Stonecroft
Stonecroft Training
Mndandanda wa Utatu
Malangizo Otsogolera
Mavesi a m'Baibulo
Adult Stonecroft International
The International Team
English YDT Teachings
Maphunziro a Ana
Malawi Moringa Projects
|
|
home >>stonecroft>>mzimu
woyera uli kuti?>> mavesi a m'baibulo >> phunziro 2 >> phunziro 3
KODO MZIMU WOVERA ULI KUTI? - Mavesi a m'Baibulo - Phunziro #3
Kuwerenga Baibulo mlungu ndi mlungu
Yohane 14: 1-14
1Mtima wanu usabvutike; mukhulupirira Mulungu, khulupirirani Inenso.2M'nyumba
ya Atate wanga alimo malo okhalamo ambiri. Ngati sikudali kutero,
ndikadakuuzani inu; pakuti ndipita kukukonzerani inu malo. 3Ndipo
ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira
inu kwa Ine ndekha; kuti kumene kuli Ineko, mukakhale inunso. 4Ndipo
kumene ndinkako Ine, mudziwa njira yace. 5Tomasi ananena ndi Iye,
Ambuye, sitidziwa kumene munkako; tidziwa njira bwanji? 6Yesu ananena
naye, ine ndinenjira, ndi coonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza
kwa Atate, koma mwa Ine.
7Mukadazindikira ine mukadadziwa Atate wanganso; kuyambira tsopano
mumzindikira iye, ndipo mwamuona iye. 8Filipo ananena ndi iye, Ambuye,
tionetsereni ife Atate, ndipo citikwanira. 9Yesu ananena naye, Kodi
ndiri ndiinu nthawi yaikuru yotere, ndipo sunandizindikira, Filipo?
iye amene wandiona Ine waona Atate; unena iwe bwanji, Mutionetsere
Atate? 10Sukhulupirira kodi kuti ndiri Ine mwa Atate, ndi Atate
ali mwa Ine? Mau amene ndinena Ine kwa inu sindilankhula kwa Ine
ndekha; koma Atate wokhala mwa Ine acita nchito zace.11Khulupirirani
Ine, kuti Inendiri mwa Atate ndi Atate ali mwa Ine; koma ngati si
comweco, khulupirirani Ine cifukwa ca nchito zomwe. 12Indetu, indetu,
ndinena kwa inu, Wokhulupirira Ine, nchito zimene ndicita Ine adzazicitanso
iyeyu; ndipo adzacita zoposa izi; cifukwa ndipita Ine kwa Atate.
13Ndipo cimene ciri conse mukafunse m'dzina langa, ndidzacicita,
kuti Atate akalemekezedwe mwa Mwana.14Ngati mudzapempha kanthu m'dzina
langa, ndidzacita.
Yohane14: 15-31
15Ngati mukonda Ine, sungani malamulo anga.
16Ndipo Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani inu Nkhoswe
yina, kuti akhale ndi inu ku nthawi yonse, 17ndiye Mzimu wa coonadi;
amene dziko lapansi silingathe kumlandira, pakuti silimuona iye,
kapena kumzindikira iye. Inu mumzindikira iye; cifukwa akhala ndi
inu nadzakhala mwa inu. 18Sindidza-kusiyani inu mukhale ana amasiye;
ndidza kwa inu. 19Katsala kanthawi, ndipo dziko lapansi silindionanso
Ine; koma inu mundiona; popeza Ine ndiri ndi moyo inunso mudzakhala
ndi moyo. 20Tsiku lo mwelo mudzazindikira kuti ndiri Ine mwa Atate
wanga, ndi inu mwa Ine, ndi Ine mwa inu. 21Iye wakukhala nao malamulo
anga, ndi kuwasunga, iyeyu ndiye wondikonda Ine; koma wondikonda
Ine adzakondedwa ndi Atate wanga, ndipo line ndidzamkonda, ndipo
ndidzadzionetsandekha kwa iye.
