home >>stonecroft>>
>> mavesi
a m'baibulo >> phunziro 2 >> phunziro 3
MULUNGU ALI NGATI CHIYANI? - Mavesi a m'Baibulo - Phunziro 3
Mavesi a m'Baibulo
Kuwerenga Baibulo kwa Mlungu ndi Mlungu
Masalmo 34:18
18Yehova ali pafupi ndi iwo a mtimawosweka,
Apulumutsa iwo a mzimu wolapadi,
Masalmo 103: 19
19Yehova anakhazika mpando wacifumu wace Kumwamba;
Ndi ufumu wace ucita mphamvu ponsepo,
Masalmo 145: 18
18Yehova ali pafupi ndi onse akuitanira kwa Iye,
Onse akuitanira kwa Iye m'coonadi.
Yesaya 37:16
16Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, amene mukhala pa akerubi,
Inu ndinu Mulungu, Inu nokha, wa maufumu onse a dziko lapansi, Inu
munalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Yesaya 40:22
22Ndi Iye amene akhala pamwamba pa malekerezo a dziko lapansi, ndipo
okhalamo akunga ziwala; amene afutukula thambo ngati cinsaru, naliyala
monga hema wakukhalamo;
Yesaya 43: 2
2Pamene udulitsa pamadzi ndiri pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje
sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsya; ngakhale lawi silidzakutentha.
Yeremiya 23:23
23Kodi ndine Mulungu wa pafupi, ati Yehova, si Mulungu wa patari?
Funso #1
1 Timothée 6:16
16amene iye yekha ali nao moyo wosatha, wakukhala m'kuunika kosakhozeka
kufikako; amene munthu sanamuona, kapena sakhoza kumuona; kwa iye
kukhale ulemu ndi mphamvu yosatha. Amen.
Funso #2
Macitidwe 17: 24-25
24Mulungu amene analenga dziko lapansi ndi zonse ziri momwemo, Iyeyo,
ndiye mwini kumwamba ndi dziko lapansi, sakhala m'nyumba zakacisi
zomangidwa ndi manja;25satumikidwa ndi manja a anthu, monga wosowa
kanthu, popeza iye mwini apatsa zonse moyo ndi mpweya ndi zinthu
zonse;
1 Mafumu 8:27
27Kodi Mulungu adzakhala ndithu pa dziko lapansi? Taonani, thambo
ndi m'Mwambamwamba zicepa kukulandirani, koposa kotani nanga nyumba
iyi ndaimangayi.
Funso #3
1 Yohane 4:12
12Palibe munthu adamuona Mulungu nthawi iri yonse; tikakondana wina
ndi mnzace, Mulungu akhala mwa ife, ndi cikondi cace cikhala cangwiro
mwa ife;
Yesaya 57:15
15Pakuti atero Iye amene ali wamtari wotukulidwa, amene akhala mwacikhalire,
amene dzina lace ndiye Woyera, Ndikhala m'malo atari ndi oyera,
pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzicepetsa, kutsitsimutsa
mzimu wa odzicepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.
Yeremiya 23:24
24Kodi munthu angathe kubisala mobisika kuti ndisamuone iye? ati
Yehova. Kodi Ine sindidzala kumwamba ndi dziko lapansi? ati Yehova.
Funso #4
Aroma 1:20
20Pakuti cilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka zace
ndizo mphamvu yace yosatha ndi umulungu wace; popeza zazindikirika
ndi zinthu zolengedwa, kuti iwo adzakhale opanda mau akuwiringula;
Aroma 2:15
15popeza iwo aonetsa nchito ya lamulolo yolembedwa m'mitima yao,
ndipo cikumbu mtima cao cicitiranso umboni pamodzi nao, ndipo maganizo
ao wina ndi mnzace anenezana kapena akanirana;
Mulungu nafe
Funso #6
Eksodo 33:14
14Ndipo anati, Nkhope yanga idzamuka nawe, ndipo ndidzakupumuza.
Masalmo 16: 11
11Mudzandidziwitsa njira ya moyo: Pankhope panu pali cimwemwe cokwanira;
M'dzanja lanu lamanja muli zokondweretsa zomka muyaya.
Masalmo 21: 6
6Pakuti mumuikira madalitso ku nthawi zonse;
Mumkondweretsa ndi cimwemwe pankhope panu.
Masalmo 31:20
20Pobisalira pamaso panu mudzawabisa kwa ciwembu ca munthu:
Mudzawabisa iwo mumsasa kuti muwalanditse pa kutetana kwa malilime.
Masalmo 89:15
15Odala anthu odziwa liu la lipenga;
Ayenda m'kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.
Masalmo 139: 7-12
7Ndidzapita kuti kuzembera mzimu wanu?
Kapena ndidzathawira kuti kuzembera nkhope yanu?
8Ndikakwera kumka kumwamba, muli komweko; Kapena ndikadziyalira
ku Gehena, taonani, muli komweko.
9Ndikadzitengera mapiko a mbanda kuca, Ndi kukhala ku malekezero
a nyanja;
10Kungakhale komweko dzanja lanu lidzanditsogolera, Nilidzandigwira
dzanja lanu lamanja.
11Ndipo ndikati, Koma mdima undiphimbe, Ndi kuunika kondizinga kukhale
usiku:
12Ungakhale mdima sudetsa pamaso panu, Koma usiku uwala ngati usana:
Mdima ukunga kuunika.
Yohane 14: 3
3Ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso, ndipo
ndidzalandira inu kwa Ine ndekha; kuti kumene kuli Ineko, mukakhale
inunso.
Genesis 2: 7
7Ndipo Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira
mpweya wa moyo m'mphuno mwace; munthuyo nakhala wamoyo.
Deuteronomo 30:19
19Ndicititsa mboni lero kumwamba ndi dziko lapansi zitsutse inu;
ndaika pamaso panu moyo ndi imfa, mdalitso ndi temberero; potero,
sankhani moyo, kuti mukhale ndi moyo, inu ndi mbeu zanu;
1 Yohane 2: 24-25
24Koma inu, cimene munacimva kuyambira paciyambi cikhale mwa Inu,
6 Ngari cikhala mwa inu cimene mudacimva kuyambira paciyambi, inunso
mudzakhalabe mwa Mwana, ndi mwa Atate. 25Ndipo 7 ili ndi lonjezano
iye anatiloniezera ife, ndiwo moyo wosatha.
|