home >>stonecroft>>
mulungu ali ngati chiyani?
>>phunziro 4 >>phunziro 5
Kodi Mulungu ndi wotani? - Phunziro #5
Oyenera kumdziwa Mulungu Ndani?
Pemphero
Atate, ndikufuna kudziwa zambiri za Inu. Ndithandizeni kuti ndimvetse
zinthu zimene ndikuwerenga. Mwandizizwitsa pakuti zolengedwa zonse
ziri pansi panu koma ngankhale ziri choncho mukufuna kuti ine
ndikhalebe bwenzi lanu. Ndapemphera mu dzina la Yesu. Amen.
Mulungu sayembekezera kuti tidziwe zonse za Iye,
koma amafunitsitsa aliyense adziwe zoonadi zake izi:
-
Mulungu ndi m’modzi, amapezeka mu Utatu:
Mulungu Atate, Mwana, ndi Mzimu Woyera
-
Mulungu Atate ndi Mzimu wa Umulungu.
- Yesu Khristu anabwera padziko lapansi mu Umulungu wake kudzakhala
munthu.
- Ngati Munthu, anakhala pano pa dziko lapansi ndi moyo wangwiro.
- Anafera pa mtanda, anayikidwa m’manda ndipo anawuka kwa
akufa.
- Atauka, Anabwelera kumwamba mu thupi lake la ulemelero.
- Mulungu Mzimu Oyera ndi wosaoneka ndi maso, koma ali nafe limodzi
panopo.
Mulungu amatidziwa. Amatidziwa bwino kuposa aliyense. Wakhala
akutidziwa. Funso nkumati – Kodi mumamudziwa Mulungu?
God knows us. He knows us better than anyone
else. He has always know us. the question is - do you know God?
Kuwerenga Baibulo m’sabata
Tsiku liri lonse m’sabata, werengani malo amene mwapatsidwa
m’Baibulo kuti muwerenge ndi kuyankha funso lotsatira:
Yohane 14:21-23
Kodi Mulungu adzadziwululira kwa yani?
Aroma 5:6-9
Ndi chifukwa chiyani Yesu anatifera pamene tinali ochimwa?
1 Timoteo 2:1-6
Ndi ndani amene Yesu akufuna apulumutsidwe?
Yakobo 4:7-10
Kodi Mulungu amafuna kuti titani kuti Iye akhale pafupi nafe?
2 Petro 3:9
Ndi chifukwa chiyani Mulungu akuchedwa kuweruza dzikoli?
Ahebri 11:6
Mukafika pamaso pa Mulungu, kodi muyenera kukhala ndi chikhulupiliro
chotani?
Mateyu 11:27-30
Kodi Mulungu amayitana ndani kuti afike kwa Iye?
* Sankhani ndime imodzi mwa ndime zimene mwawerenga kuchokera mu
Baibulo msabatayi, imene yakugwirani mtima panthawi ino. Ganizirani
tanthauzo la ndime imeneyi kwa inu ndipo kuti mungayigwiritse ntchito
bwanji pa moyo wanu?
1. Kodi Baibulo limati Chiyani za m’mene munthu angamdziwire
Mulungu?
Masalimo 46:10
Masalimo 145:18-19
Yesaya 55:3
Ahebri 10:22
2. Yesu anauza ophunzira ake za m’mene angamudziwire Mulungu.
Werengani Yohane 14:6-7 Ndipo mufotokoze zimene anawawuza.
Mulungu amadziwa kuti ndife ochimwa. Amadziwa kuti sitingadzimasule
tokha ku tchimoli. Pa Aroma 3:20-24 Baibulo limatiuza momwe tingamasukire
ku tchimo.
Liwu lakuti - khulupilira” silikungotanthauza za kuti Yesu
Khristu ndi mwana wa Mulungu, amene anapachichikidwa pantanda chifukwa
cha machimo anu. Mawuwa akutanthauza kuyika mtima wanu wonse ndi
kumudalira Yesuyo pakulapa machimo anu.
Kulapa ndi kusintha njira ndi kulondola Yesu Khristu. Izi zikutanthauza
kuti simuyenera kuyenda njira yanu. Kulapa kumatanthauza kusiya
njira zanu zakale ndi kulondola Mulungu.
Kodi mwalandira mphatso ya Mulungu ya chipulumutso?
Ngati mulibe Yesu m’moyo wanu, lankhulani ndi Mulungu mu
pemphero, lapani machimo anu, pemphani akukhulukireni nakupatsani
moyo wosatha.
Mulungu akukhululukirani chifukwa chikhululukiro komanso moyo wosatha
ndi mphatso zimene Iye akufuna kukupatsani. Mphatso izi sizokuyenerani
koma mukungoyenera kukhulupilira ndi kuzilandira.
3. Werengani mavesi otsatirawa. Kodi tipange chiyani kuti tilandire
mphatso kuchokera kwa Mulungu?
Yohane 6:29
Yohane 5:24
4. Yesu anauza munthu kuti ayenera kubadwanso mwatsopano. Werengani
Yohane 3:1-8 kuti mumve zimene Yesu ananena zakubadwira m’banja
la Mulungu?
Lembani tsiku kapena zaka zanu pamene munamkhulupilira ndi kumulandira
Yesu kukhala Mbuye ndi Mphulumutsi wa moyo wanu.
5. Pamene munkapemphera, kuti Yesu alowe mumtima mwanu, zambiri
zodabwitsa zinachitika. Talembani madalitso amane ndime zotsatilazi
zikutiwululira.
a) Yohane 3:36
b) Yohane 16:24
c) Aroma 4:7-8
d) Aroma 5:1
e) 2 Akorinto 5:17
f) Aefeso 1:13
g) Ahebri 13:5
6. Lembani pemphero lanu kwa Mulungu, kumuthokoza pokudziwani ndi
pokuwonetsani njira ya m’mene mungakhalire pa ubwebnzi ndi
Iye. Mupepmpheni kuti akhale nsanamila yanu nthawi zonse. Pa nthawi
imene mukuphunzira mwa kukambirana, mutha kugawana pemphero lanu
ndi anzanu.Lembani pemphero lanu pano.
Pemphero
Father in Heaven, we thank You for Your gift of salvation. Thank
You for making it possible for us to receive all the blessings You
have for Your children. As we study our last lesson, help us learn
how to live to please You. We pray in Jesus’ name, amen.
Mau a mchipangano chakale
Yeremiya 29:13
Ndipo mudzindifuna Ine ndi kundipeza pamene mundifuna ndi mtima
wanu wonse
Masalimo 46:10
Khalani chete, ndipo dziwani kuti ine ndine Mulungu:
Ndidzabuka mwa amitundu, ndidzabuka padziko lapansi.
Masalimo 145:18-19
Yehova ali pafupi ndi onse akuyitanira kwa Iye,
Onse akuyitanira kwa Iye mchoonadi.
Adzachita chokhumba iwo akumuwopa;
Ndidzamva kufuula kwawo nadzawapulumutsa.
Yesaya 55:3
Tcherani khutu lanu, mudze kwa ine, imvani, mzimu nudzakhala ndi
moyo;………….
Ezekieli 18:32
Pakuti sindikondwera nayo imfa ya wakufayo, ati Ambuye Yehova, chifukwa
bwelerani, nimukhale ndi moyo.
|