Yohane 15: 1-17
1Ine ndine mpesa weniweni, ndipo Atate wanga ndiye wam'munda. 2Nthambi
iri yonse ya mwa Ine yosabala cipatso, aicotsa; ndi iri y'onse yakubala
cipatso, aisadza, kuti ikabale cipatso cocuruka. 3Mwakhala okonzeka
tsopano inu cifukwa ca mau amene ndalankhula ndi inu, 4Khalani mwa
Ine, ndi Ine mwa inu. Monga nthambi siingathe kubala cipatso pa
yokha, ngati siikhala mwampesa; motere mulibe inunso ngati simukhala
mwa Ine. 5Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi zace: wakukhala mwa
Ine, ndi Ine mwa iye, ameneyo abala cipatso cambiri; pakuti kopanda
Ine simungathe kucita kanthu. 6Ngati wina sakhala mwa Ine, watayika
kunja monga nthambi, nafota; ndipo azisonkhanitsa nazitaya kumoto,
nazitentha. 7Ngati mukhala mwa Ine, ndi mau anga akhala mwa inu,
pemphani cimene ciri conse mucifuna ndipo cidzacitika kwa inu. 8Mwa
ici alemekezedwa Atate wanga, kuti mubale cipatso cambiri; ndipo
mudzakhala akuphunzira anga. 9Monga momwe Atate wandikonda Ine,
Inenso ndakonda inu; khalani m'cikondi canga. 10Ngati musunga malamulo
anga mudzakhala m'cikondi canga; monga Ine ndasunga malamulo a Atate
wanga, ndipo ndikhala m'cikondi cace. 11Izi ndalankhula ndi inu,
kuti cimwemwe canga cikhale mwa inu, ndi kuti cimwemwe canu cidzale.
12Lamulo langa ndi ili, kuti mukondane wina ndi mnzace, monga ndakonda
inu. 13Palibe munthu ali naco cikondi coposa ici, cakuti munthu
ataya moyo wace cifukwa ca abwenzi ace. 14Muli abwenzianga inu,
ngati muzicita zimene ndikulamulirani inu.
15Sindichanso inu akapolo; cifukwa kapolo sadziwa cimene mbuye
wace acita; koma ndacha inu abwenzi; cifukwa zonse zimene ndazimva
kwa Atate wanga ndakudziwitsani. 16Inu simunandisankha Ine, koma
Ine ndinakusankhani inu, ndipo ndinakuikani, kuti mukamuke inu ndi
kubala cipatso, ndi kuti cipatso canu cikhale; kuti cimene ciri
conse mukapempha Atate m'dzina langa akakupatseni inu. 17Zinthu
izi ndilamulira inu, kuti mukondane wina ndi mnzace.
Yohane 15: 18-27
18Ngati dziko lapansi lida inu, mudziwa kuti lidada Ine lisanayambe
kuda inu.19Mukadakhala a dziko lapansi, dziko lapansi likadakonda
zace za lokha; koma popeza simuli a dziko lapansi, koma Ine ndinakusankhani
inu mwa dziko lapansi, cifukwa ca ici likudani inu. 20Kumbukilani
mau amene Ine ndinanena kwa inu, Kapolo sali wamkuru ndi mbuye wace.
Ngati anandilondalonda Ine, adzakulonda-londani inunso; ngati anasunga
mau anga, adzasunga anunso.21Koma izi zonse adzakucitirani cifukwa
ca dzina langa, cifukwa sadziwa wondituma Ine. 22Sindikadadza ndi
kulankhula nao sakadakhala nalo cimo; koma tsopano alibe cowiringula
pa macimo ao. 23Iye wondida Ine, adanso Atate wanga. 24Sindikadacita
mwa iwo nchito zosacita wina, sakadakhala nalo cimo; koma tsopano
anaona, nada: Ine ndi Atate wanganso, 25Koma citero, kuti mau olembedwa
m'cilamulo cao akwaniridwe, kuti, Anandida Ine kopanda cifukwa.
