Stonecroft
Stonecroft Training
Mndandanda wa Utatu
Malangizo Otsogolera
Mavesi a m'Baibulo
Adult Stonecroft International
The International Team
English YDT Teachings
Maphunziro a Ana
Malawi Moringa Projects
|
|
home >>stonecroft>>mzimu
woyera uli kuti?>> mavesi a m'baibulo >> phunziro 4 >> phunziro 5
KODO MZIMU WOVERA ULI KUTI? - Mavesi a m'Baibulo - Phunziro #5
|
|
|
1 Akorinto 14: 1-40
1Tsatani cikondi; koma funitsitsani mphatsozauzimu, koma koposa
kuti mukanenere. 2Pakuti iye wakulankhula lilime salankhula ndi
anthu, koma ndi Mulungu; pakuti palibemunthu akumva; koma mumzimu
alankhula zinsinsi.3Koma iye wakunenera alankhula ndi anthu comangirira
ndi colimbikitsa, ndi cosangalatsa, 4Iye wakulankhula lilime, adzimangirira
yekha, koma iye wakunenera amangirira Mpingo. 5Ndipo ndifuna inu
nonse mula'nkhule malilime, koma makamaka kuti mukanenere; ndipo
wakunenera aposa wakulankhula malilime, akapanda kumasulira, kuti
Mpingo ukalandire comangirira. 6Koma tsopano, abale, ngati ndidza
kwa inu ndi kulankhula malilime, ndikaku, pindulitsani ciani, ngati
sindilankhui landi inu kapena m'bvumbulutso, kapena m'cidziwitso,
kapena m'cinenero, kapena m'ciphunzitsot 7Ngakhale zinthu zopanda
moyo, zopereka mau, ngati toliro, kapena ngoli, ngati sizisiyanitsa
maliridwe, cidzazindikirikabwanji cimene ciombedwa kapena kuyimbidwa?8Pakuti
ngad Lipenga lipereka mao osazindikirika, adzadzikonzera ndani kunkhondo?
9Momwemonso inu ngati mwa lilime simupereka mau omveka bwino, kudzazindikirika
bwanji cimene cilankhulidwa? Pakuti mudzakhala olankhula kumlengalenga.
10Iripo, kaya, mitundu yambiri yotere ya mau pa dziko lapansi, ndipo
palibe kanthu kasowa mau. 11Cifukwa cace, ngati sindidziwa mphamvu
ya mauwo ndidzakhala kwa iye wolankhulayo wakunja, ndipo wolankhulayo
adzakhala wakunja kwaine. 12Momwemo inunso, popeza muli ofunits
its a mphatso zauzimu, funani kuti mukacuruke kukumangirira kwa
Mpingo, 13Cifukwa cace wolankhula lilime, apemphere kuti amasule.
14Pakuti ngati ndipemphera m'lilime, mzimu wanga upemphera, koma
cidziwitso canga cikhala cosabala kanthu. 15Kuli ciani tsono? Ndidzapemphera
ndi mzimu, koma ndidzapempheranso ndi cidziwitso canga; ndidzayimba
ndi mzimu, koma ndidzayimbanso ndi cidziwitso. 16Cifukwa ngati udalitsa
ndi mzimu, nanga iye wakukhala wosaphunzira adzati Amen bwanji,
pa kuyamika kwako, popeza sadziwa cimene unena? 17Pakutitu iwe uyamika
bwino, koma winayo samangiriridwa. 18Ndiyanillca Mulungu kuti ndilankhula
malilime koposa inu nonse; 19koma mu Mpingo ndifuna kulankhula mau
asanu ndi cidziwitso canga, kutinso ndikalangize ena, koposa kulankhula
mau zikwi m'lilime.
20Abale, musakhale ana m'cidziwitso, koma m'coipa khalani makanda,
koma m'cidziwitso akulu misinkhu. 21Kwalembedwa m'cilamulo, Ndi
anthu amalilime ena ndipo ndi milomo yina ndidzalankhula nao anthu
awa; ndipo kungakhale kutero sadzamva Ine, anena Ambuye. 22Cotero
malilime akhala ngati cizindikilo, si kwa iwo akukhulupira, koma
kwa iwo osakhulupira; koma kunenera sikuli kwa iwo osakhulupira,
koma kwa two amene akhulupira. 23Cifukwa cace, ngati Mpingo wonse
akasonkhane pamodzi, ndi onse akalankhule malilime, ndipo akalowemo
anthu osaphunzira kapena osakhulupira, kodi sadzanena kuti mwayaruka?
