Stonecroft
Stonecroft Training
Mndandanda wa Utatu
Malangizo Otsogolera
Mavesi a m'Baibulo
Adult Stonecroft International
The International Team
English YDT Teachings
Maphunziro a Ana
Malawi Moringa Projects
|
|
home >>stonecroft>>mzimu
woyera uli kuti?>> mavesi a m'baibulo >> phunziro 1 >> phunziro 2
KODO MZIMU WOVERA ULI KUTI? - Mavesi a m'Baibulo - Phunziro #2
Kuwerenga Baibulo mlungu ndi mlungu
Yohane 3: 1-13
1Koma panali munthu wa Afarisi, dzina lace Nikodemo, mkulu wa Ayuda,2Iyeyu
anadza kwa Yesu usiku, nati kwa iye, Rabi, tidziwa kuti Inu ndinu
mphunzitsi wocokera kwa Mulungu; pakuti palibe munthu akhoza kucita
zizindikilo zimene inu mucita, ngati Mulungu sakhala naye, 3Yesu
anayankha nati kwa iye, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu
sabadwa mwatsopano, sakhoza kuona Ufumu wa Mulungu. 4Nikodemoananena
kwa iye, Munthu akhoza bwanji kubadwa atakalamba? Kodi akhoza kulowanso
m'mimba ya amace ndi kubadwa? 5Yesu anayankha, Indetu, indetu, ndinena
ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kulowa
ufumu wa Mulungu. 6Cobadwa m'thupi cikhala thupi, ndipo cobadwa
mwa Mzimu, cikhala mzimu. 7Usadabwe cifukwa ndinati kwa iwe, Uyenera
kubadwa mwatsopano. 8Mphepo iomba pomwe ifuna, ndipo ukumva mau
ace, komavsudziwa, kumene icokera, ndi kumene imuka; cotero ali
yense wobadwa mwa Mzimu. 9Nikodemo anayankha nati kwa iye, Izi zingatheke
bwanji? 10Yesu anayankha nati kwa iye, Kodi uli mphunzitsi wa Israyeli,
ndipo sudziwa izi? 11Indetu, indetu, ndinena kwa iwe, Tilankhula
cimene ticidziwa, ndipo ticita umboni za cimene taeiona; ndipo umboni
wathu simuulandira. 12Ngati ndakuuzani za pansi pano, ndipo simukhulupira,
mudzakhulupira bwanji, ngati ndikuuzani za Kumwamba? 13Ndipo kulibe
munthu anakwera Kumwamba, koma iye wotsikayo kucokera Kumwamba,
ndiye Mwana wa munthu, wokhala m'Mwambayo.
Yohane 3: 14-21
14Ndipo monga Mose anakweza njoka m'cipululu, cotero Mwana wa munthu
ayenera kukwezedwa;15kuti yense wakukhulupira akhale nao moyo wosatha
mwa iye.
16Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana
wace wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike, koma
akhale nao moyo wosatha. 17Pakuti Mulungu sanatuma Mwana wace ku
dziko lapansi, kuti akaweruze dziko lapansi, koma kuti dziko lapansi
likapulumutsidwe ndi iye.18Wokhulupirira Iye saweruzidwa; wosakhulupira
waweruzidwa ngakhale tsopano, cifukwa sanakhulupirira dzina la Mwana
wobadwa yekha wa Mulungu.19Koma ciweruziro ndi ici, kuti kuunika
kunadza ku dziko lapansi, ndipo anthu anakonda mdima koposa kuunika;
pakuti nchito zao zinali zoipa. 20Pakuti yense wakucita zoipa adana
nako kuunika, ndipo sakudza kwa kuunika, kuti zingatsutsidwe nchito
zace.
21Koma wocita coonadi adza kukuunika, kuti nchito zace zionekere
kuti zinacitidwa mwa Mulungu.
Macitidwe 1: 1-11
1TAONANI Teofilo inu, mau aja oyamba ndinakonza, za zonse Yesu anayamba
kuzicita ndi kuziphunzitsa, 2kufikira tsiku lija anatengedwa kunka
Kumwamba, atatha kulamulira mwa Mzimu Woyera atumwi amene adawasankha;
3kwa iwonso anadzionetsera yekha wamoyo ndi zitsimikizo zambiri,
zitatha zowawa zace, naonekera kwa iwo masiku makumi anai, ndi kunena
zinthu za Ufumuwa Mulungu; 4ndipo e posonkhana nao pamodzi, anawalamulira
asacoke ku Yerusalemu, komatu alindire lonjezano la Atate, limene,
anati, munalimva kwa Ine; 5pakuti Yohane anabatizadi ndi madzi;
koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera, asanapite masiku ambiri.