26Koma pamene wafika Nkhoswe, amene Ine ndidzamtuma kwa inu kucokera
kwa Atate, ndiye Mzimu wa coonadi, amene aturuka kwa Atate, Iyeyu
adzandicitira Ine umboni. 27Ndipo inunso mucita umboni, pakuti muli
ndi Ine kuyambira ciyambi.
Yohane 16: 1-15
1Izi ndalankhula ndi inu kuti mungakhumudwitsidwe. 2Adzakuturutsani
m'masunagoge; koma ikudza nthawi imene yense wakupha inu adzayesa
kuti atumikira Mulungu, 3Ndipo izi adzacita, cifukwa sanadziwa Atate,
kapena Ine.4Koma zinthu izi ndalankhula ndi inu kuti ikadza nthawi
yao, mukakumbukire kuti ndinakuuzani. Koma izi sindinanena kwa inu
kuyambira paciyambi, cifukwa ndinali pamodzi ndi inu. 5Koma tsopano
ndimuka kwa iye wondituma Ine; ndipo palibe wina mwa inu andifunsa
Ine, Munka kuti? 6Koma cifukwa ndalankhula izi ndi inu cisoni cadzala
mumtima mwanu.
7Koma ndinena Ine coonadi ndi inu; kuyenera kwa inu kuti ndicoke
Ine; pakuti ngati sindicoka, Nkhosweyo sadzadza kwa inu; koma ngati
ndipita ndidzamtuma iye kwa inu. 8Ndipo atadza Iyeyo, adzatsutsa
dziko lapansi za macimo, ndi za cilungamo, ndi za ciweruziro; 9za
macimo, cifukwa sakhulupirira Ine; 10za cilungamo, cifukwa ndinka
kwa Atate, ndipo simundionanso; 11za ciweruziro, cifukwa mkuru wa
dziko ili lapansi waweruzidwa. 12Ndiri nazo zambirinso zakunena
kwa inu, koma simungathe kuzisenza tsopano lino. 13Koma atadza Iyeyo,
Mzimu wa coonadi, adzatsogolera inu m'coonadi conse; pakuti sadzalankhula
za iye mwini; koma zinthu ziri zonse adzazimva, adzazilankhula;
ndipo zinthu zirinkudza adzakulalikirani. 14Iyeyo adzalemekeza Ine;
cifukwa adzatenga za mwa Ine, nadzalalikira kwa inu. 15Zinthu ziri
zonse Atate ali nazo ndi zanga; cifukwa cace ndinati, kuti atenga
za mwa Ine, nadzalalikira kwa inu.
Yohane 16: 16-33
16Katsala kanthawi, ndipo simundionanso Ine, ndipo kanthawinso,
ndipo mudzandiona Ine. 17Mwa akuphunzira ace tsono anati wina ndi
mnzace, ici nciani cimene anena ndi ife, Kanthawi ndipo simundiona;
ndiponso kanthawi, ndipo mudzandiona; ndipo, cifukwa ndimuka kwa
Atate? 18Cifukwa cace ananena, ici nciani cimene anena, Kanthawi?
Sitidziwa cimene alankhula.19Yesu anazindikira kuti analikufuna
kumfunsa iye, ndipo anati kwa iwo, Kodi mulikufunsana wina ndi mnzace
za ici, kuti ndinati, Kanthawi ndipo simundiona Ine, ndiponso kanthawi
nimudzandiona Ine? 20Indetu, indetu, ndinena ndi inu, kuti mudzalira
ndi kubuma maliro inu, koma dziko lapansi lidzakondwera; mudzacita
cisoni inu, koma cisoni canu cidzasandulika cimwemwe. 21Mkazi pamene
akuti abale ali naco cisoni, cifukwa yafika nthawi yace; koma pamene
wabala mwana, sakumbukilanso kusaukako, cifukwa ca cimwemwe kuti
wabadwa munthu ku dziko lapansi. 22Ndipo inu tsono muli naco cisoni
tsopano lino, koma ndidzakuonaninso, ndipo mtima wanu udzakondwera,
ndipo palibe wina adzacotsa kwa inu cimwemwe canu. 23Ndipo tsiku
limenelo simudzandifunsa kanthu. Indetu, indetu, ndinena kwa inu,
Ngati mudzapempha Atate kanthu, adzakupatsani inu m'dzina langa.