24Koma ngati onse anenera, ndipo alowamo wina wosakhulupirira kapena
wosaphunzira, atsutsidwa ndi onse; aweruzidwa ndi onse; 25zobisika
za mtima wace zionetsedwa; ndipo cotero adzagwa nkhope yace pansi,
nadzagwadira Mulungu, nadzalalikira kuti Mulungu ali ndithu mwa
inu.
26Nanga ciani tsono, abale? Pamene musonkhana, yense ali nalo salmo,
ali naco ciphunzitso, ali nalo bvumbulutso, ali nalo lilime, ali
naco cimasuliro. Mucite zonse kukumangirira. 27Ngati wina alankhula
lilime, acite ndi awiri, koma oposa atatu iai, ndipo motsatana;
ndipo mmodzi amasulire. 28Koma ngati palibe womasulira, akhale cete
mu Mpingo, koma alankhule ndi iye yekha, ndi Mulungu.29Ndipo aneneri
alankhule awiri kapena atatu, ndi ena azindikire. 30Koma ngati kanthu
kabvumbulutsidwa kwa wina wakukhalapo, akhale cete woyambayo.31Pakuti
mukhoza nonse kunenera mmodzi mmodzi, kuti onse aphunzire, ndi onse
afulumidwe; 32ndipo mizimu ya aneneri imvera aneneri; 33pakuti Mulungu
sali Mulungu wa cisokonezo koma wa mtendere; monga mwa Mipingo yonse
ya oyera mtima.
34Akazi akhale cete m'Mipingo. Pakuti vsikuloledwa kwa iwo kulankhula,
Koma akhale omvera, mongansocilamulo cmena, 35Koma ngati afuna kuphunzirakanthu
afunseamuna ao aiwo okha kwao; pakuti kunyazitsa mkazi kulankhula
mu Mpingo. 36Kodi mau a Mulungu anatutuka kwa iw? kapena anafika
kwa inu nokha?
37Ngatiwinaayesa kuti ali mneneri, kapena wauzimu; azindikire kuti
zimene ndilemba kwa inu ziri lamulo la Ambuye, 38Koma ngati wina
akhale wosadziwa, akhale wosadziwa.
39Cifukwa cace; abale anga, funitsitsani kunenera, ndipo musaletse
kulankhula malilime. 40Koma zonse zicitike koyenera ndi kolongosoka.
Kuwerenga Baibulo mlungu ndi mlungu
Kuwerenga Baibulo mlungu ndi mlungu
Agalatiya 5: 16-26
16Koma ndinena, Muyendeyende ndi Mzimu, ndipo musafitse cilakolako
ca thupi. 17Pakuti thupi lilakalaka potsutsana naye Mzimu, ndi Mzimu
potsutsana nalo thupi; pakuti izi sizilingana; kuti zimene muzifuna
musazicite. 18Ngati Mzimu akutsogolerani, simuli omvera lamulo.
19Ndipo nchito za thupi zionekera, ndizo dama, codetsa, kukhumba
zonyansa, kupembedza mafano, 20nyanga, madano, ndeu, kaduka, zopsa
mtima, zotetana, magawano, mipatuko, njiru, 21kuledzera, mcezo,
ndi zina zotere; zimene ndikucenjezani nazo, monga ndacita, kuti
iwo akucitacita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu. 22Koma cipatso
ca Mzimu ndico cikondi, cimwemwe, mtendere, kuleza mtima, cifundo,
kukoma mtima, icikhulupirtro, 23cifatso, ciletso; pokana zimenezi
palibe lamulo. 24Koma iwo a Kristu Yesu adapacika thupi, ndi zokhumba
zace, ndi zilakolako zace.
251 N gati tiri ndi moyo ndi Mzimu, ndi Mzimunso tiyende. 262 Tisakhale
odzikuza, outsana, akucitirana njiru.
