Stonecroft
Stonecroft Training
Mndandanda wa Utatu
Malangizo Otsogolera
Mavesi a m'Baibulo
Adult Stonecroft International
The International Team
English YDT Teachings
Maphunziro a Ana
Malawi Moringa Projects
|
|
home >>stonecroft>>mzimu
woyera uli kuti?>> mavesi a m'baibulo >> phunziro 3 >> phunziro 4
KODO MZIMU WOVERA ULI KUTI? - Mavesi a m'Baibulo - Phunziro #4
Kuwerenga Baibulo mlungu ndi mlungu
1 Akorinto 13: 1-13
1Ndingakhale ndilankhula malilime a anthu, ndi a angelo, koma ndiribe
cikondi, ndikhala mkuwa woomba, kapena nguli yolira. 2Ndipo ndingakhale
ndikhoza kunenera, ndipo ndingadziwe zinsinsi zonse, ndi nzeru zonse,
ndipo ndingakhale ndiri naco cikhulupiriro conse, kuti ndikasendeza
mapiri, koma ndiribe cikondi, ndiri cabe. 3Ndipo ndingakhale ndipereka
cuma cangaconsekudyetsa osauka, ndipo ndingakhalendipereka thupi
langa alitenthe m'moto, koma ndiribe cikondi, sindipindula kanthu
ai. 4Cikondi cikhala cilezere, ciri cokoma mtima; cikondi sicidukidwa;
cikondi sicidziwa kudzitamanda, sicidzikuza, 5sicicita zosayenera,
sicitsata za mwini yekha, sicipsa mtima, sicilingirira zoipa; 6sicikondwera
ndi cinyengo, koma cikondwera ndi coonadi;7cikwirira zinthu zonse,
cfkhulupirira zinthu zonse, ciyembekeza zinthu zonse, cipirira zinthu
zonse. 8Cikondi sicitha nthawizonse, koma kapena zonenera zidzakhala
cabe, kapena malilime adzaleka, kapena nzeru idzakhala cabe.9Pakuti
ife tidziwa mderamdera, ndimo tinenera mderamdera. 10Koma pamene
cangwiro cafika, tsono camderamdera cidzakhalacabe. 11Pamene ndinali
mwana, ndinalankhula ngati mwana, ndinalingirira ngati mwana, ndinawerenga
ngati mwana; tsopano ndakhala munthu, ndayesa cabe zacibwana. 12Pakuti
tsopano tipenya m'kalirole, ngati cimbuuzi; koma R pomwepo maso
ndi maso. Tsopano ndizindikira mderamdera; koma pomwepo ndidzazindikiratu,
monganso ndazindikiridwa. 13Ndipo tsopano zitsala cikhulupiriro,
dyembekezo, cikondi, zitatu izi; koma cacikuru ca izi ndico cikondi.
Aroma 8: 1-8
1Cifukwa cace tsopano iwo akukhala mwa Kristu Yesu alibe kutsutsidwa.2Pakuti
cilamulo ca mzimu wa moyo mwa Kristu Yesu candimasula ine ku lamulo
la ucimo ndi la imfa. 3Pakuti cimene cilamulo sicinathe kucita,
popeza cinafoka mwa thupi, Mulungu anatumiza Mwana wace wa iye yekha
m'cifanizo ca thupi la ucimo, ndi cifukwa ca ucimo, natsutsa ucimo
m'thupi; 4kuti coikika cace ca cilamulo cikakwaniridwe mwa ife,
amene sitiyendayenda monga mwa thupi, koma monga mwa mzimu. 5Pakuti
iwo amene ali monga mwa thupi asamalira zinthu za thupi; koma iwo
amene ali monga mwa mzimu, asamalira zinthu za mzimu: 6pakuti cisamaliro
ca thupi ciri imfa; koma cisamaliro ca mzimu ciri moyo ndi mtendere.
