home >>stonecroft>>
>> mavesi
a m'baibulo >> phunziro 5 >> phunziro 6
MULUNGU ALI NGATI CHIYANI? - Mavesi a m'Baibulo - Phunziro 6
Mavesi a m'Baibulo
Deuteronomo 29:29
29Zinsinsi nza Yehova Mulungu wathu; koma zobvumbuluka nza ife
ndi ana athu kosatha, kuti ticite mau onse a cilamulo ici.
Funso #1
Aroma 1:20
20Pakuti cilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka zace
ndizo mphamvu yace yosatha ndi umulungu wace; popeza zazindikirika
ndi zinthu zolengedwa, kuti iwo adzakhale opanda mau akuwiringula;
2 Petro 1: 20-21
20ndi kudziwa ici poyamba, kuti palibe cinenero ca lembo citanthauzidwa
pa cokha, 21pakuti kale lonse cinenero sicinadza ndi cifuniro ca
munthu; koma anthu a Mulungu, ogwidwa ndi Mzimu Woyera, analankhula.
Yohane 1:18
18Kulibe munthu anaona Mulungu nthawi zonse; Mwana wobadwa yekha
wakukhala pa cifuwa ca Atate, Iyeyu anafotokozera.
Macitidwe 1: 8
8Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo
mudzakhala mboni zanga m'Yerusalemu, ndi m'Yudeya lonse, ndi m'Samariya,
ndi kufikira malekezero ace a dziko.
1 Timoteo 1:19
19ndi kukhala naco cikhulupiriro ndi cikumbu mtima cokoma, cimene
ena adacikankha, cikhulupiriro cao cidatayika;
Yohane 5:26
26Pakuti monga Atate ali ndi moyo mwa iye yekha, momwemonso anapatsa
kwa Mwana kukhala ndi moyo mwa iye yekha;
Cibvumbulutso 4:11
11Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero
ndi ulemu ndi mphamvu; cifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa cifuniro
canu zinakhala, nizinalengedwa.
Funso #2
1 Yohane 4:16
16Ndipo ife tazindikira, ndipo takhulupirira cikondico Mulungu ali
naco pa ife. Mulungu ndiye cikondi, ndipo iye amene akhala m'cikondi
akhala mwa Mulungu, ndipo Mulungu akhala mwa iye.
Masalmo 107: 1
1Yamikani Yehova pakuti Iye ndiye wabwino; Pakuti cifundo cace ncosatha.
Masalmo 86:15
15Koma Inu, Ambuye, ndinu Mulungu wansoni ndi wacisomo, Wosapsa
mtima msanga, ndi wocurukira cifundo ndi coonadi.
2 Petro 3:15
15Koma Inu, Ambuye, ndinu Mulungu wansoni ndi wacisomo, Wosapsa
mtima msanga, ndi wocurukira cifundo ndi coonadi.
Mateyu 6: 14
14Pakuti ngati mukhululukira anthu zolakwa zao adzakhululukira inunso
Atate wanu wa Kumwamba.
Mateyu 11:29
29Senzani gori langa, ndipo phunzirani kwa Ine; cifukwa ndiri wofatsa
ndi wodzicepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.
Afilipi 4: 7
7Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana cidziwitso conse, udzasunga
mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.
Funso #3
1 Petro 1:16
16popeza kwalembedwa, Muzikhala oyera mtima, pakuti Ine ndine woyera
mtima.
Ahebri 12:14
14Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi ciyeretso cimene, akapanda
ici, palibe mmodzi adzaona Ambuye:
Funso #5
Yohane 13: 34-35
34Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzace;
monga ndakonda Inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzace. 35 Mwa
ici adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli naco
cikondano wina ndi mnzace.
Yohane 14: 15
15Ngati mukonda Ine, sungani malamulo anga.
Aroma 12: 1
1Cifukwa cace ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu,
kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa,
Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.
Aroma 12: 2
2Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika,
mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire cimene ciri cifuno
ca Mulungu, cabwino, ndi cokondweretsa, ndi cangwiro.
1 Atesalonika 4: 3
3Pakuti ici ndi cifuniro ca Mulungu, ciyeretso canu, kuti mudzipatule
kudama;
1 Atesalonika 5: 16-18
16Kondwerani nthawi zonse; 17Pempherani kosaleka; 18M'zonse yamikani;
pakuti ici ndi cifuniro ca Mulungu ca kwa inu, mwa Kristu
Masalmo 25: 4-5
4Mundidziwitse njira zanu, Yehova; Mundiphunzitse mayendedwe anu.
5Munditsogolere m'coonadi canu, ndipo mundiphunzitse; Pakuti Inu
ndinu Mulungu wa cipulumutso canga;
Inu ndikuyembekezerani tsiku lonseli.
Funso #7
Yesaya 43: 7
7yense wochedwa dzina langa, amene ndinamlenga cifukwa ca ulemerero
wanga; ndinamuumba iye; inde, ndinampanga iye.
Yohane 15: 8
8Mwa ici alemekezedwa Atate wanga, kuti mubale cipatso cambiri;
ndipo mudzakhala akuphunzira anga.