Aroma 6: 1-11
1Cifukwa cace tidzatani? Tidzakhalabe m'ucimo kodi, kuti cisomo
cicuruke?2Msatero ai. Ife amene tiri akufa ku ucimo, tidzakhala
bwanji cikhalire m'menemo? 3Kapena kodi simudziwa kuti ife tonse
amene tinabatizidwa mwa Kristu Yesu; tinabatizidwa mu imfa yace?
4Cifukwa cace tinaikldwa m'manda pamodzi ndi iye mwa ubatizo kulowa
muimfa; kuti monga Kristu anaukitsidwa kwa akufa mwa ulemerero wa
Atate, cotero ifenso tikayende m'moyo watsopano. 5Pakuti ngati ife
tinakhala olumikizidwa ndi iye m'cifanizidwe ca imfa yace, koteronso
tidzakhala m'cifani'Zidwe ca kuuka kwace; 6podziwa ici, kuti umunthu
wathu wakale unapacikidwa pamodzi ndi iye, kuti thupilo la ucimo
likaonongedwe, kuti ife tisakhalenso akapolo a ucimo; 7pakuti iye
amene anafa anamasulidwa kuucimo. 8Koma ngati ife tinafa ndi Kristu,
tikhulupirira kuti tidzakhalanso amoyo ndi iye; 9podziwa kuti Kristu
anaukitsidwa kwa akufa, sadzafanso; imfa siicitanso ufumu pa Iye.
10Pakuti pakufa iye, atafa ku ucimo kamodzi; ndipo pakukhala iye
wamoyo, akhala wamoyo kwa Mulungu. 11Cotero inunso mudziwerengere
inu nokha ofafa ku ucimo, koma amoyo kwa Mulungu mwa Kristu Yesu.
Aroma 6: 12-19
12Cifukwa cace musamalola ucimo ucite ufumu m'thupi lanu la imfa
kumvera zofuna zace: 13ndipo musapereke ziwalo zanu kuucimo, zikhale
zida za cosalungama; koma mudzipereke inu nokha kwa Mulungu, monga
amoyo ataturuka mwa akufa, ndi ziwalo zanu kwa Mulungu zikhale zida
za cilungamo,14Pakuti ucimo sudzacita ufumu pa inu; popeza simuli
a lamulo koma a cisomo.
15Ndipo ciani tsono? Tidzacimwa kodi cifukwa sitiri a lamulo, koma
a cisomo? Msatero ai. 16Kodi simudziwa kuti kwa iye amene mudzipereka
eni nokha kukhala akapolo ace akumvera iye, mukhalatu akapolo ace
a yemweyo mulikumvera iye; kapena a ucimo kulinga kuimfa, kapena
a umvero kulinga kucilungamo? 17Koma ayamikidwe Mulungu, kuti ngakhale
mudakhala akapolo a ucimo, tsopano mwamvera ndi mtima makhalidwe
aja a ciphunzitso cimene munaperekedweraco; 18ndipo pamene munamasulidwa
kuucimo, munakhala akapolo a cilungamo, 19Ndilankhula manenedwe
a anthu, cifukwa ca kufoka kwa thupi lanu; pakuti monga inu munapereka
ziwalo zanu zikhale akapolo a conyansa ndi a kusayeruzika kuti zicite
kusayeruzika, inde kotero tsopano perekani ziwalo zanu zikhale akapolo
a cilungamo kuti zicite ciyeretso.
Aroma 6: 20-23
20Pakuti pamene inu munali aka polo a ucimo, munali osatumikira
cilungamo. 21Ndipo munali nazo zobala zanji nthawi ija, m'zinthu
zimene mucita nazo manyazi tsopano? pakuti cimariziro ca zinthu
izi ciri imfa.
22Koma tsopano, pamene munamasulidwa kuucimo, ndi kukhala akapolo
a Mulungu, muli naco cobala canu cakufikira ciyeretso, ndi cimariziro
cace moyo wosatha. 23Pakuti mphotho yace ya ucimo ndi imfa; koma
mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Kristu Yesu
Ambuye wathu.