7Cifukwa cisamaliro ca thupi cidana ndi Mulungu; pakuti sicigonja
ku cilamulo ca Mulungu, pakuti sicikhoza kutero. 8Ndipo iwo amene
ali m'thupi sangathe kukondweretsa Mulungu.
Aroma 8: 9-17
9Koma inu simuli m'thupi ai, koma mumzimu, ngatitu Mzimu wa Mulungu
akhalabe mwa inu. Koma ngati munthu alibe Mzimu wa Kristu, siali
wace wa Kristu. 10Ndipo ngati Kristu akhala mwa inu, thupilo ndithu
liri lakufa cifukwa ca ucimo; koma mzimu uli wamoyo cifukwa ca cilungamo.
11Koma ngati Mzimu wa iye amene adaukitsa Yesu kwa akufa akhalabe
mwa inu, iye amene adaukitsa Kristu Yesu kwa akufa adzapatsanso
moyo matupi anu akufa, mwa Mzimu wace wakukhala mwa inu.
12Cifukwa cace, abale, ife tiri amangawa si ace a thupi ai, kukhala
ndi moyo monga mwa thupi; 13pakuti ngati mukhala ndi moyo monga
mwa thupi, mudzafa; koma ngati ndi mzimu mufetsa zocita zace za
thupi, mudzakhala ndi moyo.14Pakuti onse amene atsogozedwa ndi Mzimu
wa Mulungu, amenewo ali ana a Mulungu, 15Pakuti inu simunalandira
mzimu wa ukapolo kucitanso mantha; koma munalandira mzimu waumwana,
umene tipfuula nao, kuti, Abba, Atate, 16Mzimu yekha acita umboni
pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tiri ana a Mulungu; 17ndipo ngati
ana, pomweponso olowa nyumba; inde olowa nyumba ace a Mulungu, ndi
olowa anzace a Kristu; ngatitu ife timva zowawa pamodzi naye, kuti
tikalaodirenso ulemerero pamodzi ndi iye.
1 Akorinto 12: 1-11
1Koma za mphatso zauzimu, abale, sindifuna kuti mukhale osadziwa.2Mudziwa
kuti pamene munali amitundu, munatengedwa kunka kwa mafano aja osalankhula,
monga munatsogozedwa. 3Cifukwa cace ndikuuzani inu, kuti palibe
munthu wakulankhula mwa Mzimu wa Mulungu, anena, Yesu ngwotembereredwa;
ndipo palibe wina akhoza kunena, Yew ali Ambuye, koma mwa Mzimu
Woyera.
4Ndipo pali mphatso zosiyana, koma Mzimu yemweyo. 5Ndipo pali mautumiki
osiyana, koma Ambuye yemweyo. 6Ndipo pali macitidwe osiyana, koma
Mulungu yemweyo, wakucita zinthu zonse mwa onse. 7Koma kwa yense
kwapatsidwa maonekedwe a Mzimu kuti apindule nao. 8Pakuti kwa mmodzi
kwapatsidwa mwa Mzimu mau a nzeru; koma kwa mnzace mau a cidziwitso,
monga mwa Mzimu yemweyo: 9kwa wina cikhulupiriro, mwa Mzimu yemweyo;
ndi kwa wina mphatso za maciritso, mwa Mzimu mmodziyo; 10ndi kwa
wina macitidwe a mphamvu; ndi kwa wina cinenero; ndi kwa wina cizindikiro
ca mizimu; kwa wina malilime a mitundu mitundu; ndi kwa wina mamasulidwe
a malilime. 11Koma zonse izi acita Mzimu mmodzi yemweyo, nagawira
yense payekha monga afuna.