6Pamenepo iwowa, atasonkhana pamodzi, anamfunsa iye, nanena, Ambuye,
kodi nthawi yino mubwezera ufumu kwa Israyeli? 7Koma anati kwa iwo,
Sikuli kwa inu kudziwa nthawi kapena nyengo, zimene Atate anaziika
m'ulamuliro wace wa iye yekha. 8Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu
Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga m'Yerusalemu,
ndi m'Yudeya lonse, ndi m'Samariya, ndi kufikira malekezero ace
a dziko. 9Ndipo m'mene adanena izi, ali cipenyerere iwo, ananyamulidwa;
ndipo mtambo unamlandira iye kumcotsa kumaso kwao. 10Ndipo pakukhala
iwo cipenyerere kumwamba pomuka iye, taonani, amuna awiri obvala
zoyera anaimirira pambali pao; 11amenenso anati, Amuna a ku Galileya,
muimiranji ndi kuyang'ana kumwamba? Yesu amene walandiridwa kunka
Kumwamba kucokera kwa inu, adzadza momwemo monga munamuona alinkupita
Kumwamba.
Macitidwe 2: 1-13
1Ndipo pakufika tsiku la Penteskoste, anali onse pamodzi pa malo
amodzi.2Ndipo mwadzidzidzi anamveka mau ocokera Kumwamba ngati mkokomo
wa mphepo yolimba, nadzaza nyumba yonse imene analikukhalamo. 3Ndipo
anaonekera kwa iwo malilime ogawanikana, onga amoto; ndipo unakhala
pa iwo onse wayekha wayekha. 4Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera,
nayamba kulankhula ndi malilime ena, monga Mzimu anawalankhulitsa.
5Koma anali m'Yerusalemu okhalako Ayuda, amuna opembedza, ocokera
ku mtundu uli wonse pansi pa thambo. 6Koma pocitika mau awa, unyinji
wa anthu unasonkhana, nusokonezedwa, popeza yense anawamva alikulankhula
m'cilankhulidwe cace ca iye yekha. 7Ndipo anadabwa onse, nazizwa,
nanena, Taonani, awa onse alankhulawa sali Agalileya kodi? 8ndipo
nanga ife timva bwanji, yense m'cilankhulidwe cathu cimene tinabadwa
naco? 9Aparti ndi Amedi, ndi Aelami, ndi iwo akukhala m'Mesopotamiya,
m'Yudeya, ndiponso m'Kapadokiya, m'Ponto, ndi m'Asiya; 10m'Frugiya,
ndiponso m'Pamfuliya, m'Aigupto, ndi mbali za Libiya wa ku Kurene,
ndi alendo ocokera ku Roma, ndiwo Ayuda, ndiponso opinduka, 11Akrete,
ndi Aarabu, tiwamva iwo alikulankhula m'malilime athu zazikuru za
Mulungu. 12Ndipo anadabwa onse, nathedwa nzeru, nanena wina ndi
mnzace, Kodi ici nciani? 13koma ena anawaseka, nanena kuti, Akhuta
vinyo walero.
Macitidwe 2: 14-21
14Koma Petro, anaimirira pamodzi ndi khumi ndi mmodziwo, nakweza
mau ace, nanena kwa iwo, nati, Amuna inu Ayuda, ndi inu nonse akukhala
kwanu m'Yerusalemu, ici cizindikirike kwa inu, ndi po cherani khutu
mau anga. 15Pakuti awa sanaledzera monga muyesa inu; pakuti ndi
ora lacitatulokha la tsiku;16komatu ici ndi cimene cinanenedwa ndi
mneneri Yoeli, 17Ndipo kudzali m'masiku otsiriza, anena Mulungu,
Ndidzathira ca Mzimu wansa pa thupi liri lonse, Ndipo ana anu amuna,
ndi akazi adzanenera, Ndipo anyamata anu adzaona masomphenya, Ndi
akulu anu adzalota maloto; 18Ndiponso pa akapolo anga ndi pa adzakazi
anga m'masiku awa Ndidzathira ca Mzimu wanga; ndipo adzanenera.