24Kufikira tsopano simunapempha kanthu m'dzina langa; pemphani,
ndipo mudzalandira, kuti cimwemwe canu cikwaniridwe.
25Zinthu izi ndalankhula ndi inu m'mafanizo; ikudza nthawi imene
sindidzalankhula ndi inu m'mafanizo, koma ndidzakulalikirani inu
momveka za Atate. 26Tsiku limenelo mudzapempha m'dzina langa; ndipo
sindinena kwa inu kuti Ine ndidzafunsira inu kwa Atate; 27pakuti
Atate yekha akonda inu, cifukwa inu mwandikonda Ine, ndi kukhulupirira
kuti Ine ndinaturuka kwa Atate.28Ndinaturuka mwa Atate, ndipo ndadza
ku dziko lapansi: ndilisiyanso dziko lapansi, ndipo ndipita kwa
Atate.
29Akuphunzira ace ananena, Onani, tsopano mulankhula zomveka, ndipo
mulibe kunena ciphiphiritso, 30Tsopano tidziwa kuti mudziwa zonse,
ndipo mulibe kusowa kuti wina akafunse Inu; mwa ici tikhulupirira
kuti munaturuka kwa Mulungu. 31Yesu anayankha iwo, Kodi mukhulupirira
tsopano? 32Onani ikudza nthawi, ndipo yafika, imene mudzabalalitsidwa,
yense ku zace za yekha, ndipo mudzandisiya Ine pa ndekha. Ndipo
sindikhala pa ndekha, cifukwa Atate ali pamodzi ndi Ine, 33Zinthu
izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukakhale nao mtendere. M'dziko
lapansi mudzakhala naco cibvuto, koma limbikani mtima; ndalilaka
dziko lapansi Ine.
Mzimu Woyera mu miyoyo yathu
1. a. 1 Yohane 2:27
27Ndipo inu, 8 kudzoza kumene munalandira kucokera kwa iye, kukhala
mwa inu, ndipo simusowa kuti wina akuphunzitseni; koma 9 monga kudzoza
kwace kukuphunzitsani za zinthu zonse, ndipo kuli koona, sikuli
bodza ai, ndipo monga kudaphunzitsa inu, mukhale mwa iye.
b. Yohane 16: 13-14
13Koma atadza Iyeyo, Mzimu wa coonadi, adzatsogolera inu m'coonadi
conse; pakuti sadzalankhula za iye mwini; koma zinthu ziri zonse
adzazimva, adzazilankhula; ndipo zinthu zirinkudza adzakulalikirani.
14Iyeyo adzalemekeza Ine; cifukwa adzatenga za mwa Ine, nadzalalikira
kwa inu.
c. Aroma 8:14
14Pakuti onse amene atsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu, amenewo ali
ana a Mulungu,
d. Agalatiya 5: 22-23
22Koma cipatso ca Mzimu ndico cikondi, cimwemwe, mtendere, kuleza
mtima, cifundo, kukoma mtima, icikhulupirtro, 23cifatso, ciletso;
pokana zimenezi palibe lamulo.
e. Macitidwe 1: 8
8Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo
mudzakhala mboni zanga m'Yerusalemu, ndi m'Yudeya lonse, ndi m'Samariya,
ndi kufikira malekezero ace a dziko.
Pemphero
Marko 1:35
35Ndipo m'mawa mwace anauka usikusiku, naturuka namuka kucipululu,
napemphera kumeneko.
2. Macitidwe 8:26
26Koma mngelo wa Ambuye analankhula ndi Filipo, nanena, Nyamuka,
nupite mbali ya kumwela, kutsata njira yotsika kucokera ku Yerusalemu
kunka ku Gaza; ndiyo ya cipululu.
