Stonecroft
Stonecroft Training
Mndandanda wa Utatu
Malangizo Otsogolera
Mavesi a m'Baibulo
Adult Stonecroft International
The International Team
English YDT Teachings
Maphunziro a Ana
Malawi Moringa Projects
|
|
home >>stonecroft>>
yesu ndani? >>phunziro 1
Stonecroft - YESU NDI NDANI?- Phunziro #1
Baibulo limati
Chani za Yesu?
Yesu ndi
Ndani?
Sauli, munthu wachiyuda amene amamanga ndi kupha akristu
oyambirira, anafunsa funso lofunikira. Ndifunso lofunikira
limene tingafunse. Anafunsa, "Ndinu ndani, Ambuye?"
Analandira yankho pompopompo "
Ndine Yesu amene ukumulondalonda..."
(Machitidwe 9:5).
Munthu waukaliyu (amene anapamgitsa chipolowe mu chalitchi
choyambirira ku Yerusalem) analandira uthenga woyenera, anakhala
munthu wosandulika. Anali atatakasidwa ndi chikhulupiriro
chabodza. Ankaganiza kuti anali kukondweretsa Mulungu pochita
ntchito zake zakupha, koma iye amkalondalonda Iye.
Timachita zomwezo, pamene tikukhulupirira zinthu zimene zili
zabodza. Timachita zinthu zimene zili zoyipa kwa ife eni—nkhakhalenso
kwa anzathu. Njira yokhayo kuti tikhale ndi chidziwitso chenicheni
ndi kuzindikira ndi kukhulupirira choonadi. Maphunziro a Baibulowa
akumana ndi chosowa chanu cha choonadi. Akukankhirani ku chitsime
cha zoonadi zonse, Mau a Mulungu. Mulungu akuti,
“Thambo ndi dziko lapansi
zidzachoka,
koma mau anga sadzachokaHeaven.”
—Mateyu 24:35
Mau a Mulungu ndi oona ndipo adzaima mpaka kalekale. Anthu
ali ndi zidziwitso zolakwika za Yesu. |
People have many incorrect and strange ideas
about Jesus. Since our behavior is influenced and motivated by what
we believe, it is important that we have accurate information about
who Jesus is, who God is and who we are. When you have finished
this study, you will know beyond a shadow of a doubt who Jesus really
is.
Mumakhulupirira kuti Yesu ndi ndani?
Lero timamva maganizo osiyanasiyana. Ena amati ndiye amene anayambitsa
chipembedzo....mtsogoleri wa nkulu wa chikristu...mphunzitsi
wa nkulu wa chikhalidwe...munthu woyamba kuzunzidwa mwankhanza
mum'bado wake.
Titha kudziwa zoona pokhapoka tikakhulupirira uthenga wochokera
ku chitsime cha choonadi. Pali choonadi chimodzi—Mulungu.
Watipatsa ife Buku, limene limatiuza m'mene tingamudziwire
Iye komanso m'mene tingakhalire moyo womusangalatsa Iye ndi
ife.
Yesu sali ngati m'modzi wa atsogoleri a chipembedzo pa dziko
la pansi. Sali ngati munthu wankulu wa m'Baibulo ngati Abraham,
Mose, kapena Davide. Nthawi zonse tikamalemba tsiku kapena
chaka, timazindikira kuti zaka zikwi ziwiri (2000) zapitazo
Yesu Khristu anabwera ndi kugawa mbiri m'magawo awiri:
|
Baibulo limatiuza zinthu zambiri zodabwitsa za
Yesu. Mwachitsanzo, Yesu analipo chikhalire nthawi isanayambe.
Malo ambiri mu Baibulo amafotokoza Yesu analipo pachiyambi dziko
lisanalengedwe.
Baibulo limati,
“Ndipo Iye ali woyamba wa sonse.
. .”
—Akolose 1:17
|
Yesu analipo asanabadwe ngati munthu.
Wakhala ali chikhalire ndipo adzakhala mpaka muyaya. Palibe
mtsogoleri wa chipembedzo amwene ananena kuti adzakhala muyaya,
koma Yesu ananena. Anati,
“ . . . Asanayambe
kukhala Abraham ndipo 'Ine ndiripo'.”
—Yohane 8:58
Izi zitanthauza Yesu analipo. INE AMENE NDILI ndi dzina la
Mulungu.
