Stonecroft
Stonecroft Training
Mndandanda wa Utatu
Malangizo Otsogolera
Mavesi a m'Baibulo
Adult Stonecroft International
The International Team
English YDT Teachings
Maphunziro a Ana
Malawi Moringa Projects
|
|
home >>stonecroft>>mzimu
woyera uli kuti?>> mavesi a m'baibulo >> phunziro 5 >> phunziro 6
KODO MZIMU WOVERA ULI KUTI? - Mavesi a m'Baibulo - Phunziro #6
Kuwerenga Baibulo mlungu ndi mlungu
Aroma 7: 14-25
14Pakuti tidziwa kuti cilamulo ciri cauzimu; koma ine ndiri wathupi,
wogulitsidwa kapolo wa ucimo. 15Pakuti cimene ndicita sindicidziwa;
pakuti sindicita cimene ndifuna, koma cimene ndidana naco, ndicita
ici. 16Koma ngati ndicita cimene sindicifuna, ndibvomerezana naco
cilamulo kuti ciri cabwino. 17Ndipo tsopano si ine ndicicita, koma
ucimo wakukhalabe m'kati mwanga ndiwo. 18Pakuti ndidziwa kuti m'kati
mwanga, ndiko m'thupi langa, simukhala cinthu cabwino; pakuti kufuna
ndiri nako, koma kucita cabwino sindikupeza. 19Pakuti cabwino cimene
ndicifuna, sindicicita; koma coipa cimene sindicifuna, cimeneco
ndicicita.20Koma ngati ndicita cimene sindicifuna, si ndinenso amene
ndicicita, koma ucimo wakukhalabe m'kati mwanga ndiwo. 21Ndipo cotero
odipeza lamulo ili, kuti, pamene ndifuna cabwino, coipa ciriko.
22Pakuti monga mwa munthu wa m'kati mwanga, ine ndikondwera ndi
cilamulo ca Mulungu: 23koma ndiona lamulo lina m'ziwalo zanga, lirikulimbana
ndi lamulo la mtima wanga, ndi kundigonjetsa kapolo wa lamulo la
m'ziwalo zanga. 24Munthu wosauka ine; adzandilanditsa ndani m'thupi
la imfa iyi? 25Ndiyamika Mulungu, mwa Yesu Kristu Ambuye wathu.
Ndipo cotero ine ndekha ndi mtimatu nditumikira cilamulo ca Mulungu;
koma ndi thupi nditumikira lamulo la ucimo.
Aroma 8: 1-17
1Cifukwa cace tsopano iwo akukhala mwa Kristu Yesu alibe kutsutsidwa.2Pakuti
cilamulo ca mzimu wa moyo mwa Kristu Yesu candimasula ine ku lamulo
la ucimo ndi la imfa. 3Pakuti cimene cilamulo sicinathe kucita,
popeza cinafoka mwa thupi, Mulungu anatumiza Mwana wace wa iye yekha
m'cifanizo ca thupi la ucimo, ndi cifukwa ca ucimo, natsutsa ucimo
m'thupi; 4kuti coikika cace ca cilamulo cikakwaniridwe mwa ife,
amene sitiyendayenda monga mwa thupi, koma monga mwa mzimu. 5Pakuti
iwo amene ali monga mwa thupi asamalira zinthu za thupi; koma iwo
amene ali monga mwa mzimu, asamalira zinthu za mzimu: 6pakuti cisamaliro
ca thupi ciri imfa; koma cisamaliro ca mzimu ciri moyo ndi mtendere.
7Cifukwa cisamaliro ca thupi cidana ndi Mulungu; pakuti sicigonja
ku cilamulo ca Mulungu, pakuti sicikhoza kutero. 8Ndipo iwo amene
ali m'thupi sangathe kukondweretsa Mulungu. 9Koma inu simuli m'thupi
ai, koma mumzimu, ngatitu Mzimu wa Mulungu akhalabe mwa inu. Koma
ngati munthu alibe Mzimu wa Kristu, siali wace wa Kristu. 10Ndipo
ngati Kristu akhala mwa inu, thupilo ndithu liri lakufa cifukwa
ca ucimo; koma mzimu uli wamoyo cifukwa ca cilungamo. 11Koma ngati
Mzimu wa iye amene adaukitsa Yesu kwa akufa akhalabe mwa inu, iye
amene adaukitsa Kristu Yesu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu
akufa, mwa Mzimu wace wakukhala mwa inu.
