home >>stonecroft>>
mulungu ali ngati chiyani?
>>phunziro 1
Kodi Mulungu ndi wotani? - Phunziro #1
Mulungu ali ngati chiyani?
Mulungu Ndi
Mulungu wakhala alipo,
Ndipo adzakhalapobe!
Kupezeka kwake kwa muyaya kumatchulidwa mwamphamvu
mmawu awiri kuti: -Mulungu Ndi.
Mulungu Wamphanvu zonze, opezeka paliponse nthawi
ili yonse, amene amadziwa zonse, ali pano.
Adzakhalapobe, chifukwa - Mulungu Ndi.
“Koma opanda chikhulupiliro sikutheka
kumkondweretsa, Pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupilira
kuti alipo, ndikuti ali obwezera mphotho iwo akumfuna Iye
—Ahebri 11:6
1. Werengani Ahebri 11:6. Ndi liwu liti limene lagwiritsidwa
ntchito pofotokozera kuti Mulungu Ndi?
Mulungu ndi Wolenga
Isanayambike nthawi, kunalibe kathu koma Mulungu yekha mu ukulu
wake analipo. Kunalibe kanthu –kunalibe mlengalenga, kunalibe
dziko, kunalibe dzuwa, kunalibe mwezi ngakhalenso nyenyezi –
kunalibe kathu. Mulungu analankhula ndipo popanda kathu paja panabwera
kanthu. Kulenga zinthu popanda zinthu.
Chikhalire-Mulungu ndi olenga ndipo palibenso wina,
2. Werengani mavesi awa ndipo mufotokoze mmene mukumvera
(Mmmawu anu) choonadi chenicheni chimene mawu amenewa akuphunzitsa.
(Mawu a mchipangano chakale akupezeka pamapeto pa phunziro liri
lonse.)
Nehemiya 9:6
Akolose 1:15-16
Choonadi chenicheni chimene mavesi amenewa akuphunzitsa ndi:
Mulungu ndi wamuyaya
Mawu awiri aku "Mulungu Ndi” akutsimikitsa
kuti Mulungu ndi wa Muyaya. Umuyaya ndiwovuta kumvetsa chifukwa
cha nyengo imene tikukhala. Ndife akapolo a nthawi.
Nthawi imene tinabadwa inalembedwa mkawundula. Ndipo idzakhalaponso
nthawi ya kufa, Zimene tikuchita tili ndi moyo, kuyambira pachiyambi
mpaka pa kumapeto, zimayesedwa ndi nthawi monga zaka, masiku, maora
ndi mphindi. Nthawi zonse timazindikiritsidwa za nthawi imeneyi.
Choncho ndikovuta kuti timvetse zakukhala kunja kwa nthawi.
3. Werengani mavesi awa ndi kufotokoza mmene mukumvera choonadi
checheni chimene mavesiwa akutiphunzitsa.
Masalimo 102:12, 25-27
Mulungu sayendera nthawi. Alibe chiyambi ndipo alibe mathero. Amakhala
mu umuyaya. Sayendera nthawi.
Timakhala mnyengo zitatu - yammbuyo, yatsopano ndi yamtsogolo,
Takhala nthawi yam’mbuyo, tikukhala nthawi yatsopano ndipo
tidzakhala nthawi yamtsogolo, Mulungu analipo chikhalire ndipo adzakhalapo
mpaka kale.
Mulungu m'modzi yekha
4. Werengani mavesi awa ndipo yankhani funso lotsatilari. Kodi
mukukhulupilira kuti kuli Mulungu mmodzi? Perekani chifukwa mmene
mwayankhira.
Yesaya 44:6
Yesaya 45:5
Kodi Baibulo ndi loona?
Mabuku ena a m’baibulo analembedwa ndi aneneri. Awa ndi azitukimiki
amene ankanena uthenga wa Mulungu kwa anthu. Amanena zimene zidzachitike
mtsogolo ngakhale zaka zochuluka mtsogolomo.