1 Yohane 4: 7-21
7Okondedwa, tikondane wins ndi mnzace: cifukwa kuti cikond cicokera
kwa Mulungu, ndipo yense amene akonda, abadwa kucokera kwa Mulungu,
namzindikira Mulungu, 8iye wosakonda sazindikira Mulungu; cifukwa
Mulungu ndiye cikondi. 9Umo cidaoneka cikondi ca Mulungu mwa ife,
kuti Mulungu anamtuma Mwana wace wobadwa yekha alowe m'dziko lapansi,
kuti tikhale ndi moyo mwa iye. 10Umo muli cikondi, sikuti ife tinakonda
Mulungu, koma kuti iye anatikonda ife, ndipo anatuma Mwana wace
akhale ciombolo cifukwa ca macime athu. 11Okondedwa, ngati Mulungu
anatikonda ife kotero, ffenso tiyenera kukondana wina ndi mnzaceo
12Palibe munthu adamuona Mulungu nthawi iri yonse; tikakondana wina
ndi mnzace, Mulungu akhala mwa ife, ndi cikondi cace cikhala cangwiro
mwa ife; 13m'menemo tizindikira kuti tikhala mwa iye, ndi iye mwa
ife, cifukwa anatipatsako Mzimu wace. 14Ndipo ife tapenyera, ndipo
ticita umboni kuti Atate anatuma Mwana akhale Mpulumutsi wa dziko
lapansi. 15Iye amene adzabvomereza kuti Yesu ali Mwana wa Mulungu,
Mulungu akhala mwa iye, ndi iye mwa Mulungu. 16Ndipo ife tazindikira,
ndipo takhulupirira cikondico Mulungu ali naco pa ife. Mulungu ndiye
cikondi, ndipo iye amene akhala m'cikondi akhala mwa Mulungu, ndipo
Mulungu akhala mwa iye. 17M'menemo cikondi cathu cikhala cangwiro
kuti tikhale nako kulimbika mtima m'tsiku la mlandu; citukwa monga
Iyeyuali, momwemo tiri ife m'dziko line lapansi.18Mulibe mantha
m'cikondi; koma cikondi cangwiro citaya kunja mantha, popeza mantha
ali naco cilango, ndipo wamanthayo sakhala wangwiro m'cikondi.19Tikonda
ife, cifukwa anayamba iye kutikonda. 20Munthu akati, kuti, Ndikonda
Mulungu, nadana naye mbale wace, ali wabodza: pakuti iye wosakonda
mbale ware amene wamuona, sakhoza kukonda Mulungu amene sanamuona.
21Ndipo lamulo ili tiri nalo locokera kwa iye, kuti iye amene akonda
Mulungu akondenso mbale wace.
Galates 5: 16-26
16Koma ndinena, Muyendeyende ndi Mzimu, ndipo musafitse cilakolako
ca thupi. 17Pakuti thupi lilakalaka potsutsana naye Mzimu, ndi Mzimu
potsutsana nalo thupi; pakuti izi sizilingana; kuti zimene muzifuna
musazicite. 18Ngati Mzimu akutsogolerani, simuli omvera lamulo.
19Ndipo nchito za thupi zionekera, ndizo dama, codetsa, kukhumba
zonyansa, kupembedza mafano, 20nyanga, madano, ndeu, kaduka, zopsa
mtima, zotetana, magawano, mipatuko, njiru, 21kuledzera, mcezo,
ndi zina zotere; zimene ndikucenjezani nazo, monga ndacita, kuti
iwo akucitacita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu. 22Koma cipatso
ca Mzimu ndico cikondi, cimwemwe, mtendere, kuleza mtima, cifundo,
kukoma mtima, icikhulupirtro, 23cifatso, ciletso; pokana zimenezi
palibe lamulo. 24Koma iwo a Kristu Yesu adapacika thupi, ndi zokhumba
zace, ndi zilakolako zace.
251 N gati tiri ndi moyo ndi Mzimu, ndi Mzimunso tiyende. 262 Tisakhale
odzikuza, outsana, akucitirana njiru.
1 Petro 5: 14b
Mtendere ukhale ndi inu nonse muli mwa Kristu.
1 Yohane 1: 9
9Ngati tibvomereza macimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama
iye, kuti atikhululukire macimo athu, ndi kutisambitsa kuticotsera
cosalungama ciri conse
1. Agalatiya 5: 22-23
22Koma cipatso ca Mzimu ndico cikondi, cimwemwe, mtendere, kuleza
mtima, cifundo, kukoma mtima, icikhulupirtro, 23cifatso, ciletso;
pokana zimenezi palibe lamulo.
