home >>stonecroft>>
>> mavesi
a m'baibulo >> phunziro 1 >> phunziro 2
MULUNGU ALI NGATI CHIYANI? - Mavesi a m'Baibulo - Phunziro 2
Mavesi a m'Baibulo
Kuwerenga Baibulo kwa Mlungu ndi Mlungu
1 Akorinto 1: 9
9Mulungu ali, wokhulupirika amene munaitanidwa mwa iye, ku ciyanjano
ca Mwana wace Yesu Kristu, Ambuye wathu.
Aroma 16:27
27kwa Mulungu wanzeru Yekha Yekha, mwa Yesu Kristu, kwa Yemweyo
ukhale ulemerero ku nthawi zonse. Amen.
Luka 1:37
37Cifukwa 1 palibe mau amodzi akucokera kwa Mulungu adzakhala opanda
mphamvu.
Yohane 3:16
16Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana
wace wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike, koma
akhale nao moyo wosatha.
Numeri 23:19
19Mulungu sindiye munthu, kuti aname; Kapena mwana wa munthu, kuti
aleke; Kodi anena, osacita?
Cibvumbulutso 15: 3-4
3Ndipo ayimba nyimbo ya Mose kapolo wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa,
nanena, Nchito zanu nzazikuru ndi zozizwitsa, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse;
njira zanu nzolungama ndi zoona, Mfumu Inu ya nthawi zosatha. 4Ndani
adzakhala wosaopa ndi wosalemekeza dzina lanu Ambuye? Cifukwa Inu
nokha muli woyera; cifukwa mitundu yonse idzadza nidzalambira pamaso
panu, popeza zolungama zanu zidaonetsedwa.
Cibvumbulutso 1: 8
8Ine ndine Alefa ndi Omega, ati Ambuye Mulungu, amene ali, amene
adali, ndi amene alinkudza, Wamphamvuyonse.
Akolose 1: 15-16
15amene ali fanizo la Mulungu wosaonekayo, wobadwa woyamba wa cilengedwe
conse; 16pakuti mwa iye, zinalengedwa zonse za m'mwamba, ndi za
padziko, zooneka ndi zosaonekazo, kapena mipando yacifumu, kapena
maufumu, kapena maukulu, kapena maulamuliro; zinthu zonse zinalengedwa
mwa iye ndi kwa iye.
Funso #2
Yohane 4:24
24Mulungu ndiye mzimu; ndipo omlambira iye ayenera kumlambira mumzimu
ndi m'coonadi.
Mulungu wathu ndi Zopanda Malire
1 Mafumu 8 : 27
27Kodi Mulungu adzakhala ndithu pa dziko lapansi? Taonani, thambo
ndi m'Mwambamwamba zicepa kukulandirani, koposa kotani nanga nyumba
iyi ndaimangayi.
Yobu 11 : 7-9
7Kodi ukhoza kupeza Mulungu mwa kufunafuna?
Ukhoza kupeza Wamphamvuyonse motsindika?
8Kumpeza kutalika ngati kumwamba, ungacitenji?
Kuzama ngati kumanda, ungadziwenji?
9Muyeso wace utalikira utali wace wa dziko lapansi,
Citando cace ciposa ca nyanja.
Mulungu sitingathe kuzimvetsa
Yobu 37 : 5
5Mulungu agunda modabwitsa ndi mau ace, acita zazikuru osazidziwa
ife.
Isaiah 55 : 8-9
8Pakuti maganizo anga sali maganizo anu, ngakhale njira zanu siziri
njira zanga, ati Yehova. 9Pakuti monga kumwamba kuli kutari ndi
dziko lapansi, momwemo njira zanga ziri zazitari kupambana njira
zanu, ndi maganizo anga kupambana maganizo anu.
Aroma 11 : 33-36
33Ha! kuya kwace kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziwa kwace
kwa Mulungu! 4 Osasanthulikadi maweruzo ace, ndi njira zace nzosalondoleka!
34Pakuti 5 anadziwitsa ndani mtima wace wa Ambuye? Kapena anakhala
mphungu wace ndani? 35Ndipo 6 anayamba ndani kumpatsa iye, ndipo
adzambwezeranso? 36Cifukwa 7 zinthu zonse zicokera kwa iye, zicitika
mwa iye, ndi kufikira kwa iye. 8 K wa Iyeyo ukhale ulemerero ku
nthawi zonse. Amen.
Funso #3
1 Yohane 4: 8
8iye wosakonda sazindikira Mulungu; cifukwa Mulungu ndiye cikondi.
2 Atesalonika 3: 3
3Koma Ambuye ali wokhulupirika amene adzakukhazikitsani inu, nadzakudikirirani
kuletsa woipayo;
Yakobo 1:17
17Mphatso iri yonse yabwino, ndi cininkho ciri conse cangwiro zicokera
Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe cisanduliko,
kapena mthunzi wa citembenukiro.
Marko 10:18
18Ndipo Yesu anati kwa iye, Undicha Ine wabwino bwanji? palibe wabwino
koma mmodzi, ndiye Mulungu.
Ahebri 1: 8
8Koma ponena za Mwana, ati,
Mpando wacifumu wanu, Mulungu, ufikira nthawi za nthawi; ndipo ndodo
yacifumu yoongoka ndiyo ndodo ya ufumu wanu.