19Ndipo ndidzapatsa zodabwitsa m'thambo la kumwamba, Ndi zizindikilo
pa dziko lapansi; Mwazi, ndi moto, ndi mpweya wautsi; 20Dzuwa lidzasanduka
mdima, Ndi mweziudzasanduka mwazi, Lisanadze tsiku la Ambuye, Lalikuru
ndi loonekera; 21Ndipo kudzali, kuti yense amene akaitana pa dzina
la Ambuye adzapulumutsidwa.
Macitidwe 2: 36-42
36Pamenepo lizindikiritse ndithu banja liri lonse la Israyeli, kuti
Mulungu anamuyesa Ambuye ndi Kristu, Yesu amene inu munampacika.
37Koma pamene anamva ici, analaswa mtima, natitu kwa Petro ndi
atumwi enawo, Tidzacita ciani, amuna inu, abale? 38Koma Petro anati
kwa iwo, Lapani, batizidwani yense wa inu m'dzina la Yesu Kristu
kuloza ku cikhululukiro ca macimo anu; ndipo mudzalandira mphatso
ya Mzimu Woyera. 39Pakuti lonjezano 1 liri kwa inu, ndi kwa ana
anu, 2 ndi kwa onse akutali, 3 onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaitana.
40Ndipo ndi mau ena ambiri anacita umboni, nawadandaulira iwo, nanena,
Mudzipulumutse kwa mbadwo uno wokhotakhota.41Pamenepo iwo amene
analandira mau ace anabatizidwa; ndipo anaonjezedwa tsiku lomwelo
anthu ngati zikwi zitatu. 42Ndipo 4 anali cikhalire m'ciphunzitso
ca atumwi ndi m'ciyanjano, m'kunyema mkate ndi mapemphero.
Aroma 8:16
16Mzimu yekha acita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tiri ana
a Mulungu;
Mzimu wa Mulungu mu Chipangano Chakale
1. Genesis 1: 2
2Dziko lapansi ndipo linali lopanda kanthu; ndipo mdima unali pamwamba
pa nyanja; ndipo mzimu wa Mulungu unaliokufungatira pamwamba pa
madzi.
Yesaya 40: 12-14
12Ndani wayesa madzi m'dzanja lace, nayesa thambo ndi cikhato, ndi
kudzaza pfumbi la nthaka m'nsengwa, ndi kuyesa mapiri m'mbale zoyesera,
ndi zitunda m'mulingo?
13Ndani anapangira mzimu wa Yehova, kapena kukhala phungu lace,
ndi kumphunzitsa Iye? 14Iye anakhala upo ndi yani, ndipo ndani analangiza
Iye ndi kumphunzitsa m'njira ya ciweruzo, ndi kumphunzitsa nzeru
ndi kumuonetsa njira ya luntha?
2. a. Yobu 33: 4
4Mzimu wa Mulungu unandilenga, Ndi mpweya wa Wamphamvuyonse umandipatsa
moyo.
b. Ezekieli 36:27
27Ndipo ndidzaika mzimu wanga m'kati mwanu, ndi kukuyendetsani m'malemba
anga; ndipo mudzasunga maweruzo anga ndi kuwacita.
c. Mika 3: 8
8Koma ine ndidzala nayo mphamvu mwa Mzimu ya Yehova, ndi ciweruzo,
ndi camuna, kufotokozera Yakobo kulakwa kwace, ndi kwa Israyeli
cimo lace.
d. 2 Samueli 23: 2
2Mzimu wa Yehova unalankhula mwa ine, Ndi mau ace anali pa lilime
langa,
Yesaya 11: 2
2ndipo mzimu wa Yehova udzambalira iye mzimu wanzeru ndi wakuzindikira,
mzimu wa uphungu ndi mphamvu, mzimu wakudziwa ndi wakuopa Yehova;
Eksodo 31 :3
3ndipo ndamdzaza nd mzimu wa Mulungu, ndi luso, ndi nzeru, ndi cidziwitso,
ndi m'nchito ziri zonse,
Masalmo 51:11
11Musanditaye kundicotsa pamaso panu; Musandicotsere Mzimu wanu
Woyera.