1 Akorinto 13:13
13Ndipo tsopano zitsala cikhulupiriro, dyembekezo, cikondi, zitatu
izi; koma cacikuru ca izi ndico cikondi.
Chipatso cha Mzimu
2. Mateyu 22: 34-40
34Koma Afarisi, pakumva kuti Iye anatontholetsa Asaduki, anasonkhana.35Ndipo
mmodzi wa iwo, mphunzitsi wa cilamulo, anamfunsa ndi kumuyesa Iye,
nati, 36Mphunzitsi, lamulo lalikuru ndi liti la m'cilamulo? 37Ndipo
Yesu anati kwa iye, Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako
wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse. 38Ili ndilo lamulo
lalikuru ndi loyamba. 39Ndipo laciwiri lolingana nalo ndili, Uzikonda
mnzako monga udzikonda iwe mwini. 40Pa malamulo awa awiri mpokolowekapo
cilamulo conse ndi aneneri.
Kukonda
3. a. Akolose 3:19
19Amuna inu, kondani akazi anu, ndipo musawawire mtima iwo.
b. Luka 6: 27-28
27Koma ndinena kwa inu akumva, Kondanani nao adani anu; citirani
zabwino iwo akuda inu, 28dalitsani iwo akutemberera inu, pemphererani
iwo akucitira inu cipongwe.
c. Tito 2: 3-4
3Momwemonso akazi okalamba akhale nao makhalidwe oyenera anthu oyera,
osadierekeza, osakodwa naco cikondi ca pavinyo, akuphunzitsa zokoma;
4kuti akalangize akazi ang one akonde amuna ao, akonde ana ao,
d. Yohane 13: 34-35
34Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzace;
monga ndakonda Inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzace. 351 Mwa
ici adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli naco
cikondano wina ndi mnzace.
e. Mateyu 22:39
39Ndipo laciwiri lolingana nalo ndili, Uzikonda mnzako monga udzikonda
iwe mwini.
f. Aefeso 5: 2
2ndipo yendani m'cikondi monganso Kristu anakukondani inu, nadzipereka
yekha m'malo mwathu, copereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale pfungo
lonunkhira bwino.
Aroma 12: 9-10
9Cikondano cikhale copanda cinyengo, Dana naco coipa; gwirizana
naco cabwino. 10M'cikondano ca anzanu wina ndi mnzace mukondane
ndi cikondi ceni ceni; mutsogolerane ndi kucitira wina mnzace ulemu;
Aroma 5: 5
5ndipo ciyembekezo sicicititsa manyazi; cifukwa cikondi ca Mulungu
cinatsanulidwa m'mitima mwathu mwa Mzimu Woyera, amene wapatsidwa
kwa ife.
Chimwemwe
Afilipi 4: 4
4Kondwerani mwa Ambuye nthawi zonse: ndibwerezanso kutero, kondwerani.
Mtendere
Afilipi 4: 6-7
6Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero,
pamodzi ndi ciyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. 7Ndipo
mtendere wa Mulungu wakupambana cidziwitso conse, udzasunga mitima
yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.
Yohane 14:27
274 Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani; Ine
sindikupatsani inu monga dziko lapansi lipatsa. 5 Mtima wanu usabvutike,
kapena usacite mantha.
Chipiriro
4. Aroma 15: 5
5Ndipo Mulungu wa cipiriro ndi wa citonthozo apatse inu kuti mukhale
ndi mtima umodzi wina ndi mnzace, monga mwa Kristu Yesu;
Mtima
5. Akolose 3:12
12Cifukwa cace bvalani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi
okondedwa, mtima wacifundo, kukoma mtima, kudzicepetsa, cifatso,
kuleza mtima;
Ubwino
6. Aefeso 2:10
10Pakuti ife ndife cipango cace, olengedwa mwa Kristu Yesu, kucita
nchito zabwino, zimene Mulungu anazipangiratu, kuti tikayende m'menemo.
