Project Hope     home >>stonecroft>> kodi mulungu ndi wotani? >> mavesi a m'baibulo >> phunziro 1
MULUNGU ALI NGATI CHIYANI? - Mavesi a m'Baibulo - Phunziro 1
Women's Empowerment Program
Sports Bible Club
Living Water Bible Club

Mavesi a m'Baibulo

Mulungu ndi ...

Funso #1

Ahebri 11: 6
6koma wopanda cikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna iye.

GOD IS CREATOR

Funso #2

Nehemiya 9: 6
6Inu ndinu Yehova, nokhanu; mwalenga thambo, kumwambamwamba, ndi khamu lao lonse, dziko lapansi, ndi zonse ziri pomwepo, nyanja ndi zonse ziri m'mwemo, ndi Inu muzisunga zamoyo zonsezi, ndi khamu la kumwamba lilambira Inu.

Akolose 1: 15-16
15amene ali fanizo la Mulungu wosaonekayo, wobadwa woyamba wa cilengedwe conse; 16pakuti mwa iye, zinalengedwa zonse za m'mwamba, ndi za padziko, zooneka ndi zosaonekazo, kapena mipando yacifumu, kapena maufumu, kapena maukulu, kapena maulamuliro; zinthu zonse zinalengedwa mwa iye ndi kwa iye.

GOD IS ETERNAL

Funso #3

Masalmo 102: 12, 25-27
12Koma Inu, Yehova, mukhalabe ku nthawi yonse; Ndi cikumbukilo canu ku mibadwo mibadwo.
25Munakhazika dziko lapansi kalelo; Ndipo zakumwamba ndizo nchito ya manja anu.
26Zidzatha izi, koma Inu mukhala: Inde, zidzatha zonse ngati cabvala;
Mudzazisintha ngati maraya, ndipo zidzasinthika: 27Koma Inu ndinu yemweyo, Ndi zaka zanu sizifikira kutha.

ONLY ONE GOD

Funso #4

Yesaya 44: 6
6Atero Yehova, Mfumu ya Israyeli ndi Mombolo wace, Yehova wa makamu, Ine ndiri woyamba ndi womariza, ndi popanda Ine palibenso Mulungu.

Yesaya 45: 5
5Ine ndiri Yehova, ndipo palibe winanso; popanda Ine palibe Mulungu; ndidzakumanga m'cuuno, ngakhale sunandidziwa;

Funso #5

Mika 5: 2
2Koma iwe, Betelehemu Efrata, ndiwe wamng'ono kuti ukhale mwa zikwi za Yuda, mwa iwe mudzanditurukira wina wakudzakhala woweruza m'Israyeli; maturukiro ace ndiwo a kale lomwe, kuyambira nthawi yosayamba.

Mateyu 2: 4-6
4Ndipo pamene anasonkhanitsa ansembe akuru onse ndi alembi a anthu, anafunsira iwo, Adzabadwira kuti Kristuyo? 5Ndipo anamuuza iye, M'Betelehemu wa Yudeya; cifukwa kunalembedwa kotere ndi mneneri, kuti,
6Ndipo iwe: Betelehemu, dziko la Yudeya, Sukhala konse wamng'onong'ono mwa akuru a Yudeya.
Pakuti Wotsogolera adzacokera mwaiwe, Amene adzaweta anthu anga Aisrayeli.'

1 Samueli 16: 1
1Ndipo Yehova ananena ndi Samueli, Iwe ukuti ulire cifukwa ca Sauli nthawi yotani, popeza Ine ndinamkana kuti asakhale mfumu ya Israyeli? Dzaza nyanga yako ndi mafuta, numuke, ndidzakutumiza kwa Jese wa ku Betelehemu; pakuti ndinadzionera mfumu pakati pa ana ace.

Funso #6

Masalmo 22:18
18Agawana zobvala zanga, Nalota maere pa malaya anga,

Yohane 19: 23-24
23Pamenepo asilikari, m'mene adapacika Yesu, anatenga zobvala zace, nadula panai, natenga wina cina, wina cina, ndiponso maraya; koma maraya anaombedwa monsemo kuyambira pamwamba pace, analibe msoko.24Cifukwa cace anati wina kwa mnzace, Tisang'ambe awa, koma ticite maere, awa akhale a yani; kuti lembo likwaniridwe limene linena, Anagawana zobvala zanga mwa iwo okha, ndi pa maraya anga anacitira maere. Ndipo asilikari anacita izi.

Funso #7

7. Luka 24: 27, 44
27Ndipo anayamba kwa Mose, ndi kwa aneneri onse, nawatanthauzira iwo m'malembo onse zinthu za iye yekha.
44Ndipo anati kwa iwo, 5 Awa ndi mauwo ndinalankhula nanu, paja ndinakhala ndi inu, kuti ziyenera kukwanitsidwa zonse zolembedwa za Ine m'cilamulo ca 6 Mose, ndi aneneri, ndi masalmo.

Funso #8

2 Timoteo 3:16
16Lemba liri lonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa ciphunzitso, citsutsano, cikonzero, cilangizo ca m'cilungamo:

Ahebri 11: 6
6koma wopanda cikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna iye.

Nehemiya 9: 6
6Inu ndinu Yehova, nokhanu; mwalenga thambo, kumwambamwamba, ndi khamu lao lonse, dziko lapansi, ndi zonse ziri pomwepo, nyanja ndi zonse ziri m'mwemo, ndi Inu muzisunga zamoyo zonsezi, ndi khamu la kumwamba lilambira Inu.

Luka 24:27
27Ndipo anayamba kwa Mose, ndi kwa aneneri onse, nawatanthauzira iwo m'malembo onse zinthu za iye yekha.

Pemphero
Ambuye Mulungu. Ndayamba kuwona ukulu wanu. Ndithandizeni kuzindikira chimenechi, ngakhale kuti sindingakudziwitsitseni, Inu mukufunitsitsa nditakudziwani. Pitirizani kundiphunzitsa ndi kundithandiza kusunga choonadi chimene ndikuwerenga lero. Mudzina la Yesu ndapemphera. Amen

 
 

 

MULUNGU ALI NGATI CHIYANI?

Mavesi a m'Baibulo

 
 
Copyright ©  2023 www.UnitedCaribbean.com. All rights reserved. Disclaimer Click to Contact us