Mzimu Woyera mu chipangano chatsopano
Yohane 14:16
16Ndipo Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani inu Nkhoswe
yina, kuti akhale ndi inu ku nthawi yonse,
Mzimu Woyera mu moyo wa Khristu
3. Luka 4: 16-18
16Ndipo anadza ku Nazarete, kumene analeredwa; ndipo tsiku la Sabata
analowa m'sunagoge, monga anazolowera, naimiriramo kuwerenga m'kalata.17Ndipo
anapereka kwa iye buku la Yesaya mneneri. Ndipo m'mene iye adafunyulula
bukulo, anapeza pomwe panalembedwa, 18Mzimu wa Ambuye uli paine,
Cifukwa cace iye anandidzoza Ine ndiuze anthu osauka Uthenga Wabwino:
Anandituma Ine kulalikira am'nsinga mamasulidwe, Ndi akhungu kuti
apenyenso, Kuturutsa ndi ufuru ophwanyika,
Luka 4: 1
1Ndipo Yesu, wodzala ndi Mzimu Woyera, anabwera kucokera ku Yordano,
natsogozedwa ndi Mzimu kunka kucipululu kukayesedwa ndi mdierekezi
masiku makumi anai.
Aroma 8:11
11Koma ngati Mzimu wa iye amene adaukitsa Yesu kwa akufa akhalabe
mwa inu, iye amene adaukitsa Kristu Yesu kwa akufa adzapatsanso
moyo matupi anu akufa, mwa Mzimu wace wakukhala mwa inu.
Macitidwe 1: 1-2
1TAONANI Teofilo inu, mau aja oyamba ndinakonza, za zonse Yesu anayamba
kuzicita ndi kuziphunzitsa, 2kufikira tsiku lija anatengedwa kunka
Kumwamba, atatha kulamulira mwa Mzimu Woyera atumwi amene adawasankha;
Mateyu 1: 18-20
18Ndipo kubadwa kwace kwa Yesu Kristu kunali kotere: Amai wace Mariya
anapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asanakomane iwowo, anapezedwa
iye ali ndi pakati mwa Mzimu Woyera. 19Koma Yosefe, mwamuna wace,
anali wolungama, ndiponso sanafuna kunyazitsa iye, nayesa m'mtima
kumleka iye m'tseri, 20Koma pakusinkhasinkha iye zinthu izi, onani,
mngelo wa Ambuye anaonekera kwa iye m'kulota, nanena, Yosefe, mwana
wa Davide, usaope kudzitengera wekha Mariya mkazi wako; pakuti ico
colandiridwa mwa iye ciri ca Mzimu Woyera.
Ntchito Mzimu Woyera 'm mu kulemba Baibulo
4. 2 Petro 1 : 21
21pakuti kale lonse cinenero sicinadza ndi cifuniro ca munthu; koma
anthu a Mulungu, ogwidwa ndi Mzimu Woyera, analankhula.
1 Akorinto 2:13
13Zimenenso tilankhula, si ndi mau ophunzitsidwa ndi nzeru za munthu,
koma ophunzitsidwa ndi Mzimu; ndi kulinganiza zamzimu ndi zamzimu.
Mzimu Woyera mu miyoyo yathu
Agalatiya 3:27
27Pakuti nonse amene munabatizidwa kwa Kristu mudabvala Kristu.
Aroma 8:15
15Pakuti inu simunalandira mzimu wa ukapolo kucitanso mantha; koma
munalandira mzimu waumwana, umene tipfuula nao, kuti, Abba, Atate,
2 Akorinto 3:18
18Koma ife tonse ndi nkhope yosaphimbika popenyerera monga mwa kalirole
ulemerero wa Ambuye, tisandulika m'cithunzihunzi comweci kucokera
kuulenerero kumka kuulemerero, monga ngati kucokera kwa Ambuye Mzimu.
1 Akorinto 3: 16-17
16Kodi simudziwa kuti muli Kacisi wa Mulungu, ndi kuti Mzimu wa
Mulungu agonera mwa inu? 17Ngati wina aononga kacisi wa Mulungu,
ameneyo Mulungu adzamuononga; pakuti kacisi wa Mulungu ali wopatulika,
ameneyo ndi inu.
Yohane 6:63
23koma zinacokera ngalawa zina ku Tiberiya, pafupi pa malo pomwe
adadyapo mkate m'mene Yesu adayamika;
|
|