Pa Exodo 3:14, zaka zikwi ziwiri Yesu asanabadwe, Mulungu
anadzionetsera Yekha kwa Mose ngati "INE AMENE NDILI"
Muchiheberi dzinali litanthauza kukhala kwa chikhalire.
Yesu anaziyerekeza Yekha ndi Mulungu (Yohane 5:18) |
Kuzindikira Choonadi
Ganizani mozama ndi mwapemphero za maphunziro
mukuphunzirawa.
zifunseni mafunso awa:
Baibulo pa gawo ili likuti chani?
Zindikirani choona cha Mulungu
Baibulo pa gawo ili likuti chani?
Mvetsetsani chimene Mulungu akunena.
Mulungu akundilankhula chani?
Chitengeni choonacho muchichite pa moyo wanu. |
Mwapempero
lingalilani m'mene Mulungu akufunira kuti Muyankhe
Muvera lamulo kapena kusintha
m'mene mumaonera zinthu? |
Uthenga
wa Bwino
Mabuku oyambirira a Chipangano cha Tsopano sanalembedwe kukhala
a mbiri ya Yesu. analembedwa ndi anthu osiyanasiyana kwa magulu
osiyanasiyana ndi zifukwa zosiyanasiyana. mabuku amenewa amatchedwa
uthenga wabwino.
Awiri amabukuwa—Uthenga Wabwino wa Mateyu ndi Uthenga
Wabwino wa Yohane—unalembedwa ndi anthu awiri amene
anayenda ndi Yesu kwa zaka zitatu. anali mu gulu la anthu
khumi ndi awiri amene Yesu adawasankha ngati atumwi. Pa mu
chipangano cha Tsopano pali mndandanda wa mau amene akupereka
tanthauzo la mau amene simukuwadziwitsitsa. Onani tanthauzo
la mtumwi. . . . .
Kuyambira pa ndi gawo losonyeza maphunziro. izi zimathandiza
mukafuna kufufuza kuchoka mu Baibulo za phunziro limene mukufuna
kuphunzira. Mateyu adalemba uthenga wa bwino wa Mateyu kutsimikizira
a Yuda kuti iye ndiye Mesiya amene adakhala akumufunafuna.
Yohane adalemba uthenga wabwino wa Yohane kutsimikizira owerenga
kuti Yesu adali Mwana wa Mulungu.
Uthenga wa bwino wa Mariko udalembedwa ndi mnyamata Maliko,
amene adagwira ntchito ndi Paulo komanso Barnaba ndi Petulo.
Marko adalemba kwa amitundu kuwauza za Yesu ndi zimene
adachita.
Uthenga wa bwino wa Luka udalembedwa ndi dotolo wa chihelena
amene anapanga kafukufuku ndi ku fusa anthu amene anali kumudziwa
Yesu.
Chifukwa uthenga wabwino uluonse umalembedwa kwa anthu osiyanasiyana,
onsewo amayimira mbali zosiyana za moyo wa Khristu.
|
1. Yohane anati chani pomaliza pa uthenga wake wabwino? Yohane
21:25 . . . |
2. Ndi mayina ena ati amene Yesu amatchulidwa
mu buku la Mateyu?
a. Mateyu 1:21
b. Mateyu 1:23
c. Mateyu 3:17
d. Mateyu 12:8
e. Mateyu 16:16
f. Mateyu 19:16
3. Kodi Yesu amatchedwa yani mu mabuku limene likuyenderana ndi
Bailo?
a. Marko 5:6-7
b. Luka 5:5
c. Yohane 1:35-36
d. John 1:49
e. 1 Akolinto 1:6-7
Josephus (Joh-SEE-fus), Wodziwa za mbiri wa chi
Yuda amene anabadwa mu chaka cha A.D. 37 amene anali wosakhulupirira
, analemba zoona za kupachikidwa kwa Yesu. Ngakhale kuti Josephus
samakhulupirira kuti Yesu ndi Mesiya, analemba izi zokhudzana
ndi Yesu:
“Tsopano, panali munthu uyu wa nzeru , ngati nkoyenera
kumutcha munthu, poti anali wochita ntchito za bwino, mpunzitsi
wa anthu wa choonadi. Anakopa Ayuda ngakhale a Mitundu. Anali
Khristu, ndipo pamene Pilato pa kukhumba kwa anthu akuluakulu
mwa ife, analamula apachikidwe pa mtanda, iwo anankonda Iye
poyamba sanantaye; poti anaonekeranso kwa iwo wamoyo pa tsiku
la chitatu, monga momwe aneneri a uzimu analoserandi zikwi
khumi za zinthu zodabwitsa zokhudza Iye. Ndipo mtundu wa Akhristu
wotchedwa chifukwa cha Iye ukanalipo osatha mpaka lero.”
