home >>stonecroft>>
mulungu ali ngati chiyani?
>>phunziro 1 >>phunziro 2
Kodi Mulungu ndi wotani? - Phunziro #2
Mulungu ali
ngati chiyani?
Prayer
Eternal Father, I worship
You. I have learned that You had no beginning and will have no end.
I acknowledge You as the great Creator of all that exits. I ask
You to help me think correctly about You as I read Your Word. I
pray in the name of Jesus. Amen
1. Pogwiritsa ntchito mawu anu (Mwachindunji). Fotokozani
za m’mene mukuganizira kapena kuwonera mukamaganiza za Mulungu.
Munene mwachilungamo komanso mwatchutchutchu m’mene mumaganizira
za Mulunguyo. Pakutha pamaphunzirowa, funsoli lifunsidwanso.
Kuwerenga Baibulo sabata ndi sabata
Tsiku lirilonse msabatayi, werengani vesi la lomwe mwapatsidwa
patsiku, mchipangano chatsopano ndipo munene zam’mene mawuwo
akukambira za Muliungu.
1 Akorinto 1:9
Kodi vesi limeneli likunena chiyani za Mulungu? …
Aroma 16:27
Kodi vesi limeneli likumufotokoza bwanji Mulungu?
Luka 1:37
Kodi vesi limeneli likuti chiyani za Mulungu?
Yohane 3:16
Kodi vesi limeneli likufotokoza chiyani za Mulungu?
Numeri 23:19
Ndi ubwino wanji wa Mulungu umene ukufotokozedwa pamenepa?
Chivumbulutso 15:3-4
Ndi ubwinonso wanji wa Mulungu umene ukufotokozedwa?
Chivumbulutso 1:8
Kodi apa mawu akuti chiyani za Mulungu?
*Sankhani vesi m’baibulo limene tawerenga msabatayi limene
lakukhudzani kwambiri komanso liri ndi tanthauzo pa moyo wanu nthawi
ino. Ganizirani tanthauzo la choonadichi kwa inu ndipo muligwritse
ntchito pa moyo wanu.
Mulungu sawoneka mu thupi. Ife anthu timaganiza molakwikwa poyesa
kuti Mulungu amawoneka ndi maso komanso ali ndi malire pochita zinthu
monga ifeyo.
Ife sitinadzipezeketse tokha padziko lino, kapena kulenga mpweya,
chakudya ngakhalenso madzi zomwe zimafunikira kuti munthu akhale
ndi moyo. Komatu Mulungu alipo wathunthu mu Umulungu wake. Sakusowa
wina wake kapenanso china chirichonse kuti Iyeyo apezeke koma Iye
yekha mwa yekha.
Chiri chonse chomwe timachiwona mdziko lino chinalengedwa kapena
kukonzedwa koma Mulungu sanalengedwe kapenanso kukonzedwa. Mulungu
ndi wosiyana ndi chirichonse. Dzina lake ndi NDI INE. Aliko ndipo
analipo. Iyeyu ndi wa muyaya. Sadzakkhala ndi mathero.
Chimene chimatisiyanitsa ndi chakuti ife ndi ife anthu ndipo Mulungu
ndi Mulungu ndipo ali ndi Umulungu sawoneka ndi maso koma ifeyo
timawoneka ndi maso.
2. Kodi Yohane 4:24 imanena chiyani za Mulungu? ……
Mulungu wathu alibe malire
“Kodi Mulungu adzakhala ndithu padziko lapansi? Taonani,
thambo ndi m’Mwambamwamba zichepa kukulandirani, koposa zotani
nanga nyumba iyi ndayimangayi!”
1 Mafumu 8:27
“Kodi ukhoza kupeza Mulungu mwa kufunafuna?
Ukhoza kupeza Wamphamvu yonse motsindika?
Kumpeza kutalika ngati kumwamba, ungachitenji?
Kuzama ngati kumanda, ungadziwenji? Muyeso wake utalikira utali
wache wa dziko lapansi, Chitando chake chiposa Nyanja. “
Yobu 11:7-9
Mulungu ndi osamvetsetseka
“Mulungu agunda modabwitsa ndi mawu ake, Achita zazikulu
osazidziwa Ife”
Yobu 37:5
“Pakuti maganizo anga Sali maganizo anu, ngakhale njira zanu
siziri njira zanga, ati Yehova. Pakuti monga kumwamba kuli kutali
ndi dziko lapansi, momwemo njira zanga ziri zazitali, kupambana
njira zanu, ndi maganizo anga kupambana maganizo anu.”
Yesaya 55:8-9
3. Ukoma wa Umulungu ndi ubwino umene uli owona pofotokoza za
Mulungu. Mavesi ali munsiwa ali ndi ukoma wa umulungu. Werengani
ndi kulemba ukoma wa vesi ili yonse.
a. 1 Yohane 4:8 …
b. 2 Atesolonika 3:3 . . . .
c. Yakobo 1:17 . . . .
d. Yakobo 10:18 . . . .
e. Ahebri 1:8 . . .
f. Luka 1:78 . . . . .
g. 1 Petro 1:15-16 . . . . .
UKOMA WA MULUNGU
Mulungu ndiChikondi
Chikondi ndiukoma kapena kuti ubwino wa Mulungu koma sichitanthauza
Mulungu.
