 
              anati kwa iwo, Lolani tiana tidze kwa Ine; musatiletse: pakuti Ufumu 
              wa Mulungu uli wa totere.15Ndithu ndinena ndi inu, Munthu ali yense 
              wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati kamwana, sadzalowamo konse. 16Ndipo 
              Iye anatiyangata, natidalitsa, ndi kuika manja ace pa ito.
 Yohane 2:13-2213Ndipo Paskha wa Ayuda unayandikira, ndipo Yesu anakwera kunka 
              ku Yerusalemu. 14Ndipo anapeza m'Kacisiiwo akugulitsa ng'ombe ndi 
              nkhosa ndi nkhunda, ndi akusinthana ndalama alikukhala pansi. 15Ndipo 
              pamene adapanga mkwapulo wazingwe, anaturutsa onse m'Kacisimo, ndi 
              nkhosa ndi ng'ombe; nakhuthula ndalama za osinthanawo, nagubuduza 
              magome; 16nati kwa iwo akugulitsa nkhunda, Cotsani izi muno; musamayesa 
              nyumba ya Atate wanga nyumba ya malonda. 17Akuphunzira ace anakumbukila 
              kuti kunalembedwa, Cangu ca pa nyumba yanu candidya ine. 18Cifukwa 
              cace Ayuda anayankha nati kwa iye, Mutionetsera ife cizindikilo 
              canji, pakuti mucita izi? 19Yesu anayankha nati kwa iwo, Pasulani 
              kacisi uyu, ndipo masiku atatu ndidzamuutsa.20Pamenepo Ayuda anati, 
              Zaka makumi anai ndi zisanu ndi cimodzi analimkumanga Kacisiyu, 
              kodi inu mudzamuutsa masiku atatu? 21Koma iye analikunena za kacisi 
              wathupi lace. 22Cifukwa cace atauka kwa akufa, akuphunzira ace anakumbukira 
              kuti ananena ici; ndipo anakhulupirira colemba, ndi mau amene Yesu 
              ananena.
 Marko 11:15-17 15Ndipo anafika iwo ku Yerusalemu; ndipo Iye analowa m'Kacisi, nayamba 
              kuturutsa akugulitsa ndi akugula malonda m'Kacisimo, nagubuduza 
              magome a osinthana ndalama, ndi mipando yaogulitsa nkhunda; 16ndipo 
              sanalola munthu ali yense kunyamula cotengera kupyola pakati pa 
              Kacisi. 17Ndipo anaphunzitsa, nanena nao, Sicilembedwa kodi, Nyumba 
              yanga idzachedwa nyumba yakupempheramo anthu a mitundu yonse? koma 
              inu mwaiyesa phanga la acifwamba.
 Luka 1:29, 34; 2:19, 5129Koma iye ananthunthumira ndi mau awa, nasinkhasinkha kulankhula 
              uku nkutani. 34Koma Mariya anati kwa mngelo, ici cidzacitika bwanji, 
              popeza ine sindidziwa mwamuna?
 19Koma Mariya anasunga mau awa onse, nawalingalira mumtima mwace.
 51Ndipo anatsika nao pamodzi nadza ku Nazarete; nawamvera iwo: ndipo 
              amace anasunga zinthu izi zonse mumtima mwace.
 Yohane 1:1-3, 141PACIYAMBI panali Mau, ndipo Mau anali kwa Mulungu, ndipo Mau ndiye 
              Mulungu. 2Awa anali paciyambi kwa Mulungu, 3Zonse: zinalengedwa 
              ndi iye; ndipo kopanda iye sikunalengedwa kanthu kali konse kolengedwa,
 14Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo 
              tinaona ulemerero wace, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, 
              wodzala ndi cisomo ndi coonadi.
 1. a. Luke 3:2323Ndipo Yesuyo, pamene anayamba nchito yace, anali monga wa zaka 
              makumi atatu, ndiye (monga anthu adamuyesa) mwana wa Yosefe, mwana 
              wa Heli,
 b. 1 Yohane 4:99Umo cidaoneka cikondi ca Mulungu mwa ife, kuti Mulungu anamtuma 
              Mwana wace wobadwa yekha alowe m'dziko lapansi, kuti tikhale ndi 
              moyo mwa iye.
 2. a. Yohane 5:1717Koma Yesu anayankha iwo, Atate wanga amagwira nchito kufikira 
              tsopano, lnenso ndigwira nchito.