—Antiquities
|
Ma uneneri ochepa okhudza
Mesiya
Uneneri |
Kukwaniritsidwa |
Adzabadwa mwa namwali. |
Kubadwa mwa namwali Yesu |
Yesaya 7:14
(742B.C.)
Chifukwa chache Ambuye mwini yekha
adzakupatsani chizindikiro, taonani namwali
adzaima, nadzabala mwana wa mwamuna,
nadzamucha dzina lache Imanueli. (NASB)
|
Mateyu 1:22-23
Ndipo zonsezi zinakhala kuti chikachitidwe chonenedwa ndi
Ambuye mwa mneneri, ndi kuti, Onani namwali adzaima, nadzabala
mwana wa mwamuna dzina lace, Emanueli;
(ndilosandulika, “Mulungu nafe”). |
Malo ake obadwira
|
Kubadwa kwa Yesu mu Betelehem.
|
Micah 5:2 (710B.C.)
Ambuye akuti, “Betelehemu Efrata, ndiwe
wa ngono kuti ukhale mwa zikwi za Yuda, mwa iwe mudzatuluka
wowereza mu Israyeli;
matulukiro ake ndiwo a kale lomwe, kuyambira nthawi yosayamba.
|
Mateyu 2:1a
Yesu adabadwa mu mzinda
wa Betelehemu wa Yudea mu nthawi imene Herodi adali mfumu. |
Adzakanidwa ndi anthu Ache.
|
Yesu adakanidwa.
|
Isaiah 53:3 (712B.C.)
Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu; munthu wa zisoni,
ndiwodziwa zowawa; ndipo ananyozedwa monga munthu ombisira
anthu nkhope zao; ndipo ife sitinamulemekeza. |
Yohane 1:11
Anadza kwa zache za Iye yekha, koma dziko silidamuzindikira
Iye. |
Adzaperekedwa ndi bwenzi |
Yesu adaperekedwa ndi m'modzi mwa ophunzira.
|
Salimo 41:9 (1062B.C.)
Ngakhale bwenzi langa leni leni, amene
ndamkhulupirira, ndiye amene anadyako mkate wanga, adandikwezera
chidendene chache. |
Marko 14:10
Ndipo Yudase Iskariote, ndiye mmodzi wa khumi ndi awiriwo, anachoka
napita kwa ansembe akulu, kuti akampereke Iye kwa iwo. |
Adzauka kwa akufa. |
Yesu anauka patatha masiku atatu m'manda. |
Salimo 16:10 (1040
B.C.) …akuti simudzasiya moyo wanga kumanda;
simudzalora okondedwa wanu avunde. |
Mateyu 28:5-6
Koma ngelo anayankha nati kwa akaziwo,
"Musaope inu; pakuti ndidziwa inu muli kufuna Yesu, amene
anapachikidwa. Iye mulibe muno iai; pakuti anauka, monga ananena
.idzani muno mudzaone malo omwe anagonamo Ambuye.” |
4. Ziganizo zili mmusimu zikukamba za mbiri za Yesu. Onani pa
mafunso oti
muyankhe, ndi zofananiza malemba a chiganizo ndi mau oyenerera
mbaibulo:
a. Makolo Ake .......................b. Ubatizo Wake .....................c.
Wake choyamba chake
|
“Khristu ndi fanizo la Mulungu wosaonekayo..."
—Akolose 1:15
|
Pemphero Lotseka
Zikomo Ambuye Mulungu. Taphunzira za mbiri za Yesu mu phunziro
ili. Tiphunzitseni za mbiri pamene tikupitiliza maphunziro awa.
Tithanndizeni kupeza nthawi yowerenga phunziro ya sabata ya mawa.
Tapemphera mu dzina la Yesu, ame.
|
|