Aroma 8: 1-8
1Cifukwa cace tsopano iwo akukhala mwa Kristu Yesu alibe kutsutsidwa.2Pakuti
cilamulo ca mzimu wa moyo mwa Kristu Yesu candimasula ine ku lamulo
la ucimo ndi la imfa. 3Pakuti cimene cilamulo sicinathe kucita,
popeza cinafoka mwa thupi, Mulungu anatumiza Mwana wace wa iye yekha
m'cifanizo ca thupi la ucimo, ndi cifukwa ca ucimo, natsutsa ucimo
m'thupi; 4kuti coikika cace ca cilamulo cikakwaniridwe mwa ife,
amene sitiyendayenda monga mwa thupi, koma monga mwa mzimu. 5Pakuti
iwo amene ali monga mwa thupi asamalira zinthu za thupi; koma iwo
amene ali monga mwa mzimu, asamalira zinthu za mzimu: 6pakuti cisamaliro
ca thupi ciri imfa; koma cisamaliro ca mzimu ciri moyo ndi mtendere.
7Cifukwa cisamaliro ca thupi cidana ndi Mulungu; pakuti sicigonja
ku cilamulo ca Mulungu, pakuti sicikhoza kutero. 8Ndipo iwo amene
ali m'thupi sangathe kukondweretsa Mulungu.
Aroma 8: 9-17
9Koma inu simuli m'thupi ai, koma mumzimu, ngatitu Mzimu wa Mulungu
akhalabe mwa inu. Koma ngati munthu alibe Mzimu wa Kristu, siali
wace wa Kristu. 10Ndipo ngati Kristu akhala mwa inu, thupilo ndithu
liri lakufa cifukwa ca ucimo; koma mzimu uli wamoyo cifukwa ca cilungamo.
11Koma ngati Mzimu wa iye amene adaukitsa Yesu kwa akufa akhalabe
mwa inu, iye amene adaukitsa Kristu Yesu kwa akufa adzapatsanso
moyo matupi anu akufa, mwa Mzimu wace wakukhala mwa inu.
12Cifukwa cace, abale, ife tiri amangawa si ace a thupi ai, kukhala
ndi moyo monga mwa thupi; 13pakuti ngati mukhala ndi moyo monga
mwa thupi, mudzafa; koma ngati ndi mzimu mufetsa zocita zace za
thupi, mudzakhala ndi moyo.14Pakuti onse amene atsogozedwa ndi Mzimu
wa Mulungu, amenewo ali ana a Mulungu, 15Pakuti inu simunalandira
mzimu wa ukapolo kucitanso mantha; koma munalandira mzimu waumwana,
umene tipfuula nao, kuti, Abba, Atate, 16Mzimu yekha acita umboni
pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tiri ana a Mulungu; 17ndipo ngati
ana, pomweponso olowa nyumba; inde olowa nyumba ace a Mulungu, ndi
olowa anzace a Kristu; ngatitu ife timva zowawa pamodzi naye, kuti
tikalaodirenso ulemerero pamodzi ndi iye.
1. Aroma 5: 8-10
8Koma g Mulungu atsimikiza kwa ife cikonai cace ca mwini yekha m'menemo,
kuti pokhala ife cikhalire ocimwa, Kristu adatifera ife. 9Ndipo
tsono popeza inayesedwa olungama ndi mwazi wace, makamaka ndithu
tidzapulumuka mkwiyo wa Mulungu mwa Iyeyo. 10Pakuti ngati, pokhala
ife adani ace, tinayanjanitsidwa ndi Mulungu mwa imfa ya Mwana wace,
makamaka ndithu, popeza ife tayanjanitsidwa, tidzapulumuka ndi moyo
wace.
2. Aefeso 1: 18-20
18ndiko kunena kuti maso amitima yanu awalitsike, ktiti mukadziwe
inu ciyembekezo ca kuitana kwace nciani; cianinso cuma ca ulemerero
wacolowa cace mwa oyera mtima, 19ndi ciani ukuru woposa wa mphamvu
yace ya kwa ife okhulupira, monga mwa macitidwe a mphamvu yace yolimba,
20imene anacititsa mwa Kristu, m'mene anamuukitsa kwa akufa, 1 namkhazikitsa
pa dzanja lace lamanja m'zakumwamba,
2 Akorinto 13: 4
4pakuti anapacikidwa m'ufoko, koma ali ndi moyo mu mphamvu ya Mulungu.
