home >>stonecroft>>mzimu
woyera uli kuti?>> mavesi a m'baibulo >> phunziro 1
KODO MZIMU WOVERA ULI KUTI? - Mavesi a m'Baibulo - Phunziro #1
1. Yohane 14:26
26Koma 2 Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamtuma m'dzina
langa, 3 Iyeyo adzaphunzitsa Inu zonse, nadzakumbutsa inu zinthu
zonse zimene ndinanena kwa inu.
2. Yohane 15:26
26Koma pamene wafika Nkhoswe, amene Ine ndidzamtuma kwa inu kucokera
kwa Atate, ndiye Mzimu wa coonadi, amene aturuka kwa Atate, Iyeyu
adzandicitira Ine umboni.
Macitidwe 13: 2
2Ndipo pa kutumikira Ambuye iwowa, ndi kusala cakudya, Mzimu Woyera
anati, Mundipatulire Ine Bamaba ndi Saulo ku nchito imene odinawaitanirako.
Aroma 8:14
14Pakuti onse amene atsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu, amenewo ali
ana a Mulungu,
Aroma 8:26
26Ndipo momwemonso Mzimu athandiza kufoka kwathu; pakuti cimene
tizipempha monga ciyenera, sitidziwa; koma Mzimu mwiniatipempherera
ndi zobuula zosatheka kuneneka;
3. 2 Akorinto 1: 21-22
21Koma iye wakutikhazika pamodzi ndi inu kwa Kristu, natidzoza ife,
ndiye Mulungu; 22amenenso anatisindikiza cizindikilo, natipatsa
cikole ca Mzimu mu mitima yathu.
4. Yohane 16: 7-11
7Koma ndinena Ine coonadi ndi inu; kuyenera kwa inu kuti ndicoke
Ine; pakuti ngati sindicoka, Nkhosweyo sadzadza kwa inu; koma ngati
ndipita ndidzamtuma iye kwa inu. 8Ndipo atadza Iyeyo, adzatsutsa
dziko lapansi za macimo, ndi za cilungamo, ndi za ciweruziro; 9za
macimo, cifukwa sakhulupirira Ine; 10za cilungamo, cifukwa ndinka
kwa Atate, ndipo simundionanso; 11za ciweruziro, cifukwa mkuru wa
dziko ili lapansi waweruzidwa.
Yesaya 5:20
20Tsoka kwa iwo amene ayesa zoipa zabwino, ndi zabwino zoipa; amene
aika mdima m'malo mwa kuyera, ndi kuyera m'malo mwa mdima; amene
aika zowawa m'malo mwa zotsekemera, ndi zotsekemera m'malo mwa zowawa!
Jude 1: 14-16
14Ndipo kwa iwo, Henoke, wacisanu ndi ciwiri kuyambira kwa Adamu,
ananenera kuti, Taona, wadza Ambuye ndi oyera ace zikwi makumi,
15kudzacitira onse ciweruziro, ndi kutsutsa osapembedza onse, pa
nchito zao zonse zosapembedza, zimene anazicita kosapembedza, ndi
pa zolimba zimene ocimwa osapembedza adalankhula pa iye. 16Amenewo
ndiwo odandaula, oderera, akuyenda monga mwa zilakolako zao (ndipo
pakamwa pao alankhula zazikuruzikuru), akutama anthu cifukwa ca
kupindula nako.
Aroma 6:23
23Pakuti mphotho yace ya ucimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya
Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.
Muthu Mzimu wa Mulungu
5. a. Yohane 3: 5-7
5Yesu anayankha, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa
mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kulowa ufumu wa Mulungu. 6Cobadwa m'thupi
cikhala thupi, ndipo cobadwa mwa Mzimu, cikhala mzimu. 7Usadabwe
cifukwa ndinati kwa iwe, Uyenera kubadwa mwatsopano.
b. Tito 3: 4-7
4Koma pamene kukoma mtima, ndi cikondi ca pa anthu, ca Mpulumutsi
wathu Mulungu zidaoneka, 5zosati zocokera m'nchito za m'cilungamo,
zimene tidazicita ife, komatu monga mwa cifundo cace anatipulumutsa
ife, mwa kutsuka kwa kubadwanso ndi makonzedwe a Mzimu Woyera,
Yohane 3:16
16Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana
wace wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike, koma
akhale nao moyo wosatha.
6. Cibvumbulutso 22:17
17Ndipo Mzimu ndi mkwatibwi anena, Idzani, Ndipo wakumva anene,
Idzani. Ndipo wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo
kwaulere.
Mulungu ali m'modzi
Aroma 8: 9
9Koma inu simuli m'thupi ai, koma mumzimu, ngatitu Mzimu wa Mulungu
akhalabe mwa inu. Koma ngati munthu alibe Mzimu wa Kristu, siali
wace wa Kristu.
7. 1 Akorinto2:11
11Pakuti ndani wa anthu adziwa za munthu, koma mzimu wa munthuyu
uli mwa iye? momwemonso za Mulungu palibe wina azidziwa, koma Mzimu
wa Mulungu.
Ahebri 9:14
14koposa kotani nanga mwazi wa Kristu amene anadzipereka yekha wopanda
cirema kwa Mulungu mwa Mzimu wosatha, udzayeretsa cikumbu mtima
canu kucisiyanitsa ndi nchito zakufa, kukatumikira Mulungu wamoyo?
Aroma 8: 2, 10
2Pakuti cilamulo ca mzimu wa moyo mwa Kristu Yesu candimasula ine
ku lamulo la ucimo ndi la imfa.
10Ndipo ngati Kristu akhala mwa inu, thupilo ndithu liri lakufa
cifukwa ca ucimo; koma mzimu uli wamoyo cifukwa ca cilungamo.
|