Kukhulupirika
Luka 16: 10-12
10Iye amene akhulupirika m'cacing'onong'ono alinso wokhulupirika
m'cacikuru; ndipo iye amene ali wosalungama m'cacing'onong'ono alinso
wosalungama m'cacikuru. 11Cifukwa cace ngati simunakhala okhulupirika
m'cuma ca cosalungama, adzakhulupirira inu ndani ndi cuma coona?
12Ndipo ngati simunakhala okhulupirika ndi zace za wina, adzakupatsani
inu ndani za inu eni?
7. 2 Atesalonika 3: 3
3Koma Ambuye ali wokhulupirika amene adzakukhazikitsani inu, nadzakudikirirani
kuletsa woipayo;
Kudzichepetsa
Afilipi 2: 3-8
3musacite kanthu monga mwa cotetana, kapena monga mwa ulemerero
wopanda pace, komatu ndi kudzicepetsa mtima, yense ayese anzace
omposa iye mwini; 4munthu yense asapenyerere zace za iye yekha,
koma yense apenyererenso za mnzaceo 5Mukhale nao mtima m'kati mwanu
umene unalinso mwa Kristu Yesu, 6ameneyo, pokhala nao maonekedwe
a Mulungu, sanaciyesa colanda kukhala wofana ndi Mulungu,7koma anadzikhuthula
yekha, natenga maonekedwe akapolo, nakhala m'mafanizidwe a anthu;
8ndipo popezedwa m'maonekedwe ngati munthu, anadzicepetsa yekha,
nakhala womvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya pamtanda.
Kudzigwira
Tito 2: 11-12
11Pakuti caonekera cisomo ca Mulungu cakupulumutsa anthu onse, 12ndi
kutiphunzitsa ife kuti, pokana cisapembedzo ndi zilakolako za dziko
lapansi, tikhale ndi moyo m'dziko lino odziletsa, ndi olungama,
ndi opembedza;
Afilipi 1:11
11odzala nacocipatso ca cilungamo cimene ciri mwa Yesu Kristu, kucitira
Mulungu ulemerero ndi ciyamiko.
Mphatso za mzimu
Agalatiya 5:22-23
22Koma cipatso ca Mzimu ndico cikondi, cimwemwe, mtendere, kuleza
mtima, cifundo, kukoma mtima, icikhulupirtro, 23cifatso, ciletso;
pokana zimenezi palibe lamulo.
1 Akorinto 12:11
11Koma zonse izi acita Mzimu mmodzi yemweyo, nagawira yense payekha
monga afuna.
1 Petro 4:10
10monga yense walandira mphatso, mutumikirane nayo, ngati adindo
okoma a cisomo ca mitundu mitundu ca Mulungu;
8. 1 Petro 4:10
10monga yense walandira mphatso, mutumikirane nayo, ngati adindo
okoma a cisomo ca mitundu mitundu ca Mulungu;
9. 1 Akorinto 12: 8-10
8Pakuti kwa mmodzi kwapatsidwa mwa Mzimu mau a nzeru; koma kwa mnzace
mau a cidziwitso, monga mwa Mzimu yemweyo: 9kwa wina cikhulupiriro,
mwa Mzimu yemweyo; ndi kwa wina mphatso za maciritso, mwa Mzimu
mmodziyo;
Aroma 12: 6-8
6Ndipo pokhala ife ndi mphatso zosiyana, monga mwa cisomo copatsidwa
kwa ife, kapena mphatso yakunenera, tinenere monga mwa muyeso wa
cikhulupiriro;7kapenayakutumikira, tidzipereke ku utumiki uwu; kapena
iye wakuphunzitsa, kukuphunzitsako;
1 Akorinto 12:11
11Koma zonse izi acita Mzimu mmodzi yemweyo, nagawira yense payekha
monga afuna.
|
|