12Cifukwa cace, abale, ife tiri amangawa si ace a thupi ai, kukhala
ndi moyo monga mwa thupi; 13pakuti ngati mukhala ndi moyo monga
mwa thupi, mudzafa; koma ngati ndi mzimu mufetsa zocita zace za
thupi, mudzakhala ndi moyo.14Pakuti onse amene atsogozedwa ndi Mzimu
wa Mulungu, amenewo ali ana a Mulungu, 15Pakuti inu simunalandira
mzimu wa ukapolo kucitanso mantha; koma munalandira mzimu waumwana,
umene tipfuula nao, kuti, Abba, Atate, 16Mzimu yekha acita umboni
pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tiri ana a Mulungu; 17ndipo ngati
ana, pomweponso olowa nyumba; inde olowa nyumba ace a Mulungu, ndi
olowa anzace a Kristu; ngatitu ife timva zowawa pamodzi naye, kuti
tikalaodirenso ulemerero pamodzi ndi iye.
Akolose 3: 1-17
1Cifukwa cace ngati munaukitsidwa pamodzi ndi Kristu, funani zakumwamba,
kumene kuli Kristu wokhala pa dzanja lamanja la Mulungu. 2Lingalirani
zakumwamba osati za padziko ai. 3Pakuti munafa, ndipo moyo wanu
wabisika pamodzi ndi Kristu mwa Mulungu, 4Pamene Kristu adzaoneka,
ndiye moyo wathu, pamenepo inunso mudzaonekera pamodzi ndi iye m'ulemerero.
5Cifukwa cace fetsani ziwalozo ziri padziko; dama, cidetso, cifunitso
ca manyazi, cilakolako coipa, nelicisiriro, cimene ciri kupembedza
mafano;6cifukwa ca izi zomwe ukudza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera;7zimene
munayendamo inunso kale, pamene munakhala ndi moyo wanu m'menemo,
8Koma tsopano tayani inunso zonsezi: mkwiyo, kupsa mtima, dumbo,
mwano, zonyansa zoturuka m'kamwa mwanu: 9musamanamizana wina ndi
mnzace; popeza mudabvula munthu wakale pamodzi ndi nchito zace,10ndipo
munabvala watsopano, amene alikukonzekawatsopano, kuti akhale naco
cizindikiritso, mousa mwa cifaniziro ca iye amene anamlenga iye;11pamene
palibe Mhelene ndi Ayuda, mdulidwe ndi kusadulidwa, wachedwa wakunja,
Mskuti, kapolo, mfulu, komatu Kristu ndiye zonse, ndi m'zonse.
12Cifukwa cace bvalani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima
ndi okondedwa, mtima wacifundo, kukoma mtima, kudzicepetsa, cifatso,
kuleza mtima; 13kulolerana wina ndi mnzace, ndi kukhululukirana
eni okha, ngati wina ali naco cifukwa pa mnzace; monganso Ambuye
anakhululukira inu, teroni inunso;14koma koposa izi zonse khalani
naco cikondano, ndico comangira ca mtima wamphumphu. 15Ndipo mtendere
wa Kristu ucite ufumu m'mitima yanu, kulingakonso munaitanidwa m'thupi
limodzi; ndipo khalani akuyamika. 16Mau a Knstu akhalitse mwa inu
cicurukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni
okha ndi masalmo, ndimayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuyimbira
Mulungu ndi cisomo mumtima mwanu. 17Ndipo ciri conse mukacicita
m'mau kapena muncbito, citani zonse m'dzina la Ambuye Yesu, ndi
kuyamika Mulungu Atate mwa iye.
Aroma 12: 1-8
1Cifukwa cace ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu,
kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa,
Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera. 2Ndipo musafanizidwe ndi
makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso
kwa mtima wanu, kuti mukazindikire cimene ciri cifuno ca Mulungu,
cabwino, ndi cokondweretsa, ndi cangwiro.
3Pakuti ndi cisomo capatsidwa kwa ine, ndiuza munthu ali yense
wa inu, kuti asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa; koma aganize
modziletsa yekha, monga, Mulungu anagawira kwa munthu ali yense
muyeso wa cikhulupiriro, 4Pakuti monga m'thupi limodzi tiri nazo
ziwalo zambiri, ndipo ziwalo zonsezo siziri nayo nchito imodzimodzi;
5comweco ife, ndife ambiri, tiri thupi limodzi mwa Kristu, ndi ziwalo
zinzace, wina ndi wina. 6Ndipo pokhala ife ndi mphatso zosiyana,
monga mwa cisomo copatsidwa kwa ife, kapena mphatso yakunenera,
tinenere monga mwa muyeso wa cikhulupiriro;7kapenayakutumikira,
tidzipereke ku utumiki uwu; kapena iye wakuphunzitsa, kukuphunzitsako;
8kapena iye wakudandaulira, kukudandaulirako; wakugawira acite ndi
mtima woona; iye wakuweruza, aweruze ndi cangu; iye wakucita cifundo,
acite ndi kukondwa mtima.