Cholinga cha uneneri mu Baibulo nkutidziwitsa kuti Mulungu alipo
ndipo ali ndi cholinga pa dziko lino ngakhalenso anthu. Pakunenera
za anthu, malo, ndi zochitika zaka za mtsogolo, Mulungu amakhala
akutidziwitsa za cholinga chake pa dziko mtsogolomo. Kupherezera
kwa uneneri ndi chitsimikizo kuti Baibulo ndi mawu a Mulungu
5. Baibulo limaonekera kudalirika pakuwona kupherezera kwa uneneri.
Mneneri Mika ananenera za malo obadwira a Ambuye Yesu zaka 700
Ambuye Yesuwo asanabadwe.
Mika 5:2
“Koma iwe, Betelehemu Efrata, ndi iwe wamng’ono kuti
ukhale mwa zikwi za Yuda, mwa iwe mudzanditulukira wina wakudzakhala
woweruza m’Israyeli; maturukiro ace ndiwo a kale lomwe, kuyambira
nthawi yosayamba”
Uneneri uwu unakwaniritsidwa pa Mateyu 2:4-6.
Kodi Ambuye Yesu anabadwira kuti? ……
Munthawi yayikulu mchiyembekezero cha Ambuye Yesu, Maria amakhala
kumpoto kwa Israyeli ku Nazarete. Betelehem anali kum’mwera
kwa Israyeli. Koma boma la a Aroma linalamula kalembera. Aliyense
amayenera kubwelelera kwa makolo ake kukalembetsa. Yosefe ndi Maria
anali ochokera banja la chifumu la Davide omwe kwawo kunali ku Betelehemu
– (1 Samueli 16:1). Malemba anakwaniritsidwa Ambuye Yesu anabadwira
ku Betehemu osati ku Nazarete. Ndi Mulungu yekha amene amapanga
zithu kutheka. Mulunguyo anatheketsadi.
6. Davide ananenera za kupachikidwa kwa Ambuye Yesu zaka
chikwi Ambuye Yesu aasanabadwe.
Mwachitsanzo, Werengani
Masalimo 22:18
“Agawana zovala zanga, Nalota maere pa Malaya anga.”
Uneneriwu unakwaniritsidwa pa Yohane 19:23-24.
Kodi asilikali aja anapanga chiyani?
Uneneri uwu unakwaniritsidwa ndi asilikali a chi Roma amene sanadziwa
nkomwe za uneneri wa Chiyuda. Sanakatha kulumikiza ndi munthu amene
anangompachika kumene. Ndi Mulungu yekha amene anakanenera zimenezi
ndikudziwitsa kuti uneneriwu wakwaniritsidwa.
7. Fotokozani mwachidule zimene Ambuye Yesu ananena zokhudza chipangano
chakale. Luka 24:27, 44
8. Kodi pa 2 Timoteo 3:16 pakuti chiyani za m’mene
Baibulo limatitakasira miyoyo yathu?
9. Kodi mawu akuti Mulungu Ndi akutanthauza chiyani kwa
inuyo pamene mwamaliza phunziro limeneli? …
Pemphero
Ambuye Mulungu. Ndayamba kuwona ukulu wanu. Ndithandizeni kuzindikira
chimenechi, ngakhale kuti sindingakudziwitsitseni, Inu mukufunitsitsa
nditakudziwani. Pitirizani kundiphunzitsa ndi kundithandiza kusunga
choonadi chimene ndikuwerenga lero. Mudzina la Yesu ndapemphera.
Amen
Pemphero
Atate wa muyaya. Ndikukupembedzani. Ndaphunzira kuti mulibe chiyambi
ndiponso mulibe mathero. Ndikuvomereza kuti inu ndi wolenga wamkulu
ndipo palibenso wina. Ndikupempha kuti mundithandize kuganiza bwino
za Inu pamene ndikuwerenga mawu anu. Ndapempha izi kudzera mudzina
la Yesu Khristu. Amen
|