 3. a. Marko 1:2121Ndipo iwo analowa m'Kapemao; ndipo pomwepo pa dzuwa la Sabata 
              iye analowa m'sunagoge naphunzitsa,
 b. Marko 1:32-3432Ndipo madzulo, litalowa dzuwa, anadza nao kwa Iye onse akudwala, 
              ndi akugwidwa ndi ziwanda. 33Ndipo mudzi wonse unasonkhana pakhomo. 
              34Ndipo anaciritsa anthu ambiri akudwala nthenda za mitundu mitundu, 
              naturutsa ziwanda zambiri; ndipo sanalola ziwandazo zilankhule, 
              cifukwa zinamdziwa Iye.
 c. Marko 1:3535Ndipo m'mawa mwace anauka usikusiku, naturuka namuka kucipululu, 
              napemphera kumeneko.
 d. Marko 1:3838Ndipo ananena nao, Tiyeni kwina, ku midzi iri pafupi apa, kuti 
              ndilalikire komwekonso; pakuti ndadzera nchito imene.
 e.Marko 6:7-12Ndipo anadziitanira khumi ndi awiriwo, nayamba kuwatumiza Iwo awiri 
              awiri; nawapatsa mphamvu pa mizimu yonyansa; 8ndipo anawauza kuti 
              asatenge kanthu ka paulendo, koma ndodo yokha; asatenge mkate, kapena 
              thumba, kapena ndalama m'lamba lao; 9koma abvale nsapato; ndipo 
              anati, Musabvale malaya awiri. 10Ndipo ananena nao, Kumene kuli 
              konse mukalowa m'nyumba, khalani komweko kufikira mukacokako. 11Ndipo 
              pamalo ponse sakulandirani, kapena kumvera inu, pakucoka kumeneko, 
              sansani pfumbi liri ku mapazi anu, likhale mboni ya kwa iwo. 12Ndipo 
              anaturuka nalalikira kuti anthu atembenuke mitima.
 Yohane 21:2525Koma palinso zina zambiri zimene. Yesu anazicita, zoti zikadalembedwa 
              zonse phe, ndilingalira kuti dziko lapansi silikadakhala nao malo 
              a mabuku amene akadalembedwa. Amen.
 Zozizwitsa Zake 4. a. Luka 4:33-3633Ndipo munali m'sunagoge munthu, wokhala naco ciwanda conyansa; 
              napfuula ndi mau olimba, kuti, 34Ha! tiri ndi ciani ndi Inu, Yesu 
              wa ku N azarete? kodi munadza kutiononga ife? ndikudziwani Inu muli 
              yani, ndinu Woyera wace wa Mulungu. 35Ndipo Yesu anamdzudzula iye, 
              nanena, Tonthola, nuturuke mwa iye. Ndipo ciwandaco m'mene cinamgwetsa 
              iye pakati, cinaturuka mwa iye cosampweteka konse. 36Ndipo anthu 
              onse anadabwa, nalankhulana wina ndi mnzace, nanena, Mau amenewa 
              ali otani? cifukwa ndi ulamuliro ndi mphamvu angolamulira mizimu 
              yonyansa, ndipo ingoturuka.
 b. Luka 5:4-104Ndipo pamene iye analeka kulankhula, anati kwa Simoni, Kankhira 
              kwa kuya, nimuponye makoka anu kukasodza. 5Ndipo Simoni anayankha, 
              nati, Ambuye, tinagwiritsa nchito usiku wonse osakola kanthu, koma 
              pa mau anu ndidzaponya makoka. 6Ndipo pamene anacita ici, anazinga 
              unyinji waukuru wansomba; ndipo makoka ao analinkung'ambika; 7ndipo 
              anakodola anzao a m'ngalawa yinayo, adze awathangate. Ndipo anadza, 
              nadzaza ngalawa zonse ziwiri, motero kuti zinalinkumira. 8Koma Simoni 
              Petro, pamene anaona, anagwa pansi pa mabondo ace a Yesu, nanena, 
              Mucoke kwa ine, Ambuye, cifukwa ndine munthu wocimwa. 9Pakuti cizizwo 
              cidagwira iye, ndi onse amene anali naye, pa kusodzako kwa nsomba 
              zimene anazikola; 10ndipo cimodzimodzinso Yakobo ndi Yohane, ana 
              a Zebedayo, amene anali anzace a Simoni. Ndipo Yesu anati kwa Simoni, 
              Usaope, kuyambira tsopano udzakhala msodzi wa anthu.