1 Petro 4:11
11akalankhula wina, alankhule ngati manenedwe a Mulungu; wina akatumikira,
acite ngati mu mphamvu imene Mulungu ampatsa, kuti m'zonse Mulungu
alemekezedwe mwa Yesu Kristu, amene ali nao ulemerero ndi mphamvu
ku nthawi za nthawi. Amen.
Masalmo 16:11
11Mudzandidziwitsa njira ya moyo: Pankhope panu pali cimwemwe cokwanira;
M'dzanja lanu lamanja muli zokondweretsa zomka muyaya.
Kuwerenga Baibulo kwa Mlungu ndi Mlungu
Marko 12: 28-31
28Ndipo anadza mmodzi wa alembi, namva iwo alikufunsana pamodzi,
ndipo pakudziwa kuti anawayankha bwino, anamfunsa Iye, Lamulo la
m'tsogolo la onse ndi liti? 29Yesu anayankha, kuti, La m'tsogolo
ndili, Mvera, Israyeli; Ambuye Mulungu wathu, Ambuye ndiye mmodzi;
30ndipouzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo
wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu yako yonse. 31Laciwiri
ndi ili, Uzikonda mnzako monga udzikonda mwini. Palibe lamulo lina
lakuposa awa.
Mateyu 4:10
10Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Coka Satana, pakuti kwalembedwa,
Ambuye Mulungu wako udzamgwadira, Ndipo Iye yekha yekha udzamlambira.
Mateyu 12:50
50Pakuti 6 ali yense amene adzacita cifuniro ca Atate wanga wa Kumwamba,
yemweyo ndiye mbale wanga, ndi mlongo wanga, ndi amai wanga.
Yohane 14:23
23Yesu anayankha nati kwa iye, Ngati wina akonda Ine, adzasunga
mau anga; ndipo Atate wanga adzamkonda, ndipo tidzadza kwa iye,
ndipo tidzayesa kwa iye mokhalamo.
Afilipi 1: 9-11
9Ndipo ici ndipempha, kuti cikondi canu cisefukire cionjezere, m'cidziwitso,
ndi kuzindikira konse; 10kuti mukayese inu zinthu zosiyana; kuti
mukakhale a mtima woona ndi wosalakwa, kufikira tsiku la Kristu;
11odzala nacocipatso ca cilungamo cimene ciri mwa Yesu Kristu, kucitira
Mulungu ulemerero ndi ciyamiko.
1 Akorinto 10:31
31Cifukwa cace 2 mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale
mucita kanthu kena, citani zonse ku ulemerero wa Mulungu.
1 Mbiri 16: 23-29
23Myimbireni Yehova, inu dziko lonse lapansi, Lalikirani cipulumutso
cace tsiku ndi tsiku, 24Fotokozerani ulemerero wace mwa amitundu,
Zodabwiza zace mwa mitundu yonse ya anthu.
25Pakuti Yehova ali wamkuru, nayenera kulemekezedwa kwakukulu; Ayenera
amuope koposa milungu yonse.
26Pakuti milungu ya mitundu ya anthu ndiyo mafano; Koma Yehova analenga
zakumwamba.
27Pamaso pace pali ulemu ndi ukulu, M'malo mwace muli mphamvu ndi
cimwemwe.
28Mcitireni Yehova, inu mafuko a mitundu ya anthu, Mcitireni Yehova
ulemerero ndi mphamvu.
29Mcitireni Yehova ulemerero wa dzina lace; Bwerani naco copereka,
ndipo fikani pamaso pace; Lambirani Yehova m'ciyero cokometsetsa,
Akolose 3: 1-10
1Cifukwa cace ngati munaukitsidwa pamodzi ndi Kristu, funani zakumwamba,
kumene kuli Kristu wokhala pa dzanja lamanja la Mulungu. 2Lingalirani
zakumwamba osati za padziko ai.
3Pakuti munafa, ndipo moyo wanu wabisika pamodzi ndi Kristu mwa
Mulungu, 4Pamene Kristu adzaoneka, ndiye moyo wathu, pamenepo inunso
mudzaonekera pamodzi ndi iye m'ulemerero.
5Cifukwa cace fetsani ziwalozo ziri padziko; dama, cidetso, cifunitso
ca manyazi, cilakolako coipa, nelicisiriro, cimene ciri kupembedza
mafano;6cifukwa ca izi zomwe ukudza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera;7zimene
munayendamo inunso kale, pamene munakhala ndi moyo wanu m'menemo,
8Koma tsopano tayani inunso zonsezi: mkwiyo, kupsa mtima, dumbo,
mwano, zonyansa zoturuka m'kamwa mwanu: 9musamanamizana wina ndi
mnzace; popeza mudabvula munthu wakale pamodzi ndi nchito zace,10ndipo
munabvala watsopano, amene alikukonzekawatsopano, kuti akhale naco
cizindikiritso, mousa mwa cifaniziro ca iye amene anamlenga iye;
Funso #8
Haleluya!
Lemekezani Mulungu m’malo ake oyera;
Mulemekezeni mthambo la mphamvu yake.
Mlemekezeni chifukwa cha ntchito zake zolimba;
Mlemekezeni monga mwa ukulu wake wa unyinji!
Zonse zakupuma zilemekeze Yehova.
Haleluya!
—Masalimo 150:1-2, 6
|