6. Yesu anafa pa mtanda ndi kuukanso kuti
tikakhululukidwe ndi kukhala pa ubale
ndi Iye. Tikuyenera kumfusa Yesu atikhululukire ndi kumuitana
kulowa m'moyo
mwathu. Ichi ndi chinthu chimene tikuyenera kuchita pa tokha.
Palibe angatichitire
ichi. Ngati simukukumbukira nthawi imene munamuitana Yesu
kulowa mu mtima
mwanu mutha kumuitana pompano.
Kuika chikhulupiriro chanu mwa Yesu ndi kulandira chikhululukiro
ndi mphatso ya moyo wosatha.—
a. Zindikirani Yesu anakulengani inu kuti mukakhale pa chiyanjano
ndi Iye. Amakukoni ndipo amafuna inu mumkonde ndi zanu zonse.
b. Zindikirani ndinu ochimwa. Simungadzipulumutse nokha.
c. Khulupirirani Yesu anafa pa mtanda kupereka dipo la tchimo
lanu, kuti anauka kwa akufa, ndipo kuti ali wamoyo lero. Khulupirirani
izi mu mtima mwanu osati mu mutu mwanu mokha.
d. Lankhulani ndi Mulungu m'moyo mwanu:
1) Funsani Yesu alowe m'moyo mwanu.
2) Bvomerezani ndipo mulape machimo anu, zimene zitanthauza
kubwerera ku
machimo anu ndi kutembenukira kwa Mulungu.
3) Mufunseni akhululukire machimo anu.
4) Perekani moyo wanu kwa Yesu. Mloleni akhale mbuye wanu.
e. Uzani ena zimene mwachita.
f. Uzani gulu lanu la za chisankho chanu chimene mwapanga.
g. Ngati mwalandira Yesu Christu ngati mpulumutsi, lembani
tsiku. Ndi tsiku loti
mudzilikumbukira! Ngati munamulandira pa kale, lembani tsiku
limene
munamulandirira (perekani tsiku longoganizira kapena zaka
ngati simuli
otsimikizika za nthawi imene munamulandira Yesu)
|