Stonecroft
Stonecroft Training
Mndandanda wa Utatu
Malangizo Otsogolera
Mavesi a m'Baibulo
Adult Stonecroft International
The International Team
English YDT Teachings
Maphunziro a Ana
Malawi Moringa Projects
|
|
home >>stonecroft>>
yesu ndani? >>phunziro 3 >>phunziro 4
Stonecroft - YESU NDI NDANI?- Phunziro #4
Chifukwa chani Yesu anabwera?
Pemphero
Wokondedwa Atate a Kumwamba, zikomo pa zonse matiphunzitsa za Mwana
Wanu, Yesu
Khristu. Tikufuna tidziwe nchifukwa chani anabwera ku dziko la pansi.
Tiphunzitseninso
kuchokera m'mau anu. Tapemphera mu dzina la Yesu, ame.
Kuwerenga Baibulo kwa Sabata:
Werengani gawo la Baibulo pansipa ndipo mulembe m'mau anu
zimene limanena
za chifukwa chimene Yesu anabwerera ku dziko lapansi.
Mateyu 5:1-2, 17-20
Yohane 6:35-38
Machitidwe 2:23-24
1 Yohane 3:5-6
Aheberi 2:14-15
Chibvumbulutso 3:20-21
Chibvumbulutso 5:9-10
|
1. Chifukwa chani Yesu anabwera pa
tdziko la pansi? Baibulo likutipatsa zifukwa
zambiri pansipa.
a. Mateyu 5:17
b. Yohane 1:18 |
c. Mateyu 20:28
d. Luka 4:42-43
e. Luka 19:10
f. Yohane 3:17
g. Yohane 10:7-10
h. 1 Timoteyo 1:15
|
“Yese
wachimwa ndi kutalikilana ndi kupezeka kopulumutsa kwa
Mulungu.”
—Aroma 3:23
Chilango cha uchimo chinalengezedwa ndi Mulungu kwa Adamu
ndi Hava pa chiyambi. Chilango chinali cha imfa ya kuuzimu
ndi kuthupi. Genesis 2:17 ikuti, “Koma mtengo wa kudziwitsa
chabwinio ndi choyipa musadye, pakuti tsiku limene mudzadya
mudzafa." |
“Pakuti tchimo lili ndi dipo lake—imfa; koma
mphatso ya ulele ya
Mulungu ndi moyo wosatha mu ubale ndi Khristu Yesu Mbuye wathu.”
—Aroman 6:23
|
Yesu ndi mlowa malo wathu
Kuyambira ku Chipangano cha Kale, mulungu amavumbulutsa
kuti mlowamalo
wosalakwa, wosachimwa afe chifukwa cha tchimo la wina. koma
tangowerenga
Aroma 3:23, imene ikuti onse anachimwa. Sipanakhaleko munthu
ochimwa,
kupatulako Yesu Khristu. |
“Khristu
analibe tchimo Christ . . . .”
—2 Akolinto 5:21
|
2. Yesu ananeneratu momveka bwino
kuti adzaphedwa ndi kuuka kwa akufa.
Anawuza yani, ndipo anawawuza chani tikawerenga pansipa?
a. Luka 18:31-33
b. Mateyu 12:38-40
c. Marko 8:31-32a
|
3. Kodi adani a Mulungu akanampeza
Iye olakwa? Luke 23:4
4. Poti Yesu sanachimwepo kapena kuphwanya lamulo lililonse,
chifukwa chani
anaweruzidwa kuti afe. Marko 14:61-64
|
Yesu amadziwa zonse izi zidzachitika. Dzilko lisanalengedwe.,
Anakonza kubwera
ku dziko kufa ngati Mlowa malo wa munthu. Iyi inali njira yokhayo
imene anthu
akanapulumutsidwira kuchoka ku zotsatira za tchimo. Yesu anadziwa
mazunzo
amene amayenera kudutsamo. |
5. Pa zomangidwa zonse, imfa, ndi kukwiriridwa
kwa Yesu, kuyamba pa
Marko 14:43–15:47.
Izi zinalembedwa M'mauthenga Abwino onse anayi. Wolemba wina
aliyense
akutsindika zinthu zosiyana malingana ndi m'mene amawonera.
mu zolemba zina,
timaphunzira kunali ziweruzo zambiri chifukwa kunali kovuta
kuti amuweruze pa
chinthu choyipa. Timaphunziranso zina zimene Yesu ananena
pa mtanda.
Mateyu analemba zinthu kwa zimene anthu a Chiyu amafuna kumva
(Mateyu 27:27–28:15). Analemba za boma kutumiza asilikali
kukatseka manda. Mateyu akufotokoza izo zidzchitika pamene
Yesu anawuka kwa akufa.
Yohane anakamba zambiri za anthu amene Yesu anakamba nawo
atauka kwa akufa.Anafotokoza za boma kutumiza asilikali kukatseka
ndi kulondera manda. (Yohane 19:16-21:25).
Luka analemba ma buku awiri, Uthenga wa Bwino wa Luka ndi
buku la Machitidwe.
Mu ma buku onse. (Luka 23:26–24:52 and Machitidwe 1:1-11),
anafotokoza za m'mene Yesu anatengedwera ku mwamba masiku
makumi anayi atatha chiukireni kwa akufa. |
6. Baibulo limaphnzitsa momveka bwino Yesu anabwera pa dziko ndi kufa m'malo
mwako chifukwa cha machimo ako. poti Yesu anafa chifukwa cha
iwe, yankho lanu lidzakhala lotani?
|
7. Lowezani Machitidwe 4:12.
Lembani Machitidwe 4:12 pano.
........................................................................................................................................................ |
8. Uzani ambuye kuti ndinu ayamika
bwanji kuti Iye amakukondani ndipo
anakuferani pa mtanda kulipira dipo la tchimo lanu. Lembani
pemphero lanu apa. |
Pemphero Lotsekera
Tikuyamikani, Atate wa kumwamba, chifukwa cha chiplumutso munapereka
kwa ife.
Zikomo chifukwa cha chikondi chanu . Tikuthokozani Atate kumwamba,
chifukwa cha
chipulumutso mudapereka kwa ife. zikomo chifukwa cha chikondi chanu
chosasinthasintha pa ife ngat anthu. Tiphunzitseni tichite zonse
mwatiphunzitsa pa moyo
wathu. Tapemphera mu dzina la mphamvu la Yesu Khristu, ame.
|
|