Mulungu ndiye amamasulira kuti chikondi ndi chiyani. Koma chikondi
sichinena kuti Mulungu ndi chiyani kapena kuti ndi ndani? Chikondi
chimangofotokoza momwe Mulungu aliri monganso m’mene ma ubwino
ena a Mulungu akufotokozera. Kukhulupirika, kukoma mtima, chifundo,
chilungamo komanso chiyero zimafotokozera ubwino ndi cholinga chimene
Mulungu amapezekera. Amakhala mu zonsezi nthawi ili yonse. Chikondi
cha Mulungu ndi choyera nthawi zonse, ndi chabwino nthawi zonse,
ndi chokhulupilika nthawi zonse, ndi chachifundo komanso ndi choonadi.
Mulungu ndi okhulupirika
Titha kudalira Mulungu chifukwa Iye ndi okhulupilika. Amasunga
malonjezano ake. Titha kukhala mchiyembekezo mtsogolo chifukwa kukhulipilika
kwa Mulungu sikulephera.
Mulungu sasintha
Umodzi mwa ubwino wa Mulungu umene sitidautchule ndi wakuti Iyeyu
sasitha. Tikudziwa bwino lomwe kuti Mulungu sangakhale osakhulupilika
chifukwa zikatero akuyeneranso kusintha. Mulungu ndi wolungama komanso
sangalephere. Werengani Malaki 3:6
Mulungu ndi wabwino
Ubwino wa Umulungu ndi osiyana ndi ubwino wa umunthu. Izi ziri
chomwechi chifukwa Mulungu ali olondola muzake zones komanso nthawi
ili yonse. Yesu anati: - Ndi Mulungu yekha amene ali wabwino? Werengani
Masalimo 107 vesi 1
Mulungu ndi Wachilungamo
Mulungu akamapanga chilungamo, samapanga mofuna kulingana ndi chilungamo
cha munthu. Iye amapanga zimene iye amadziwa. Mulungu ndi Mulungu
ndipo adzakhala Mulungu ndipo sangakhalenso chiri chonse. Iye ndi
Mulungu basi. Ndi wa chilungamo. Werengani Deutoronomo 32 Vesi 4
Mulungu ndi wachifundo
Chifundo ndiubwino wa Mulungu. Amakhudzidwa, ndiwachifundo nthawi
zonse komanso ndi wachilungamo. Ngakhale pamene akuweruza amachita
chifundo. Amamchitira munthu chifundo mosatopa. Chifundo cha Umulungu
sichalero kapena mawa lokha koma ndi ubwino wa Mulungu wa muyaya.
Mulungu ndi wachifundo kuyambira kale ndipo ndichopitilira mpaka
muyaya.
Werengani 2 Akorinto 1:3
Mulungu ndi Woyera
Kuyera kwa Umulungu ndi kwachikhalire. Ndi kwapadera, kosafikilika,
kosapezeka komanso kovuta kukumvetsa. Mulungu ndi opanda banga ndi
umoyo wake ndi wangwiro. Ubwino wa Umulungu wa chiyero ndi wapaderadera
kwa Mulungu.
4a. Kodi Mulungu amayembekezera chiyani kuchokera kwa aKhristu?
1 Petro 1:13-16
b. Malinga ndi 1 Akorinto 1:30, Kodi tingakhale
bwanji woyera? . . . . .
Atero Yehova wanzeru “Asadzitamandire m’nzeru zache,
wamphamvu asadzitamandire m’mphamvu yache,
wa chuma asadzitamandire m’chuma chache;
Koma wakudzatamandira adzitamandire adzikweze umo,
kuti ali wakuzindikira, ndi kundidziwa Ine, kuti ndine Yehova wochita
zokoma mtima, chiweruziro, ndi chilungamo m’dziko lapansi,
pakuti m’menemo ndikondwera, atero Yehova.”
Yeremiya 9:23-24
Ubwino utatu wapaderadera
Mulungu ndi wamphamvu zonse. Analenga dziko ndi zonse zam’dzikoli
ndi mawu. Amaliramulira. Ali ndi mphamvu yochita zozizwa. Choncho
titha kunena kuti Mulungu ndi wamphamvu zonse.
Mulungu amadziwa chirichonse. Palibe chimene sadziwa. Mphamvu za
Mulungu ndi nzeru zake ndi zophatikizana ndipo palibe angazipatule.
Choncho timamutcha Mulungu wa nzeru zonse.
Mulungu amapezeka paliponse nthawi imodzi. Choncho timamutcha Mulungu
opezeka paliponse.
5. Werengani mavesi otsatirawa ndipo mulembe ma ubwino atatu apaderaderawa
malinga ndi vesi ili yonse momwe iliri – Mulungu ndi Wamphamvu
yonse, Opezeka pali ponse ndiponso Wanzeru zakuya.
“. . . Ine ndiri pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro
cha nthawi ya pansi pano.”
Mateyu 28:20
“. . . Ine ndine Mulungu Wamphayonse . . . Kodi chiripo chinthu
chomulaka Yehova?”
Genesesi. 17:1; 18:14
“Ndipo palibe cholengedwa chosawonekera pamaso pache, koma
zonse zikhala za pambalambanda ndi zovundukuka pamaso pache pa Iye
amene tichita naye.”
Ahebri 4:13
Pemphero
Mulungu wa mphamvu zonse, Zikomo chifukwa cha zonse zimene ndaphunzira
zokhudza inu. Zikomo chifukwa mukupezeka pali ponse, chifukwa ndi
Inu wamphamvu zonse, ndipo mumadziwa chirichonse. Ndi Inu Mulungu
odabwitsa. Ndiine okondwa kuti mumakonda ndi kumvetsetsa anthu omwe
munawalenga. Ndikukuwezani chifukwa cha chakutidalitsa. Mudzina
la Yesu Khristu, amen
|