Aroma 12: 9-21
9Cikondano cikhale copanda cinyengo, Dana naco coipa; gwirizana
naco cabwino. 10M'cikondano ca anzanu wina ndi mnzace mukondane
ndi cikondi ceni ceni; mutsogolerane ndi kucitira wina mnzace ulemu;
11musakhale aulesi m'macitidwe anu; khalani acangu mumzimu, tumikirani
Ambuye; 12kondwerani m'ciyembekezo, pirirani m'masautso; limbikani
cilimbikire m'kupemphera,13Patsani zosowa oyera mtima; cerezani
aulendo. 14Dalitsani iwo akuzunza inu; dalitsani, musawatemberere.
15Kondwani nao iwo akukondwera; lirani nao akulira. 16Mukhale ndi
mtima umodzi wina ndi mnzace. Musasamalire zinthu zazikuru, koma
phatikanani nao odzicepetsa, Musadziyesere anzeru mwa inu nokha.
17Musabwezere munthu ali yense coipa cosinthana ndi coipa. Ganiziranitu
zinthu za ulemu pamaso pa anthu onse. 18Ngati nkutheka, monga momwe
mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse. 19Musabwezere coipa,
okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera
kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati Ambuye. 20Koma ngati mdani wako
akumva njala, umdyetse, ngati akumva ludzu, ummwetse; pakuti pakutero
udzaunjika makala a mota pamutu pace. 21Musagonje kwa coipa, koma
ndi cabwino genietsani coipa.
Aroma 15: 1-13
1Ndipo ife amene tiri olimba tiyenera kunyamula zofoka za opanda
mphamvu, ndi kusadzikondweretsa tokha. 2Yense wa ife akondweretse
mnzace, kumcitira zabwino, zakumlimbikitsa. 3Pakuti Kristunso sanadzikondweretsa
yekha; koma monga kwalembedwa, Minyozo ya iwo amene anakuoyoza iwe
Inagwa pa Ine,4Pakuti zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza,
kuti mwa cipiriro ndi citonthozo ca malembo, tikhale ndi ciyembekezo.
5Ndipo Mulungu wa cipiriro ndi wa citonthozo apatse inu kuti mukhale
ndi mtima umodzi wina ndi mnzace, monga mwa Kristu Yesu; 6kuti nonse
pamodzi, m'kamwa mmodzi, mukalemekeze Mulungu ndi Atate wa Ambuye
wathu Yesu Kristu. 7Cifukwa cace mulandirane wina ndi mnzace, monganso
Kristu anakulandirani inu, kukacitira Mulungu ulemerero.
8Ndipo ndinena kuti Kristu anakhala mtumiki wa mdulidwe, cifukwa
ca coonadi ca Mulungu, kuti alimbikitse malonjezo opatsidwa kwa
makolo, 9ndi kuti anthu a mitundu yina akalemekeze Mulungu, cifukwa
ca cifundo; monga kwalembedwa,
Cifukwa ca icindidzakubvomerezani Inu pakati pa anthu amitundu,
Ndidzayimbira dzina lanu.
10Ndiponso anena, Kondwani, amitundu inu, pamodzindi anthu ace.
11Ndiponso, Tamandani Ambuye, inu a mitundu yonse; Ndipo anthu onse
amtamande.
12Ndiponso, Yesaya ati, Padzali muzu wa Jese, Ndi iye amene aukira
kucita ufumu pa anthu amitundu; Iyeyo anthu amitundu adzamuyembekezera.
13Ndipo Mulungu wa ciyembekezo adzaze inu ndi cimwemwe conse ndi
mtendere m'kukhulupira, kuti mukacuruke ndi ciyembekezo, mu mphamvu
ya Mzimu Woyera.