Luka 1:78
78Cifukwa ca mtima wacifundo wa Mulungu wathu.
M'menemo mbanda kuca wa kumwamba udzaticezera ife;
1 Petro 1: 15-16
15komatu monga iye wakuitana inu ali woyera mtima, khaiani inunso
oyera mtima m'makhalidwe anu onse; 16popeza kwalembedwa, Muzikhala
oyera mtima, pakuti Ine ndine woyera mtima.
Malingaliro a Mulungu
Mulungu ndiye chikondi
1 Yohane 4: 7-16
7Okondedwa, tikondane wins ndi mnzace: cifukwa kuti cikond cicokera
kwa Mulungu, ndipo yense amene akonda, abadwa kucokera kwa Mulungu,
namzindikira Mulungu, 8iye wosakonda sazindikira Mulungu; cifukwa
Mulungu ndiye cikondi. 9Umo cidaoneka cikondi ca Mulungu mwa ife,
kuti Mulungu anamtuma Mwana wace wobadwa yekha alowe m'dziko lapansi,
kuti tikhale ndi moyo mwa iye.
10Umo muli cikondi, sikuti ife tinakonda Mulungu, koma kuti iye
anatikonda ife, ndipo anatuma Mwana wace akhale ciombolo cifukwa
ca macime athu. 11Okondedwa, ngati Mulungu anatikonda ife kotero,
ffenso tiyenera kukondana wina ndi mnzaceo 12Palibe munthu adamuona
Mulungu nthawi iri yonse; tikakondana wina ndi mnzace, Mulungu akhala
mwa ife, ndi cikondi cace cikhala cangwiro mwa ife; 13m'menemo tizindikira
kuti tikhala mwa iye, ndi iye mwa ife, cifukwa anatipatsako Mzimu
wace. 14Ndipo ife tapenyera, ndipo ticita umboni kuti Atate anatuma
Mwana akhale Mpulumutsi wa dziko lapansi. 15Iye amene adzabvomereza
kuti Yesu ali Mwana wa Mulungu, Mulungu akhala mwa iye, ndi iye
mwa Mulungu. 16Ndipo ife tazindikira, ndipo takhulupirira cikondico
Mulungu ali naco pa ife. Mulungu ndiye cikondi, ndipo iye amene
akhala m'cikondi akhala mwa Mulungu, ndipo Mulungu akhala mwa iye.
Aefeso 2: 4-5
4koma Mulungu, wolemera cifundo, cifukwa ca cikondi cace cacikuru
cimene anatikonda naco, 5tingakhale tinali akufa m'zolakwa zathu,
anatipatsa moyo pamodzi ndi Kristu (muli opulumutsidwa ndi cisomo),
Mulungu ndi wokhulupirika
Deuteronomo 7: 9
9Cifukwa cace dziwani kuti Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu; ndiye
Mulungu wokhulupirika, wakusunga cipangano ndi cifundo ndi iwo akumkonda
ndi kusunga malamulo ace, kufikira mibadwo zikwi.
Masalmo 92: 1-2
1Nkokoma kuyamika Yehova, ndi kuyimbira nyimbo dzina lanu, Wam'mwambamwamba
Inu: 2Kuonetsera cifundo canu mamawa, Ndi cikhulupiriko canu usiku
uli wonse.
Mulungu sasintha
Malaki 3: 6
6Pakuti Ine Yehova sindisinthika, cifukwa cace inu ana a Yakobo
simunathedwa.
Mulungu ndi wabwino
Masalmo 107: 1
1Yamikani Yehova pakuti Iye ndiye wabwino; Pakuti cifundo cace ncosatha.
Mulungu basi
Deuteronomo 32: 4
4Thanthwe, nchito yace ndi yangwiro; Pakuti njira zace zonse ndi
ciweruzo;
Mulungu wokhulupirika ndi wopanda cisalungamo; Iye ndiye wolungama
ndi wolunjika,
Mulungu ndi wachifundo
2 Akorinto 1: 3
3Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu, Atate
wa zifundo ndi Mulungu wa citonthozo conse,
Mulungu ndi woyera
1 Samueli 2: 2
2Palibe wina woyera ngati Yehova; Palibe wina koma Inu nokha; Palibenso
thanthwe longa Mulungu wathu.
Masalmo 99: 9
9Mkwezeni Yehova Mulungu wathu, Ndipo gwadirani pa phiri lace loyera;
Pakuti Yehova Mulungu wathu ndiye woyera.
Funso #4
1 Petro 1: 13-16
13Mwa ici, podzimanga m'cuuno, kunena za mtima wanu, mukhale odzisunga,
nimuyembekeze konse konse cisomo cirikutengedwa kudza naco kwa inu
m'bvumbulutso la Yesu Kristu; 14monga ana omvera osadzifanizitsanso
ndi zilakolako zakale, pokhala osadziwa inu; 15komatu monga iye
wakuitana inu ali woyera mtima, khaiani inunso oyera mtima m'makhalidwe
anu onse; 16popeza kwalembedwa, Muzikhala oyera mtima, pakuti Ine
ndine woyera mtima.
1 Akorinto 1:30
30Koma kwa iye muli inu mwa Kristu Yesu, 7 amene anayesedwa kwa
ife nzeru ya kwa Mulungu, ndi cilungamo ndi ciyeretso ndi ciombolo;
|