 c. Marko 1:40-4240Ndipo anadza kwa Iye wodwala khate, nampempha Iye, namgwadira, 
              ndi kunena ndi Iye, Ngati mufuna mukhoza kundikonza. 41Ndipo Yesu 
              anagwidwa cifundo, natansa dzanja namkhudza iye, nanena naye, Ndifuna; 
              khala wokonzedwa. 42Ndipo pomwepo khate linamcoka, ndipo anakonzedwa.
 d. Mateyu 15:1-91Pomwepo anadza kwa Yesu Afarisi ndi alembi, ocokera ku Yerusalemu, 
              nati,2Ophunzira anu alumphiranji miyambo ya makolo? pakuti sasamba 
              manja pakudya. 3Ndipo Iye anayankha, nati kwa iwo, Inunso mulumphiranji 
              lamulo la Mulungu cifukwa ca miyambo yanu? 4Pakuti Mulungu anati,
 Lemekeza atate wako ndi amako; ndipo, Wakunenera atate wace ndi 
              amace zoipa, afe ndithu.
 5Koma inu munena, Amene ali yense anena kwa atate wace kapena kwa 
              amace, Ico ukanathandizidwa naco, neoperekedwa kwa Mulungu; 6iyeyo 
              sadzalemekeza atate wace. Ndipo inu mupeputsa mau a Mulungu cifukwa 
              ca miyambo yanu.7Onyenga inu! Yesaya ananenera bwino za inu, ndikuti, 
              8Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yao; Koma mtima wao uli kutari 
              ndi Ine.
 9Koma andilambira Ine kwacabe, Ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo 
              a anthu.
 e. Luka 7:11-1711Ndipo kunali, katapita kamphindi, iye ana pita kumudzi, dzina 
              lace Nayini; ndipo ophunzira ace ndi mpingo waukuru wa anthu anapita 
              nave. 12Ndipo pamene anayandikira ku cipata ca mudziwo, onani, anthu 
              analikunyamula munthu wakufa, mwana wamwamuna mmodzi yekha, amace 
              ndiye mkazi wamasiye; ndipo anthu ambiri a kumudzi anali pamodzi 
              naye. 13Ndipo pamene Ambuye anamuona, anagwidwa ndi cifundo cifukwa 
              ca iye, nanena naye, Usalire.14Ndipo anayandikira, nakhudza cithatha; 
              ndipo akumnyamulawo anaima. Ndipo iye anati, Mnyamata iwe, ndinena 
              ndi iwe, Tauka. 15Ndipo wakufayo anakhala tsonga, nayamba kulankhula. 
              Ndipo anampereka kwa amace. 16Ndipo mantha anagwira onsewo: ndipo 
              analemekeza Mulungu, nanena kuti, Mneneri wamkuru wauka mwa ife; 
              ndipo Mulungu wadzaceza ndi anthu ace. 17Ndipo mbiri yace imeneyo 
              inabuka ku Yudeya lonse, ndi ku dziko lonse loyandikira.
 Luka 3:21-22Cholinga Chantchito21Ndipo panali pamene anthu onse anabatizidwa, ndipo Yesu anabatizidwa, 
              nalikupemphera, kuti panatseguka pathambo, 22ndipo Mzimu Woyera 
              anatsika ndi maonekedwe a thupi lace ngati nkhunda, nadza pa iye; 
              ndipo munaturuka mau m'thambo, kuti, Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa, 
              mwa Iwe ndikondwera.
 5. a. Yohane 6:3838Pakuti ndinatsika Kumwamba, si kuti ndicite cifuniro canga, koma 
              cifuniro ca iye amene anandituma Ine.
 b. Yohane 7:16-1716Pamenepo Yesu anayankha iwo, nati, Ciphunzitso canga siciri canga, 
              koma ca iye amene anandituma Ine. 17Ngati munthu ali yense afuna 
              kucita cifuniro cace, adzazindikira za ciphunzitsoco, ngati cicokera 
              kwa Mulungu, kapena ndilankhula zocokera kwa Ine ndekha.
 c. Afilipi 2:1313pakuti wakucita mwa inu kufuna ndi kucita komwe, cifukwa ca kukoma 
              mtima kwace, ndiye Mulungu,
 6. Aroma 12:22Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, 
              mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire cimene ciri cifuno 
              ca Mulungu, cabwino, ndi cokondweretsa, ndi cangwiro.