Pakuti ifenso tiri ofok a mwa iye, koma tidzakhala ndi moyo pamodzi
ndi iye, mu mphamvu ya Mulungu, ya kwa inu.
Aefeso 2:10
10Pakuti ife ndife cipango cace, olengedwa mwa Kristu Yesu, kucita
nchito zabwino, zimene Mulungu anazipangiratu, kuti tikayende m'menemo.
Aroma 8: 9-10
9Koma inu simuli m'thupi ai, koma mumzimu, ngatitu Mzimu wa Mulungu
akhalabe mwa inu. Koma ngati munthu alibe Mzimu wa Kristu, siali
wace wa Kristu. 10Ndipo ngati Kristu akhala mwa inu, thupilo ndithu
liri lakufa cifukwa ca ucimo; koma mzimu uli wamoyo cifukwa ca cilungamo.
3. Aefeso 5: 18-20
18Ndipo musaledzere naye vinyo, m'mene muli citayiko; komatu mudzale
naye Mzimu,19ndi kudzilankhulira nokha ndi masalmo, ndi mayamiko,
ndi nyimbo zauzimu, kuyimbira ndi kuyimba m'malimba Ambuye mumtima
mwanu; 20ndi kuyamika Mulungu Atate masiku onse, cifukwa ca zonse,
m'dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu;
1 Akorinto 3: 1-3
1Ndipo ine, abale, sindinakhoza kulankhula ndi inu manga ndi auzimu,
koma monga athupi, monga makanda mwa Kristu. 2Ndinaiyetsa inu mkaka,
si cakudya colimba ai; pakuti simunaeikhoza; ngakhale tsopano lino
simucikhoza; pakuti mulinso athupi; 3pakuti, pokhala pali nkhwidzi
ndi ndeu pakati pa inu simuli athupi kodi, ndi kuyendayenda monga
mwa munthu?
Macitidwe 9:17; 19b -20
17Ndipo anacoka Hananiya, nalowa m'nyumbayo; ndipo anaika manja
ace pa iye, nati, Saulo, mbale, Ambuye wandituma ine, ndiye Yesu
amene anakuonekerani pa njira wadzerayo, kuti upenyenso, ndi kudzazidwa
ndi Mzimu Woyera.
Ndipo anakhala pamodzi ndi akuphunzira a ku Damasiko masiku ena.
20Ndipo pomwepo m'masunagoge analalikira Yesu, kuti iye ndiye Mwana
wa Mulungu.
4. Aroma 6:19
19Ndilankhula manenedwe a anthu, cifukwa ca kufoka kwa thupi lanu;
pakuti monga inu munapereka ziwalo zanu zikhale akapolo a conyansa
ndi a kusayeruzika kuti zicite kusayeruzika, inde kotero tsopano
perekani ziwalo zanu zikhale akapolo a cilungamo kuti zicite ciyeretso.
Aroma 12: 1
1Cifukwa cace ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu,
kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa,
Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.
1 Petro 4:19
19Koteronso iwo akumva zowawa monga mwa cifuniro ca Mulungu aike
moyo wao ndi kucita zokoma m'manja a Wolenga wokhulupirika.
Aroma 12: 2
2Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika,
mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire cimene ciri cifuno
ca Mulungu, cabwino, ndi cokondweretsa, ndi cangwiro.
Aroma 8: 1-5
1Cifukwa cace tsopano iwo akukhala mwa Kristu Yesu alibe kutsutsidwa.2Pakuti
cilamulo ca mzimu wa moyo mwa Kristu Yesu candimasula ine ku lamulo
la ucimo ndi la imfa. 3Pakuti cimene cilamulo sicinathe kucita,
popeza cinafoka mwa thupi, Mulungu anatumiza Mwana wace wa iye yekha
m'cifanizo ca thupi la ucimo, ndi cifukwa ca ucimo, natsutsa ucimo
m'thupi; 4kuti coikika cace ca cilamulo cikakwaniridwe mwa ife,
amene sitiyendayenda monga mwa thupi, koma monga mwa mzimu. 5Pakuti
iwo amene ali monga mwa thupi asamalira zinthu za thupi; koma iwo
amene ali monga mwa mzimu, asamalira zinthu za mzimu:
|
|