Project Hope     home >>stonecroft>> >> mavesi a m'baibulo >> phunziro 3 >> phunziro 4
MULUNGU ALI NGATI CHIYANI? - Mavesi a m'Baibulo - Phunziro 4
Women's Empowerment Program
Sports Bible Club
Living Water Bible Club

Mavesi a m'Baibulo

Kuwerenga Baibulo kwa Mlungu ndi Mlungu

Yohane 6:37
37Cinthu conse cimene anandipatsa Ine Atate cidzadza kwa Ine; ndipo wakudza kwa Ine sindidzamtaya iye kunja.

Yobu 34:21
21Pakuti maso ace ali pa njira ya munthu ali yense,
Napenya moponda mwace monse.

Masalmo 139: 1-4
1Munandisanthula, Yehova, nimundidziwa.
2Inumudziwakukhalakwangandi kuuka kwanga, Muzindikira lingaliro langa muli kutali.
3Muyesa popita ine ndi pogona ine, Ndi njira zanga zonse muzolowerana nazo.
4Pakuti asanafike mau pa lilime langa, Taonani, Yehova, muwadziwa onse.

Miyambi 15: 3, 11
3Maso a Yehova ali ponseponse, Nayang'anira oipa ndi abwino.
11Kumanda ndi kucionongeko kuli pamaso pa Yehova; Koposa kotani nanga mitima ya ana a anthu?

2 Mafumu 16: 9
9Nimmvera mfumu ya Asuri, nikwera kumka ku Damasiko mfumu ya Asuri, niulanda, nipita nao anthu ace andende ku Kiri, nimupha Rezini.

Ahebri 13: 5
5Mtima wanu ukhale wosakonda cuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.

Jean 14:21
21Iye wakukhala nao malamulo anga, ndi kuwasunga, iyeyu ndiye wondikonda Ine; koma wondikonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga, ndipo line ndidzamkonda, ndipo ndidzadzionetsandekha kwa iye.

Funso #1

Mateyu 18: 12-14
12Nanga muyesa bwanji? ngati munthu ali nazo nkhosa makumi khumi, ndipo ikasokera imodzi ya izo, kodi saleka zija makumi asanu ndi anai mphambu manu ndi zinai, napita kumapiri, kukafuna yosokerayo? 13Ndimo akaipeza, indedi ndinena kwa inu, akondwera nayo koposa ndi makumi asanu ndi anai mphambu zisanu ndi zinai zosasokera. 14Comweco siciri cifuniro ca Atate wanu wa Kumwamba kuti mmodzi wa ang'ono awa atayike.

Funso #2

Aefeso 2:10
10Pakuti ife ndife cipango cace, olengedwa mwa Kristu Yesu, kucita nchito zabwino, zimene Mulungu anazipangiratu, kuti tikayende m'menemo.

Masalmo 100: 3
3Dziwani kuti Yehova ndiye Mulungu; Iyeyu anatilenga, ndipo ife ndife ace; Ndife anthu ace ndi nkhosa za pabusa pace.

Funso #4

Masalmo 139: 1-18
1Munandisanthula, Yehova, nimundidziwa.
2Inumudziwakukhalakwangandi kuuka kwanga, Muzindikira lingaliro langa muli kutali.
3Muyesa popita ine ndi pogona ine, Ndi njira zanga zonse muzolowerana nazo.
4Pakuti asanafike mau pa lilime langa, Taonani, Yehova, muwadziwa onse.
5Munandizinga kumbuyo ndi kumaso, Nimunaika dzanja lanu pa ine.
6Kudziwa ici kundilaka ndi kundidabwiza: Kundikhalira patali, sindifikirako.
7Ndidzapita kuti kuzembera mzimu wanu?
Kapena ndidzathawira kuti kuzembera nkhope yanu?
8Ndikakwera kumka kumwamba, muli komweko; Kapena ndikadziyalira ku Gehena, taonani, muli komweko.
9Ndikadzitengera mapiko a mbanda kuca, Ndi kukhala ku malekezero a nyanja;
10Kungakhale komweko dzanja lanu lidzanditsogolera, Nilidzandigwira dzanja lanu lamanja.
11Ndipo ndikati, Koma mdima undiphimbe, Ndi kuunika kondizinga kukhale usiku:
12Ungakhale mdima sudetsa pamaso panu, Koma usiku uwala ngati usana: Mdima ukunga kuunika.
13Pakuti Inu munalenga imso zanga; Munandiumba ndisanabadwe ine.
14Ndikuyamikani cifukwa kuti cipangidwe canga ncoopsa ndi codabwiza; Nchito zanu nzodabwiza; Moyo wanga ucidziwa ici bwino ndithu.
15Thupi langa silinabisikira Inu popangidwa ine mobisika, Poombedwa ine monga m'munsi mwace mwa dziko lapansi.
16Ndisanaumbidwe ine maso anu anandipenya, Ziwalo zanga zonse zinalembedwa m'buku mwanu, Masiku akuti ziumbidwe, Pakalibe cimodzi ca izo.
17Potero, Mulungu, ndiziyesa zolingalira zanu za mtengo wace ndithu!
Mawerengedwe ace ndi ambirimbiri!
18Ndikaziwerenga zicuruka koposa mcenga: Ndikauka ndikhalanso nanu.

Funso #5

Masalmo 139: 23-24
23Mundisanthule, Mulungu, nimudziwe mtima wanga; Mundiyese nimudziwe zolingalira zanga.
24Ndipo mupenye ngati ndiri nao mayendedwe oipa, Nimunditsogolere pa njira yosatha.