 Genesis 1:27-28Mulungu ndipo adalenga munthu mu chifanizo chache; m'chifanizo cha 
              Mulungu adalenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi anawalenga. 
              Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, "Mubalane 
              muchuluke; mudzadze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa somba 
              za m'nanja, ndi pa mbalame za m'mlengalenga, ndi pa za moyo zonse 
              zakukwawa pa dziko lapansi."
 Genesis 2:15Ndipo Yehova Mulungu anatenga munthuyo namuika iye m'munda wa Eden 
              kuti
 aulime nauyanganire.
 Genesis 3:17Kwa Adamu ndipo anati, Chifukwa kuti wamvera mawu a mkazi wako, 
              nudya za mtengo umene ndinakuza iwe kuti Usadyeko; "nthaka 
              ikhale yotembeleledwa chifukwa cha iwe; m'kusauka udzadyako masiku 
              onse a moyo wako."
 7.a 2 Atesalonika 3:1010Pakutinso pamene tinali nanu tidakulamulirani ici, Ngati munthu 
              safuna kugwira nchito, asadyenso.
 b. Aroma 12:1111musakhale aulesi m'macitidwe anu; khalani acangu mumzimu, tumikirani 
              Ambuye;
 8. Aefeso 6:5-85Akapolo inu, mverani iwo amene ali ambuye anu monga mwa thupi, 
              ndi kuwaopa ndi kunthunthumira nao, ndi mtima wanu wosakumbukila 
              kanthu kena, monga kwa Kristu; 6si monga mwa ukapolo wa pamaso, 
              monga okondweretsa anthu, komatu monga akapolo a Kristu, akucita 
              cifuniro ca Mulungu cocokera kumtima; 7akucita ukapolo ndi kubvomereza 
              mtima, monga kutumikira Yesu Kristu, si anthu ai; 8podziwa kuti 
              cinthu cokoma ciri conse yense acicita, adzambwezera comweci Ambuye, 
              angakhale ali kapolo kapena mfulu.
 9. a. 1 Akorinto 10:3131Cifukwa cace mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale mucita 
              kanthu kena, citani zonse ku ulemerero wa Mulungu.
 b. 1 Akorinto 16:1414Zanu zonse zicitike m'cikondi.
 c. Akolose 3:2323ciri conse mukacicita, gwirani nchito mocokera mumtima, monga 
              kwa Ambuye, osati kwa anthu ai;
 Yohane 13:34-3534Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzace; 
              monga ndakonda Inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzace. 351 Mwa 
              ici adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli naco 
              cikondano wina ndi mnzace.
 Eksodo 31:15Agwire ntchito masiku asanu ndi limodzi; koma la chisanu ndi chiwiri 
              ndilo Sabata lopumula, lopatulika la Yehova; aliyense ogwira ntchito 
              tsiku la Sabata, aphedwe ndithu.
 Mateyu 5:1717Musaganize kuti ndinadza Ine kudzapasula cilamulo kapena ane, 
              neri: sindinadza kupasula, koma kukwaniritsa.
 Marko 6:3131Ndipo Iye ananena nao, Idzani inu nokha padera ku malo acipululu, 
              mupumule kamphindi, Pakuti akudza ndi akucoka anali piringu piringu, 
              ndipo analibe nthawi yokwanira kudya.
 Mateyu 11:28-3028Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani 
              inu. 29Senzani gori langa, ndipo phunzirani kwa Ine; cifukwa ndiri 
              wofatsa ndi wodzicepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo 
              yanu. 30Pakuti 1 gori langa liri lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.
 10. a. Yohane 6:2929Yesu anayankha nati kwa iwo, Nchito ya Mulungu ndi iyi, kuti mukhulupirire 
              iye amene Iyeyo anamtuma.
 b. Yohane 3:1616Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana 
              wace wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike, koma 
              akhale nao moyo wosatha.
 1 Akolinto 3:13-1513nchito ya yense idzaonetsedwa; pakuti tsikulo lidzaisonyeza, cifukwa 
              kuti yabvumbuluka m'moto; ndipo mota wokha udzayesera nchito ya 
              yense ikhala yotani. 14Ngati nchito ya munthu ali yense khala imene 
              anaimangako, adzaandira mphotho. 15Ngati nchito ya wina itenthedwa, 
              zidzaonongeka zace; koma iye yekha adzapulumutsilwa; koma monga 
              momwe mwa noto.
 
 |  |