1 Yohane 5: 14-15
14Ndipo uku ndi kulimbika mrima kumene tiri nako kwa iye, kuti ngati
tipempha kanthu monga mwa cifuniro cace, atimvera; 15ndipo ngati
tidziwa kuti atimvera ciri conse ticipempha, tidziwa kuti tiri nazo
izi tazipempha kwa iye.
3. a. 1 Atesalonika 5:17
17Pempherani kosaleka;
4. a. Mateyu 6: 5-6
5Ndipo pamene mupemphera, musakhale monga onyengawo; cifukwa iwo
akonda kuimirira ndi kupemphera m'masunagoge, ndi pa mphambano za
makwalala, kuti aonekere kwa anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo
alandiriratu mphotho zao. 6Koma iwe popemphera, Iowa m'cipinda cako,
nutseke citseko cako, nupemphere Atate wako ali m'tseri, ndipo Atate
wako wakuona m'tseri adzakubwezera iwe.
b. Masalmo 55:17
17Madzulo, m'mawa, ndi msana ndidzadandaula, ndi kubuula, Ndipo
adzamva mau anga.
Kuwerenga Baibulo
1 Akorinto 1:18
18Pakuti mau a mtanda ali ndithu cinthu copusa kwa iwo akutayika,
koma kwa ife amene tirikupulumutsidwa ali mphamvu ya Mulungu.
Kumvera
6. Yakobo 1: 22-25
22Khalani akucita mau, osati akumva okha, ndi kudzinyenga nokha.
23Pakuti ngati munthu ali wakumva mau wosati wakucita, iyeyu afanana
ndi munthu wakuyang'anira nkhope yace ya cibadwidwe cace m'kalirole;
24pakuti wadziyang'anira yekha nacoka, naiwala pompaja nali wotani.25Koma
iye wakupenyerera m'lamulo langwiro, ndilo laufulu, natero cipenyerere,
ameneyo, posakhala wakumva wakuiwala, komatu wakucita nchito, adzakhala
wodala m'kucita kwace.
Agalatiya 5:17
17Pakuti thupi lilakalaka potsutsana naye Mzimu, ndi Mzimu potsutsana
nalo thupi; pakuti izi sizilingana; kuti zimene muzifuna musazicite.
1 Akorinto 10:13
13Sicinakugwerani inu ciyeso koma ca umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika,
amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi
ndi ciyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.
7. Aefeso 4: 25-32
25Mwa ici, mutataya zonama, lankhulani zoona yense ndi mnzace; pakuti
tiri ziwalo wina ndi mnzace. 26 Kwiyani, koma musacimwe; dzuwa lisalowe
muli cikwiyire, 27ndiponso musampatse malo mdierekezi. 28Wakubayo
asabenso; koma makamaka agwiritse nchito, nagwire nchito yokoma
ndi manja ace, kuti akhale naco cakucereza wosowa. 29 Nkhani yonse
yobvunda isaturuke m'kamwa mwanu, koma ngati pali yina yabwino kukumangirira
monga mofunika ndiyo, kuti ipatse cisomo kwa iwo akumva. 30Ndipo
musamvetse cisoni Mzimu Woyera wa Mulungu, amene munasindikizidwa
cizindikilo mwa iye, kufikira tsiku la maomboledwe. 31 Ciwawo conse,
ndi kupsya mtima, ndi mkwiyo, ndi ciwawa, ndi mwano zicotsedwe kwa
inu, ndiponso coipa conse.32Koma mukhalirane okoma wina ndi mnzace,
a mtima wacifundo,
1 Akorinto 6: 19-20
19Kapena simudziwa kuti thupi lanu liri kacisi wa Mzimu Woyera,
amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu? Ndipo simukhala
a inu nokha. 20Pakuti munagulidwa ndi mtengo wace wapatali; cifukwa
cace lemekezani Mulungu m'thupi lanu.
8. Agalatiya 5:16
16Koma ndinena, Muyendeyende ndi Mzimu, ndipo musafitse cilakolako
ca thupi.
|
|