3. Yohane15: 1-8
1Ine ndine mpesa weniweni, ndipo Atate wanga ndiye wam'munda. 2Nthambi
iri yonse ya mwa Ine yosabala cipatso, aicotsa; ndi iri y'onse yakubala
cipatso, aisadza, kuti ikabale cipatso cocuruka. 3Mwakhala okonzeka
tsopano inu cifukwa ca mau amene ndalankhula ndi inu, 4Khalani mwa
Ine, ndi Ine mwa inu. Monga nthambi siingathe kubala cipatso pa
yokha, ngati siikhala mwampesa; motere mulibe inunso ngati simukhala
mwa Ine. 5Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi zace: wakukhala mwa
Ine, ndi Ine mwa iye, ameneyo abala cipatso cambiri; pakuti kopanda
Ine simungathe kucita kanthu. 6Ngati wina sakhala mwa Ine, watayika
kunja monga nthambi, nafota; ndipo azisonkhanitsa nazitaya kumoto,
nazitentha. 7Ngati mukhala mwa Ine, ndi mau anga akhala mwa inu,
pemphani cimene ciri conse mucifuna ndipo cidzacitika kwa inu. 8Mwa
ici alemekezedwa Atate wanga, kuti mubale cipatso cambiri; ndipo
mudzakhala akuphunzira anga.
Kulepheretsa Mzimu Woyera
5. Macitidwe 7:51
51 Ouma khosi ndi osadulidwa mtima ndi makutu inu, mukaniza Mzimu
Woyera nthawi zonse; monga anacita makolo anu, momwemo inu.
1 Atesalonika 5: 19-20
19Musazime Mzimuyo;
20Musanyoze maaenero;
Yesaya 63:10
10Koma iwo anapandukira ndi kumvetsa cisoni mzimu wace woyera, cifukwa
cace Iye anasandulika mdani wao, nawathira nkhondo Iye yekha.
Macitidwe 5: 3
3Koma Petro anati, Hananiya, Satana anadzaza mtima wako cifukwa
ninji kudzanyenga Mzimu Woyera, ndi kupatula pa mtengo wace wa mundawo?
6. Afilipi 4: 6-7
6Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero,
pamodzi ndi ciyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. 7Ndipo
mtendere wa Mulungu wakupambana cidziwitso conse, udzasunga mitima
yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.
Aroma2:15
15popeza iwo aonetsa nchito ya lamulolo yolembedwa m'mitima yao,
ndipo cikumbu mtima cao cicitiranso umboni pamodzi nao, ndipo maganizo
ao wina ndi mnzace anenezana kapena akanirana;
1 Samueli 10: 7
7Ndipo zitakufikirani zizindikilo izi mudzacita monga mudzaona pocita,
pakuti Mulungu ali nanu.
2 Timoteo 3:16
16Lemba liri lonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa ciphunzitso,
citsutsano, cikonzero, cilangizo ca m'cilungamo:
7. 1 Yohane 3 : 1
1Taonani, cikondico Atate watipatsa, kuti tichedwe ana a Mulungu;
ndipo tiri ife otere. Mwa ici dziko lapansi silizindikira ife, popeza
silimzindikira iye.
Yohane 15 :15
15Sindichanso inu akapolo; cifukwa kapolo sadziwa cimene mbuye wace
acita; koma ndacha inu abwenzi; cifukwa zonse zimene ndazimva kwa
Atate wanga ndakudziwitsani.
Afilipi 3 :20-21
20Pakuti ufulu wathu uli Kumwamba; z kucokera komwenso tilindirira
Mpulumutsi, Ambuye Yesu Kristu; 21amene adzasanduliza thupi lathu
lopepulidwa, lifanane nalo thupi lace la ulemerero, monga mwa macitidwe
amene akhoza kudzigonjetsera nao zinthu zonse.
Aefeso 3 :12
12amene tiri naye cokhazikika mtima ndi ciyandiko eolimbika, mwa
cikhulupiriro ca pa iye.
1 Akorinto 6 :19-20
19Kapena simudziwa kuti thupi lanu liri kacisi wa Mzimu Woyera,
amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu? Ndipo simukhala
a inu nokha. 20Pakuti munagulidwa ndi mtengo wace wapatali; cifukwa
cace lemekezani Mulungu m'thupi lanu.
Yakobo 1: 2-5
2Muciyese cimwemwe cokha, abale anga, m'mene mukugwa m'mayesero
a mitundu mitundu; 3pozindikira kuti ciyesedwe ca cikhulupiriro
canu cicita cipiriro.4Koma cipiriro cikhale nayo nchito yace yangwiro,
kuti mukakhale angwiro ndi opanda cirema, osasowa kanthu konse.
5Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa
kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye,
Yauzimu
8. b. Aefeso 6: 10-18
10Cotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m'kulimba kwa mphamvu
yace.11Tabvalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kucirimika
pokana macenjerero a mdierekezi. 12Cifukwa kuti kulimbana kwathu
sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro,
ndi akucita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi a uzimu a
coipa m'zakumwamba. 13Mwa ici mudzitengere zida zonse za Mulungu,
kuti mudzakhoza kuima citsutsire pofika tsiku loipa, ndipo, mutacita
zonse, mudzacirimika. 14Cifukwa cace cirimikani, mutadzimangira
m'cuuno mwanu ndi coonadi, mutabvalanso capacifuwa ca cilungamo;
15ndipo mutadzibveka mapazi anu ndi makonzedwe a Uthenga Wabwino
wa mtendere; 16koposa zonse mutadzitengeranso cikopa ca cikhulupiriro,
cimene mudzakhoza kuzima naco mibvi yonse yoyaka moto ya woipayo.
17Mutengenso cisoti ca cipulumutso, ndi lupanga la Mzimu, ndilo
Mau a Mulungu; 18mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthawi
yonse mwa Mzimu, ndipo poeezera pamenepo cicezerere ndi kupembedzera
oyera mtima onse,
9. Yakobo 4: 7-8
7Potero mverani Mulungu; koma kanizani mdierekezi, ndipo adzakuthawani
inu. 8Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu, Sambani
m'manja, ocimwa inu; yeretsani mitima, a mitima iwiri inu.
1 Petro 5: 8-10
8Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdierekezi, monga mkango
wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire: 9ameneyo mumkanize
okhazikika m'cikhulupiriro, podziwa kuti zowawa zomwezo zirimkukwaniridwa
pa abale anu ali m'dziko.10Ndipo Mulungu wa cisomo conse, amene
adakuitanani kulowa ulemerero wace wosatha mwa Kristu, mutamva zowawa
kanthawi, adzafikitsa inu opanda cirema mwini wace, adzakhazikitsa,
adzalimbikitsa inu.
Aefeso 6:13
13Mwa ici mudzitengere zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoza kuima
citsutsire pofika tsiku loipa, ndipo, mutacita zonse, mudzacirimika.
Aefeso 4: 22-27
22kuti mubvule, kunena za makhalidwe anu oyamba, munthu wakale,
wobvunda potsata zilakolako za cinyengo; 23koma kuti 1 mukonzeke,
mukhale atsopano mu mzimu wa mtima wanu, 242 nimubvale munthu watsopano,
amene analengedwa monga mwa Mulungu, m'cilungamo, ndi m'ciyero ca
coonadi.
25Mwa ici, mutataya zonama, 3 lankhulani zoona yense ndi mnzace;
4 pakuti tiri ziwalo wina ndi mnzace. 265 Kwiyani, koma musacimwe;
dzuwa lisalowe muli cikwiyire, 27ndiponso 6 musampatse malo mdierekezi.
10. 2 Akorinto 10: 3-5
3Pakuti pakuyendayenda m'thupi, siticita nkhondo monga mwa thupi,
4(pakuti zida za nkhondo yathu siziri za thupi, koma zamphamvu mwa
Mulungu zakupasula malinga); 5ndi kugwetsa matsutsano, ndi cokwezeka
conse cimene cidzikweza pokana ddziwitso ca Mulungu, ndi kugonjetsa
ganizo lonse ku kumvera kwa Kristu;
2 Akorinto 6: 7
7m'mau a coonadi, mu mphamvu ya Mulungu; mwa camuna ca cilungamo
kulamanja ndi kulamanzere,
Aefeso 6:17
17Mutengenso cisoti ca cipulumutso, ndi lupanga la Mzimu, ndilo
Mau a Mulungu;
Masalmo 50:15
15Ndipo undiitane tsiku la cisautso:
Ndidzakulanditsa, ndipo iwe udzandilemekeza.
1 Yohane 4: 4
4Inu ndinu ocokera mwa Mulungu, tiana, ndipo munailaka; pakuti iye
wakukhah mwa inu aposa iye wakukhala m'dzi ko lapansi. Iwo ndiwo
ocoken m'dziko lapansi;
11. a. 2 Petro 3:18
18Koma kulani n'cisomo ndi cizindikiritso ca Ambure wathu ndi Mpulumutsi
Yesu vistu; kwa iye kukhale uleme'ero, tsopano ndi nthawi zonse.
Amen.
12. Agalatiya 5:16
16Koma ndinena, Muyendeyende ndi Mzimu, ndipo musafitse cilakolako
ca thupi.
|
|