Funso #6

Mateyu 6: 25-34
25Cifukwa cace ndinena kwa inu, Musadere nkhawa moyo wanu, cimene mudzadya ndi cimene mudzamwa; kapena thupi lanu, cimene mudzabvala. Kodi moyo suli woposa cakudya, ndi thupi loposa cobvala? 26Yang'anirani mbalame za kumwamba, kuti sizimafesa ai, kapena sizimatema ai, kapena sizimatutira m'nkhokwe; ndipo Atate wanu wa Kumwamba azidyetsa. Nanga inu mulibe kusiyana nazo kuziposa kodi? 27Ndipo ndani wa inu ndi kudera nkhawa angathe kuonjezera pa msinkhu wace mkono umodzi?28Ndipo muderanji nkhawa ndi cobvala? Tapenyetsani maluwa a kuthengo, makulidwe ao; sagwiritsa nchito, kapena sapota: 29koma ndinena kwa inu, kuti angakhale Solomo mu ulemerero wace wonse sanabvala monga limodzi la amenewa. 30Koma ngati Mulungu abveka cotero maudzu a kuthengo, akhala lero, ndi mawa oponyedwa pamoto, nanga si inu kopambana ndithu, inu akukhulupirira pang'ono? 31Cifukwa cace musadere nkhawa, ndi kuti, Tidzadya ciani? kapena, Tidzamwa ciani? kapena, Tidzabvala ciani? 32Pakuti anthu akunja azifunitsa zonse zimenezo; pakuti Atate wanu wa Kumwamba adziwa kuti musowa zonse zimenezo. 33Koma muthange mwafuna Ufumu wace ndi cilungamo cace, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu. 34Cifukwa cace musadere nkhawa za mawa; pakuti mawa adzadzidera nkhawa iwo okha, Zikwanire tsiku zobvuta zace.

1 Petro 5: 6-7
6Potero dzicepetseni pansi pa dzanja la mphamvu lao Mulungu, kuti panthawi yace akakukwezeni; 7ndi kutaya pa iye nkhawa yanu yonse, pakuti iye asamalira inu.

Mateyu 6: 8
8Cifukwa cace inu musafanane nao: pakuti Atate wanu adziwa zomwe muzisowa, inu musanayambe kupempha Iye.

Aroma 8: 28-39
28Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwacitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wace. 29Cifukwa kuti iwo amene iye anawadziwiratu, iwowa anawalamuliratu afanizidwe ndi cifaniziro ca Mwana wace, kuti iye akakhale mwana woyamba wa abale ambiri; 30ndipo amene iye anawalamuliratu, iwo anawaitananso; ndimo iwo amene iye anawaitana, iwowa anawayesanso olungama; ndi iwo amene iye anawayesa olungama, iwowa anawapatsanso olemerero.
31Ndipo tidzatani ndi zinthu izi? Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza ndani?32iye amene sanatimana Mwana wace wa iye yekha, koma anampereka cifukwa ca ife tonse, adzalekeranji kutipatsanso ife zinthu zonse kwaulere pamodzi ndi iye? 33Ndani adzaneneza osankhidwa a Mulungu? 8 Mulungu ndiye ameneawayesa olungama; 349 ndani adzawatsutsa? Kristu Yesu ndiye amene adafera, inde makamaka, ndiye amene adauka kwa akufa, amene akhalanso pa dzanja lamanja la Mulungu, amenenso atipempherera ife.35Adzatisiyanitsa ndani ndi cikondi ca Kristu? nsautso kodi, kapena kupsinjika mtima, kapena kuzunza, kapena njala, kapena usiwa, kapena zoopsya kapena lupanga kodi? 36Monganso kwalembedwa, Cifukwa ca Inu tirikuphedwa dzuwa lonse; Tinayesedwa monga nkhosa zakupha, 37Koma m'zonsezi, ife tilakatu, mwa iye amene anatikonda. 38Pakuti ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu ziripo, ngakhale zinthu zirinkudza, ngakhale zimphamvu, 39ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale colengedwa cina ciri conse, sicingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi cikondi ca Mulungu, cimene ciri mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.

Funso #7

Masalmo 37: 4-5
4Udzikondweretsenso mwa Yehova; Ndipo iye adzakupatsa zokhumba mtima wako.
5Pereka njira yako kwa Yehova; Khulupiriranso Iye, adzacicita.

Miyambi 3: 5-6
5Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, Osacirikizika pa luntha lako; 6Umlemekeze m'njira zako zonse, Ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.

Yeremiya 29:13
13Ndipo mudzandifuna Ine, ndi kundipeza, pamene mundifuna ndi mtima wanu wonse.

Funso #9

Yeremiya 29:11
11Pakuti ndidziwa malingiriro amene ndilingiririra inu, ati Yehova, malingiriro a mtendere, si a coipa, akukupatsani inu adzukulu ndi ciyembekezero.

Funso #10

Aroma 5: 6-9
6Pakuti pamene tinali cikhalire ofok a, pa nyengo yace Kristu anawafera osapembedza. 7Pakuti ndi cibvuto munthu adzafera wina wolungama; pakuti kapena wina adzalimbika mtima kufera munthu wabwino. 8Koma g Mulungu atsimikiza kwa ife cikonai cace ca mwini yekha m'menemo, kuti pokhala ife cikhalire ocimwa, Kristu adatifera ife. 9Ndipo tsono popeza inayesedwa olungama ndi mwazi wace, makamaka ndithu tidzapulumuka mkwiyo wa Mulungu mwa Iyeyo.

Funso #11

Masalmo 147: 5
5Ambuye wathu ndi wamkuru ndi wa mphamvu zambiri; Nzeru yace njosatha.

 

 
 

 

MULUNGU ALI NGATI CHIYANI?

Mavesi a m'Baibulo

 
 
Copyright ©  2023 www.UnitedCaribbean.com. All rights reserved. Disclaimer Click to Contact us